Khalani ndi Lingaliro Loyenera la Nyimbo
NYIMBO masiku ano ndi malonda amene akupanga mabiliyoni ambiri a ndalama. Oimba otchuka ndi owachirikiza akupanga ndalama zochuluka kwambiri. Komabe, n’zoona kuti moyo wa oimba ena otchuka wakhala wosasangalatsa, amafa msanga, ndiponso akhala akudzipha. Ndipo pali chitsimikizo chokwanira chakuti nyimbo zina, zimaipitsa khalidwe, malingaliro, ndi uzimu ndipo zingachititse chiwawa, ndi khalidwe loipa.
Komabe, ndibwino kukhala ndi lingaliro loyenera la nyimbo. Ngakhale kuti pali zinthu zambiri zolakwika komanso zoipa pa luso limeneli, nyimbo zina zingachititse moyo kukhala wosangalatsa ndiponso kubweretsa chimwemwe ndi kukhutira. Zingathe kutilimbikitsa mwamaganizo komanso mwauzimu. Taganizirani za zitsanzo zingapo zotsatirazi.
Masalmo a m’Baibulo okwanira 150 ali zolembedwa zaluso—mawu a ndakatulo, nyimbo zopatulika, komanso mapemphero. Lero anthu amawaŵerenga mosangalala m’zinenero mazanamazana. Komabe, Ahebri akale sanali kungoŵerenga chabe masalmowo; komanso anali kuwaimba. Nthaŵi zambiri ankatero mopokolezana ndi nyimbo zosangalatsa—imene inali njira yamphamvu kwambiri yodzilunzanitsira ku nzeru za Mulungu wawo, Yehova, monga mmene mawu awo m’nyimbozo amalongosolera, kuphatikizaponso mmene oimba aluso amakhudzira maganizo a owamvetsera. Sizinali za zii kapena zachikale, mwachionekere nyimbo za Ahebri zinali zapamwamba kuposa za mitundu yowazungulira panthaŵiyo.
Kenaka, Akristu a m’zaka za zana loyamba anali kuimba masalmo ndi nyimbo zina kuti atamande Mulungu komanso kuti akhazike mitima ya opsinjika maganizo pansi. Motero nyimbo zinali kuwachititsa kukhala osangalala. Ndipo mwakuimba nyimbo zozikidwa m’Baibulo, anali kutsendereza chidziŵitso cha Mulungu m’mitima mwawo, chimene anali kufuna kuti chiwatsogolere m’moyo wawo.—Mateyu 26:30; Machitidwe 16:25.
Agiriki akale anali kukhulupirira kuti nyimbo zimaumba bwino khalidwe la munthu ndipo zimapangitsa munthu wamwamuna kapena wamkazi kukhala weniweni. M’dziko la m’zaka za zana la 20 lino, limene limati chofunika kwambiri ndicho kuphunzira sayansi, zachuma, komanso za maganizo a munthu, kuumba bwino maganizo mwakugwiritsa ntchito maluso nthaŵi zambiri kumanyalanyazidwa.
Khalani Achikatikati
Kumvetsera kanyimbo kenakake kabwino kungakhale kothandiza ndiponso kosangalatsa. Komatu, munthu angathe kusangalala kuposa apa poimba chida chinachake choimbira kapena poimba ndi gulu la anzake. Kuphunzira kuimba kungabweretse chisangalalo chachikuludi.
N’zoona kuti monga kulili ndi zinthu zina zonse zabwino m’moyo, kusachita mopitirira muyezo n’kofunika, kuona zinthu bwino, komanso kusankha bwino zosangalatsa zoterezi. Tiyenera kukhala wosamala osati pa kusankha mtundu wa nyimbo wokha komanso kuchuluka kwa nthaŵi imene tizikhala tikumvetsera kapena kuimba nyimbozo.
Ngati mtundu winawake wa nyimbo ukukhudza moipa maganizo, zochita, komanso maubwenzi anu, ndiye kuti sankhani mtundu wina. Motero tetezani makutu anu kuti muteteze malingaliro anu kuti muteteze mtima ndi maganizo anu.
Zimenezi ndi zoona makamaka kumbali ya mawu a m’nyimbo. Angathe kuyamba kuumba maganizo anu kuti muziona moyo komanso khalidwe mmene anthu amaganizo osiyana ndi anu amazionera, amene amalimbikitsa moyo wosaopa Mulungu, komanso wopanda khalidwe. Nthaŵi zina ngakhale mutu wa nyimboyo ungayambitse munthu kuganiza molakwika.
Mawu a Mulungu, Baibulo, amalimbikitsa anthu amene akufuna kumukondweretsa kuti “[a]pereke matupi a[wo] nsembe yamoyo, yoyera, yolandirika kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika ndi mphamvu ya[wo] ya kulingalira.” (Aroma 12:1, NW) Mwachionekere, malingaliro athu ali mbali ya ‘nsembe yamoyo’ imeneyo. Motero pamene tangoona kuti chifukwa cha mphamvu ya nyimbo, malingaliro athu ayamba kutiletsa kuganiza modzitsutsa, komanso mwanzeru ndipo akutilakwitsa, ndiye kuti tiyenera kusintha chizoloŵezi chathu cha kumvera nyimbo. Kumbukirani: Mphamvu za nyimbo zingathe kukhudza mtima wanu komanso maganizo anu m’njira yabwino kapena yoipa!
[Bokosi/Chithunzi patsamba 10]
Kupititsa Patsogolo Mphamvu ya Kuphunzira
“Kufufuza kukusonyeza kuti kumvera nyimbo za mavume kawirikawiri kungathe kupititsa patsogolo mphamvu ya kuphunzira ya khanda. Koma m’nyumba zambiri makanda samva nyimbo zoterezi ayi.”—Magazini ya Audio, March 1999.