Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 May tsamba 20-25
  • Dzina la Yehova Ndi Lofunika Kwambiri kwa Yesu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dzina la Yehova Ndi Lofunika Kwambiri kwa Yesu
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “NDACHITITSA KUTI IWO ADZIWE DZINA LANU”
  • “DZINA LANU LIMENE MWANDIPATSA”
  • “ATATE LEMEKEZANI DZINA LANU”
  • “NDIKUPEREKA MOYO WANGA”
  • “NDAMALIZA KUGWIRA NTCHITO IMENE MUNANDIPATSA”
  • Dzina la Yehova Ndi Lofunika Kwambiri kwa Ife
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • “Tamandani Dzina la Yehova”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Dipo Limatiphunzitsa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • “Sankhani . . . Amene Mukufuna Kum’tumikira”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 May tsamba 20-25

NKHANI YOPHUNZIRA 22

NYIMBO NA. 15 Tamandani Mwana Woyamba Kubadwa wa Yehova

Dzina la Yehova Ndi Lofunika Kwambiri kwa Yesu

“Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo.”—YOH. 17:26.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi, tiona mmene Yesu anathandizira anthu kudziwa dzina la Yehova komanso mmene anayeretsera dzinali.

1-2. (a) Kodi Yesu anachita chiyani atatsala pang’ono kuphedwa? (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

LINALI Lachinayi madzulo pa Nisani 14, mu 33 C.E., ndipo Yesu anali atatsala pang’ono kuperekedwa, kuweruzidwa, kuchitiridwa nkhanza komanso kuphedwa. Iye anali atangomaliza kumene kudya chakudya chapadera ndi ophunzira ake okhulupirika m’chipinda cha m’mwamba. Atangomaliza chakudyacho, Yesu anauza ophunzirawo mawu omaliza owalimbikitsa. Iwo asanatuluke m’chipindacho, Yesu anaima kaye ndipo anapemphera nawo pemphero lofunika kwambiri. Mtumwi Yohane analemba pempheroli ndipo timalipeza mu Yohane chaputala 17.

2 Kodi pemphero la Yesuli limasonyeza kuti iye ankadera nkhawa kwambiri za chiyani? Kodi limasonyeza kuti n’chiyani chomwe chinali chofunika kwambiri kwa iye pa nthawi yonse ya utumiki wake? Tiyeni tikambirane mayankho a mafunso amenewa.

“NDACHITITSA KUTI IWO ADZIWE DZINA LANU”

3. Kodi Yesu ananena chiyani zokhudza dzina la Yehova, nanga ankatanthauza chiyani? (Yohane 17:​6, 26)

3 M’pemphero lake, Yesu ananena kuti: “Ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu.” Ndipotu kawiri konse, iye ananena kuti anadziwikitsa dzinalo kwa ophunzira ake. (Werengani Yohane 17:​6, 26.) Kodi Yesu ankatanthauza chiyani? Kodi ankatanthauza kuti anawadziwitsa dzina limene iwo sankalidziwa? Ophunzira akewo anali Ayuda, choncho iwo ankadziwa kale kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Dzinali linkapezeka maulendo ambirimbiri m’Malemba a Chiheberi. Choncho Yesu sankatanthauza kuwadziwitsa dzina la Mulungu, m’malomwake ankanena za zimene dzinalo linkaimira. Yesu anathandiza ophunzira akewo kudziwa bwino Yehova, zolinga zake, zochita zake komanso makhalidwe ake. Ndipotu anachita zimenezi chifukwa iye yekha ndi amene amadziwa bwino Yehova.

4-5. (a) Kodi kudziwa dzina la munthu kumatanthauza chiyani? Perekani chitsanzo. (b) Kodi ophunzira a Yesu anadziwa dzina la Yehova m’njira iti?

4 Tiyerekeze kuti mumpingo mwanu muli mkulu dzina lake David ndipo ndi dokotala. Mwakhala mukumudziwa m’baleyo kwa zaka zambiri. Koma tsiku lina mwadwala kwambiri ndipo akutengerani kuchipatala komwe m’baleyo amagwirako ntchito. David akugwiritsa ntchito luso lake kuti apulumutse moyo wanu. Kuchokera tsiku limenelo, n’chiyani chizibwera m’maganizo mwanu mukamva dzina la m’baleyo. Muziganizira kuti, sikuti wangokhala chabe m’bale amene mukumudziwa, koma ndi dokotala amene anapulumutsa moyo wanu.

5 Mofanana ndi zimenezi, ophunzira a Yesu ankadziwa kale dzina la Yehova. Koma dzinali linakhala lofunika kwambiri kwa iwo chifukwa kudzera mwa Yesu, anafika podziwa bwino Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa zimene Yesu ankalankhula komanso kuchita zinasonyeza bwino makhalidwe a Atate wake. Choncho ophunzirawo ‘anadziwa’ bwino Yehova pomvetsera zimene Yesu ankaphunzitsa komanso poona mmene ankachitira zinthu ndi anthu.—Yoh. 14:9; 17:3.

“DZINA LANU LIMENE MWANDIPATSA”

6. Kodi Yehova anapereka dzina lake kwa Yesu m’njira yotani? (Yohane 17:​11, 12)

6 Yesu anapempherera ophunzira ake kuti: “Ayangʼanireni chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa.” (Werengani Yohane 17:​11, 12.) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tsopano Yesu amayenera kudziwika ndi dzina lakuti Yehova? Ayi. Onani kuti m’pempheroli Yesu anatchula dzina la Yehova kuti “dzina lanu.” Choncho Yesu sanatenge dzina la Yehova kukhala dzina lake. Ndiye kodi Yesu ankatanthauza chiyani pomwe ananena kuti Mulungu wamupatsa dzina lake? Choyamba, kumbukirani kuti Yesu ankaimira Yehova komanso kulankhula m’malo mwake. Iye anabwera m’dzina la Atate wake ndipo anachita zinthu zambiri zamphamvu m’dzina limeneli. (Yoh. 5:43; 10:25) Kuwonjezera pamenepo, dzina lakuti Yesu limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Chipulumutso.” Choncho dzina la Mulungu ndi logwirizana kwambiri ndi dzina la Yesu.

7. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yesu ankalankhula m’dzina la Yehova.

7 Tingayerekezere zimenezi ndi kazembe wa dziko. Iye amaimira mtsogoleri wa dziko. Zimene angalankhule kazembeyo zimakhala ndi mphamvu yofanana ndi zimene angalankhule mtsogoleri wake. Mofanana ndi zimenezi, Yesu ankaimira Yehova ndipo ankalankhula ndi anthu m’dzina la Yehovayo.—Mat. 21:9; Luka 13:35.

8. Kodi dzina la Yehova linali “mwa” Yesu m’njira yotani asanabwere padziko lapansi? (Ekisodo 23:​20, 21)

8 Pa udindo wake monga Mawu, Yesu wakhala akutumikira Yehova monga womulankhulira popereka mauthenga komanso malangizo kwa angelo ndi anthu. (Yoh. 1:​1-3) Yesu ayenera kuti ndi mngelo amene Yehova anamutumiza kuti akasamalire Aisiraeli pa ulendo wawo pamene anali m’chipululu. Pouza Aisiraeli kuti azimvera mngeloyo, Yehova anati: “Popeza dzina langa lili mwa iye.”a (Werengani Ekisodo 23:​20, 21.) Dzina la Yehova linali “mwa” Yesu chifukwa iye ankaimira Yehova komanso ndi amene ankalemekeza kwambiri ndi kuyeretsa dzina la Atate wake.

“ATATE LEMEKEZANI DZINA LANU”

9. Kodi dzina la Yehova linali lofunika bwanji kwa Yesu? Fotokozani.

9 Monga mmene taonera, dzina la Yehova linali lofunika kwambiri kwa Yesu ngakhale pamene anali asanabwere pano padziko lapansi. N’chifukwa chake ali padzikoli, zonse zimene Yesu ankachita zinkasonyeza kuti amaona kuti dzinali ndi lofunika kwambiri. Chakumapeto kwa utumiki wake, Yesu anapemphera kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” Nthawi yomweyo, Atate wake anayankha ndi mawu amphamvu kuchokera kumwamba kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”—Yoh. 12:28.

10-11. (a) Kodi Yesu analemekeza bwanji dzina la Yehova? (Onaninso chithunzi.) (b) N’chifukwa chiyani dzina la Yehova liyenera kuyeretsedwa?

10 Nayenso Yesu analemekeza dzina la Atate wake. Kodi anachita bwanji zimenezi? Njira imodzi inali kuuza ena zokhudza makhalidwe ndi zochita za a Atate wake. Koma iye anachitanso zambiri polemekeza dzinali. Dzina la Yehova komanso mbiri yake zinkayenera kuyeretsedwa. Yesu anasonyeza kufunika kochita zimenezi pamene anaphunzitsa ophunzira kuti azipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.”—Mat. 6:9.

11 N’chifukwa chiyani dzina la Yehova linkafunika kuyeretsedwa? Chifukwa m’munda wa Edeni, Satana Mdyerekezi ananyoza komanso kunena mabodza okhudza Yehova Mulungu. Iye ananena kuti Yehova ndi wabodza komanso ankamana Adamu ndi Hava zinthu zabwino. (Gen. 3:​1-5) Ponena zimenezi, Satana anasonyezanso kuti Yehova sachita zinthu m’njira yoyenera. Mabodza a Satanawa anaipitsa mbiri ya Yehova, kapena kuti dzina lake. Kenako m’nthawi ya Yobu, Satana ananena kuti anthu amatumikira Yehova chifukwa cha zinthu zabwino zimene wawachitira. Mngelo wabodzayu ananenanso kuti palibe munthu amene amakonda Yehova moti akhoza kumamutumikirabe atakumana ndi mavuto. (Yobu 1:​9-11; 2:4) Choncho pankafunika nthawi yokwanira kuti zidziwike kuti wabodza ndi ndani pakati pa Yehova ndi Satana.

Yesu akuphunzitsa gulu la anthu pa ulaliki wa phiri.

Yesu anaphunzitsa otsatira ake kufunika koyeretsa dzina la Mulungu (Onani ndime 10)


“NDIKUPEREKA MOYO WANGA”

12. Kodi Yesu anali wofunitsitsa kuchita chiyani chifukwa chokonda dzina la Yehova?

12 Popeza kuti ankakonda Yehova, Yesu ankafunitsitsa kuchita zonse zomwe akanatha kuti ayeretse dzina la Atate wake. Iye anati: “Ndikupereka moyo wanga.” (Yoh. 10:​17, 18) Izi zikusonyeza kuti iye anali wokonzeka kufera dzina la Yehova.b Adamu ndi Hava, omwe anali angwiro, sanamvere Yehova ndipo anasankha kukhala kumbali ya Satana. Mosiyana ndi anthu awiriwa, Yesu anali wofunitsitsa kubwera padziko lapansi kudzasonyeza kuti amakonda Yehova. Iye anachita zimenezi pomvera Yehova pa zinthu zonse. (Aheb. 4:15; 5:​7-10) Iye anakhalabe wokhulupirika mpaka pamene anafa imfa yopweteka kwambiri pamtengo wozunzikirapo. (Aheb. 12:2) Izi zinasonyeza kuti iye ankakonda Yehova komanso dzina la Atate wake.

13. N’chifukwa chiyani Yesu anali woyenera kusonyeza kuti Satana ndi wabodza? (Onaninso chithunzi.)

13 Pa zonse zimene ankachita, Yesu anasonyeza kuti wabodza ndi Satana, osati Yehova. (Yoh. 8:44) Yesu ankamudziwa bwino Yehova kuposa munthu aliyense. Zikanakhala kuti zimene Satana ankamuneneza Yehova zinali zoona, Yesu akanadziwa zimenezo. Koma Yesu anatsimikiza kuti ayeretsa dzina la Yehova komanso mbiri yake chifukwa ankadziwa kuti zimene Satana ananena zinali zabodza. Ngakhale pamene zinkaoneka ngati Yehova wamusiya, Yesu anali wofunitsitsa kufa ali wokhulupirika m’malo mosiya kumvera Atate wake.—Mat. 27:46.c

Yesu ali pamtengo wozunzikirapo.

Zimene Yesu ankachita zinasonyeza bwino kuti wabodza ndi Satana, osati Yehova (Onani ndime 13)


“NDAMALIZA KUGWIRA NTCHITO IMENE MUNANDIPATSA”

14. Kodi Yehova anadalitsa bwanji Yesu chifukwa chokhalabe wokhulupirika?

14 M’pemphero limene anapereka pa tsiku limene anali atatsala pang’ono kufa, Yesu ananena kuti: “Ndamaliza kugwira ntchito imene munandipatsa.” Iye ankakhulupirira kuti Yehova amupatsa mphoto chifukwa chokhalabe wokhulupirika. (Yoh. 17:​4, 5) Ndipo Atate wake sanamugwiritse mwala. Yehova sanalole kuti iye akhalebe m’manda. (Mac. 2:​23, 24) Anamuukitsa ndipo anamupatsa udindo waukulu kumwamba. (Afil. 2:​8, 9) Pamapeto pake, Yesu anayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Kodi Ufumu umenewu udzachita chiyani? M’mbali yachiwiri ya pemphero lachitsanzo, Yesu anati: “Ufumu wanu ubwere. Zofuna zanu zichitike padziko lapansi pano ngati mmene zilili kumwamba.”—Mat. 6:10.

15. Kodi Yesu adzachitanso zinthu ziti?

15 Posachedwapa Yesu adzamenya nkhondo yolimbana ndi adani a Mulungu komanso kuwononga onse oipa pankhondo ya Aramagedo. (Chiv. 16:​14, 16; 19:​11-16) Pambuyo pake adzaponyera Satana ‘kuphompho’ komwe sadzatha kuchita chilichonse. (Chiv. 20:​1-3) Ndiyeno Yesu adzabwezeretsa mtendere komanso kuthandiza anthu kuti akhalenso angwiro mu Ulamuliro wa Zaka 1,000. Iye adzaukitsa akufa komanso kukonza dzikoli kuti likhalenso Paradaiso. Apa cholinga cha Yehova chidzakhala chitakwaniritsidwa.—Chiv. 21:​1-4.

16. Kodi moyo udzakhala wotani pofika kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000?

16 Kodi zinthu zidzakhala bwanji pofika kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000? Uchimo udzakhala utatheratu. Anthu sadzafunikiranso kupempha kuti akhululukidwe kudzera mu nsembe ya dipo. Sadzafunikiranso mkhalapakati kapena wansembe. ‘Imfa nayonso [yobwera chifukwa cha Adamu], yomwe ndi mdani womaliza, idzakhala itawonongedwa.’ Pa nthawiyo akufa adzakhala ataukitsidwa ndipo anthu onse padzikoli adzakhala angwiro.—1 Akor. 15:​25, 26.

17-18. (a) Kodi chidzachitike n’chiyani kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000? (b) Kodi Yesu adzachita chiyani nthawi yake yolamulira ikadzatha? (1 Akorinto15:​24, 28) (Onaninso chithunzi.)

17 N’chiyaninso chomwe chidzachitike kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000? Pa nthawiyo padzachitika chinthu china chapadera kwambiri. Nkhani yokhudza kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova idzakhala itatha. N’chifukwa chiyani tikutero? M’munda wa Edeni, Satana ananena kuti Yehova ndi wabodza ndipo salamulira anthu mwachikondi. Kuchokera nthawi imeneyo, anthu amene amamukonda komanso kumulemekeza akhala akuyeretsa dzina lake. Choncho kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000, mbiri ya Yehova idzakhala itayeretsedwa. Iye adzakhala atasonyeza kuti ndi Atate wachikondi.

18 Pamapeto pake, zonse zimene Satana amanena zokhudza Yehova zidzadziwika kuti ndi zabodza. Ndiye kodi Yesu adzachita chiyani nthawi yake yolamulira ikadzatha? Iye sadzaukira ulamuliro wa Yehova ngati mmene Satana anachitira. (Werengani 1 Akorinto 15:​24, 28.) Yesu adzabwezera Ufumu kwa Atate wake. Iye adzagonjera ulamuliro wa Yehova. Mosiyana ndi Satana, Yesu ndi wokonzeka kuchita zimenezi chifukwa amakonda kwambiri Yehova.

Yesu ali kumwamba ndipo akubwezera Ufumu kwa Yehova.

Pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu akubwezera Ufumu kwa Yehova (Onani ndime 18)


19. Kodi dzina la Yehova ndi lofunika bwanji kwa Yesu?

19 M’pake kuti Yehova anali wofunitsitsa kupereka dzina lake kwa Yesu. Yesu anasonyeza bwino kwambiri mmene Atate wake alili. Ndiye kodi dzina la Yehova ndi lofunika bwanji kwa Yesu? Ndi lofunika kwambiri kuposa china chilichonse. Iye anali wofunitsitsa kufa chifukwa cha dzinali ndipo ndi wokonzeka kudzabwezera chilichonse kwa Yehova pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000. Ndiye kodi tingamutsanzire bwanji Yesu? Tidzakambirana yankho la funso limeneli munkhani yotsatira.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Yesu anathandiza bwanji ophunzira ake kudziwa dzina la Yehova?

  • Kodi Yesu anapatsidwa dzina la Yehova m’njira iti?

  • Kodi Yesu anali wokonzeka kuchita chiyani chifukwa cha dzina la Yehova, nanga n’chifukwa chiyani?

NYIMBO NA. 16 Tamandani Yehova Chifukwa cha Mwana Wake Wodzozedwa

a Nthawi zinanso angelo ankaimira Yehova akamapereka mauthenga m’dzina lake. N’chifukwa chake m’malo ena m’Baibulo, mngelo amatchulidwa ngati kuti ndi Yehova mwiniwakeyo. (Gen. 18:​1-33) Malemba amanena kuti Mose analandira Chilamulo kuchokera kwa Yehova. Koma mavesi ena amasonyeza kuti Yehova anagwiritsa ntchito angelo popereka Chilamulocho m’dzina lake.—Lev. 27:34; Mac. 7:​38, 53; Agal. 3:19; Aheb. 2:​2-4.

b Imfa ya Yesu inatsegulanso mwayi woti anthu adzapeze moyo wosatha.

c Onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya April 2021, tsamba 30-31.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena