Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 12/8 tsamba 7-10
  • ‘Manja Anu Adzaza ndi Mwazi’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Manja Anu Adzaza ndi Mwazi’
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Atsogoleri ndi Anthu Adzamvetsera?
  • Osati Chisonkhezero cha Mtendere
  • Zipembedzo Zinakakumana ku Assisi Pofuna Mtendere
    Galamukani!—2002
  • Mapemphero Kaamba ka Mtendere—Kodi Ndani Amamvetsera ku Iwo?
    Galamukani!—1987
  • Kodi Zipembedzo za Dziko Zikupereka Chitsogozo Choyenera?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Nsanja ya Babele Yamakono?
    Galamukani!—1987
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 12/8 tsamba 7-10

‘Manja Anu Adzaza ndi Mwazi’

“POCHURUKITSA mapemphero anu sindidzamva; manja anu adzala mwazi.” Anatero Mulungu wamphamvuyonse kwa awo omwe anadzinenera kukhala akumtumikira iye koma amene anadzilowetsa m’kukhetsa mwazi wosachimwa.—Yesaya 1:15.

Kodi zipembedzo zadziko lino ziri ndi liwongo la kukhetsa mwazi wosachimwa? Inde, izo ndithudi ziri. M’nkhondo iriyonse ya m’zana lathu la 20, zipembedzo zadziko lino ndi atsogoleri awo a chipembedzo achirikiza kukhetsa mwazi. Ichi chatsogolera ngakhale ku ziwalo za chipembedzo chimodzimodzicho kuphana wina ndi mnzake paunyinji wokulira.

Komabe, Yesu anaphunzitsa otsatira ake ‘kubwezera lupanga lawo m’chimake.’ (Mateyu 26:52) Mtumwi Paulo ananena kuti: “Zida za nkhondo yathu siziri za thupi.” (2 Akorinto 10:4) Uthenga wamphamvu wa Mawu a Mulungu uli wakuti awo amene amapanga chipembedzo chowona ayenera kukondana wina ndi mnzake ndipo sayenera kukhetsa mwazi: “M’menemo awoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdyerekezi: Yense wosachita chilungamo siali wochokera kwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake; osati monga Kaini anali wochokera kwa woipayo, namupha mbale wake.”—1 Yohane 3:10-12.

Ngati chipembedzo sichisonyeza mtundu uwu wa chikondi, mapemphero ake sadzamvedwa ndi Mulungu. Baibulo limanena kuti: “Ndipo chimene chirichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.” (1 Yohane 3:22) Koma zipembedzo zadziko lino sizinasunge malamulo a Mulungu. M’malo mwake, izo mofooka zapitiriza kupha kwa ena a mamiliyoni zana a anthu mu nkhondo ya zana lino lokha!

Kodi Atsogoleri ndi Anthu Adzamvetsera?

M’mawu ake omaliza pa Assisi, John Paul II ananena kuti: “Tikuitana atsogoleri a dziko kuzindikira kupembedzera kwathu kodzichepetsa kwa Mulungu kaamba ka mtendere.” Kodi atsogoleri andale zadziko ndi anthu awo mwachisawawa adzamvetsera ku pempho limeneli? Kuti tipeze tiyeni tiyang’ane pa mbiri yakale.

Mbiri yakale imavumbula kuti mapangano ndi mapemphero kaamba ka mtendere siziri zinthu zatsopano. Mu Mibadwo Yapakati, mapangano kaamba ka mtendere kaŵirikaŵiri ankatchedwa mapangano a Mulungu kapena mapangano oyera. Iwo analalikidwa pa mapwando a chipembedzo a Dziko la Chipembedzo, mkati mwa amene kuyambana konse kunayenera kutha. Koma osati ngakhale chiwopsyezo cha kuchotsedwa mu tchalitchi kaamba ka awo omwe analakwira mapanganowo chinali chokwanira kupangitsa anthu kulemekeza iwo.

M’chaka cha 1915, Papa Benedict XV anapereka pempho kwa mitundu kuika kumapeto “kupha kochititsa mantha” kwa nkhondo ya dziko yoyamba. Iye anapemphera kwa Mulungu kaamba ka “kutha kwa mliri woipawo.” Koma osati ngakhale atsogoleri a utundu kapena anthu awo anakhoza kumvetsera. Ndipo, mwanzeru, Mulungu sanamvetsere chifukwa chakuti omenyana a mbali zonse ziŵiri anali ziwalo za chipembedzo chimodzimodzicho. Chotero, m’Katolika anapha m’Katolika, ndipo m’Protesitanti anapha m’Protesitanti, chosiyana kotheratu ndi malamulo a Mulungu.

Mu ngululu ya 1939, pamene mitambo ya mdima bii ya nkhondo ya dziko yachiŵiri inali kusonkhanitsidwa, Pius XII analinganiza “gulu la nkhondo lachikristu la mapemphero a poyera kaamba ka mtendere.” August wotsatira, kokha nkhondo isanawulike, iye anapereka pempho kwa atsogoleri a mitundu ndi anthu awo kuchoka ku “kupatsana liwongo, kuwopsyeza, ndi zochititsa za kusakhulupirirana” kotero kuti apewe zoipitsitsa.

Koma mapemphero onsewo ndi mapempho sanaletse makina a nkhondo a Germany wa Chikatolika ndi chiProtesitanti; ndiponso sanasonyeze njira yonkira ku mtendere kwa Italy wa Chikatolika kapena Japan wa chiShinto. Ndipo kuchotsedwa sikunawopsyezedwe kwa ziwalo za chipembedzo chirichonse chifukwa cha kupha ena a chipembedzo chimodzimodzicho. Chotero kupha kwa mbale ndi mbale kunapitirizabe kwa zaka zisanu ndi chimodzi, kochirikizidwa ndi mtsogoleri wa chipembedzo wa mtundu uliwonse.

M’kuvomereza ku pempho la papa ku Assisi, m’malo ena kumenyana kunaimitsidwa pa October 27, 1986. Koma m’maiko ena kunapitirizabe. Mu zochitika zambiri amenewa anali maiko a chipembedzo chomwe chinaimiridwa pa Assisi. Mwachitsanzo, omenya nkhondo ya chiweniweni a Chikatolika a IRA anamenya ndi mabomba pa Ireland. A Sikhs anamenya mu India. Mu Afghanistan, Ethiopia, Lebanon, Iran, ndi Iraq, limodzinso ndi magawo ena, kukhetsa mwazi kunapitirizanso. Ndipo ngakhale kumene panganolo linali kusungidwa kwa tsiku limodzi limenelo, imfa ndi chiwopsyezo zinabzalidwanso tsiku lotsatira lenilenilo. Mtendere wachilendo ndithudi!

Kodi “Mulungu wa mtendere” angadalitse zoyesayesa zoterozo zimene mosakhala mwachindunji zimavomereza awo amene lerolino akuleka kupha kokha kuti ayambenso m’mawa? Kodi Mulungu anavomereza Kaini pambuyo pa kupha Abeli? Ndithudi ayi!—Ahebri 13:20.

Osati Chisonkhezero cha Mtendere

Kufufuza kwaposachedwapa kochitidwa m’mitundu yosiyanasiyana kumasonyeza kuti chiŵerengero chokulira cha anthu amalingalira zipembedzo zadziko kukhala zosonkhezera za nkhondo m’malo mwa kukhala zopititsa patsogolo mtendere. Momwemo ndi mmene 47 peresenti ya anthu a chiFrench ndi 48 peresenti ya anthu a chiIsrayeli amadzimverera.

John Taylor, mlembi wamkulu wa Msonkhano wa Dziko Lonse wa Zipembedzo kaamba ka Mtendere, ananena mu magazini ya mwezi ndi mwezi ya chiFrench ya Chikatolika L’Actualité Religieuse dans le Monde: “Tinadzinyenga ife eni kulingalira kuti chipembedzo chingathe ndipo kuti chidzabweretsa kuwala ndi ufulu kukukanthana, ndipo kuti tidzapindula mokulira kuchokera ku mphamvu zogwirizanitsidwa motsutsana ndi nkhondo, motsutsana ndi zida za nkhondo. Koma pamene tinali kusanthula mavuto amenewa, mwapang’onopang’ono tinazindikira kuti nkhondo sizimachititsidwa ndi zida za nkhondo, koma ndi udani ndi kusagwirizana pakati pa anthu . . . Ndipo pano chipembedzonso chimachita mbali yake.”

Wodziŵa mbiri yakale Ernesto Galli Della Loggia, mu magazini ya tsiku ndi tsiku ya Chikatolika Avvenire, ananena ngakhale mwachindunji koposa kuti: “Chipembedzo sichikuwoneka kukhala chitamanga mbali zogwirizanitsa pakati pa amuna ndi pakati pa anthu, m’malo mwake chikuchita chosiyana kotheratu. Chakhala chiri tero kwa zaka mazana ambiri. Osati kokha kuti zipembedzo zazikulu koposa zokhulupirira mwa Mulungu mmodzi zinamenyana motsutsana wina ndi mnzake mu nkhondo yopanda chifundo koma ena a iwo—makamaka Akristu ndi Asilamu—apereka mphamvu zawo zonse ku kuthetsa zipembedzo zokhulupirira mu zinthu za chilengedwe zotchedwa anthu osaphunzira. Ichi chachitika chifukwa chakuti chipembedzo ndi mphamvu za ndale zadziko ziri mbali imodzimodzi ya ponda apa nane mpondepo.”

Kaamba ka ichi ndi zifukwa zina, maboma amanyalanyaza atsogoleri a chipembedzo kapena kulekerera iwo ngati iwo ali chovutitsa choyenerera. Ndipo chipembedzo cha dziko icho cheni chiri kokha khungu lokhala ndi chiyambukiro chochepa kapena lopanda phindu la chiyambukiro pa munthu kapena mikhalidwe ya dziko.

Pa mapeto a tsiku la mapemphero, papa iyemwini anavomereza thayo la Chikatolika mu kukhetsa mwazi konseko. Iye ananena kuti: “Ndiri wokonzekera kuvomereza kuti Akatolika nthaŵi zonse sanakhale okhulupirika ku chigwirizano cha chikhulupiriro.” Ndipo kenaka iye anawonjezera kuti: “Nthaŵi zonse sitinakhale ‘opanga mtendere.’ Kwa ife, chotero, koma mwinamwakenso, mwanzeru, kwa onse, chokumana nacho chimenechi pa Assisi chiri kachitidwe ka kulapa machimo.”

Koma kodi chipembedzo chamakono chasonyeza mwa kachitidwe kake kuti chinasintha kawonedwe kake kulinga ku nkhondo? Kodi icho mowonadi chalapa za mkhalidwe wake wochititsa manyazi wapitawo? Kulankhula ponena za nkhondo yamakono, Ernesto Galli Della Loggia ananena kuti: “Nthaŵi zisanu ndi zinayi pa nthaŵi khumi kusagwirizana kumeneku kulinso, ngati sipamwamba pa zonse, kusagwirizana kwa zipembedzo.”

Mapemphero kaamba ka mtendere chotero akhala opanda phindu. Ndiponso osatinso atsogoleri a chipembedzo kapena anthu akhala akumvetsera ku iwo ndi kuchita m’chigwirizano ndi iwo; ndipo osatinso Mulungu, popeza iye wanena kuti: “Pochulukitsa mapemphero anu, Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.” (Yesaya 1:15) Chimenecho ndicho chifukwa chake Chaka cha Mtendere wa Mitundu Yonse cha 1986 chosonkhezeredwa ndi Mitundu Yogwirizana ndi chochirikizidwa ndi mapemphero a zipembedzo zadziko lino chinali cholephera motero.

[Bokosi patsamba 10]

Kufufuza mu Italy

Magazini ya Galamukani! inachita kufufuza m’mizinda yosiyanasiyana ya mu Italy, mkati mwa kufufuza kumene mazana a anthu anafunsidwa, ochulukira a iwo Akatolika. Pamene anafunsidwa kuti kaya ngati zoyesayesa zonga zija za pa Assisi za tsiku la mapemphero kaamba ka mtendere ndi kuletsa nkhondo zidzathandiza kuthetsa nkhondo ndi zida za nkhondo, 70 peresenti inanena kuti ayi, 17 peresenti inanena kuti linali chabe sitepi loyamba, ndipo kokha 10 peresenti analingalira kuti chinali chinthu chothekera kuchichita.

Wansembe wochokera kumpoto kwa mzinda wa mu Italy wa Bergamo ananena kuti: “Ndikulingalira kuti kuyeserako kudzakhala kukugwira ntchito kokha ngati uthenga wake udzagwiritsiridwa ntchito. Chiri chiyambi chabwino chimene sichifunikira kupatulidwa.”

Koma mkazi wachichepere wa Chikatolika wochokera kugawo limodzimodzilo ananena kuti: “Wina sangathe kupewa kukhala wokanthidwa motheratu ndi kunyenga kwa anthu omwe akhala akumenyana kwa zaka zingapo, ndiponso kaamba ka zifukwa za chipembedzo, ndipo amene kenaka amaika pansi zida zawo ndi kupemphera kaamba ka mtendere wa dziko lonse, akudziŵa bwino lomwe kuti tsiku lotsatira adzapitiriza kumenyana.” Ndipo wachichepere wochokera ku Brescia ananena kuti: “Misonkhano yonga iyi siithandiza m’kuthetsa kusiyana kwa zipembedzo. Matchalitchi ayenera kukhala osangalatsidwa mocheperako mu ndale zadziko ngati akufuna Mulungu kumvetsera kwa iwo.”

M’kuyankha ku funso lakuti, “Kodi nchiyani chimene chipembedzo chiyenera kuchita kuti chigawireko mokhutiritsa ku mtendere?” M’Katolika wochokera ku Turin ananena kuti “ziyenera kudzilekanitsa izo zokha kuchoka ku kudzigwirizanitsa kwa kanthaŵi ku zinthu zoipa ndi kuphunzitsa anthu kukhala opanda zida.” Mkazi wachichepere wa Chikatolika wochokera ku Cremona ananena kuti: “Tchalitchi chikanakhazikitsa chitsanzo chabwino kumbuyoko mwa kusalowerera m’nkhondo ndi ndale zadziko. Koma tsopano kuli kuchedwa kwambiri.”

Atafunsidwa kuti, “Nchiyani chimene ukulingalira ponena za kuyesayesa kwa papa kwa mtendere?” loya wochokera ku dera la Pesaro anayankha kuti: “Tchalitchi chikugwiritsira ntchito vuto la mtendere ku ubwino wake kukupititsa patsogolo Chikatolika m’dziko.” Mkazi wa zaka 84 za kubadwa wa Chikatolika ananena kuti: “Chiri chosathandiza. Ngati iwo akufuna nkhondo, iwo adzayambitsa imodzi.”

Kulankhula ponena za “makonzedwe a ndale zadziko” a chipembedzo, chofalitsidwa cha ku Milan Il Corriere della Sera chinapanga ndemanga yowonekera iyi: “Tchalitchi chikutengera mwaŵi wa kubweretsa mtendere ndi kupititsa patsogolo zoyesayesa zomwe zikutheketsa kulamulira kwake m’malo mwakukhala wogonjera ku iko, kutsutsana kwalingaliro la poyera pa mafunso a akulu a ndale zadziko a panthaŵiyo.”

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Mapemphero anaperekedwa ndi anthu ochokera ku mbali zonse zadziko

Anthu ambiri achichepere ali osangalatsidwa mu mtendere wa dziko lonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena