Mapemphero Kaamba ka Mtendere—Kodi Ndani Amamvetsera ku Iwo?
KODI nchiyani chimene munthu wa chiIndia wokhala ku America, wovala chovala ku mutu chodzazidwa ndi nthenga, anali kuchita pa pulatiformu imodzimodzi monga wansembe wa Greek Orthodox? Kodi nchifukwa ninji Dalai Lama wa chiBudha anakhala limodzi ndi Bishopo Wamkulu wa ku Canterbury? Kodi nchiyani chimene rabi wa chiYuda anali nacho chofanana ndi wokhala m’mzinda waukulu wa Tchalitchi cha Russia Orthodox? Ndipo nchifukwa ninji Papa John Paul II wa Tchalitchi cha Chikatolika ankayang’anira pa kusonkhana koteroko?
Osati kale kwenikweni chikanakhala chosalingalirika kwa papa kugawana pulatiformu ya pemphero ndi atsogoleri a zipembedzo zina zazikulu. Koma, kumapeto kwa 1986, m’mzinda wa chiItaly wa Assisi, iye anagwirizana ndi atsogoleri ena onsewo a zipembedzo mkuchita madyerero a “Tsiku Lamapemphero Kaamba ka Mtendere.” Kusonkhanaku kunapititsidwa patsogolo ndi papa m’chigwirizano ndi chosankha cha Mitundu Yogwirizana cha 1986 monga Chaka cha Mtendere wa Mitundu Yonse.
Ku Assisi, kunali mapemphero osiyanasiyana kaamba ka mtendere. Koma kodi ndani amene anamvetsera ku iwo? Mulungu wa Utatu wa Dziko la Chipembedzo? Kapena Mulungu wa Ayuda? Allah wa Asilamu? The Great Thumb and Roaring Thunder wa uchinyama? Kodi aliyense wa milungu imeneyi anamvetsera ku mapemphero amenewa? Tsopano pakuti nthaŵi yaitali yapitapo chiyambire chochitika cha pa Assisi, mayankho ali otsimikizirika.
Chimene Chinachitika
Mapemphero a atsogoleri a chipembedzo amenewo anali kufika pa chiindeinde kwa tsiku la mapemphero la mitundu yonse lochitidwa pa Assisi pakati pa Italy pa October 27. Pulatiformu yaikulu inamangidwa, yokhala ndi liwu lakuti “MTENDERE” m’zinenero 14 kumbuyo kwake. Ondandalitsidwa m’mzera waukulu wokhota pang’ono, kukhala ndi papa pakati, atsogoleri oposa 60 a zipembedzo zazikulu anatenga mbali m’kupemphera pa pulatiformu. Macamera a wailesi ya kanema anaphimba chochitikacho chomwe chikunenedwa kukhala chinawonedwa ndi anthu mamiliyoni 500 kuzungulira padziko lonse lapansi.
Oyambirira kupemphera anali a Budha, omwe anafunsa kaamba ka “nyanja ya chimwemwe ndi chisangalalo.” Kenaka a Hindu anapembedzera “mtendere pa zolengedwa zonse.” Asilamu anapemphera: “Ulemerero ukhale kwa Mulungu, Mbuye wa Chilengedwe.”
“Tipatseni ife mtendere,” linali pembedzero la okhulupirira mu zolengedwa a ku Africa pamene anapembedzera milungu yawo. “Tikupereka Kaliwo kwa Mzimu Waukulu, kwa Amayi wa Dziko Lapansi,” anatero anthu a ku India okhala ku America pame-ne anasuta kaliwo wa mtendere. “Perekani mtendere ku dziko lapansi,” anafunsa tero Ayuda.
“M’mtendere ndi umodzi tiloleni ife tipemphe Ambuye Mulungu wathu,” linali pemphero la oimira Akatolika, Anglican, Lutheran, ndi Greek Orthodox. A Sikhs, Zoroastrians, Shintoists, ndi Jains nawonso anapemphera kaamba ka mtendere wa chilengedwe chonse.
Chochitika Chopatsidwa Malo Apamwamba
Inali nthaŵi yoyamba, akuchitira ndemanga ofalitsa nkhani, kuti atsogoleri a chipembedzo apamwamba oterowo a zipembedzo zadziko anasonkhana pamodzi pa malo amodzi kupemphera. Kaamba ka chifukwa ichi msonkhanowo watchulidwa monga “chochitika cha m’mbiri.”
Ena amakhulupirira kuti ulosi wa Baibulo unakwaniritsidwa pamenepo. Popeza Assisi ali pa phiri, iwo amalingalira icho kukhala phiri lophiphiritsira la Mika mutu 4, versi 2. Ripotilo linanena kuti kusonkhana kwa pa Assisi kunali “msonkhano umene mneneri Mika anali ataneneratu zaka 2,700 zapita: ‘Pa [nthaŵi] ya mapeto phiri pamene kachisi wa Ambuye amaima lidzakhala lalitali koposa . . . Anthu onse adzasonkhana pa phazi lake ndipo adzanena kuti: Tiyeni tikwere ku phiri la Ambuye. Iye adzatiphunzitsa chimene tiyenera kuchita.’”—Voce delle Contrade.
Magazini ya Il Sabato motenthedwa maganizo inanena kuti: “Iri nthaŵi yoyamba kuti chirichonse cha mtundu wake chinachitika chiyambire pa Nsanja ya Babele. Kenaka, chifukwa cha chikhumbo chawo chakufika kumwamba, anthu anagawanikana. Lerolino, m’dzina la lingaliro la chipembedzo lomwe linatsegulira iwo ku mphatso ya Mulungu, mtendere, anthu ali ogwirizana.”
Mafunso Osamalitsa Adzutsidwa
Chochitikacho mosakaikira chinali chowonekera. Komabe, chinadzutsa mafunso mwa lamulo. Magazini ya tsiku ndi tsiku La Nazione inafunsa kuti: “Kodi uthenga umenewo unatumikira cholinga chake? Kodi iwo unafika m’mitima ya openyerera theka la biliyoni? Kodi iwo ungakhale unapanga ming’ankha m’malo amatanthwe a awo amene, mwachindunji kapena mosakhala mwachindunji, amafunitsitsa ndi kutsogoza zochitika ndi mwaŵi wa dziko?”
Anthu olingalira amafunsa mafunso ena opyoza: Kodi Mulungu amalandira mapemphero onse mosasamala kanthu za mtundu wa kulambira kochitidwa? Kodi chiri chokwanira kungopemphera kaamba ka chinachake popanda kutsimikizira za kawonedwe ka Mulungu pa nkhaniyo? Kodi anthu asonkhezeredwa ndi msonkhano umenewu kugwira ntchito kaamba ka mtendere? Kodi nchiyani chimene zakale zikutiphunzitsa ife? Ndipo pamwamba pa zonse, kodi nchiyani chimene Malemba amanena ponena za mmene mtendere wa dziko udzafikiritsidwira?
Tiyeneranso kufunsa kuti: Kodi kusonkhana kwa zipembedzo zadziko pa Assisi m’chenicheni kunali Nsanja ya Babele yamakono?