Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 11/8 tsamba 10-11
  • Tanthauzo Lenileni la 1914

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tanthauzo Lenileni la 1914
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 1914 Iyambitsa Nthaŵi ya Nsautso
  • Ufumu wa Mulungu Uyamba Kulamulira Pakati pa Adani Ace
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kodi Chiwonongeko cha Dziko Chonenedweratucho Chidzadza Liti?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Kodi Dongosolo Lamakonoli Lidzakhala Kwautali Wotani?
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Mbadwo Wa 1914—Kodi Nchifukwa Ninji Uli Wapadera?
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 11/8 tsamba 10-11

Tanthauzo Lenileni la 1914

MONGA momwe tsamba 4 likusonyezera, “magazini ino imalimbikitsa chidaliro mu lonjezo la Mlengi la dziko latsopano lamtendere ndi losungika mbadwo umene unawona zochitika za 1914 usanathe.”

Mosakayikira oŵerenga athu ambiri amaona mawuwo kukhala odabwitsa. Komabe, kalelo mu December 1879—pafupifupi zaka 35 isanafike 1914—Nsanja ya Olonda (yotchedwa Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence panthaŵiyo) inapereka umboni wa Baibulo wosonyeza kuti chaka cha 1914 chikakhala chofunika kwambiri. Ngakhale 1879 isanafike—chapakati pa zaka za zana la 19—ophunzira Baibulo ena anali atatchulapo kuti mosakayikira chaka cha 1914 chinasonyezedwa mu ulosi wa Baibulo.a

Ulosi wafotokozedwa kukhala mbiri yolembedwa pasadakhale. Mbali imeneyi ya Baibulo imapereka umboni wakuti linachokera kwa Mulungu. Kuwonjezera pa kutiuza za zochitika za mtsogolo, Baibulo nthaŵi zina limatchula utali wa nthaŵi imene idzapitapo chinthu china chisanachitike. Ena a maulosi akutiakuti ameneŵa amanena za masiku angapo, ena zaka, ndipo ena zaka mazana ambiri.

Danieli, amene analosera za nthaŵi ya kuonekera koyamba kwa Mesiya, anavumbulanso nthaŵi pamene Mesiya akabweranso kaamba ka “kukhalapo” kwake imene imatchedwa “nthaŵi ya chimaliziro.” (Danieli 8:17, 19; 9:24-27) Ulosi wa Baibulo umenewu umakuta nyengo ya nthaŵi yaitali, osati chabe zaka mazana angapo, koma zaka zoposa zikwi ziŵiri—zaka 2,520! Pa Luka 21:24, Yesu amatcha nyengo imeneyi “nthaŵi zawo za anthu akunja.”b

1914 Iyambitsa Nthaŵi ya Nsautso

Kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo kumasonyeza kuti takhala tili m’nthaŵi ya mapeto kuyambira 1914. Yesu anafotokoza nthaŵi imeneyi kukhala ya “zoŵaŵa zoyamba.” (Mateyu 24:8) Pa Chivumbulutso 12:12, timaŵerenga kuti: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa [M]dyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” Zimenezi zikufotokoza chifukwa chimene dziko lakhalira m’chipwirikiti chachikulu chiyambire 1914.

Komabe, nthaŵi ya mapeto imeneyi ili nyengo yaifupi kwambiri—yokuta mbadwo umodzi. (Luka 21:31, 32) Kukhalapo kwathu kwa zaka 80 tsopano pambuyo pa 1914 kukusonyeza kuti tingayembekezere chilanditso posachedwa chimene Ufumu wa Mulungu udzabweretsa. Zimenezi zikutanthauza kuti tidzaona “wolubukira anthu”—Yesu Kristu—akutenga ulamuliro wonse wa “ufumu wa anthu” ndi kudzetsa dziko latsopano lamtendere, ndi lolungama.—Danieli 4:17.

[Mawu a M’munsi]

a Mu 1844, mtsogoleri wachipembedzo Wachibritishi, E. B. Elliott, anasumika maganizo pa 1914 kukhala deti lothekera la mapeto a “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri” za m’Danieli chaputala 4. Mu 1849, Robert Seeley, wa ku London, analongosola nkhaniyo mofananamo. Joseph Seiss, wa ku United States, anasonyeza 1914 kukhala deti lofunika kwambiri m’kuŵerengera zaka kwa Baibulo m’chofalitsidwa chokonzedwa pafupifupi mu 1870. Mu 1875, Nelson H. Barbour analemba m’magazini ake a Herald of the Morning kuti 1914 inali mapeto a nyengo imene Yesu anatcha “nthaŵi zawo za anthu akunja.”—Luka 21:24.

b Kuti mupeze malongosoledwe atsatanetsatane a ulosi wa Danieli, onani Kukambitsirana za m’Malemba, masamba 231-33, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Bokosi patsamba 11]

Ndemanga Zonena za 1914 ndi Pambuyo Pake

“Mwinamwake, pambuyo pa nkhondo zadziko ziŵiri zooneka kukhala zosapeŵeka, kupangidwa kwa zida za nyukliya kunali chenjezo, limene linatipulumutsa pa nkhondo yachitatu ya mitundu yaikulu ndi kuyambitsa nyengo yaitali koposa ya mtendere wofala, ngakhale kuti uli mtendere wa mantha, kuyambira m’nthaŵi za Mfumukazi Victoria. . . . Kodi chinalakwika nchiyani ndi anthu? Kodi nchifukwa ninji chiyembekezo cha m’zaka za zana la khumi ndi chisanu ndi chinayi chinatayika? Kodi nchifukwa ninji zaka za zana la makumi aŵiri zinakhala nyengo ya mantha kapena, monga mmene ena anganenere, yoipa?”—A History of the Modern World—From 1917 to the 1980s, lolembedwa ndi Paul Johnson.

“Pa masinthidwe onse ogwedeza dziko a dongosolo la Ulaya, Nkhondo Yaikuluyo ndi kukhazikitsidwa kwa mtendere zinadzetsa mwadzidzidzi mkhalidwe wosiyana kwambiri ndi wakale, m’zachuma ndi zakakhalidwe limodzinso ndi zandale. . . . Ulemerero wosangalatsa wa dongosolo lobala zipatso ndi logwira ntchito mwaufulu limenelo unazimiririka m’nkhondo yosakazayo. Mmalomwake, Ulaya anakakamizika kulimbana ndi kuchepa kwa chuma ndi kugwedezeka konse kwa zachuma. . . . Kuwonongekako kunali kwakukulu kwambiri kwakuti chuma cha Ulaya sichinakonzeke nkhondo yadziko yotsatira isanayambe.”—The World in the Crucible 1914-1919, lolembedwa ndi Bernadotte E. Schmitt ndi Harold C. Vedeler.

“M’Nkhondo Yadziko Yachiŵiri chomangira chilichonse pakati pa anthu chinawonongedwa. Maupandu anachitidwa ndi Ajeremani pansi pa ulamuliro wa Hitler umene anagonjera umene ukulu ndi kuipa kwake zili zosalingana ndi za wina uliwonse umene waipitsa mbiri ya anthu. Kupululutsidwa mwa mchitidwe wolinganizidwa kwa mamiliyoni asanu ndi limodzi kapena asanu ndi aŵiri a amuna, akazi ndi ana m’misasa yophera ya ku Germany kumaposa kupha kwauchinyama kwa Genghis Khan, ndipo ukulu wake umakuposeratu. Kupululutsa dala mafuko athunthu kunalinganizidwa ndi kuchitidwa ndi Germany ndi Russia yemwe m’nkhondo ya Kummaŵa. . . . Pomalizira pake tatuluka m’chochitika chosakaza zinthu ndi chowononga makhalidwe chimene anthu a m’zaka mazana ambiri apitawo sanachilingalirepo konse.”—The Gathering Storm, Voliyumu I ya The Second World War, lolembedwa ndi Winston S. Churchill.

“Tsopano zoyenera za anthu a magulu onse, mitundu, ndi mafuko zikuzindikiridwa; komabe taloŵa m’kulimbana kwa magulu, utundu, ndi ufuko woipa kwambiri umene mwinamwake sunachitikepo. Mzimu woipa umenewu umasonkhezera nkhanza zauchinyama zolinganizidwa ndi sayansi; ndipo mkhalidwe woombana umenewu ndi miyezo imeneyi ya khalidwe zilipo lerolino, zonse pamodzi, osati chabe padziko lonse lapansili, koma nthaŵi zina m’dziko limodzimodzi ndipo ngakhale mwa munthu mmodzimodzi.”—Civilization on Trial, lolembedwa ndi Arnold Toynbee.

“Monga mzukwa umene unapyola panthaŵi yoikika, zaka za zana lakhumi ndi chisanu ndi chinayi—ndi bata lake lalikulu, kudzidalira kwake, ndi chikhulupiriro chake m’chitukuko chaumunthu—zinakhalapobe kufikira mu August 1914, pamene maulamuliro aakulu a ku Ulaya onse anachita misala imene inachititsadi kuphedwa kwankhanza kwa mbadwo wa achichepere abwino koposa okwanira mamiliyoni ambiri. Zaka zinayi ndi theka pambuyo pake, pamene dziko linayesa kubwezeretsa mtendere pambuyo pa tsoka losakaza la Nkhondo Yaikulu, kunakhala koonekeratu kwa openyerera ambiri a panthaŵiyo (koma osati onse) kuti zizindikiro zomalizira zotsala za dongosolo lakalelo zinali zitafafanizidwa, ndi kuti mtundu wa anthu unali utaloŵa m’nyengo yatsopano imene kumlingo wokulira inali yosamvetsetsa ndi yosakhululukira kupanda ungwiro kwa munthu. Awo amene anayembekezera kuti mtendere ukadzetsa dziko labwino anapeza kuti ziyembekezo zawo zinagwiritsidwa mwala mu 1919.”—Mawu oyamba m’buku la 1919—The Year Our World Began, lolembedwa ndi William K. Klingaman.

[Chithunzi patsamba 10]

Mapiri a Alps a ku Bavaria

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena