Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 8/8 tsamba 15-17
  • Kodi Ndingadzichinjirize Motani ku Kuukiridwa ndi Gulu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingadzichinjirize Motani ku Kuukiridwa ndi Gulu?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Magulu ndi Mawonekedwe Awo
  • Kukhala Wosiyana Kumathandiza!
  • Peŵani Ngozi
  • Zimene Tifunikira Kudziŵa Ponena za Magulu Aupandu
    Galamukani!—1998
  • Kodi Ndiyenera Kuphatikana ndi Gulu?
    Galamukani!—1991
  • Kutetezera Ana Athu ku Magulu Aupandu
    Galamukani!—1998
  • Mliriwo Ufalikira
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 8/8 tsamba 15-17

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingadzichinjirize Motani ku Kuukiridwa ndi Gulu?

MADZULO ena ozizira m’nyengo ya mphakasa, Tom wazaka 12 zakubadwa anapita kusitolo ya m’mudzimo kukagula zinthu zina. Tom anali kuchita mantha chifukwa chakuti anali m’gawo lolamuliridwa ndi gulu la m’khwalala, ndipo posakhalitsa mantha ake anatsimikizira kukhala enieni. Mwadzidzidzi, ziŵalo zingapo za gulu zinamfikira, kumgwetsera pansi ndi zibakera.

Chifukwa cha ‘kuchuluka kwa kusayeruzika’ konenedweratu, ambiri amakhala m’midzi imene ili yachiwawa kotero kuti ngakhale olamulira samatha kuchiletsa. (Mateyu 24:12) Ndipo ngati mumakhala m’dera limene zochita za gulu ziri zochuluka, chokumana nacho cha Tom chingakhale chozoloŵereka. Mwachitsanzo, talingalirani mkhalidwe wa ku Los Angeles County, U.S.A. Malinga nkunena kwa magazini a Maclean’s, pa imfa zokwanira 257 zogwirizanitsidwa ndi gulu zomwe zinachitika kumeneko mu 1988, theka linaphatikizako kuphedwa popanda kuwaputa kwa osakhala mamembala a gululo! Chotero, achichepere amene amakhala m’madera mmene magulu ali okangalika amayang’anizana ndi chitokoso chenicheni ichi: kudzichinjiriza okha.

Nkhani yapapitapo inasonyeza kupusa kwakuphatikana ndi gulu.a Inalongosola kuti kukhala membala wa gulu kumawonjezeradi upandu wa kuvulazidwa kwanu, kumangidwa, kapena ngakhale kuphedwa. Ndipo ponena za kunyamula mpeni, mfuti, kapena chida china chirichonse, kumasemphana ndi uphungu Wabaibulo wa pa Yesaya 2:4 ndi Mateyu 26:52. Ndiponso, kuteroko kukakulitsa mkangano m’malo mwakuuthetsa. Zofananazo zinganenedwe ponena za kuphunzira maluso odzichinjiriza, monga ngati judo kapena karate, monga njira yodzichinjirizira. Pamenepo, nkwabwino koposa kupeŵa kukumana mwachindunji ndi gulu. Koma motani?

Magulu ndi Mawonekedwe Awo

Poyamba, lingalirani kavalidwe kanu, kapesedwe ndi mkhalidwe. Magulu ambiri amavala zovala zapadera, mawonekedwe, kapena chizindikiro chimene chimawasiyanitsa ndi magulu ena. Kansalu kominira kapena ngakhale kavalidwe ka chisoti kangakhazikitse umembala wagulu. Nthaŵi zambiri, magulu amatsanzira majesichala akutiakuti ndi mpambo wawowawo wa mawu ndi kaimidwe.

Vuto nlakuti mawonekedwe a magulu ndi zizindikiro zina kaŵirikaŵiri zimakhala m’fashoni pakati pa achichepere—kuphatikizapo omwe simamembala. Nyuzipepala ya ku Canada ya The Globe and Mail inafotokoza kuti: “Achichepere akutha msinkhu ena amatsanzira kavalidwe ka magulu akutiakuti, ngakhale kuti sali mamembala ake. . . . Angakhale akuyesa kusangalatsa azaka zapakati pa 13 ndi 19 ena.”

Mwachiwonekere achichepere ena amalingalira kuti chovala chakutichakuti chidzawapanga kuwonekera amphamvu ndi owopsa. Ena amalingalira kuti kuvala mofanana ndi gulu kungawapatse chitetezo. Iwo amaganiza kuti ena adzakhala osakhoterera kuwakwiitsa, akumalingalira kuti ali ogwirizana ndi gulu lakutilakuti. Kodi kumeneku kuli kulingalira kolama? Kutalitali. The Globe and Mail inanena mosabisa mawu kuti: “Iwo amadziika paupandu wakumenyedwa ngati awonedwa ndi mamembala enieni a gululo.”

Bernard, yemwe kale anali membala wa gulu koma tsopano ndi mmodzi wa Mboni za Yehova, akutsimikizira kusanthula kumeneku. Akumakumbukira masiku akale, iye akuti: “Ngati winawake anavala mofanana ndi ife ndipo sanali mmodzi wa ife, mothekera kwenikweni iye akakhala chandamale. Kaya iye akayenera kuphatikana ndi gulu lathu kapena kuvulazidwa.”

Kukhala Wosiyana Kumathandiza!

Kudziŵa zimenezi kuyenera kulamulira kusankha kwanu zovala. Ndiiko komwe, kodi kavalidwe kathu sikamanena chinachake ponena za ife—ngakhale kutizindikiritsa? Izi zinali zowona zaka zikwi zambiri zapitazo pamene Baibulo linali kulembedwa. M’bukhu la 2 Mafumu, timaŵerenga za athenga omwe anakasimba kwa Mfumu Ahaziya wa Israyeli. Iwo anasimba kuti anakumana ndi munthu wina yemwe anawapatsira uthenga wakutiwakuti. Mfumuyo inafunsa kuti, ‘Nanga maonekedwe ake a munthu anakwerayo . . . ndi otani?’ Pamene anafotokoza zovala zake, nthaŵi yomweyo mfumuyo inati, ‘Ndiye Eliya [mneneri, NW].’ Kodi anadziŵa bwanji? Chifukwa chakuti Eliya anavala chovala chapadera cha mneneri. (2 Mafumu 1:5-8) Lerolino, mofanana ndi panthaŵiyo, kavalidwe kathu kangatigwirizanitse ndi gulu lakutilakuti la anthu, ngakhale kuti sitingamachite zimene amachita kapena kukhulupirira zimene amakhulupirira. Ena adzalingalira kuti tikugwirizana ndi anthu a kagulu kamene kamavala motero.

Michael, membala wakale wa gulu wogwidwa mawu mu Sports Illustrated akunena kuti: “Nsapato, majaketi ndi zisoti ziri zizindikiro chabe . . . Ndikhoza kuyenda m’galimoto m’khwalala ndikusonyeza membala wa gulu mwakungowona kavalidwe kake.”

Pamenepo, kukakhala kupanda nzeru chotani nanga kwa wachichepere Wachikristu kupesa, kuvala, kuyenda, kulankhula, kapena ngakhale kutengera kaimidwe kofanana ndi mamembala a gulu la m’khwalala! Uphungu wa Yesu ‘wakusakhala mbali ya dziko’ ukakhala wogwira ntchito mwapadera panopo. (Yohane 17:16, NW) Ndithudi, kaŵirikaŵiri mamembala a gulu samakhala ndi vuto kudziŵa awo amene sali mbali yawo. Michael amakumbukira kuti: “Timawona mnyamata wovala buluku, juzi yabwino, nsapato zachikopa zachitende chachifupi. Simungandikhutiritse kuti ali membala wa gulu.”

Bernard, wogwidwa mawu poyambirirapo, akuwonjezera kuti: “Kaŵirikaŵiri mamembala a gulu amavala zovala zamakono kwenikweni.” Polingalira zimenezi, muyenera kukhala wosamala ndi wochenjera musanatengere sitayelo ya kavalidwe ndi kapesedwe kamene kangakhale kowanda pasukulu kapena m’mudzi mwanu koma kangakupangitseni kukhala chandamale chosavuta cha chiwawa cha gulu chifukwa cha kuzindikiridwa molakwika. Kuvala chovala chodekha kungatsimikizire kukhala chinjirizo.—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 2:9.

Khalaninso wosamala ponena za chinenero ndi mpambo wa mawu umene mumagwiritsira ntchito. Ngati muyesa kutsimikizira kuti mukuyendera limodzi ndi fashoni mwakugwiritsira ntchito mawu ongopeka ogwiritsiridwa ntchito mofala ndi mamembala a gulu, mungakokedi chidwi cha mamembala a gulu. Peŵani kusonyeza mkhalidwe wamphamvu ndi wowopsa. Kumbukirani kuti: ‘Galu wamoyo aposa mkango wakufa.’—Mlaliki 9:4.

Chinjirizo lina ndilo kupeŵa kukhala ‘bwenzi la dziko’ pamene musankha oyanjana nawo. (Yakobo 4:4) Mungalingalire kuti kukhala ndi mabwenzi “amphamvu” kukakupindulitsani. Koma mwa chokumana nacho chake chakukhala m’gulu, Bernard akuti: “Ngati muli ndi mabwenzi omwe ali m’gulu, mothekera kwenikweni mudzakakamizidwa kuphatikana ndi gululo.” Ngakhale zoyesayesa zakutsogoza mamembala a gulu ku njira ya moyo ziyenera kuchitidwa mochenjera kwenikweni.—Mateyu 28:19, 20.

Inde, chinjirizo lanu labwino koposa lingakhale mbiri yanu yabwino monga Mkristu wopereka chitsanzo chabwino. Zowonadi, chifukwa chakuti ‘simuthamanga nawo kufikira kusefukira komwe kwa chitaiko, angakuchitireni mwano.’ (1 Petro 4:4) Koma iwo angakulemekezeninso mokakamizika. Ndipo chabwino koposa, sadzakulingalirani kukhala munthu wothekera kukhala membala wa gululo.

Peŵani Ngozi

Chikhalirechobe, kukhala ndi mbiri yabwino nthaŵi zonse sikumakhala kokwanira kukuchinjirizani ku kuvulazidwa. Miyambo 27:12 imapereka uphungu wabwino uwu: ‘Wochenjera awona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira nalipitsidwa.’ Uphungu wabwino umenewu umagogomezera kufunika kwa luntha ndi kukhala maso pamene muyang’anizana ndi mikhalidwe yothekera kukhala yaupandu. Mwachitsanzo, ngati mwaitanidwa kupita kumalo kapena chochitika chakutichakuti, dzifunseni kuti, Kodi ndani adzakhalako? Kodi ndimalo odziŵika kumene gulu limabisala?

Membala wina wakale wa gulu akupereka uphungu wofananawo: “Peŵani malo amene magulu amabisala. Tengani njira ina ngati kuli kotheka.” Inde, peŵani kupanga ulendo wosayenerera kupita ku madera odziŵika kukhala opanda chisungiko. Ndipo ngati chiwawa chibuka, musalole kuti kufunitsitsa kudziŵa zinthu kukuphetseni. Miyambo 17:14 imati: ‘Chiyambi cha ndewu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.’

Koma talingalirani kuti mosasamala kanthu za zoyesayesa zanu zakupeŵa mavuto, mwakumanizana ndi anthu amene akukufunani kuti muphatikane ndi gulu lawo. Afotokozereni mokhazika mtima kuti simungagwirizane nawo. Kaŵirikaŵiri achichepere omwe ndi Mboni za Yehova amawonjezera kuti nthaŵi yawo ndi zoyesayesa zawo zimagwiritsiridwa ntchito mu uminisitala Wachikristu. Chirichonse chimene munganene, peŵani kukhala wopanda ulemu kapena wotsutsa. Yesu anauza ophunzira ake pa Mateyu 10:16 kuti: ‘Khalani ochenjera monga njoka, ndi owona mtima monga nkhunda.’ Kachiŵirinso, mayendedwe anu, kavalidwe, ndi kapesedwe ziyenera kugwirizana ndi kaimidwe kamene mwakatenga.

Komabe, zindikirani kuti ngakhale zochinjiriza zopambanitsa sizingatsimikizire chisungiko chanu. (Mlaliki 9:11) Koma ndi kuyesayesa kwinakwake, mothekera kwenikweni mungapeŵe kukhala mnkhole wa chiwawa cha gulu.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani yakuti “Kodi Ndiyenera Kuphatikana ndi Gulu?” yowonekera m’kope la Galamukani! la June 8, 1991.

[Chithunzi patsamba 16]

Thawani malo achiwawa. Musalole kuti kufunitsitsa kudziŵa zinthu kukuphetseni

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena