Mawu Oyamba
Kodi mumafunitsitsa mutakhala m’dziko lopanda nkhondo komanso zachiwawa? Anthu ambiri amakhulupirira kuti zimenezi n’zosatheka. Baibulo limanena chifukwa chake ndi zosatheka kuti anthu athetse nkhondo. Limafotokozanso chifukwa chake muyenera kukhulupirira kuti posachedwapa padziko lonse padzakhala mtendere.
M’magaziniyi, mawu akuti “nkhondo” ndi “zachiwawa” akuimira mikangano ya pakati pa mayiko komanso magulu andale amene amagwiritsira ntchito zida zankhondo pomenyana. Mayina a anthu ena amene atchulidwa m’magaziniyi asinthidwa.