Dziko Lapansi Chiyambire 1914
Gawo 2: 1929-1934 Kupsyinjika kwa Dziko Lapansi Ndipo ku Nkhondo Kachiŵirinso
“NGATI PANALI tsiku pamene mwaŵi unamwetulira United States ndi kale lonse panalidi pa tsiku limenelo.” Analongosola motero wodziwa za mbiri yakale David A. Shannon tsiku mu 1929 pa limene prezidenti Herbert Hoover analumbira udindo wake. Shannon akulongosola kuti: “Chinali chaka chamtendere, panalibe mitambo ya nkhondo pali ponse, ndipo chuma cha Amerika chinali kukula molimba m’maiko a kutsidya la nyanja ndi kusintha mikhalidwe mu mbali za dziko zopanda mwaŵi wa chuma.”
Koma pamapeto a uprezidenti wa Hoover, “mkhalidwe wonse wa dziko unabwerera m’mbuyo. M’malo mwa kuyembekezera zabwino panali kuyembekezera tsoka, kusowa chochita, mlingo waukulu wa kupanda chiyembekezo.” Kodi nchiyani chimene chinachitika?
‘Lachinayi Lamavuto’—Kutha kwa Nyengo
Pa Lachitatu, October 23, 1929, chiŵerengero ndithu cha ogulitsa popanda chifukwa chenicheni anayamba kugulitsa zinthu pa mtengo woposerapo pa nsika wa zinthu wa mu New York. Tsiku lotsatira, Lachinayi, ndi kudera nkhaŵa kwa kufuna kugulitsa pamene zinthu zawo zisanakhale zopanda mtengo kwambiri, eni zinthu anaika selu imene mu miyezi yochepera inapangitsa kupeza koposa pa madola 15 biliyoni mu mtengo wa zinthu ndiponso mkati mwa miyezi ingapo yotsatira mabiliyoni ambiri owonjezereka. Kunayamba motero kupsyinjika kwakukulu.
Odziwa za chuma ndi odziwa za mbiri yakale alidi ndi nthanthi zambiri ponena za chomwe chinalakwika. Koma, monga mmene m’modzi wa iwo analozera, chiri chodziŵika bwino lomwe kuti zochititsa kupsyinjika zambiri “zinali zozikidwa mwakuya mu kukhoza kwa m’zaka za makumi aŵiri.” Popeza kukhoza kwawo “kunamangidwa pa maziko osalimba . . . , kugwa kwa nsika wa zinthu . . . mwadzidzidzi kunavumbula kusowa mtengo kwa chuma kowabisalira [iwo].”—The United States in the Twentieth Century, masamba 10, 12.
Pa mlingo uliwonse, zaka za kupambana za Kubangula kwa m’Makumi Aŵiri zinali zitapita. Zomwe zinapitanso zinali ziyembekezo za kupambana zomwe izi zinabweretsa. “Kugwa kwakukulu kwa nsika wa zinthu kwa mu 1929 kunagwetsa magwero,” watero wodziŵa za mbiri yakale F. Freidel ndi N. Pollack. “Pamene zambiri zinabwerera m’mbuyo, zikusiya mamiliyoni akuvutika ndi kusungulumwa, zaka za m’makumi aŵiri zinawoneka kukhala osati china koma kudukiza kosatsimikizirika kapena masewera a nkhalwe—nyengo ya jazi ya makhalidwe oipa, nyengo ya kukonda zinthu za kuthupi.”—American Issues in the Twentieth Century, tsamba 115.
Mwadzidzidzi mamiliyoni anali opanda ntchito. Anthu omwe anali ndi ngongole anataya zinthu zomwe anagula pa ngongole, kuphatikizapo nyumba zawo. Mabanja anagwirizana kuti apulumutse zowonongedwa. Pamene mitengo ya zinthu inatsika kwakukulukulu, mwaŵi unatheratu modabwitsa. Mabizinesi anatsekedwa. Pfunde la kudzipha linazizwitsa dziko pamene zikwi za mabanki a mu U.S. anatseka zitseko zawo. Wolemba nkhani za masewero wina anapangitsa kuseka kwambiri pamene ananena kuti iye anazolowera kulandira macheki obwezedwa ndi banki kuti “kulibe ndalama.” Koma tsopano iye ankawalandira olembedwa “kulibe banki.”
Kugwa kwa chuma kunali m’chiyang’aniro cha dziko lonse ndi kofika kutali mu ziyambukiro zake. Mchenicheni, bukhu lakuti The United States and Its Place in World Affairs 1918-1943 linalongosola kuti “tsoka la chumali linakhudza dziko lirilonse ndi mbali iriyonse ya moyo, mayanjano ndi ndale zadziko, pamalopo ndi dziko lonse.”
Panthaŵiyo, mu Japan ankhondo anali kugwiritsiranso mkhalidwe wa chuma ku mwaŵi wawo. Yatero The New Encyclopædia Britannica kuti: “Lingaliro lakuti chitukuko kupyolera mkugonjetsa kwa magulu a nkhondo kukathetsa mavuto a chuma a Japan kunatenga ulamuliro pa ndalama mkati mwa Kupsyinjika Kwakukulu kwa mu 1929.” Kusakhazikika kwa koyambirira kwa ma-30 kunalola magulu ankhondo amenewa kutenga kulamulirako kotero kuti anali okhoza—ngakhale popanda chivomerezo cha boma la uchete—kulimbana ndi Manchuria ndi kuligonjetsa mu miyezi isanu yokha. Chodziŵika monga chankhanza ndi Chigwirizano cha Mitundu, Japan inayankha, osati mwakuchoka ku Manchuria, koma mwakuchoka mu Chigwirizano.
Ine Poyamba!
Mwakugogomezera pa zosangalatsa ndi kusonkhezera zinthu zakuthupi, zaka za m’Makumi Aŵiri Zobangula zinabweretsa mkhalidwe wa ine poyamba umene unathetsa zauzimu. Koma “chivomezi cha chuma chimene chinayamba mu 1929,” monga mmene bukhu lotchulidwa pamwambalo The United States and Its Place in World Affairs 1918-1943 limachitchulira, chinapangitsa tsopano mkhalidwewu ngakhale kumveketsedwa moposerapo. Tero motani? Chifukwa chakuti Kupsyinjika “kunachotsapo kuzindikira konse kwa zikondwerero za chitaganya zimene zinkakula, ndipo kunapangitsa banja limodzi ndi limodzi kukhala lolunjika m’kudzipulumutsa, mosasamala kanthu ndi zotulukapo zimene ichi chikadzetsa pa ena. M’modzi ndi m’modzi kaamba ka iyemwini, kupulumutsa matupi athu enieniwo, mosasamala kanthu za yemwe adzatenga chochepetsa!”
Mu anthu kudzikuza kotero, mkhalidwe wa kudzikonda, ndi wosalingalira unawonedwa mwachisawawa ndi kunyodola. Koma pansi pa kuphimbidwa kwa kudzikonda, mkhalidwe wolingana nawo kumbali ya magulu a ufuko kaŵirikaŵiri unakometseredwa, panthaŵi zina ngakhale kukhumbidwa. Kupsyinjika Kwakukulu kunasonkhezera mzimu woterowo.
Wodziŵa za mbiri yakale Hermann Graml akutero kuti “vuto la chuma cha dziko linatsanulira nkhonya ya kufa nayo pa kumvana kwa mitundu yonse ndi kugwirizana kowonekera mu Chigwirizano cha Mitundu,” ndi kuti ichi chinatsegula njira kaamba ka “kukula koipa kwa kudzikuza kumbali ya mtundu umodzi ndi umodzi.” Iye akutero kuti “mitundu yambiri inachititsidwa kusaganizira—koma komveketsedwa—kusalingalira ena kozikidwa pa kudzipulumutsa okha kumene kunapangitsa khamu kuthedwa nzeru.”—Europa zwischen den Kriegen (Europe Pakati pa Nkhondo), tsamba 237.
Mwinamwake palibe pamene mkhalidwewu unalongosoledwa mosalingalira kwambiri kuposa mu nkhani yoperekedwa ndi Heinrich Himmler wa Chinazi Germany zaka zingapo pambuyo pake. “Kuwona mtima, ubwino, kukhulupirika, ubwenzi,” iye anati, “zifunikira kusonyezedwa pochita ndi aja abanja limodzi, osati wina aliyense. Chimene chimachitika kwa mu Russia, kwa muCzech, sichimandikondweretsa ine m’pang’ono pomwe. . . . Ngakhale kuti mitundu imakhala yolemera kapena yosauka ndi njala ya kufa nayo monga ng’ombe chimene chimandikondweretsa ine chiri kokha kuti tiwafuna iwo kukhala monga akapolo ku mwambo wathu. . . . Ngakhale ngati akazi a Chirussia 10,000 agwa pansi kaamba ka kutopa pokumba dzenje la msampha wa akasinja chomwe chindikondweretsa ine chiri kokha kuti dzenje la Germany la msampha wa akasinja latha.”
Kwa ponse paŵiri anthu ndi mitundu kusonyeza mkhalidwe wa ine poyamba woterowo ndi kusasamala koteroko kwa malamulo a Mulungu akukonda “mnzako monga iwemwini,” kodi mtendere ukapezedwa mothekera motani kapena kusungiliridwa? (Luka 10:27) “Akukonda chilamulo chanu ali nawo mtendere wambiri,” likutero Baibulo pa Masalmo 119:165. Koma popeza kuti chikondichi chinasoweka, mitundu inaikidwa mosavuta m’malo kaamba ka nkhondo yatsopano. Mwapadera, ponse paŵiri kusoweka kwa chikondi ndi mkhalidwe wa ine poyamba zinazindikiritsa “masiku otsiriza” a dongosolo loipa la Satana.—2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:3, 12.
Kodi ndi Mwayani Momwe Munthu Afunikira Kukhulupirira?
Kodi mkhalidwe wa dziko womaipaipabe mwachiwonekere umapangitsa anthu kutembenukira kwa Mulungu yemwe anamuika kumbuyo mkati mwa Kubangula kwa M’zaka za m’Makumi Aŵiri? M’mbali zina, unatero. Anthu ambiri anayankha ku uthenga wolengezedwa ndi Mboni za Yehova, dzina lotengedwa mu 1931 ndi Akristu ogwirizana ndi Watch Tower Society. Koma mitundu chapamodzi sinayankhe, inaika chikhulupiriro chawo osati mwa Mulungu koma mwa anthu “omveka”.
Mwachitsanzo, pachiyambiyambi cha ma-1930 Mohandas Gandhi anapeza chichirikizo chowonjezereka mu India kaamba ka ndawala yake yamphamvu yopanda chiwawa ya kusamvera kwa aliyense. Ambiri anayembekeza kuti ufulu kuchokera ku ulamuliro wa Chibritish umene iye ankafuna ukatsogolera ku India wokhazikika ndi wamtendere. Kodi unatero?
Chaka chimodzimodzicho Prezidenti wa ku China Chiang Kai-shek anadzakhala chiwalo cha Chipembedzo cha Methodist. Ambiri anayembekeza kuti kutembenuka kwake ku Chikristu kukatsegula njira ya kugwirizana kwathithithi pakati pa China ndi maiko a Kumadzulo otchedwa mitundu ya Chikristu. Kodi kunatero?
Mu 1932, pa madyerero ochitikira ku Vatican, Mussolini anakondwerera chaka chake cha chikhumi mu ulamuliro. Ambiri anayembekeza kuti madalitso a upapa otsanuliridwa pajapo akatsimikiziritsa opembedza a Chitalian, wolamulira wawo, ndi chisungiko chosatha cha dziko lawo ndi kuchirikiza. Kodi zinatero?
Ndiponso mu 1932 Franklin D. Roosevelt, prezidenti wosankhidwa chatsopano wa United States, analonjeza anthu a m’dziko lake Kachitidwe Katsopano ka kupangitsa zinthu kugwiranso ntchito. Chaka chimodzi pambuyo pake iye anandandalitsa ziganizo za U.S. zakuleka kupanga zida za nkhondo ndipo anadandaulira kudziko kuti achotsepo zida zonse zopangitsa kuputana. Ambiri anayembekeza kuti Kachitidwe Katsopanoka kakatsogolera ku kutha kwa kusowa ntchito ndi kusauka ndiyeno kupeza mtendere. Kodi zinatero?
Mu 1933 Hitler anadzakhala mtsogoleri watsopano wa Germany. Mwamsanga pambuyo pake, mu kulankhula kwake kotchedwa Nkhani ya Mtendere, imodzi yogwira mtima yomwe sanaperekepo ndi kale lonse, iye anapeputsa nkhondo kukhala “kupenga kopitirizabe” komwe “kukapangitsa kugwa kwa mayanjano atsopano ndi kuyenera kwa ndale zadziko.” Iye anagogomezera kufunitsitsa kwa Germany kwa kuleka kupanga zida za nkhondo, m’chigwirizano ndi kufunsira kwa Roosevelt, akumati: “Germany ali wokonzekera kuvomera ku kuvomerezana kuli konse kwa lamulo kopanda nkhanza, chifukwa sakulingalira za kumenya nkhondo koma kokha kufuna chisungiko.” Ambiri anayembekeza kuti lamulo limeneli likabweretsa kuwona mtima ndi ulemu wa mtundu wa Chigermany ndipo mwanjira za mtendere kutsimikiza kulamulira kwamphamvu kwa mtsogoleri wawo kwa zaka chikwi. Kodi zinatero?
Ndipo mwakutero kunali gulu “lalikulu” lija, Chigwirizano cha Mitundu. Ponena za ilo magazini ya Nsanja ya Olonda ya May 15, 1932, m’Chingelezi, inati: “Mafumu a dziko lapansi, mwakuwunikiridwa ndi ansembe, . . . anagwirizana pamodzi mu Chigwirizano cha Mitundu ndi kukhulupirira mwa icho ndi mu luso la munthu la kupulumutsa dziko lothedwa nzeru ndi lovutika kuchoka ku kupanikizidwa kwake kulipoku.” Ambiri anayembekeza—ngakhale kuti Mboni za Yehova sizinali pakati pawo—kuti Chigwirizano ndithudi chikapulumutsa dziko kuchoka mu kupanikizidwa kwake. Kodi chinatero?
Kwa zaka zoposa zikwi ziŵiri zapitazo, wamasalmo analemba kuti: “Musadalire pa anthu omveka—okhoza kufa achabe omwe sangapatse chithandizo chirichonse.” Ndi kupindulira mu zomwe zachitika, kodi simungavomerezane ndi nzeru za mawuwa?—Masalmo 146:3, Moffatt.
Pakadapanda Kukhala Kupsyinjika . . .
“Chikadakhala kumasulira kopambanitsa ndi kopusa kuika thayo lonse la zochitika ndi zizolowezi za m’makumi atatu pa khomo la kupsyinjika.” Watero mkonzi wa bukhu The United States and Its Place in World Affairs 1918-1943. “Komabe,” amavomereza kuti, “kukhumba kofalikira ndi kupanda chisungiko kwa zaka zoperewera kunakonzekeretsa bwalo, kunapereka osewera ndi zoseweretsa zawo zamphamvu, kunawonjezera zochitika zazikulu ku zochitachita za tsoka, ndipo kunapatsa openyerera kulimba mtima kwatsopano kuti avomereze kapena kuphophonya kwatsopano kupangitsa kung’ung’udza.” Iwo anamaliza kuti pakadapanda kukhala kupsyinjika, chiri chothekera kwenikweni kuti sipakadakhala nkhondo ya dziko yachiŵiri.
Koma panalidi kupsyinjika kwa dziko lonse, ndipo panali nkhondo yachiŵiri ya dziko. Chotero ndithudi, mosasamala kanthu ndi kuchirikiza kwa achipembedzo, Chigwirizano cha Mitundu chinalephera kukwaniritsa mtendere womwe chinapangidwira kusungilira. Kungochokera pa chiyambi pake penipeni Chigwirizano chinaweruzidwa. Koma icho sichinafe mwamsanga. Icho chinadzandira pang’onopang’ono ku imfa yake. Ŵerengani ponena za icho m’kope lathu lotsatira.
[Bokosi patsamba 17]
Zinthu Zina Zomwe Zinapanga Mbiri
1929—Zopatsidwa mwalamulo ndi Academy of Motion Picture Arts and Sciences (Mphatso zopatsidwa chifukwa cha kupambana) zopatsidwa mu Hollywood kwa nthaŵi yoyamba
1930—Pulaneti ya Pluto ipezedwa
Wopambana woyamba wa ku Uruguay wa chikho cha mpikisano wa Mpira wa Dziko lonse
1931—Chigumula mu China chisiya akufa oposa 8,000 ndi 23 miliyoni opanda nyumba
Oposa 2,000 akufa mu chivomezi cha ku Nicaragua
Nyumba yosanjikana yaitali koposa mu dziko panthaŵi ija, New York’s Empire State Building, itsirizidwa
1932—Kupezedwa kwa neutron ndi deuterium (haidrojini yamphamvu) kuthandiza kupanga kwa zida za nyukiliya kukhalapo
1933—Kuchoka kwa Germany mu Chigwirizano cha Mitundu; Hitler alengezedwa mtsogoleri; ndende ya chibalo yoyamba, mu Dachau, itsegulidwa; kuvomerezana kwa upapa pakati pa Germany ndi Vatican kusainidwa; kutenthedwa kwapoyera kwa mabukhu osafunidwa mu Berlin
1934—FBI (Federal Bureau of Investigation) ilinganizidwa mu United States kuti ilimbane ndi uchifwamba
Red Army ya chiChinese ya asirikari okwanira 90,000 iyamba Ulendo Wake Wautali wopita ku Yenan
[Chithunzi patsamba 16]
Mu nthaŵi yochepa yokha, mamiliyoni anasiyidwa opanda ntchito
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
A. Rothstein/Dover