Nsanja ya Babele Yamakono?
NSANJA ya Babele yakale inakhala chizindikiro cha kusokonezeka ndi kugawanikana. Panali pamenepo, chifupifupi zaka 4,000 zapita, pamene Mulungu anasokoneza chinenero cha anthu. Chifukwa ninji? Chifukwa cha kuukira kwawo motsutsana ndi iye. Iwo anakana kumvera Mulungu ndipo m’malo mwake anazika miyoyo yawo pa makonzedwe a anthu opanda ungwiro. Chotero Mulungu anawabalalitsa iwo.—Genesis 11:1-9.
Kodi chimene chinachitika pa Assisi chinali chosiyanako? Kodi anthu anagwirizanitsidwa moyenerera kumeneko? Kodi atsogoleri a chipembedzo a anthu oposa mabiliyoni aŵiri mowonadi anapititsa patsogolo mtendere wa dziko lonse?
Kodi Panali Umodzi?
M’nkhani yoperekedwa kokha masiku ochepa lisanafike tsikulo, papa anagogomezera kuti: “Chimene chidzachitika pa Assisi kwenikwenidi sichidzakhala kugwirizana [umodzi] kwa chipembedzo.” Iye anawonjezera kuti: “Sitingapempherere pamodzi, kunena kuti, kugwirizana pamodzi m’pemphero limodzi, koma tingakhalepo pamene ena akupemphera.”
Chotero papa anasonyeza kuti kaimidwe kowonedwa m’kupemphera kaamba ka mtendere kanali kaja kakubwera pamodzi kudzapemphera, osati kaja kakupempherera pamodzi. Ena anawona kuti iye anafuna kupewa kutenga mbali m’pemphero lofala. M’njira imeneyi iye sakadzudzulidwa ndi Akatolika chifukwa cha kusakaniza zikhulupiriro zosiyanasiyana za chipembedzo.
Ichi chikuwoneka m’mawu a malonje a papa kwa atsogoleri a chipembedzo m’mawa umenewo. Iye mogogomezera anachidziŵikitsa icho kuti: “Chenicheni chakuti tabwera pano sichitanthauza cholinga chirichonse cha kufuna kugwirizana kwa chipembedzo pakati pathu kapena kukambitsirana za chikhulupiriro chathu. Ndiponso sichikutanthauza kuti zipembedzo zingagwirizanitsidwe pa maziko ofanana a kudzipereka mu ntchito ya padziko lapansi yomwe idzapitirira zonse za izo.”
Chotero, ndithudi, sipangakhale kuyesayesa kwa kugwirizanitsa ziphunzitso zambiri za zipembedzo zosiyanasiyana zoimiridwa ndi awo amene anasonkhana pa Assisi. Umodzi wa chipembedzo chotero ukakhala wosatheka. Kusokonezeka kwa ‘chinenero cha zipembedzo’ kukapitiriza. Chotero, palidi kufanana kwenikweni ndi Nsanja ya Babele yakale.
Kusagwirizana kwa chipembedzo kumeneku kuli kuwonekera mu zitsanzo za zikhulupiriro. Mwachitsanzo, chiBudha sichimavomereza kukhalako kwa Mulungu waumwini, akumaphunzitsa kuti chonulirapo chomalizira cha munthu ndi Nirvana, mkhalidwe wa kudalitsidwa kotheratu kofikiridwa kupyolera mu kusakhalako kwa munthu. Ahindu amakhulupirira mu mamiliyoni a milungu ndipo m’zungulirezungulire wopita patsogolo wa kusinthasintha kumene kumatsogolera ku Nirvana. Zipembedzo za Chikatolika, chiOrthodox, ndi chiProtesitanti zimakhulupirira mu Utatu. Koma Asilamu amakhulupirira kuti pali Mulungu mmodzi, Allah, ndipo kuti Muhammad ali mneneri wake; komabe, iwo sakhulupirira kuti Mulungu ali ndi mwana. Ayuda amalambira Mulungu mmodzi koma samavomereza Yesu monga Mesiya. Zipembedzo za ku Africa zimakhulupirira kuti zomera, zinyama, ndi zinthu zopanda moyo ziri ndi mzimu. Anthu a ku India okhala ku America amalambira mphamvu za chilengedwe.
Ngakhale kuli tero, mtendere weniweni umasonyeza kuti pali chifupifupi maziko akubwera pamodzi, kapena kugwirizana, kwa anthu osiyanasiyana. Koma zipembedzo zimene zinakumana pa Assisi zinali zogawanika mochititsa chifundo kotero kuti sizikakhoza kuvomereza ku pemphero limodzi! Ndithudi, Mulungu sangavomereze malingaliro owombana amenewa chifukwa, analemba mtumwi Paulo, “Mulungu [ali] Mulungu, [osati] wa chisokonezo, koma wa mtendere.”—1 Akorinto 14:33, NW.
Kodi Mulungu Akumvetsera?
Ndimotani mmene Mulungu yekha wowona, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, angamvetserere mwachiyanjo ku mapemphero a atsogoleri a chipembedzo omwe alibe cholinga cha kugwirira ntchito kulinga ku umodzi wowona? Mawu ouziridwa a Mulungu amanena momvekera bwino kuti awo amene amachita kulambira kowona “anene chimodzimodzi iwo onse, ndi kuti pasakhale malekano pakati [pawo], koma [amangike] mu mtima womwewo ndi m’chiweruzo chomwecho.”—1 Akorinto 1:10.
Ngati Mulungu anamvetsera ku zipembedzo zogawanikana zimenezi, iye angakhale akudzitsutsa iyemwini. Chikasonyeza kuvomereza ku chimene iye amatsutsa—kupatukana. Koma Mulungu wa chowonadi sangakhale ndi liwongo la kaimidwe kaŵiri. Iye sangatsutse Mawu ake, popeza “Mulungu . . . sanama.” (Tito 1:2) Chotero, iye samvetsera ndi chiyanjo ku mapemphero oterowo a kulambira kogawanikana.
Baibulo momvekera bwino limasonyeza kuti Mulungu amavomereza kokha kulambira kumene kuli m’chigwirizano ndi chifuno chake. Yesu ananena kuti: “Siyense wa kunena kwa ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa mu Ufumu wa kumwamba, koma wakuchita chifuniro cha Atate wanga wa kumwamba.” Iye ananenanso kuti Mulungu “afuna,” kunena kuti, iye amavomereza ndi kumvetsera kokha kwa awo amene amlambira iye “mu mzimu ndi m’chowonadi.” Chimenecho chimachitidwa mwa kusunga Mawu ake ndi kumvera malamulo ake. Chotero Mulungu samavomereza zipembedzo zimene sizichita chifuniro chake, mofanana ndi mmene iye sanavomerezere omanga a Nsanja ya Babele, amenenso sanali kuchita chifuniro chake. Iye amakana oterowo. Monga mmene Yesu ananenera kwa awo amene amachita chifuno chawo m’malo mwa chifuno cha Mulungu: “Chokani kwa Ine, inu akuchita kusayeruzika.”—Mateyu 7:21-23; Yohane 4:23, 24.
Chotero, mkhalidwe wauzimu wa zipembedzo zomwe zinakumana pa Assisi uli wotsutsana ndi chimene Mulungu amafuna kwa alambiri owona. M’malo mwa kukhala ogwirizana m’malingaliro amodzi ndi maganizo, iwo ali opatukana ndi kusagwirizana, monga mmene zinaliri pa Nsanja ya Babele.
Chenicheni chakuti Mulungu samvetsera ndi chiyanjo ku mapemphero a zipembedzo zadziko lino zonga Babele chimakhala chowonekera kwambiri pamene tisanthula umboni wa mbiri yakale. Kodi ndi chithunzi chotani chimene mbiri imeneyi imapereka?
[Chithunzi patsamba 6]
Nsanja ya kachisi ya chiBabulo