Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 5/8 tsamba 17-19
  • Kodi Kuthaŵa Kuli Yankho?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kuthaŵa Kuli Yankho?
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chimene Chimachitika Kaŵirikaŵiri
  • Kodi ndi Zosankha Zotani Zimene Ziripo?
  • Nchifukwa Ninji Pali Ana Othaŵa Ambiri?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Otayidwa ndi Othaŵa Kwawo
    Galamukani!—1995
  • Mmene Mungalimbitsire Zomangira za Banja
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Zakumapeto
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 5/8 tsamba 17-19

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Kuthaŵa Kuli Yankho?

MU BUKHU lakuti Tom Sawyer, mkonzi Mark Twain akunena za nthaŵi imene Tom anathaŵa kuchoka panyumba ndi mabwenzi ake apamtima, Joe Harper ndi Huckleberry Finn. Anyamata atatuwo anathaŵa pakati pa usiku, akumayenda ndi bwato ku chisumbu cha kutali ku mbali ina ya mtsinje. Kumeneko iwo anatsiriza mbali yabwino ya mlungu, akumakhala ndi zakudya zimene anabwera nazo ndi nsomba zomwe iwo anagwira. Mwamsanga iwo anadzakhala owonerera ku chochitika cha anthu a mu mzindawo akumafufuza mtsinjewo kaamba ka matupi awo “omirawo.” Potsirizira pake, Tom, Joe, ndi Huck anathaŵa kubwerera ku mzindawo, anabisala m’chipinda chowonetsera cha tchalitchi, ndi kuchitira umboni kachitidwe ka kuika maliro awo. Chochitikacho chinatha ndi iwo kukhala atagwirizanitsidwa mwachimwemwe ndi banja ndi mabwenzi, ndi kuwapsyompsyona ndi kusonyeza kuyamikira.

Kwa Tom, Joe, ndi Huck, kuthaŵa kunali kachitidwe kochezera malo koseketsa ndi kokhala ndi mathedwe achimwemwe. Kunali kosangalatsa. Chimenecho sichiri tero ndi achichepere ambiri omwe amathaŵa lerolino. “Kwa othaŵa kwawo ambiri, vuto liri kalongosoledwe kapadera ka moyo kochititsa kuthaŵa,” watero Margaret O. Hyde m’bukhu lake lakuti My Friend Wants to Run Away. “Othaŵa kwawo oŵerengeka m’chenicheni amapeza ntchito ndi kudzikhalira iwo eni. Koma, kwa ambiri a iwo, moyo umaipirako kuposa mmene unaliri poyamba asanachoke kunyumba.”

Mwinamwake inu mukudzimva kuti mudzakhala osiyanako. Ndithudi, zinthu zidzakhala bwino kuposa mkhalidwe umene ulipo panyumba. Amy analingalira tero. Iye anathaŵa pamene anali ndi zaka zakubadwa 14 chifukwa chakuti anasowa kuyanjana kwathithithi ndi makolo ake ndipo sanakhoze kulankhula ndi iwo. “Ndinadzimva kuti panalibe aliyense yemwe anakhoza kundimvetsetsa ine,” iye anatero. “Ndinadzimva kuti kukhala kutali kuchoka kwa makolo anga ndi kupita kunyumba ya ‘bwenzi’ kukakhala bwino. Ndinali wotsimikiza kuti ‘bwenzi’ langa likamvetsetsa.”

Sandi, atakanidwa ndi amayi ake ndi kuipsyidwa ndi agogo ake amuna omlera, anathaŵa pamene anali wa zaka 12. Peggy anachoka panyumba ali wa zaka 16. “Ndakhala ndi zodidikiza zochulukira panyumba,” iye anatero. “Amayi anga ankafuula kwa ine kwambiri ndi kundiitana ine ndi maina oipa.” Amayi ake anampangitsa iye kudzimva kukhala wosafunidwa ndi wosakondedwa, “ngati kuti anakhumba kuti chikanakhala bwino ngati iye sanabadwe kapena chinachake.” Atakhala wosakhoza kulankhula kwa amayi ake popanda kupikisana ndipo akumaikidwa pansi mosalekeza ndi kupangidwa kukhala monga chitsiru, iye anathaŵa kukafunafuna kaamba ka chimwemwe kwinakwake.

Julie anathaŵa chifukwa chakuti kwa zaka zingapo anakhala akuipitsidwa mwa kugonana panyumba. Danny anathaŵapo kaŵiri. Nthaŵi yoyamba inali ya kufuna kupewa amayi wake opeza omwe ananena zinthu zoipa ponena za iye. Iye mwamsanga anazindikira mmene chinaliri chovuta kunja popanda chirikizo lirilonse, chotero iye anabwerera kunyumba—kokha kungodzafikira mu kukangana koipa ndi kukanidwa ndi atate ake kachiŵirinso. Onse aŵiri Julie ndi Danny anali kokha zaka 12 zakubadwa.

Inde, moyo panyumba kwa othaŵa kwawo ambiri umawoneka wosapiririka. Amafuna kuchoka ku iwo. Amafuna kukhala aufulu. “Koma a zaka zakubadwa za pakati pa 13 ndi 19 samapeza ufulu m’makwalala,” inadziŵitsa tero magazini ya ’Teen. “M’malomwake, amangopeza othaŵa kwawo ena kapena otaidwa—monga iwo eni—akumakhala m’nyumba zokanidwa, kumene sakhala ndi chitetezero chirichonse kwa ogwirira chigololo kapena achifwamba. Iwo amapezanso anthu ochulukira omwe amachipangitsa icho kukhala malonda awo kudyerera anthu achichepere, ndipo a zaka zapakati pa 13 ndi 19 othaŵa kwawo amakhala minkhole yopepuka.”

Chimene Chimachitika Kaŵirikaŵiri

“Bwenzi” la Amy, mwachitsanzo, mwamuna wa zaka zakubadwa 22 linamlora iye kulipira kaamba ka kukhala kwake “mwa kugonana ndi iye ndi mabwenzi ake ena asanu ndi anayi.” Iye “analedzeranso ndi kumwa anamgoneka ambiri.” Sandi anakhala mkazi wadama, akumakhala m’makwalala ndi kugona m’mabenchi a m’mapaki kapena kulikonse kumene iye anakhoza. Izo ziri zapadera kaamba ka othaŵa kwawo ambiri. Nchifukwa ninji chimachitika mwa njira imeneyo?

“Pamene mwana athaŵa kwa nthaŵi yoyamba, iye angakhoze kukhala ndi ndalama zochepera m’thumba lake, iye angakhozenso kukhala atasunga ndalama zina, koma mwamsanga zitatha, iye amakhala ndi zosankha zoŵerengeka,” analongosola tero Sajenti Jose Elique, yemwe kale anali mtsogoleri wa New York’s Port Authority Runaway Squad Police. “Pamene achichepere amamva njala, iwo amafunikira kudya, ndipo pamene amva kuzizira, iwo amafunikira kupeza chipinda, chotero iwo ndithudi alibe zofunikira kuchita zambiri. Ngati chichitika kuti winawake anawafikira iwo pamene iwo ali kwenikweni ndi njala ndi otopetsedwa ndi kuwafunsa iwo kuchita chinachake—icho chikakhala nambala iriyonse ya zochita zosakhala za lamulo kapena mikhalidwe yoipitsidwa, kaamba ka ndalama kapena anamgoneka—kenaka mwana ameneyu akakhala womvetsera kwenikweni, mosasamala kanthu ndi mmene iye angakhalire atadzimverera ponena za kugonana ndi anamgoneka poyambapo.”

Othaŵa kwawo ambiri ali ndi kuyeneretsedwa kokhoza kupeza chuma kochepera. Iwo amapeza chitaganya chamakono kukhala kokha chovutirapo kwenikweni ndi chocholowanacholowana kuchita nacho. Iwo nthaŵi zambiri samakhalanso ndi kuyeneretsedwa kwabwino kwa ntchito yolemba iriyonse yakuti alembedwe nayo: Alibe chipepala chosonyeza masiku akubadwa, kardi ya chisungiko cha mayanjano, keyala yokhazikika. “Ndinafunikira kuba, kupemphapempha,” anatero Luis, “koma makamaka kuba chifukwa chakuti palibe aliyense amene angakupatse chirichonse kunja kumeneko.” Maperesenti 60 a othaŵa kwawo ali atsikana. “Nchiyani chimene mtsikana wa zaka za kubadwa 13 angachite pambali pa kungosonyeza thupi lake?” anafunsa tero mtsikana mmodzi. Iye anapatsidwa ndalama zambiri kaamba ka kuvula thupi lake. Mwachidziŵikire kwenikweni zithunzithunzi zimenezo zikagwiritsiridwa ntchito pambuyo pake monga kulanda kwa chinyengo kumpangitsa iye kuti achite zochulukira.

Ojambula zithunzithunzi za maliseke, ogulitsa anamgoneka, ndi adama amayendayenda pokwerera mabasi akumayang’ana kaamba ka othaŵa kwawo kuti awadyere masuku pamutu. Iwo ali akatswiri a kusonkhezera. Iwo amalonjeza achichepere owopsyezedwawo malo ogona ndi zakudya zokadya. Iwo amawapatsa iwo chomwe amasowa panyumba—kudzimva kwakuti iwo alidi apadera ndi okondedwa. Iwo amadziŵitsidwa kwa achichepere ena, ophatikizidwamo kale, omwe amawalonjera iwo kuwapanga kudzimva olandirika. Pang’onopang’ono iwo amazoloŵera. Wadama angakhoze ngakhale kukonzekera kaamba ka wina kuti achite chigololo chogwirira kwa mtsikanayo ndipo kenaka kulonjeza kumtetezera iye kuti chimenecho chisadzachitikenso. Kapena kuti angakhoze kuyambitsa wa zaka zakubadwa za pakati pa 13 ndi 19 ku anamgoneka, kumamumwereketsa iye, ndipo kenaka kukakamiza kuti iye agwire ntchito kaamba ka iye ngati iye akufuna kupitiriza kupeza zoperekedwa zake. Ena amadalira pa kumenya kapena kukakamiza kwachifwamba kuti apeze njira yawo. Monga mmene chingalingaliridwe, othaŵa kwawo ambiri amangothera m’kuvulazidwa kapena ngakhale kufa.

Kodi ndi Zosankha Zotani Zimene Ziripo?

Wachichepere wa zaka za pakati pa 13 ndi 19 yemwe akulingalira za kuthaŵa angadzimve kuti pali zosankhapo zoŵerengeka, makamaka ngati iye ali wosafunidwa kapena wosalandiridwa panyumba. Oterowo amatchedwa othamangitsidwa kapena otaidwa. Ndiponso, achichepere ambiri othaŵa amadziŵa kuti atapezedwa ndi apolisi, makolo awo adzawuzidwa, ndipo mwachidziŵikire kwenikweni adzatumizidwa kunyumba. Ndipo ngati mkhalidwe kunyumba sunasinthe, iwo adzathaŵanso. Komabe, kuchepera kumene iwo ali ndi kutalikira kumene iwo amakhala pa msewu, kumakhalanso kuthekera kochulukira kwa mavuto. Chotero yankho limafunika kupezedwa.

Choyamba, yesani kugwirirapo ntchito panyumba. Pangani kuyesayesa kulikonse—ndipo chimenecho chimatanthauza kuposa kamodzi kokha—kulankhula ndi makolo anu. Aloleni adziwe mmene mumadzimverera ndi chimene chikuchitika. Ngati chimenecho chalephera, lankhulani kwa winawake yemwe angathandize. Achichepere ena alankhula kwa m’phungu wawo wa ku sukulu, wogwira ntchito ya mayanjano, kapena woyang’anira pa ntchito ya achichepere. Ena agwiritsira ntchito magulu ofunsira uphungu aulere omwe akhazikitsidwa m’maiko ena kuthandiza ponse paŵiri makolo ndi ana. Achichepere Achikristu, ngakhale ndi tero, akhala ndi mwaŵi wa kutembenukira kwa akulu mu mpingo wawo ndi kulandira thandizo lachikondi, laumwini ndi uphungu wozikidwa m’Baibulo. Koma kumbukirani mawu a mfungulo: KULANKHULA. Chiri chinthu chimene chidzathandiza ponse paŵiri inu ndi makolo anu. “Zolingalira zirimidwa popanda upo,” likutero Baibulo, “koma pochuluka aphungu zikhazikika.”—Miyambo 15:22.

Chokwaniritsidwa chingakhale umoyo wa panyumba woongokera womwe udzakupatsani inu chiyembekezo kaamba ka mtsogolo. Iko kungakonzenso zironda zakale ndi kusindikiza kudzimva kwa kukhulupirika, chikondi, ndi chimwemwe. Inu mudzakumva kuyenera kwanu monga munthu. Ngakhale ngati moyo panyumba sungakhale wosangalatsa, sungani m’malingaliro kuti zinthu zoipa kwenikweni zingachitike pamene muthaŵa.

Uliwonse umene uli mkhalidwe wanu, kumbukirani kuti nthaŵi zonse kuli Winawake yemwe amasamala ndi yemwe angakonde kuthandiza. Awo omwe amatembenukira kwa Mulungu angatsimikiziridwe za thandizo lake ndi chinjirizo.—Miyambo 18:10.

[Chithunzi patsamba 19]

Winawake angakulonjezeni inu chakudya, chipinda, ndi nthaŵi yabwino. Koma kodi nchiyani chimene iye akufuna m’kubwezera?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena