Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Mulungu Amayankha Mapemphero Anga?
“NDIFUNIKIRA kudziŵa ngati Yehova amayankha mapemphero anga,” akutero Sandra wazaka 11, “chifukwa chakuti sindiri wotsimikiza ngati iye amatero. Ndimadziŵa achichepere ena ambiri amene ali ndi vuto lofananalo.” Alyssa wazaka khumi ndi zisanu panthaŵi ina anali ndi vuto limodzimodzilo la pemphero. “Kaŵirikaŵiri ndinadzimva kuti ndinali kudzilankhuza ndekha,” iye akuvomereza motero.
Malinga ndi kufufuza kwa ku Gallup kwa mu 1988, 87 peresenti ya achichepere mu United States akhala akupemphera mwakamodzikamodzi, koma ochepera patheka amatero mokhazikika. Mwachiwonekere ena amalingalira kuti mapemphero awo samayankhidwa konse. Nthaŵi zina, inunso mungakhale ndi malingaliro akuti palibe amene amamvetsera mapemphero anu. Komabe, Baibulo limatitsimikizira kuti pamene munthu apereka pemphero lowona mtima lachikhulupiriro, “Wakumva pemphero” amakhala akumvetsera! (Salmo 65:2) Koma kodi mungadziŵe motani kuti iye sali chabe wakumva wamphwayi—amene amamvetsera modekha koma osachitapo kanthu kwenikweni kapena osayankha konse?
Atatcha Mulungu kukhala Wakumva pemphero, wamasalmo anati: “Mudzatiyankha nazo zowopsa m’chilungamo, Mulungu wachipulumutso chathu.” (Salmo 65:5; yerekezerani ndi Salmo 66:19, 20.) Pamenepa, kodi nchifukwa ninji ena amalingalira kuti mapemphero awo samayankhidwa?
Zopinga Pemphero
Chifukwa chingakhale kusoŵeka kwa unansi weniweni ndi Mulungu. Achichepere ena amakaikira kukhalako kwake kwenikweniko. Ena amakhulupirira koma amamlingalira kukhala wotalikirana nawo, ndi kuti ali mkhalidwe chabe osati munthu. Pemphero limakhala chochita chomalizira pamene zoyesayesa zonse zilephera mumkhalidwe wopanikiza. “Ndimakhulupirira Mulungu,” anatero wachichepere wina Wachikatolika. “Pamene ndiri m’vuto, pamene ndifunikira chithandizo, nthaŵi zonse ndimapempha chithandizo Chake.” Wachichepere wina ananena mosabisa kuti: “Nthaŵi zina ndimapemphera kokha pamene ndimafunitsitsa chinthu china.”
Komabe, pemphero liyenera kukhala chisonyezero cha chikhulupiriro, kuwopa kwaulemu, kudzipereka, ndi chidaliro—osati chabe cha kuthedwa nzeru kapena cha chikhumbo chadyera. Ndipo sikokwanira kupemphera chifukwa chakulingalira kuti mwina Mulungu aliko. “Iye wakudza kwa Mulungu,” limatero Baibulo, “ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwereza mphotho iwo akumfuna iye.” (Ahebri 11:6) Okayikakayika samayankhidwa mapemphero awo. (Yakobo 1:6-8) Yehova amamvetsera kwa amene afikira pakumdziŵa ndi kumkonda; amene samapemphera kokha pamene apanikizika. Monga momwe 1 Atesalonika 5:17 akufulumizira, iwo ‘amapemphera kosaleka,’ kapena monga momwe An American Translation imanenera, iwo “samaleka konse kupemphera.”
Mwachisoni, achichepere ena Achikristu afikira pakudziŵa Yehova koma sanakulitsedi ubwenzi ndi iye. (Salmo 25:14) Mapemphero awo amakhala oŵerengeka ndi akamodzikamodzi, osagwira mtima, ndi osayankhidwa. Kodi ndimmene ziliri ndi mapemphero anu? Ngati ndichoncho, “yandikirani kwa Mulungu” mwakumdziŵa. (Yakobo 4:8) Alyssa wachichepere uja, wotchulidwa poyamba, anali ndi zikayikiro zake ponena za Yehova. Koma phunziro Labaibulo laumwini pang’onopang’ono linafafaniza zikayikiro zake ndi kumthandiza kukulitsa unansi ndi Mulungu.
Kaimidwe kamaganizo ka munthu ndi mkhalidwe wake zingakhalenso zopinga zazikulu za pemphero. Wamasalmo anati: “Ndikadasekera zopanda pake m’mtima mwanga, [Yehova, NW] sakadamvera.” (Salmo 66:18; Miyambo 15:29) Kodi kukakhala kwanzeru kuyembekezera Mulungu kuyankha mapemphero anu ngati munali kuchita zinthu zomkwiyitsa—kugwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa, kusuta, kumvetsera nyimbo zoluluzika, kapena kuchita chisembwere? Kutalitali. Chotero Yehova amakana mapemphero a awo amene amakhala ndi moyo wapaŵiri, ‘akumabisa amene ali’ mwachinyengo. (Salmo 26:4) Iye amamvetsera kokha “wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zowonadi mumtima mwake.” (Salmo 15:1, 2) Chotero ngati mukhala ndi lingaliro lakuti mumadzilankhuza nokha pamene mukupemphera, dzipendeni nokha. Mwinamwake mufunikira kupanga masinthidwe.
Kugwiritsira Ntchito Pemphero Molakwa
Kodi ndizinthu zotani zimene mungapemphe kwa Mulungu? Yesu akutitsimikizira kuti: “Ngati mudzapempha atate kanthu [kalikonse, NW] adzakupatsani inu m’dzina langa.” (Yohane 16:23) Liwu lodabwitsa limenelo—kanthu kalikonse! Kodi Mulungu amangokulabadirani m’kalikonse mofanana ndi nyanga yamatsenga? Kodi iye adzayankha pempho lanu lirilonse, ngakhale pakanthu kakang’ono? Yesu analankhula mawu akewo patangotsala maola oŵerengeka asanafe imfa yake yoŵaŵa. Ndithudi iye sanakhale ndi nkhaŵa zopanda pake! Chifukwa chake Yakobo 4:3 amachenjeza ponena za kugwiritsira ntchito pemphero molakwa. Iye amati: “Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.”
Ambiri lerolino amagwiritsira ntchito molakwa mwaŵi wa pemphero. Timu ina ya mpira wa basketball inkagwada pansi pakati pa bwalo loseŵerera ndi kupemphera pambuyo pa mpikisano uliwonse. Koma kodi muganiza kuti Mulungu alidi wochemerera mpira wa basketball kapena kuti angapereke chisamaliro pamaseŵera opikisana? (Yerekezerani ndi Agalatiya 5:26.) Kapena bwanji ponena za mkazi Wachikatolika amene akusimbidwa kuti amapempherera nsapato? “Nthaŵi zina sitolo la nsapato lingatsale ndi peyala imodzi kapena aŵiri okha a nsapato za saizi yanga,” iye akutero, “ndipo ngati nthaŵi yomweyo ndiribe ndalama, ndimapempha Mulungu kuti zidzakhalepo pamene ndipeza ndalamayo.” Pamenepa, kupemphera kaamba ka kusoŵa nkosiyana kotheratu ndi kuyembekezera Mulungu kukupezerani zinthu zogula.
Mofananamo, kukakhala kosayenera—ndi kopanda pake—kupemphera kwa Mulungu kuti akutchinjizireni kuchilango chokuyenerani kapena kudzudzulidwa. (Ahebri 12:7, 8, 11) Ndipo simungakhale ndi chipambano kwenikweni ngati mupempha Mulungu kuti akupezetseni giredi yabwino pamayeso amene simunakonzekere mokwanira kapena kusakonzekera konse.—Yerekezerani ndi Agalatiya 6:7.
Mapemphero “Monga mwa Chifuniro Chake”
Mtumwi Yohane akufotokoza mfundo yofunika ponena za pemphero kuti: “Uku ndi kulimbika mtima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera.” (1 Yohane 5:14) Pemphero lachitsanzo la Yesu (Pemphero la Ambuye) limasonyeza zina za zinthu zimene pemphero loterolo lingaphatikizepo. Iye anapempherera (1) kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu, (2) kudza kwa Ufumu wa Mulungu, (3) kuchitidwa kwa chifuniro cha Mulungu, (4) kuperekedwa kwa zosoŵa zakuthupi ndi zauzimu, ndi (5) chithandizo chakupeŵa misampha ya Satana.—Mateyu 6:9-13.
Pamaziko ameneŵa, ziripo nkhani zina zoyenera zimene munthu angapempherere. Ndithudi, 1 Petro 5:7 amafulumiza Akristu ‘kutaya pa Mulungu nkhaŵa zawo zonse, pakuti iye asamalira iwo.’ Zimenezo zikutanthauza kuti nkoyenera kupempherera kwenikweni mbali iriyonse ya moyo wathu. Kodi mufunikira kupanga chosankha, monga ngati kusankha makosi anu apasukulu? Pemphererani nzeru yaumulungu. (Yakobo 1:5) Kodi munachitapo cholakwa chopusa? Pamenepo pemphani chikhululukiro cha Mulungu.—Yesaya 55:7; 1 Yohane 1:9.
Koma muyenera kuchita mogwirizana ndi pemphero lanu. Talingalirani wachichepere Clint. Iye anakhala mlaliki wanthaŵi zonse atamaliza sukulu yake yasekondale. Kwa miyezi yambiri sanathe kupeza aliyense wokondwerera kuphunzira Baibulo. Chotero anaika nkhaniyo m’pemphero. Komabe, sanayembekezere munthu wofuna kuphunzira Baibulo kubwera mozizwitsa. Anapitirizabe mwakhama kugogoda pamakomo, ndipo m’kupita kwa nthaŵi anapeza anthu angapo ofunitsitsa kuphunzira Baibulo.
Mmene Mulungu Amayankhira
Nthaŵi zina kupemphera kwenikweniko kumathandiza. Sandy wachichepere anali kulimbana ndi vuto lakuchita psotopsoto. Msungwanayo akuti: “Kupemphera ndi kuitanira pa Yehova kumandithandiza chifukwa ndimadziŵa kuti nditampempha kundithandiza kusachita psotopsoto, ndibwino kuti ndisachite.”
Komabe, nthaŵi zina kumawoneka monga ngati kuti Mulungu amayankha mapemphero mwakuchititsa zinthu zina. Ken wachichepere panthaŵi ina anafunikira kupita ku Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova kukapereka nkhani ya Baibulo yaifupi imene anagaŵiridwa. Mwatsoka, panalibe amene anali wokhoza kumnyamula m’galimoto. Anapempherera nkhaniyo ndi mtima wonse. Patapita mphindi zoŵerengeka mchemwali wake, amene sankamchezera kaŵirikaŵiri, anafika. Ngakhale kuti analibe chikondwerero m’chipembedzo chake, anampititsa. Yankho lachindunji kupemphero lake? Mwinamwake. Mulimonse mmene zingakhalire, nkoyenera nthaŵi zonse kuyamikira Mulungu pamene zinthu zitiyendera bwino. Paulo anafulumiza kuti: “M’zonse yamikani.”—1 Atesalonika 5:18.
Komabe, musayembekezere kuti Mulungu adzayankha mapemphero anu mwanjira yodabwitsa. Ndiponso simuyenera kuyesa kanthu kakang’ono kokuchitikirani kalikonse kukhala chisonyezero cha chifuniro cha Mulungu. Mapemphero athu kaŵirikaŵiri amayankhidwa m’njira zosadziŵika: Zingakhale mwakuŵerenga kanthu kena m’Baibulo kapena mabuku ofotokoza Baibulo; kholo kapena bwenzi Lachikristu kukupatsani uphungu. Ndithudi, pangafunikire kulingalira mwakuya kuti mudziŵe chimene chiri chifuniro cha Mulungu kwa inu. Kaŵirikaŵiri zinthu zimadziŵika m’kupita kwanthaŵi.
Inde, nthaŵi! Musayembekezere Mulungu kukupatsani yankho pamene inuyo mukulingalira kuti ayenera kutero. “Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova,” analemba motero Yeremiya. (Maliro 3:26) Ndiponso, simuyenera kukhala wotsimikizira kulandira yankho limene mulikhumba. Mtumwi Paulo anapempha Mulungu katatu kuti amchotsere chimene anatcha “munga m’thupi.” Yankho la Mulungu linali iyayi. (2 Akorinto 12:7-9) Komabe, Paulo sanataye chiyamikiro cha mphatso ya pemphero koma anapitirizabe muutumiki wa Yehova. Analinso iye amene analemba kuti: “Chitani khama m’kupemphera.” (Akolose 4:2) Chotero ‘pemphanibe, . . . funafunanibe, ndipo . . . gogodanibe.’ (Mateyu 7:7) Mwakutero, mudzayandikira kwa Mulungu, ndipo mungalandire bwino lomwe mayankho a mapemphero anu.
[Zithunzi patsamba 15]
Pemphero siliyenera kukhala la mapempho opanda pake a zinthu zakuthupi