Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 7/8 tsamba 3-4
  • Kodi Nchiyani Chimene Chikuchitikira Agogo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchiyani Chimene Chikuchitikira Agogo?
  • Galamukani!—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ena a Mavutowo ndi Otani?
    Galamukani!—1995
  • Kodi Nditani Kuti Ubale Wanga ndi Agogo Ulimbe?
    Galamukani!—2001
  • Kukhala Pamodzi Mwachikondi
    Galamukani!—1995
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kudziŵana ndi Agogo Anga?
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 7/8 tsamba 3-4

Kodi Nchiyani Chimene Chikuchitikira Agogo?

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU ITALY

“Monga gogo wachimuna, sindinakhulupirire kuti ndidzachitiridwa mwachikondi choncho ndi zidzukulu zanga. Iwo ali mphatso—nthumwi zolimbikitsa mgwirizano wachikondi, zokoma mtima, ndi zoona mtima.”—Ettore, gogo wachimuna.

MOSASAMALA kanthu za unansi wabwino wonenedwawu, agogo, makolo, ndi zidzukulu samagwirizana nthaŵi zina masiku ano. M’malo mwa kugwirizana, kaŵirikaŵiri mibadwo itatuyi imawombana. Ndi zotulukapo zotani? Kuwonjezereka kwa kukhala okha ndi chisoni pakati pa okalamba, agogo—ziŵalo za banja zimene kaŵirikaŵiri zimakhala zofooka kwambiri ndi zopatulidwa, zimene nthaŵi zina ziŵalo za banja zimatembenukirako pamene zili m’mavuto andalama. Kodi mkhalidwewo ngwotani m’banja mwanu? Kodi agogo amaŵerengeredwadi?

M’zaka makumi angapo zapitazo, kusintha koonekeratu kwa kakhalidwe padziko lonse kwayambukira banja ndi maunansi ake, zikumachititsa kuti banja limene mphamvu yake ili kuchimuna litsale pang’ono kuzimiririka. Ku Ulaya, anthu okalamba 2 peresenti okha amakhala ndi ana awo. Ngakhale zili choncho, chifukwa cha kuwonjezereka komwe kulipo kwa avareji ya utali wa moyo ndi kutsika kwa chiŵerengero cha obadwa, chiŵerengerocho cha agogo ndi anthu onse chikuwonjezereka mosalekeza m’maiko otukuka. Agogo aakazi ndi aamuna amapanga 26 peresenti ya anthu a ku Ulaya, ndipo malinga ndi zopendedwa zimene zinafalitsidwa ndi European Union, chiŵerengerocho “chidzakula.” Japan, ikutero Asahi Evening News, “ndi wonyadira mwambo wake wa kusamalira nzika zake zokalamba.” Komabe, pali chizoloŵezi chimene chikufala mowonjezereka, makamaka m’mizinda, cha kusiya agogo m’zipatala ndi m’makiliniki apadera ngakhale pamene munthuyo ali wosafunikira kwenikweni kuikidwa m’chipatala. Nakonso ku South Africa, kumene mwamwambo anthu okalamba anali kulemekezedwa, tsopano kuli chikhoterero choipa cha kutaya okalamba, malinga ndi kunena kwa nyuzipepala ina ya ku Cape Town The Cape Times. Lipotilo likusonyeza kuti mabanja akufuna “kusangalala ndi moyo monga momwe angathere” ndipo “akudzinyenga kwambiri ndi maganizo akuti pamene aika agogo kunyumba yosungirako okalamba, ndiye kuti achita zonse zimene ayenera kuchita.”

Nyuzipepala imodzimodziyo ikulankhula za nkhani ina yonena za gogo wina wachikazi amene waikidwa ndi ana ake atatu m’nyumba yosungirako okalamba yokhala ndi zonse, “akumalonjeza kuti adzakhala akumsamalira ndi kumamzonda nthaŵi zonse.” Koma kodi nchiyani chimene chikumchitikira? “Poyamba kuzondako kukuchitika tsiku ndi tsiku. Patapita masabata angapo kukuchepa ndi kukhala kochitidwa katatu pasabata. Ndiyeno kukukhala kwa kamodzi pasabata. Patapita chaka chimodzi kukuchitidwa kaŵiri kapena katatu pamwezi, patapita nthaŵi kukuchitidwa kasanu kapena kasanu ndi kamodzi pachaka ndipo potsirizira pake sikukuchitidwanso.” Kodi gogo wachikazi ameneyu anatha motani masiku ake onyong’onyawo? Nkhani yovutitsa mtimayo ikuti: “Chipinda chake chinali ndi zenera loonerapo mtengo wina, ndipo mabwenzi ake okha amene analipo anali nkhunda ndi mbalame za starling zimene zinateramo. Anali kuyembekezera kwambiri kufika kwawo monga ngati kuti anali achibale apafupi.”

Chifukwa cha kusintha kwa moyo wa ku South Africa Kutsatira Wakumadzulo, umene umasonkhezera ambiri kukafuna ntchito m’mizinda, chinthu chofananacho chikuchitika m’mabanja amwambo. Kuwonjezera pa kakhalidwe ka anthu komasintha, zifukwa zina zotayira agogo ndizo kuzimiririka kwa mikhalidwe yaumunthu imene imachirikiza moyo wachimwemwe wa chitaganya ndi wa banja—ubwino, kulemekeza mnansi, chikondi cha m’banja—ndi kufalikira kwa mzimu wadyera, kuika mtima pa zokondweretsa, kunyada, ndi chipanduko. Malinga ndi kunena kwa Malemba, kunyonyotsoka kwa makhalidwe abwino kumeneko ndiko chizindikiro chakuti tikukhala ndi moyo mu “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5) Motero, m’malo mwa kuŵerengera agogo awo monga magwero a kulemerera ndi bata, kaŵirikaŵiri ana ndi zidzukulu amawaona ngati chopinga chovutitsa, osayenderana ndi kusintha kofulumira m’chikhalidwe cha anthu.a

Kusiyana kwa mibadwo kukuwonjezereka kwambiri, ndipo kumachititsa mavuto aakulu, makamaka pamene anthu okalamba akukhala pamodzi ndi mabanja awo. Komabe, chichirikizo cha agogo chingakhale chopindulitsa kwambiri! Nangano kodi ndi mavuto ena aakulu ati amene ali pakati pa mibadwo yosiyana amene amadodometsa unansi wachikondi pakati pa agogo, ana, ndi zidzukulu? Ndipo kodi ndimotani mmene agogo angachitirenso mbali yawo yofunika m’banja?

[Mawu a M’munsi]

a Kuyenera kuzindikiridwa kuti m’zochitika zina chifukwa cha kufooka kwa maganizo ndi kudwaladwala kwambiri, malo osungirako okalamba okhala ndi antchito odziŵa bwino angakhale makonzedwe achikondi kwambiri ndi othandiza kwa makolo ena okalamba.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena