Zamoyo Zakuthambo—Kupeza Yankho
PA FEBRUARY 17, 1600, munthu wotchedwa Giordano Bruno anatenthedwa wamoyo pabwalo lapoyera la Roma, Italy. Chifukwa? Zolemba zake zinakwiyitsa tchalitchi. Pakati pa zinthu zina, iye anaphunzitsa kuti panali maiko ambiri okhalidwa ndi anthu m’chilengedwe chonse. Kumbuyoko m’zaka za zana la 11, tchalitchi chinali chitalengeza chiphunzitsocho, kuchuluka kwa maiko, kukhala kukana chikhulupiriro. Kuchiphunzitsa kunatanthauza imfa. Bruno anamwalira.
Kufikira zaka za zana la 19, kutsutsana kwakuti kaya moyo ulipo pa maiko ena kunachitidwa m’mabwalo achipembedzo. Kwa zaka mazana ambiri, atsogoleri achipembedzo ndi asayansi pansi pa chisonkhezero chawo aumirira kuti dziko lapansi linali pakati pa chilengedwe chonse; kuti chilengedwe chonse chinalengedwa mu 4004 B.C.E.; ndi zina zotero.
Pamenepa, nzosadabwitsa kuti asayansi ambiri ndi ena ali ndi ulemu wochepa kaamba ka chipembedzo. Komabe, m’chochitikacho, ambiri atayanso ulemu wawo kaamba ka Baibulo, akumalingalira kuti linali magwero a kulingalira kolakwika konseko. Palibe chimene chingakhale kutali ndi chowonadi.
Baibulo silimanena kuti liri bukhu lophunzirira lasayansi. Komabe, siliri losalongosoka pamene likhudza nkhani za chilengedwe chonse kapena nkhani iriyonse ya sayansi. Mwachitsanzo, Baibulo silinena konse kuti dziko lapansi ndi munthu ali pakati pa chilengedwe chonse. Mosiyanako, alembi ake ouziridwa anasonyeza mowonekera mmene munthu wosazindikirika akuyerekezeredwa ndi chilengedwe chachikulu.—Salmo 8:3, 4.a
Pamenepa, mogwirizana ndi Baibulo, kodi kuli aliyense kunja kumeneko?
Baibulo Likuyankha
Mogwirizana ndi Baibulo, moyo wa zamoyo zakuthambo suliko kokha koma uliko wambiri. Uli wocholoŵana kwambiri, wosangalatsa kwambiri, ndipo wokhulupiririka kwambiri kuposa china chirichonse chimene achisinthiko, olemba nkhani zopeka zasayansi, ndi opanga mafilimu analotapo. Ndiiko komwe, chamoyo chakuthambo ndicho cholengedwa chochokera kunja kwa dziko lapansi ndi malo ake olizinga.
Asayansi amazizwa ngati pangakhale mitundu ya zamoyo kupyola pa luso lathu la kuizindikira. Baibulo limatitsimikizira kuti zolengedwa zoterozo zirikodi. Koma izo siziri zotulukapo za chisinthiko. Mofanana ndi zamoyo zonse pa chilengedwe chonse, mosasamala kanthu za mtundu wake, izo zimachokera ku Magwero a moyo, Yehova Mulungu. Iye ali Chamoyo chauzimu, ndipo walenga zikwi makumimakumi a zolengedwa zina zauzimu za mitundu yosiyanasiyana: angelo, akerubi, ndi aserafi. Iwo amachita ntchito zosiyanasiyana ndi zochita m’gulu lake locholoŵana lakumwammba.—Salmo 104:4; Ahebri 12:22; Chibvumbulutso 19:14.
Kodi Bwanji Ponena za Moyo pa Mapulaneti Ena?
Anthu ena achipembedzo achisonkhezero aumirira kuti Mulungu sangalenge dziko lirilonse popanda cholinga ndipo kuti maiko onse okhalika ayenera kukhala ali ndi anthu. Kodi zimenezo ndi zimene Baibulo limanena? Ayi. Baibulo limasonyeza kuti nzosayenerera kuti Mulungu pa nthaŵi ino walenga zolengedwa zakuthupi zaluntha pa mapulaneti ena oposa pa lathu. Tero motani?
Ngati Mulungu analenga zamoyo zoterozo, anatero asanalenge Adamu ndi Hava. Zamoyo zimenezo mwinamwake zinakhala zokhulupirika kwa Mlengi wawo, kapena mofanana ndi Adamu ndi Hava, zinachimwa ndi kukhala zopanda ungwiro.
Koma ngati zinakhala zopanda ungwiro, zinafunikira moombolo. Monga mmene wolemba nkhani wina akulongosolera kuti: “Munthu amakhala ndi lingaliro lochititsa mantha limeneli kuti Lachisanu [tsiku limene Yesu Kristu anaphedwa], Lachisanu lirilonse, kwinakwake m’chilengedwe chonse Yesu akupachikidwa pamwamba kaamba ka machimo a winawake.” Koma zimenezo Sizamalemba. Baibulo limatiuza kuti Yesu ‘anafa ku uchimo kamodzi.’—Aroma 6:10.
Kodi bwanji ngati zamoyo zimenezi zinakhalabe zangwiro? Chabwino, pamene Adamu ndi Hava anachimwa, iwo, kwenikwenidi, ankakaikira kuyenera kwa Mulungu kwa kulamulira pa dziko la zamoyo zaluntha zakuthupi. Ngati pulaneti lina linalipo pa nthaŵiyo, dziko lodzaza ndi zamoyo zakuthupi zaluntha zimene zinali kukhala mogwirizana ndipo zomvera pansi pa ulamuliro wa Mulungu, kodi izo sizikanaitanidwa monga mboni kutsimikizira kuti ulamuliro wa Mulungu umathandizadi? Kumaliza kumeneku kukuwoneka kukhala kosapeŵeka, popeza kuti wagwiritsira kale ntchito anthu opanda ungwiro monga mboni zake pa nkhani imodzimodziyo.—Yesaya 43:10.
Pamenepa, kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu analenga dzuŵa mamiliyoni osaŵerengeka onsewo (ndi mapulaneti ngati aliko) popanda chifuno? Kutalitali. Pamene tikudziŵa, polingalira za kupatulika kwa Yesu Kristu, kuti dziko lapansi ndilo pulaneti lokha lokhalidwa ndi anthu m’chilengedwe chonse pa nthaŵi ino, ndikudziŵanso, kuti kwa nthaŵi yonse lidzakhala lapadera monga pulaneti pa limene Mlengi analemekeza kuyenera kwa kulamulira kwake, zimene mtsogolo mulinacho sitidziŵa.
Sitiri Tokha
Tsiku ndi tsiku, chaka ndi chaka, akatswiri a zakuthambo a SETI amapitirizabe kufufuza kuthambo kaamba ka zizindikiro zochokera ku zamoyo zaluntha. Amalingalira kuti kufufuza kwawo kungatenge zaka khumi zina, kapena kungatenge zaka zana. Nzoseketsa motani! Iwo akuwononga miyoyo yawo, ziyembekezo zawo, ndi maunyinji aakulu a ndalama kufunafuna chizindikiro chimene mtundu wa anthu unalandira zaka mazana apitawo. Popeza kuti Baibulo lenilenilo ndilo uthenga wochokera kwa chamoyo chakuthambo Chaluntha, ndipo n’lapamwamba m’njira iriyonse kuposa zizindikiro zimene asayansi olingalira bwino kwambiri analingalirapo.—Onani bokosi patsamba 10.
Kodi ndimotani mmene mtundu wa anthu wavomerezera ku uthenga wokha wowona wochokera kwa chamoyo chakuthambo? Pomalingalira za nsongazi, kodi ndimotani mmene anthu amavomerezera ku Baibulo? Iwo amalinyalanyaza. Mwadala amaligwiritsira ntchito molakwa kukwaniritsa zofuna zawo. Iwo ananyoza Wolitumiza ndi zokometsera zoipa zopanda maziko ndi ziphunzitso zamalaulo. Iwo amalitcha kukhala chinyengo ndi kukana kukhalako kwa Wolitumiza. Nzosachita kufunikira kunena kuti Mlengi wathu sakukondweretsedwa konse ndi chivomerezo cha anthu. Komabe, wapitiriza kulankhula. Kupyolera mwa Mawu ake, iye akuphunzitsa mamiliyoni a anthu lerolino m’njira za mtendere. Anthuwa amaimira Yehova ndi kupereka zolankhula zake ku dziko. Koma oŵerengeka ochepera a mtundu wa anthu amawamvetsera. Mwachisawawa dziko silimvetsera.—Yesaya 2:2-4; Mateyu 24:14.
Komabe, mosangalatsa, aliyense wa ife angalankhule ndi Chamoyo chachikulu koposa m’chilengedwe chonse, ndipo popanda luso la zopangapanga lamtengo koposa, popanda kudikirira kwa zaka zambiri kuti mauthengawo adutse thambo lopanda kanthu. Mungamvetsere tsopano mwakuphunzira Baibulo ndi kutsimikiza nokha kaya ngati limachokeradi ku Magwero oposa aumunthu. Mungavomereze mwa pemphero ndi njira imene mumakhalira ndi moyo wanu. Sitiri tokha. Mlengi wathu akulonjeza kuti “sakhala patali ndi yense wa ife.”—Machitidwe 17:27; onaninso 1 Mbiri 28:9.
Iye sanathebe kulankhula ndi anthu. Walonjeza kusinthiratu njira ya mbiri ya dziko, kuthetsa liŵiro la mtundu wa anthu la kudziwononga mwakuchotseratu dongosolo la zinthu losagwira ntchitoli ndi kuliloŵa m’malo ndi boma lake, limene lidzakhaladi labwino kaamba ka onse. (Danieli 2:44; Yesaya 9:6, 7) Inde, kulankhulana kwina kochokera ku chamoyo chakuthambo Chaluntha kukulonjeza kudza m’kachitidwe, osati mawu.—2 Atesalonika 1:6-9.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka umboni wakuti Baibulo limagwirizana ndi sayansi yotsimikiziridwa, chonde onani bukhu lakuti The Bible—God’s Word or Man’s? lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Bokosi patsamba 10]
Mauthenga Amene Asayansi Uthenga
Akuyembekezera Umene
m’Kufufuza Kwawo kaamba ka Amanyalanyaza
Chamoyo Chakuthambo —Mawu a Mulungu,
Chaluntha: Baibulo:
*Angakhale machenjezo onama, *Umachokera ku chamoyo chakuthambo
popeza kuti zimenezi sizachilendo; Chalunthaa loposa la umunthu.
zinyengo nzothekera. —Yesaya 55:9; 2 Timoteo 3:16.
*Angapereke maphunziro ndi mapindu *Ukupereka maphunziro kwa mamiliyoni,
a zaka mamiliyoni a kuzoloŵera. okhala ndi mapindu a nzeru yakalekale kuposa
chilengedwe chonse.—Yobu 36:26; Salmo 103:14;
*Angatiphunzitse kupeŵa chipululutso *Umaphunzitsa mtendere kwa mamiliyoni pa
cha nyukiliya ndi nkhondo yonse. nthaŵi ino; Mkonzi wake akulonjeza kusunga
dziko lapansi kosatha ndi kuwononga awo
amene akuliwononga.—Salmo 104:5;
*Angapereke zochiritsa ku matenda *Mkonzi wake wasonyeza luso lake la kuchiritsa
ndipo ngakhale imfa; imfa yamwangozi matenda onse; walonjeza kuthetsa ndi kuchotsa
yokha ndiyo ingatsale. ziyambukiro za imfa, kubweretsa moyo wosatha.
*Angathetse ‘kusungulumwa *Pakali pano Mkonzi wa Baibulo “sakhala
kwachilengedwe’ kwa mtundu wa anthu. patali ndi yense wa ife.”—Machitidwe 17:27.
*Angakupange kukhala kosatheka *Ali wofikirika mosavuta ku banja la anthu.
kumasulira; kungatenge zikwi Tingaliŵerenge tsopano ndi kuvomereza.
—mwinamwake mamiliyoni—a zaka Mauthenga athu amalandiridwa pa nthaŵi
kuti avomereze ndi kukambitsirana. yomweyo.—Yohane 17:3; 1 Atesalonika 5:17;
*Zonse zapamwambazi nzozikidwa pa *Chikhulupiriro chathu m’zapamwambazo
zongolingalira ndi kuganiza. nchozikidwa pa umboni ndi chifukwa.—Ahebri 11:1.
[Chithunzi patsamba 11]
Tingalankhule ndi Chamoyo chachikulu koposa m’chilengedwe chonse