NOVEMBER 17-23
NYIMBO YA SOLOMO 6-8
Nyimbo Na. 34 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muzikhala Khoma, Osati Chitseko
(10 min.)
Azichimwene ake a Msulami ankafuna kuti iye asagonane ndi mwamuna aliyense asanalowe m’banja (Nym 8:8, 9; it “Nyimbo ya Solomo” ¶11)
Iye anapeza mtendere chifukwa anayesetsa kupeweratu makhalidwe oipa (Nym 8:10; yp 188 ¶2)
Iye ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa achinyamata pa nkhani imeneyi (yp2 33)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndingathandize bwanji Akhristu omwe sali pabanja mumpingo wathu kuti akhale khoma osati chitseko?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Nym 8:6—N’chifukwa chiyani chikondi chenicheni chimatchulidwanso kuti “lawi la Ya”? (w15 1/15 29 ¶3)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Nym 7:1-13 (th phunziro 12)
4. Ulendo Woyamba
(2 min.)KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gwiritsani ntchito khadi lodziwitsa anthu za jw.org kuti muyambe kukambirana ndi munthu. (lmd phunziro 4 mfundo 4)
5. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Gwiritsani ntchito kapepala kuti muyambe kukambirana ndi munthu kumaofesi kapena malo ena ogwirira ntchito. (lmd phunziro 1 mfundo 4)
6. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Yambani kucheza ndi munthu, koma machezawo athe musanamulalikire. (lmd phunziro 2 mfundo 4)
7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
(5 min.) Chitsanzo. ijwfq nkhani Na. 43—Mutu: Kodi a Mboni za Yehova Amatsatira Mfundo Ziti Zokhudza Kukhala pa Chibwenzi? (th phunziro 7)
Nyimbo Na. 121
8. Thawani Chiwerewere
(15 min.) Nkhani yokambirana.
M’buku la Nyimbo ya Solomo, m’busa anaitana Msulami kuti akayende naye ngati njira yosonyezerana chikondi. (Nym 2:10-14) Ngakhale kuti m’busayo analibe zolinga zoipa, azichimwene ake a Msulami, mwanzeru, anamupatsa ntchito zoti agwire n’cholinga choti asapite kokayendako. (Nym 2:15) Azichimwene akewo ankadziwa kuti anthu amene amakondana akakhala awiriwiri, akhoza kuyesedwa kuti achite tchimo.
Baibulo limauza Akhristu kuti ‘athawe chiwerewere.’ (1Ak 6:18) Tiyenera kupewa chilichonse chomwe chingatichititse kuti tichite tchimo. Amene analemba buku la Nyimbo ya Solomo, anauziridwanso kulemba kuti: “Munthu wochenjera akaona tsoka amabisala, koma wosadziwa zinthu amangopitabe ndipo amakumana ndi mavuto.”—Miy 22:3.
Onerani VIDIYO yakuti Mulungu “Amadziwa Zinsinsi za Mumtima.” Kenako funsani funso ili:
Kodi mwaphunzira chiyani muvidiyoyi?
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 36-37