Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 7/8 tsamba 26-27
  • Ma UFO—Kodi Ali Amithenga Ochokera kwa Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ma UFO—Kodi Ali Amithenga Ochokera kwa Mulungu?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mapulani a Alendowo Akupulumutsa Dziko
  • Kulankhulana Pakati pa Mulungu ndi Anthu
  • Zamoyo Zakuthambo—Kupeza Yankho
    Galamukani!—1990
  • Zamoyo Zakuthambo—Loto Lakalekale
    Galamukani!—1990
  • Zamoyo Zakuthambo—Kodi Ziri Kuti?
    Galamukani!—1990
  • Kodi Kuli Aliyense Kunja Kumeneko?
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 7/8 tsamba 26-27

Lingaliro la Baibulo

Ma UFO—Kodi Ali Amithenga Ochokera kwa Mulungu?

PAMENE zaka za zana la 20 zikufika kumapeto ake ndipo mikhalidwe padziko lapansi ikupitiriza kunyonyotsoka, chikhulupiriro m’zinthu zotchedwa unidentified flying objects (UFO’s) (zinthu zouluka zosadziŵika) ndi ozikwera ake, zamoyo zakuthambo, chikufalikirafalikira. Kodi ma UFO angokhala nthano chabe, chinyengo, zopeka zoyambitsidwa ndi anthu amene amakonda kumaseka kunyengeka msanga kwa anthu anzawo?

Amene amati anaona ma UFO kapena ozikwera ake akuthambo amaphatikizapo anthu ooneka kukhala abwino ndi odalirika; kwenikweni, amene amakhulupirira za alendo ameneŵa ochokera ku mapulaneti ena amaphatikizapo maprofesa ophunzira kwambiri ndi asayansi. Iwo ali otsimikiza kuti zamoyo zakuthambo zimapenyerera anthu, ndipo nthaŵi zina, kulankhulana nawo. Pali otchedwa mabungwe ochirikizana a zakuthambo othandiza anthu amene amati akumana ndi alendo ochokera kuthambo.a

Mapulani a Alendowo Akupulumutsa Dziko

M’buku la Aliens Among Us, Ruth Montgomery akufunsa ena a anthu omawonjezereka amene ali otsimikiza kuti iwo ali alendo akuthambo okhala m’matupi aumunthu. Ena a ameneŵa amene amati ali zamoyo zakuthambo zokhala m’matupi a anthu amalosera kuti m’chaka cha 2000, kudzakhala “chochitika chakuthambo chimene makamu a angelo ndi olamulira akhala akukonzekera.” Anthu monga John amakhulupirira kuti zamoyo zina zakuthambo zikugwiritsira ntchito ma UFO kunyamula ndi kusunga zomera ndi nyama zamitundumitundu kapena kuti ma UFO adzagwiritsiridwa ntchito monga zombo zopulumutsira anthu mamiliyoni ku chiwonongeko chomayandikira cha dziko lapansi. Pambuyo pa chiwonongeko chachikulucho, anthu adzabwezedwa padziko lapansi kuyamba “New Age (Nyengo Yatsopano) ndi New Order (Dongosolo Latsopano)” la chidziŵitso chauzimu. Mnyamata wina wa ku Colorado, U.S.A., wa m’gulu lomwe limadzitcha “Alien Youth” (Achichepere Alendo), anauza Galamukani! monenetsa kuti: “Ine ndi mabwenzi anga tikuyembekezera makolo athu alendo kudzatitenga.”

Angapo mwa awo amene amanenetsa kuti ali zamoyo zakuthambo amati Mulungu ndiye akuwatsogolera, ndipo ena amati amalankhula naye momasuka kupempha uphungu umene angathandize nawo anthu. Kodi Mulungu akugwiritsira ntchito alendo ochokera ku mapulaneti ena kupulumutsa anthu ku tsoka likudzalo la dziko?

Kulankhulana Pakati pa Mulungu ndi Anthu

Pachiyambi m’mbiri ya munthu, Mulungu analankhulana ndi anthu. Mbiri ya Baibulo imasimba za kulankhulana kwa Mulungu ndi Adamu ndi Hava, Nowa, Abrahamu, ndi ena.b (Genesis 3:8-10; 6:13; 15:1) Maloto, mawu, ndi masomphenya anagwiritsiridwa ntchito kusonyeza chifuniro cha Mulungu ndi kuchititsa Baibulo kulembedwa. Komabe, pambuyo poti Baibulo lamalizidwa, kodi kulankhulana kwachindunji pakati pa anthu ndi miyamba kunali kofunika? Ayi, pakuti Baibulo limanena kuti Malemba Opatulika ‘amakhalitsa munthu wa Mulungu . . . wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.’ (2 Timoteo 3:17) Malinga ndi Baibulo, chitsogozo kaamba ka nthaŵi zino zovuta chimachokera m’Mawu a Mulungu olembedwa. Chikhalirechobe, kodi pali chifukwa chilichonse chokhulupirira kuti tingalandire mawu kapena malangizo apadera mwachindunji kuchokera kwa Mulungu kupyolera mwa wolankhuliramo wakuthambo? Ayi, pakuti mtumwi Paulo anati: “Ngakhale ife, kapena mngelo wochokera kumwamba, ngati akakulalikireni uthenga wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.”—Agalatiya 1:8.

Ngakhale kuti nkhani za zimene amati zamoyo zakuthambo zimachita ngati zikugwirizana ndi maulosi a Baibulo akuti dziko lapansi posachedwapa lidzaona kusintha kwakukulu kowononga, zimapereka njira yopulumukira yodalira pa zolengedwa. Baibulo silimalimbikitsa anthu kuthaŵira kopulumukira m’chimene amati chombo cha alendo kapena malo ena alionse. M’malo mwake, limatiuza kufuna chitetezo mu unansi wodzipatulira ndi Mulungu, kudzipatulira kumene kumasonyezedwa ndi ubatizo wa m’madzi. (1 Petro 3:21; yerekezerani ndi Salmo 91:7; Mateyu 28:19, 20; Yohane 17:3.) Ndipo Yesu anati “iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.”—Mateyu 24:13.

Kodi malemba ameneŵa sakusonyeza kuti unansi wauzimu ndi Mulungu ndiwo umadzetsa chipulumutso osati malo enieni opulumukirako? Chifukwa chake, m’malo mothandiza anthu kupulumuka, zokambidwa pa ‘zamoyo zosakhala anthu’ zimachotsa maganizo a anthu pa zimene Mulungu amafuna kwenikweni kaamba ka ubwino wawo wosatha.

Kodi ndani amene angayese kuchotsa anthu panjira ya Mulungu ya chipulumutso, komano nanena kuti akuimira Mulungu? Ed Conroy, m’buku lake lakuti Report on Communion, akuti “akatswiri akhama a zinthu zouluka zosadziŵika [amene amaphunzira za ma UFO] odziŵa za “sayansi ya zamaganizo ndi kakhalidwe ka anthu” amaphatikiza pakufufuza kwawo maphunziro oyerekezera a “‘alendo a m’chipinda chogona,’ mizukwa, mizimu yophokosera, zilengwa, masomphenya achipembedzo, ndi zimene zayesedwa ziŵanda.” Akatswiri ambiri a zinthu zouluka zosadziŵika ndi aja amene amati ndiwo zamoyo zakuthambo m’matupi aumunthu amanena kuti kugwiritsira ntchito zombo za m’mlengalenga kuli kosafunikira kwenikweni. Iwo amanena kuti zamoyo zimenezi zingayende mosaoneka ndi kusandulika kulikonse padziko lapansi popanda kubwera ndi chombo cha m’mlengalenga.

Baibulo limachenjeza kuti Satana ndi ziŵanda zake atsimikiza kusocheretsa anthu. Pa kutaya mtima ndi kuthedwa nzeru kwa anthu amapezerapo mwaŵi wa kupereka njira zokopa koma zonama zothetsera mavuto. (2 Akorinto 11:14) Chifukwa chake, Baibulo limachenjeza kuti: “M’masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziŵanda.”—1 Timoteo 4:1.

Momwemonso lerolino, oyesedwa maulendo alionse ndi chitsogozo chooneka ngati chopindulitsa zochokera ku zamoyo zotero ziyenera kukanidwa, kaya zibwere mumpangidwe wotani. Awo okonda kutsatira uphungu wa “zamoyo zakuthambo” m’malo mwa Mawu a Mulungu adzasocheretsedwadi—kuphonya kowopsa m’nthaŵi zino zovuta.

[Mawu a M’munsi]

a Ngati mufuna nkhani yofotokoza ma UFO ndi moyo wakuthambo, onani kope la Galamukani! la April 8, 1990, ndi kope lachingelezi la November 8, 1990.

b Mlembi wa Baibulo Ezekieli anaona chimene ena afotokoza kukhala UFO. (Ezekieli, chaputala 1) Komabe, ameneŵa anali ena a masomphenya ambiri ophiphiritsira ofotokozedwa ndi Ezekieli ndi aneneri ena, osati chinthu chenicheni chonga zomwe amanena nthaŵi ino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena