Mutu 1
Madalitso Akuru Ali Pafupi Kwenikweni!
1. Pomalingalira za mikhalidwe ya dziko yomaipaipabe, kodi ndi mafunso otani amene amabuka?
KODI mumafuna kukhala mumtendere ndi m’cibwino ndi moyo wautali kaamba ka inu mwini ndi okondedwa anu? Kodi mukukhumba kukuona kuipa ndi kubvutika kutatha? Munthu ali yense woona mtima amakhumba zinthu zimenezi. Koma lerolino, m’mbali zonse za dziko lapansi, ciwawa, upandu, njala, ndi matenda zikuonjezereka. Kodi ncifukwa ninji dziko zimatanthauzanji? Kodi pali cifukwa ciriconse comvekera bwino ca kukhulupirira kuti mikhalidweyo idzaongokera mu nthawi ya moyo wathu?
2. (a) Kodi ndi bukhu liti limene limatipatsa ife cifukwa ca kukhalira ndi ciyembekezo? (b) Kodi ncifukwa ninji tingalingalire mwanzeru kuti Mlengi wacikondiyo adzaithetsa mikhalidwe imene imacititsa cisoniyo?
2 Inde, pali cifukwa cabwino ca kukhalira ndi ciyembekezero coteroco, ndipo calongosoledwa m’bukhu limene lafalitsidwa mu zinenero zambiri koposa bukhu lina lirilonse m’dziko. Bukhu limenelo ndilo Baibulo. Limatiuza ife za cifuno ca Mulungu ca kulikhazikitsa dongosolo latsopano kotheratu la zinthu kaamba ka mtundu wa anthu. Ngati inu mukadakhala ndi mphamvu ya kucitira conco, kodi simukanaithetsa mikhalidwe imene imadzetsa cisoni cocurukayo? Ndithudi inu mukadatero! Kodi tinayenera kulingalira kuti Mlengi wa mtundu wa anthu sadzatero? Baibulo limatiuza ife kuti “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) Ndithudi Atate wakumwamba wacikondi ameneyu amacidziwa cimene mtundu wa anthu umacifuna. Iye ali ndi mphamvu ya kuzikwaniritsa zofunika zimenezo, ndipo iye motsimikizirikadi adzatero, pakuti Salmo 145:16a ponena za Mulungu limati: “Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsa zamoyo zonse cokhumba cao.”—Onani Deuteronomo 32:4.
3. (a) Kodi patsala nthawi yaitali Mulungu asanazikhutiritse zikhumbo za munthu za mtendere ndi cimwemwe? (b) Kodi mikhalidwe ya dziko yomaipaipabeyi iri umboni wa ciani?
3 Kodi ndi liti pamene Mulungu adzacikwaniritsa cokhumba ca munthu kaamba ka mtendere weniweni ndi cimwemwe, limodzi ndi thanzi losatha ndi moyo? Kodi mtundu wa anthu uyenera kuyembekezera kwa zaka zina zikwi zocuruka? Ai! Nthawiyo yayandikira kwenikweni! Koma kodi ici cingathekere motani? Mikhalidwe ya m’dziko ikuipaipabe, osati kuongokera. Zoonadi, koma Baibulo linasonyeza moonekera bwino, kale lomwe, kuti mikhalidwe imeneyi idzakhala citsimikiziro cakuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a dongosolo ili la zinthu loipali. (2 Timoteo 3:1-5) Posacedwapa Mlengi wacikondiyo adzakuthetsa kuipa limodzi ndi awo amene amakucititsa. Koma Mulungu adzawadalitsa kwakukurukuru anthu oona mtima amene amafuna kucita cimene ciri coyenera, pakuti iye amalonjeza kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi cilakolako cace; koma iye amene acita cifuniro ca Mulungu akhala ku nthawi zonse.”—1 Yohane 2:17.
CIMENE MULUNGU ADZAUCITIRA MTUNDU WA ANTHU
4. (a) Mu dongosolo latsopano la Mulungu, kodi ndi zocititsa kupanda cimwemwe zotani zimene zidzathetsedwa? (b) Kodi ndi motani mmene Mulungu adzalikwaniritsira lonjezo lace la mtendere?
4 Ha, ndi kusintha kotani nanga kumene dziko lapansili lidzakhala nako! Sipadzakhalanso nkhondo, kapena mabvuto alionse amene nkhondo imawabweretsa. Cidani, dyera, upandu ndi ciwawa zonsezo zidzakhala zinthu zakale. M’malo mwace, padzakhala mtendere wangwiro ndi cisungiko pa dziko lapansi. Mau a Mulungu mwiniyo amalengeza kuti: “Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti; . . . koma ofatsa adzalandira dziko lapansi, nadzakondwera nao mtendere wocuruka.” (Salmo 37:10, 11 [36:10, 11, Dy]) Mtendere woterowo udzakhalapo, osangoti kokha pakati pa mitundu, komanso pakati pa anthu oyandikana ndiponso m’banja lirilonse. Talingalirani za mmene limenelo lingadzakhalire dalitso lalikuru kwa inu! Ndipo ha, ndi kolimbikitsa cotani nanga kudziwa kuti kukwaniritsidwa kwa lonjezo lodzutsa maganizo limeneli sikumadalira pa anthu! Ali Mulungu amene adzakucita uko. Motani? Mwa kuwaononga oipa ndi kuwaphunzitsa anthu ace mu njira za mtendere.—Miyambo 2:21, 22; Yesaya 54:13.
5. (a) Mu dongosolo latsopano, kodi nciani cimene cidzacitikira pa matenda ndi imfa? (b) Kodi ndi mafunso otani amene amabuka ponena za kufupika kwa zaka za moyo wa munthu kwamakono?
5 Pakati pa madalitso ambiri amene anthu adzasangalala nawo mu dongosolo latsopano lopangidwa ndi Mulungu pali thanzi labwino. Ngakhale imfa, imene imadzetsa cisoni cacikuru kwa tonsefe, sidzakhalaponso. Lonjezo la Mlengiyo ndilo lakuti: “Ndipo [Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuicotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena cowawitsa . . . Taonani, ndicita zonse zikhale zatsopano.” (Cibvumbulutso 21:4, 5)b Cimeneco ciri cinthu cimene palibe wolamulira waumunthu, palibe wasayansi, palibe dotolo amene angathe kucicita; koma ciri cinthu cimene Mulungu adzacicita. Kodi kuli kwanzeru kuti cifuno cokha ca Mulungu kaamba ka munthu ndico cakuti munthuyo azikhala kwa zaka makumi awiri akumakula, kapenanso zaka zina makumi awiri kapena makumi atatu akumaphunzira ndi kucipeza cidziwitso, ndipo mwamsanga pambuyo pa cimeneco kuyamba kumakalamba, kubvutika ndi matenda ndi kufa? Kodi ncifukwa ninji moyo wa munthu unayenera kukhala waufupi motero pamene ngakhale kamba amakhala zaka zokwanira mazana awiri ndipo mtengo umakhala zaka zocuruka kupambana pamenepo? Mulungu anampanga munthu kuti akhale ndi moyo, osati kuti afe. Mlengiyo amalonjeza kuti posacedwapa kudzakhala kothekera kusangalala ndi moyo kosatha, pompano pa dziko lapansi. (Yesaya 25:8) Pokhala ndi anansi okonda mtendere, thanzi labwino ndi nchito yokhutiritsa maganizo kuitanganitsa miyoyo yathu, ha, ndi cosangalatsa cotani nanga mmene cimeneco cidzakhalira!
6. Kodi tingatsimikizire bwanji kuti dongosolo latsopano limeneli lidzabwera?
6 Kodi ndi motani mmene mungatsimikizirire kuti dongosolo latsopano limeneli lidzadza? Kodi ndi motani mmene mungatsimikizirire kuti silinangokhala loto cabe? Mungakhale otsimikizira cifukwa cakuti Mulungu Wamphamvuyonseyo walilonjeza. Uyo amene analenga ndi kumacicirikiza cilengedwe caponseponseci wacipereka citsimikiziro cace cakuti ilo lidzadza. “Mulungu . . . sanganame.” (Tito 1:2, NW) Mau ace samakhala osakwaniritsidwa.—Yoswa 23:14.
7. Ngakhale kuli kwakuti anthu anagwiritsiridwa nchito kulilemba Baibulo, ncifukwa ninji tingalilingalire ilo moona kukhala “mau a Mulungu”?
7 Coonadi codzutsa mtima cimeneci cikupezeka m’Mau a Mulungu, Baibulo, Malemba Opatulika. Palibe magwero ena a cidziwitso amene ali opezeka kwa munthu amene amacilongosola mokhutiritsa cifukwa cace ca zimene zacitika pa dziko lapansi ndi cifuno ca Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu. Pamene anthu anagwiritsidwa nchito kulilemba Baibulo, iwo anatero motsogozedwa ndi mphamvu yogwira nchito ya Mulungu kapena mzimu woyera, kotero kuti “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu.” (2 Timoteo 3:16) Monga momwe ceza cosaoneka ca radio cimakutengerani inu nkhani, coteronso mphamvu yosaoneka ya Mulungu inawatsogoza olemba Baibulo kuzilemba zimene iye anafuna kuti mtundu wa anthu uzidziwe. Cimeneco ndico cifukwa cace mmodzi wa alembi amenewo, mtumwi Paulo, anali wokhoza kunena kuti: “Pakulandira mau a a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13; onaninso 2 Petro 1:20, 21.
KUSINTHA KWA PA DZIKO LONSE KULI PAFUPI
8. Kodi ndi zocitika zina zotani zimene Yesu ananena kuti zikawadziwikitsa masiku otsiriza a dongosolo loipa ili?
8 Mau a Mulungu a coonadi amatiuza ife momvekera bwino kuti tikukuyandikira mofulumira kusintha kwa dziko lonse. Iwo amatisonyeza ife kuti nthawi yathuyi ndiyo imene Yesu Kristu anali kuilingalira pamene iye ananeneratu za mapeto a dongosolo loipali. Yesu ananeneratu za zinthu zambiri zimene atsatiri ace amtsogolo anayenera kuzifunafuna m’malo mwakuti adziwe pamene mapeto anali pafupi. Iye ananena kuti masiku otsiriza a dongosolo loipa ili la zinthu adzadziwikitsidwa ndi zinthu zonga ngati nkhondo za dziko lonse, kuperewera kwa zakudya, kuonjezereka kwa kusaweruzika ndi kukulakula kwa kutaya cikhulupiriro mwa Mulungu. (Mateyu 24:3-12) Iye ananena kuti padzakhala “cisauko ca mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru.” (Luka 21:25) Takuona kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa mu nthawi ya moyo wathu.
9. Perekani citsanzo cimodzi kapena ziwiri ponena za cimene anthu amene amaziphunzira zocitika za dziko akunena ponena za nthawi yathu.
9 Anthu ambiri amene amaziphunzira zocitika za dziko lapansi ali otsimikizira kuti kusintha kwakukuru kulinkhudza motsimikizirika. Mlembi wocuka Walter Lippmann anati: “Kwa ife tonse dziko lapansi liri lopanda cilongosoko ndi laupandu, losalamuliridwa ndipo moonekera bwino losalamulirika. Kuli konse kuli kudera nkhawa kwakukuru ndi kupenga.” Iye anaonjezerapo kuti zonsezi “ndikukhulupirira kuti zikusonyeza ceniceni caumbiri cakuti tikukhala cakumapeto kwa njira ya moyo yokhazikitsidwa ndi ya nthawi zonse.”c Ndiponso, monga momwe kunasimbidwira mu 1960, United States Secretary of State wakalelo, Dean Acheson, analengeza kuti nthawi yathuyi iri “ngengo ya kusakhazikika kopanda kwina kofanana nako, ya ciwawa copanda cina cofanana naco.” Ndipo iye anacenjeza kuti: “Ndikudziwa zocuruka ponena za zimene zikucitika kukutsimikizirani inu kuti, mu zaka khumi ndi zisanu kucokera pa lerolino, dziko ili lidzakhala loopsa kwambiri kukhalamo.d
10. (a) Kodi tikudziwa motani kuti kusintha kwa dziko kuli pafupi kwambiri? (b) Kodi kusintha kwa dziko lonse kumene kukudzako kukutanthauza cionongeko ca ciani?
10 Zinthu zonse zocuruka zonenedweratu m’Mau a Mulungu a coonadi zimasonyeza kuti nthawi ya kusintha kwa dziko yatikwanira ife tsopano lino! Zimene tikuziona zikumacitika pa dziko lonse lapansi lerolino m’kakwaniritsidwe ka ulosi wa Baibulo zimasonyeza kuti nthawi yathuyi ndiyo imene idzaciona cionongeko ca dongosolo lonse loipa ili la zinthu. Maboma amakono adzacotsedwa kuti pakhale mpata wa ulamuliro wa dziko lonse lapansi ndi boma la mulungu. (Danieli 2:44; Luka 21:31, 32) Palibe cinthu ciriconse cimene cingakuletse kusintha kumeneku, cifukwa cakuti amene wakufuna ndiye Mulungu.
COONADI CIMENE CIMATSOGOLERA KU MOYO WAMUYAYA
11. (a) Kodi tingazipewe ziyambukiro za kusintha kwa dziko lonse kumene kukudzako? (b) Cotero, ngati tikufuna kukhalabe ndi moyo, kodi tiyenera kucita ciani, malinga ndi kunena kwa 1 Timoteo 2:4 ndi Yohane 17:3?
11 Kusintha kwa dziko lonse kumene kukudzako kudzamuyambukira munthu aliyense amene ali pa dziko lapansi pano, kuphatikizapo inuyo. Ngati mumakonda moyo ndipo mumafuna kukhala ndi moyo, muyenera kucita mwacangu kucilandira cidziwitso colongosoka ca Mulungu, zifuno zace ndi zofuna zace. Cimeneco ndico cimene Mulungu amafuna inu kuti mucicite, pakuti ciri cifuniro cace kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindirkira coonadi.” (1 Timoteo 2:4) Cidziwitso colongosoka cocokera m’Mau a Mulungu a coonadi cidzawatheketsa anthu oona mtima kuwapulumuka mapeto a dongosolo lamakono loipa ili. (Zefaniya 2:3)e Cidzaibvumubulanso njira ya ku moyo wamuyaya mu dongosolo labwino kopambana latsopano la zinthu. M’pemphero kwa Mulungu Yesu Kristu anati: “Ici citanthauza moyo wosatha, kucilandira kwao cidziwitso ca inu, Mulungu woona yekha, ndi ca uyo amene munamtuma, Yesu Kristu”—Yohane 17:3, NW; onaninso Yohane 4:14.
12. Kodi ndi zifukwa zamphamvu zotani zimene tiri nazo za kufunira kuphunzira coonadi cocokera m’Baibulo?
12 Ha, ndi kolimbikitsa cotani nanga kudziwa kuti posacedwapa tidzawaona mapeto a mabvuto onse a dziko lapansi! Ha, ndi kodzutsa maganizo cotani mmene kwakhalira kudziwa kuti tiri ndi ciyembekezo ca kulowa mu dongosolo latsopano posacedwapa kumene tingasangalale ndi moyo kosatha mwacikwanekwane! Ici cinayenera kumpatsa aliyense wa ife zifukwa zamphamvu za kufunira kuphunzira coonadi kucokera m’Baibulo. Mwa kufunafuna coonadi ici timayamba kuwakhazikitsa “maziko abwino kopambana kaamba ka mtsogolo, m’malo mwakuti tiugwiritse moyo weniweniwo,” “moyo wamuyaya” mu dongosolo latsopano la zinthu la Mulungu.—1 Timoteo 6:19; AV.
[Mawu a M’munsi]
a Salmo 144:16, Douay Version.
b Bukhu la Baibulo la Cibvumbulutso limachedwa Apocalypse mu Douay Version.
c Newsweek, October 9, 1967, tsamba 21.
d U.S. News & World Report, June 13, 1960, tsamba 116, 119.
e Sophonias 2:3, Douay Version.
[Chithunzi patsamba 4]
“Mulungu . . . adzwapukutira misozi yonse kuicotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena cowawitsa.”—Cibv. 21:3, 4.