Inu Ogula Chenjerani! Zinthu Zopeka Zingatayitse Miyoyo
ANTHU osadziŵa, osayembekezera kalikonse angapusitsidwe. Watchi yamaonekedwe apamwambayo imene wogulitsa zinthu m’khwalala akukusonyezani pamtengo wochepa—kodi ili yeniyeni kapena yopeka? Kodi mudzagula? Khoti yambambande ya ubweya imene akukusonyezani pazenera la galimoto m’khwalala—wogulitsayo akumati ndi mink. Kodi kukongola kwake ndi mtengo wake wotsika zidzakudyani moyo moti nkulephera kuzindikira bwino? Mphete yadiamondi yomwe ili kuchala cha mkazi wosudzulidwa posachedwapa—tsopano wosoŵa ndalama ndi nyumba, akuyembekezera tireni pasiteshoni yapansi pa nthaka ku New York—mungaigule ndalama zochepa. Kodi mungaganize kuti malondawo achipa kwambiri moti simungawalekerere? Chifukwa chakuti mafunsowa abuka m’nkhaniyi yofotokoza za zinthu zopeka ndiponso chifukwa cha mikhalidwe yosonyezedwa, nzothekera kuti mudzayankha kuti “SINDINGAZIGULE AYI!”
Chabwino, tiyeni tisinthe malo ake ndi mikhalidwe tione kuti mudzayankha motani. Bwanji ponena za chikwama chodula chotchuka chokhala ndi dzina la wochipanga chimene chili paselo m’sitolo yabwinobwino pamtengo wabwino kwambiri? Wisiki wa dzina lotchuka amene akugulitsidwa m’sitolo la moŵa lapagulaye? Aaa, apa palibe chovuta. Talingaliraninso za filimu yokhala ndi dzina lodziŵika imene ili paselo m’sitolo la mankhwala kapena m’shopu ya makamera. Tsopano watchi yodula ija yogulidwa madola zikwi mwaipeza, osati kwa wogulitsa m’khwalala, koma m’sitolo yolemekezeka. Mtengo wake watsika kwambiri. Ngati munali kufuna watchi yodula imeneyo, mukanaigula kodi? Ndiyeno pali nsapato zamaina otchuka pamtengo wabwino m’shopu ina imene mabwenzi anu akusonyezani. Kodi muli wotsimikiza kuti zimenezo sizili zinthu zongoyerekezera zosalimba?
M’zamaluso ojambulajambula, mumakhala maselo aakulu akuti osunga zinthu zamtengo wake azizigula m’nyumba zoonetsera zithunzithunzi zokoka mtima. “Chenjerani,” anachenjeza motero katswiri wina wa zaluso. “Akatswiri odziŵa bwino apusitsidwa. Ngakhalenso amalonda. Ndi oyang’anira mamyuziyamu omwe.” Kodi muli wodziŵa kwambiri kwakuti mungalingane kuchenjera ndi amene angakhale opeka zinthu? Chenjerani! Zinthu zonse zotchulidwa pamwambazi zingakhale zopeka. Nthaŵi zambiri zimakhala zotero. Kumbukirani, ngati chinthu chili chosapezekapezeka ndipo nchamtengo wapatali, munthu wina kwina adzayesa kuchipeka.
Kupeka zinthu ndiko malonda opanga $200 biliyoni padziko lonse ndipo “akukula mofulumira kuposa maindasitale amene akubera,” anatero magazini a Forbes. Zitsulo zopeka za galimoto zimatayitsa opanga galimoto a ku America ndi ozigulitsa $12 biliyoni pachaka zimene zimasoŵa padziko lonse. “Maindasitale opanga galimoto a [United States] akuti akhoza kulemba ntchito anthu enanso 210,000 ngati angakhoze kuletsa ogulitsa malonda a zitsulo zonyenga,” anatero magaziniwo. Zamveka kuti pafupifupi theka la mafakitale opeka zinthu ali kunja kwa United States—paliponse.
Zopeka Zimene Zikhoza Kupha
Mitundu ina ya zinthu zopeka njowopsa kwenikweni. Manati, mabauti, ndi misomali yamazinga yoodedwa kunja imapanga 87 peresenti ya $6 biliyoni ya msika wa United States. Komabe, umboni womwe ulipo usonyeza kuti 62 peresenti ya zomangira zimenezi zili ndi maina a eni ake kapena zidindo zosayenerera zachilolezo. Lipoti la 1990 loperekedwa ndi General Accounting Office (GAO) linasonyeza kuti mu America, m’zosachepera 72 za “nyumba zamagetsi anyukiliya munali zomangira zosayenera, zina zinali m’zipangizo zotsekera makina ake otulutsa mphamvu ngati patachitika ngozi yanyukiliya. Vutolo likukulirakulira, anatero a GAO. . . . Ukulu wa vutolo, ndalama zotayidwa ndi okhoma misonkho kapena ngozi zimene zingakhalepo chifukwa chogwiritsira ntchito zinthu [zachabe] zimenezo nzosadziŵika,” inatero Forbes.
Mabauti achitsulo, amene mphamvu yake njosakwanira pa chifuno chake, apekedwa ndi kuzembetsedwa kuloŵa mu United States ndi amalonda achinyengo. “Iwo angaike pangozi maofesi, nyumba zamagetsi, maulalo ndi zida za asilikali,” malinga ndi kunena kwa American Way.
Mabuleki opeka anachititsa ngozi ya basi ku Canada zaka zingapo zapitazo imene inapha anthu 15. Zamveka kuti zitsulo zopeka zapezeka ndi m’malo osayembekezera monga mahelikoputala a asilikali ndi chombo cha m’mlengalenga cha United States. “Munthu wamba wogula zinthu savutika maganizo mukamalankhula za watchi yopeka ya Cartier kapena ya Rolex,” anatero wofufuza zinthu zopeka wotchuka, “koma pamene thanzi lanu ndi chisungiko zikhala pangozi, zinthu zimasintha.”
Zinthu zopeka zimene zingakhale zangozi zimaphatikizapo zipangizo zothandiza mtima kugunda zogulitsidwa ku zipatala 266 za mu United States; mapilisi opeka oletsa kubala amene analoŵa pamsika wa America mu 1984; ndi mankhwala ophera tizilombo, amene anali ndi choko wochuluka, amene anawononga mbewu ya khofi ku Kenya mu 1979. Pali mankhwala opeka ambiri amene angaike pangozi miyoyo ya ogula. Imfa zochitika padziko lonse chifukwa cha mankhwala opeka zingakhale zodabwitsa kuchuluka kwake.
Palinso nkhaŵa yomakula ya zipangizo zamagetsi zazing’ono za m’nyumba zopeka. “Zina za zinthu zimenezi zili ndi maina onyenga kapena zilolezo zonga zija za Underwriters Laboratory,” inatero American Way. “Koma sizopangidwa malinga ndi miyezo yachitetezo imeneyo, chotero zidzaphulika, kubutsa moto m’nyumba ndi kuchititsa chipangizo chonse kukhala changozi,” anatero injiniya wina wa zachitetezo.
Ku United States ndi ku Ulaya, makampani a ndege alinso ndi nkhaŵa. Mwachitsanzo, makampani a ndege ku Germany apeza zitsulo zopeka zakuinjini ndi kumabuleki m’mitokoma yawo. Kufufuza “kukuchitika ku Ulaya, Canada ndi United Kingdom, kumene akukhulupirira kuti zitsulo zosavomerezedwa (manati akumchira) zinachititsa ngozi yoipa posachedwapa ya helikoputala,” akuluakulu a zakayendedwe anatero. “Ofufuza agwira zitsulo zopeka zambiri za injini ya ndege, mabuleki, mabauti ndi zomangira zosalimba, mipope ya mafuta ndi zipangizo zoulukira zowonongeka, makina osayenera m’chipinda cha oyendetsa ndi mbali za makompyuta zofunika kwambiri pa chisungiko cha ndege,” inatero Flight Safety Digest.
Mu 1989 ndege yahaya yopita ku Germany kuchokera ku Norway inazyolika mwadzidzidzi kugwa kuchokera m’mwamba pamtunda wa mamita 6,600 pamene inali kuthamanga kwambiri. Chakumchira chinaguluka, chikumachititsa ndegeyo kugwa chozyolika moipa kwakuti mapiko ake onse aŵiri anaduka. Anthu onse 55 anali momwemo anafa. Patapita zaka zitatu za kufufuza, akatswiri a zandege a ku Norway anapeza kuti chimene chinachititsa ngoziyo anali mabauti osakhala bwino, otchedwa ma locking pin, amene analunzanitsa mchira wake ndi thupi lake. Kupenda nyonga yake kunasonyeza kuti mabautiwo anapangidwa ndi chitsulo chosalimba konse chimene sichikanapirira mphamvu yokoka yakuuluka. Ma locking pin osakhala bwinowo anali opeka—liwu limene akatswiri a zachitetezo cha ndege alidziŵa kwambiri kulikonse, pakuti kupeka zinthu ndiko vuto lomakula limene likuika pangozi miyoyo ya oyendetsa ndege ndi okweramo.
Pamene wailesi yakanema inafunsa insipekitala wamkulu wa Department of Transportation ku United States, iye anati: “Makampani onse a ndege alandira zitsulo zopeka. Onse ali nazo. Onse ali nalo vutolo.” Maindasitalewo akuvomereza, iye anawonjezera motero, “kuti ali ndi mitokoma ya zitsulo zosagwira ntchito imene mtengo wake uli ngati madola mabiliyoni aŵiri kapena atatu.”
Pakufunsa kumodzimodziko, mlangizi wa zachitetezo cha ndege, amene anauza a FBI za malonda achizembera a zitsulo zopeka, anachenjeza kuti zitsulo zopekazo zili zangozi kwenikweni. “Ndiganiza mosapeneka kuti tsiku lina mtsogolomu tidzakhala ndi ngozi yaikulu ya ndege chifukwa cha zimenezi,” iye anatero.
Tsiku layandikira loŵerengera mlandu aja amene umbombo wawo umawalola kuika zikhumbo zawo zadyera patsogolo m’malo mwa miyoyo ya ena. Mawu ouziridwa a Mulungu amanena motsimikiza kuti anthu aumbombo sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.—1 Akorinto 6:9-10.
[Zithunzi patsamba 29]
Wopeka zinthu angapezerepo phindu pa zovala, majuwelo, zojambula, mankhwala, zitsulo za ndege—chilichonse chamtengo
[Chithunzi patsamba 30]
Zitsulo zopeka za injini, mabauti osalimba, makina a m’chipinda cha oyendetsa ndege, mbali zina za makompyuta, ndi zitsulo zina zopeka zachititsa ngozi zimene zatayitsa miyoyo