Bungwe la Matchalitchi Lapadziko Lonse Kodi Ndichigwirizano Kapena Chisokonezo?
Ndi mlembi wa Galamukani! ku Australia
MSONKHANOWO unayamba pa February 7, 1991, pamalo okometseredwa ndi zithunzithunzi a Australian National University ku Canberra, Australia, likulu la dzikolo. Anthu wamba oyerekezeredwa kukhala 4,000 ndi atsogoleri amatchalitchi pafupifupi 316 ochokera kumaiko oposa zana limodzi anapezekapo. Misonkhano yapapitapo isanu ndi umodzi ya WCC (World Council of Churches) inali itachitidwira m’maiko osiyanasiyana mkati mwa nyengo ya zaka 35, kuyambira mu 1948 ku Amsterdam, Netherlands.
Kodi WCC nchiyani? Siliri tchalitchi chopambana. Ndilo kuyanjana kwa matchalitchi, msonkhano wosinthanira malingaliro. Nkhani yolonjera mamembala amsonkhano wachisanu ndi chiŵiri umenewu inakambidwa ndi nduna yaikulu yaboma, Robert J. Hawke—ngakhale kuli kwakuti iye ali wodzinenera kukhulupirira kusadziŵika kwa Mulungu. Mutu wankhani wosankhidwa wa msonkhano umenewu wamilungu iŵiri unali mumpangidwe wa pemphero lakuti: “Idza Mzimu Woyera—Konzaninso Chilengedwe Chonse!”
Komabe, kusintha kosayembekezeredwa kwa zochitika zapadziko lonse kunapambutsa malingaliro ndi ziyembekezo za nthumwi kuchoka kukukonzanso kochitidwa ndi mzimu woyera kumka kundale zadziko ndi kuyenerera kwa nkhondo ya ku Persian Gulf. Kusintha kwamwamsangaku kuchokera kukukambitsirana zauzimu kunachititsa Bwana Paul Reeves, arkibishopu wa Anglican ndi amene kale anali bwanamkubwa wamkulu wa New Zealand, kulankhula za kudabwitsidwa kwake kuti: “Timakhoterera, mumisonkhao yonga uwu, kulimbanira mphamvu, imene simakhudza kwambiri Mzimu Woyera.” Arkibishopu wa Canberra anayesa kulungamitsa phindu la kusagwirizana kumati: “Umodzi ndiwo mphatso ya Mzimu Woyera. Kusagwirizana kwabwino ndiko mphatso ya Mzimu Woyera umodzimodzi- wo.”
David Gill, mlembi wamkulu wa Bungwe la Matchalitchi la Australia, nayenso anasonyeza nkhaŵa kuti umphumphu wa WCC weniweniwo unali paupandu, akumanena kuti gululo linali kukhala logonja mowonjezereka kukuchititsa timagulu tolekana timene tikufunafuna pulatifomu polankhulira nkhaŵa zawo zenizeni.
Kuikidwa kwa Akazi—Kusagwirizana Kowonjezereka
Thayo la akazi m’tchalitchi chamakono linalinso pampambo wankhani zoti zikambitsiridwe, koma akaziwo sanali okondwera. Unyinji wa iwo anaiwona monga yolamulidwa ndi amuna. Lois Wilson wa ku Canada anafotokoza motsimikizira kuti: “Ndale zadziko za WCC zimanunkha kufikira kumwamba kwenikweniko ndipo ndiganiza kuti sizimene Yesu anali nazo m’maganizo.” Kodi nchiyani chinapangitsa kugwiritsidwa mwala kumeneku? Nyuzipepalayo Canberra Times inanena izi: “Munali kudandaula kwambiri m’zimbuzi za akazi chifukwa akaziwo anaponderezedwa kuwalepheretsa kulandira kusankhidwa kukhala ziŵalo za komiti yaikulu ya bungwelo. Mkazi wina anali atauzidwa kuti akachotsedwa m’tchalitchi chake poyesa kumulefula maganizo kuti asalandire kusankhidwako.”
Kodi Nchiyani Chinachitikira Mutu Wankhani Wauzimu?
Ena anali odera nkhaŵa kuti msonkhanowo sunagogomezere mokwanira mkhalidwe Wabaibulo kapena wazaumulungu wa ntchito yake. Zimenezi sizodabwitsa, pakuti zambiri za nkhani zazikulu pampambo wankhani zoti zikambitsiridwe zinali ndimkhalidwe wandale zadziko. Kunena zowona, mumalipoti osindikizidwa onena za msonkhanowo, woŵerenga anapeza chisonyezero chimodzi chabe cha Baibulo.
Magazini achipembezowo National Outlook ananena kuti David Gill “akusonyeza malingaliro a ena amene anapezekapo pamisonkhano ya WCC posachedwapa, ndipo amene, monga momwe munthu wina ananenera posachedwa, anapitako ali ndi chiyembekezo chachikulu koma anachokako osakhutira ndi opanda kanthu.”
Mosiyana, pamene anjala ndi aludzu mwauzimu anadza kwa Kristu Yesu, sanachoka “osakhutira ndi opanda kanthu.” Iwo anachoka ali otsitsimulidwa: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa liri lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”—Mateyu 11:28-30.