Kuchira Nkotheka
“Tiyenera kupanga chosankha: Kuleka kumwa ndi kuchira, kapena kupitiriza kumwa ndi kufa.”—Chidakwa yemwe akuchira.
TANGOYEREKEZERANI kuti mwangogalamuka usiku nkupeza kuti nyumba yanu ikupsa. Mwamsanga pabwera okuthandizani ndi kuzima motowo. Kodi mungangoloŵa mkati ndikuchita ngati kuti palibe chimene chachitika? Ndithudi ayi. Nyumbayo yawonongeka, ndipo idzafuna kukonzanso musanayambe kukhala bwino monga kale.
Chidakwa amakhala ndi chitokoso chofananacho pamene ayamba kuchira. Moyo wake unasakazidwa ndi moŵa, mwinamwake kwa zaka zambiri. Tsopano waleka kumwa. “Motowo” wazima, koma kukonzanso kaimidwe kamaganizo, njira ya moyo, ndi makhalidwe nzofunika kotero kuti chidakwayo alekeretu kumwa. Njira zotsatirazi zingathandize chidakwa kulekeratu kumwa.
1. Dziŵani Mdani Wanu
Baibulo limanena kuti zilakolako zathupi ‘zichita nkhondo pa moyo.’ (1 Petro 2:11) Liwu Lachigiriki lomasuliridwa ‘zichita nkhondo’ m’lingaliro lenileni limatanthauza “kumenya nkhondo,” ndipo limapereka lingaliro la nkhondo yosakaza.—Yerekezerani ndi Aroma 7:23-25.
Monga momwedi msirikali waluso aliyense amapendera machenjera a mdani wake choyamba, chidakwa ayenera kuphunzira mkhalidwe wa uchidakwa ndi mmene umawonongera chidakwayo ndi amene amakhala naye.a—Ahebri 5:14.
2. Lekani Kumwa ndipo Sinthani Kalingaliridwe Kanu
“Kuleka kumwa kumatanthauza kutaya botolo ndi chibwana chomwe,” akutero dokotala wina. Kunena m’mawu ŵena, zambiri ziyenera kusintha kuwonjezera pakuleka kumwa; munthu wamkati ayeneranso kusintha.
Baibulo limachenjeza mwanzeru kuti: ‘Mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu.’ (Aroma 12:2) “Vulani umunthu wakale ndi ntchito zake.” (Akolose 3:9, NW) Ngati zochita zisintha koma umunthu ukhalirabe, chidakwayo adzangotembenukira ku chomwerekeretsa china—kapena kubwerera ku chakale.
3. Pezani Wokamba Naye Zakukhosi Womvetsetsa
Mwambi Wabaibulo umati: ‘Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.’ (Miyambo 18:1) Ngakhale ataleka kumwa, chidakwa amadzilungamitsabe. Chifukwa chake, amafunikira munthu wokamba naye zakukhosi womvetsetsa koma wolimba (kaŵirikaŵiri wotchedwa wochirikiza). Kumakhala kwabwinopo ngati wokamba nayeyo nayenso anali chidakwa amene tsopano akuchira ndi amene anatha kulaka mavuto akuleka kumwa. (Yerekezerani ndi Miyambo 27:17.) Wokamba nayeyo ayenera kulemekeza zikhulupiriro zachipembedzo zachidakwayo ndipo ayenera kukhala wodzimana ndi wodzipereka kuthandiza nthaŵi zonse.—Miyambo 17:17.
4. Khalani Woleza Mtima
Kuchira kumachitika mwapang’onopang’ono. Kumatenga nthaŵi kuti chidakwa akonzenso moyo wake. Pangakhale mavuto a ndalama, mavuto pantchito, ndi panyumba. Kumasuka ku moŵa sikumatanthauza kumasuka ku mavuto. Poyamba chidakwa yemwe akuchirayo angakhale ndi nkhaŵa pamene akuchita ndi moyo wopanda moŵa monga ‘chothetsera mavuto.’ Pamene nkhaŵa zoterozo ziwonekera kukhala zosakhoza kutha, chidakwayo ayenera kukumbukira mawu otonthoza a wamasalmo awa: ‘Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo iye adzakugwiriziza: Nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.’—Salmo 55:22.
5. Pezani Mabwenzi Amakhalidwe Abwino
Chidakwayo ayenera kudzifunsa mowona mtima kuti: ‘Kodi mabwenzi anga amachirikiza kuleka kwanga moŵa kapena kodi nthaŵi zonse amalankhula za “nthaŵi zakale zosangalatsa,” kundichititsa kumva kuti ndikusoŵeka kenakake?’ Miyambo 18:24 imati: ‘Woyanjana ndi ambiri angodziwononga; koma liripo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.’ Pamafunikira kulingalira mwanzeru kuti muwone amene ali mabwenzi enieni ndi amene angakhale mabwenzi owononga.
6. Peŵani Kudzidalira Kopambanitsa
“Ndilibwino—ndilibenso chikhumbo chakumwa mpang’ono ponse!” Chidakwa wonena zimenezo amakulitsa molakwa chipambano chake ndipo amachepsa uchidakwa wake. Chisangalalo choyambirira cha kuchira chimakhala chosatsimikizirika ndi chosakhalitsa. “Yesetsani kukhala ndi malingaliro achikatikati,” likunena motero bukhu lakuti Willpower’s Not Enough. “Mukapanda kutero mudzagweranso m’vuto lanu, ndipo kudzakhala kovuta kuchiranso.”—Yerekezerani ndi Miyambo 16:18.
7. Chenjerani ndi Zomwerekeretsa Zina
Ambiri amaleka kumwa, komano amakhala ndi mavuto ena akadyedwe kapena kukonda kugwira ntchito mopambanitsa, otchova juga omwerekera, ndi zina zotero. Chidakwa womachirayo angalingalire kuti: ‘Kodi choipapo nchiyani? Chachikulu nchakuti sindimamwa.’ Zowonadi, zochita zina zingakhale zothandiza. Koma pamene chinthu chirichonse kapena ntchito igwiritsiridwa ntchito kugodomalitsa malingaliro anu, zimapatsa chisungiko chachinyengo, chosakhalitsa.
8. Sinthirani ku Mikhalidwe Yatsopano m’Banja
Kwa zidakwa zambiri, kachitidwe kakuchira kamabutsa mavuto pamene zinthu zifika pakukhala bwino! Motani? Chifukwa chakuti kuleka kumwa ndimkhalidwe watsopano. Chidakwayo angakhale ndi chikhumbo cha moyo wake wakale. Ndiponso, pamene chidakwayo aleka kumwa nakhala wodekha, zimagwedeza banja lonse zimenezo. Chotero, chiŵalo chirichonse chabanja chiyenera kusintha mkhalidwe wake. “Malembo onse a drama ya banjalo ayenera kutaidwa ndikulemba atsopano,” kakutero kabukhu kakuti Recovery for the Whole Family. Nchifukwa chake kuchirako kumatchedwa chochitika choloŵetsamo banja lonse.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 12:26.
9. Chenjerani ndi Kubwevuka
Kudzidalira kopambanitsa, mayanjano oipa, zomwerekeretsa zina, ndi kudzipatula kaŵirikaŵiri zingakhale njira zobwevutsa. Lankhulanani momasuka ndi munthu amene mumauza zakukhosi ponena za zikhoterero zoterozo.
Chidakwa wina yemwe akuchira anati: “Zidakwa zonse zimaleka kumwa. Enafe tiri ndi mwaŵi kuti tinaleka tidakali ndi moyo.”
[Mawu a M’munsi]
a Alipo malo ambiri opereka chithandizo, zipatala, ndi maprogramu othandiza amene angapereke malangizo pazimenezo. Galamukani! panopa sikusankhira munthu aliyense njira yakuchiritsa yakutiyakuti. Amene amafuna kutsatira malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo ayenera kusamala kusadziloŵetsa m’zochita zimene zikawapangitsa kulolera molakwa malamulo amakhalidwe abwino Amalemba. Munthu yemwe ndimmodzi wa Mboni za Yehova adzapeza zitsogozo zothandiza mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1983, masamba 9-13.
[Bokosi patsamba 25]
Ngati Mankhwala Ali Ofunika Kwenikweni
Mankhwala alionse okhalamo zoledzeretsa angadzutse chikhumbo ndi kuyambitsanso kumwa.
Dr. James W. Smith analemba kuti: “Sikwachilendo kuwona wodwala yemwe anali chidakwa kuyambiranso pambuyo pakuleka kumwa kwa zaka zambiri chifukwa chakumwa mankhwala achifuwa okhala ndi zoledzeretsa.” Chidakwa amayambukiridwa moipa ndi mankhwala onse odzetsa tulo. Ngati mankhwala odzetsa tulo ali ofunika kwenikweni, chidakwayo ayenera . . .
1. kuwonana ndi katswiri wopereka mankhwala kuti amuuze upandu wa mankhwalawo.
2. kudziŵitsa wokamba naye zakukhosi, ndipo ngati nkotheka, kumuitana nthaŵi zonse asanamwe mankhwalawo.
3. kulemba ponena za mankhwala amene amamwa.
4. kuleka kumwa mankhwalawo mwamsanga monga momwe kungathekere.
5. kutaya mankhwala alionse pamene ntchito yake yatha.