PHUNZIRO 9
Kusinthasintha Mawu
PAMENE mutsindika ganizo, mumathandiza omvera anu kumvetsa zimene mukunena. Koma pamene musinthasintha bwino mphamvu ya mawu, liŵiro, ndi kamvekedwe ka mawu, nkhani yanu imamveka yokoma kwambiri. Komanso, zingaonetse omvera anu mmene nkhani yanu ikukukhudzirani. Mmene nkhaniyo mukuionera ndi mmenenso omvera anu angaionere. Ndi mmenetu zimachitikira kaya mukulankhula papulatifomu kapena kwa munthu mmodzi mu utumiki wa kumunda.
Mawu a munthu ndi chida chodabwitsa kwabasi! Chimatha kugwira ntchito zosiyanasiyana kwambiri. Mukawagwiritsa ntchito moyenerera, amatha kuika umoyo m’nkhani yanu, kukhudza mtima, ndi kulimbikitsa kuchitapo kanthu. Komabe, zimenezi sizingatheke mwa kungoika zizindikiro m’malo oyenera kusintha mphamvu ya mawu, kusintha liŵiro, kapena kusintha mamvekedwe a mawu. Kusinthasintha mawu kongotsatira zizindikiro zimene mwalembamo sikumveka kwachibadwa. M’malo mochititsa nkhani yanu kumveka yaumoyo ndi yokoma, omvera anu sangasangalale nayo. Kusinthasintha mawu koyenerera kumachokera mumtima.
Pamene wokamba nkhani asinthasintha mawu mwanzeru, sachititsa omvera kulingalira kwambiri za iye. M’malo mwake, amathandiza omverawo kutengeka ndi mzimu wa nkhani yomwe akulankhulayo.
Sinthasinthani Mphamvu ya Mawu. Njira imodzi yosinthira mamvekedwe anu ndiyo kusinthasintha mphamvu ya mawu anu. Koma sizikutanthauza kungomakweza ndi kutsitsa mawu chisawawa. Zimenezo zingasokoneze tanthauzo la zimene mukunena. Ngati mukweza mawu pafupipafupi kwambiri, anthu amaipidwa nazo.
Mphamvu ya mawu anu iyenera kuyenerana ndi nkhaniyo. Kaya mukuŵerenga lamulo lofuna kulabadira mwamsanga, ngati lija lopezeka pa Chivumbulutso 14:6, 7 kapena pa Chivumbulutso 18:4, kapena mawu osonyeza chidaliro champhamvu, ngati aja olembedwa pa Eksodo 14:13, 14, m’pofunika kuwonjezera mphamvu ya mawu. Komanso, mukamaŵerenga chidzudzulo champhamvu cha m’Baibulo, ngatichija chopezeka pa Yeremiya 25:27-38, kusinthasintha mphamvu ya mawu kudzachititsa mawu ena kuonekera kwambiri.
Ganiziraninso cholinga chanu. Kodi mukufuna kulimbikitsa omvera kuchitapo kanthu? Kodi mukufuna kumveketsa bwino mfundo zazikulu m’nkhani yanu? Kuwonjezerako mphamvu ya mawu, ndi kuigwiritsa ntchito mosamala, kumathandiza kukwaniritsa zolinga zimenezi. Komabe, kuwonjezera mphamvu ya mawu kokha kungawononge cholinga chanu. Motani? Zimene mukunena zingafune kuonetsa mzimu wa ubwenzi ndi kukhudzika mtima m’malo mokweza mawu. Tidzafotokoza zimenezi m’Phunziro 11.
Kutsitsa mawu mozindikira bwino, kumalimbikitsa omvera kuyembekezera kanthu kena. Mukatero, nenani mawu oonetsa kukhudzika mtima kwanu. Kutsitsa mawu limodzi ndi kuonetsa kukhudzika mtima kungagwiritsidwe ntchito pofuna kusonyeza nkhaŵa ndi mantha. Mungatsitsenso mawu posonyeza kuti zimene mukunena sizofunika kwenikweni poyerekeza ndi zina. Komabe, ngati mawu anu akhala otsika nthaŵi zonse, kungaonetse kuti mukukayikira kapena mulibe chidaliro, kapenanso kuti mulibe chidwi chenicheni ndi nkhaniyo. Mwachidziŵikire, mawu ofeŵa kwambiri tiyenera kuwagwiritsa ntchito mosamala.
Sinthani Liŵiro Lanu. M’kulankhula kwathu kwa tsiku ndi tsiku, mawu amangotuluka mwachibadwa. Tikasangalala, timakonda kulankhula mofulumira kwambiri. Pamene tifuna kuti ena akakumbukire zimene tikunena, timalankhula modekha.
Komabe, atsopano amene amatha kusinthasintha mawu papulatifomu ndi ochepa. Chifukwa chiyani? Chifukwa amakonzekera kwambiri mawu oti akalankhule. Nthaŵi zina amalemba mawu onsewo. Ngakhale kuti nkhaniyo sanaikonze m’njira yokaiŵerenga, mawu ake amawaloŵeza kwambiri. Chifukwa cha zimenezo, amatchula chilichonse paliŵiro lofanana. Angawongolere chofooka chimenechi mwa kuphunzira kulankhula kuchokera pa autilaini.
Peŵani kuŵirikiza liŵiro lanu modzidzimukira muja amachitira mphaka. Amadziyendera pang’onopang’ono mwachifatse, kenako mwadzidzidzi jo! uyo n’kuthaŵa; inde akaona galu. Ndipo musalankhule mothamanga kwambiri moti mawu anu n’kusamveka bwino.
Kuti mukhoze kusinthasintha liŵiro lanu, musamangokweza ndi kutsitsa mawu chisawawa. Kalankhulidwe koteroko kadzasokoneza nkhani yanu m’malo moimveketsa bwino. Kusinthasintha liŵiro kuyenera kudalira zimene mukunena, makhalidwe okhudza mtima amene mukufuna kuonetsa, ndi cholinga chanu. Kambani nkhani yanu paliŵiro loyenera. Polankhula zosangalatsa, lankhulani mofulumirirapo, muja mumachitira pamoyo wanu wa tsiku ndi tsiku. Teroninso potchula mfundo zazing’ono kapena pofotokoza zochitika wamba. Zimenezi zikachititsa nkhani yanu kukhala yosatopetsa ndi yosalemerera kwambiri. Komabe, zifukwa zokulirapo, mfundo zazikulu, ndi mbali zina zofunikira kutsindika zimafuna kuchepetsa liŵiro.
Siyanitsani Mamvekedwe a Mawu Anu. Yerekezani munthu amene akuimba chida choimbira kwa ola limodzi kapena kuposerapo. M’kati mwa nthaŵi yonseyo, akungoimba noti imodzi—choyamba mokweza kwambiri, kenako motsikirapo, nthaŵi zina mothamanga kwambiri, kenakonso pang’onopang’ono. N’zoona kuti akusinthasintha mphamvu ya mawu ndi liŵiro, koma chuni ndi chimodzi. “Nyimboyo” siingakome kwenikweni. Mofananamo, popanda kusinthasintha mamvekedwe, mawu athu sangakome m’makutu mwa ena.
Koma dziŵani kuti kusintha mamvekedwe sikukhala ndi cholinga chofanana m’zinenero zonse. M’zinenero zina, ngati Chitchaina, kusintha mamvekedwe kumasinthanso tanthauzo la mawu. Komabe, ngakhale m’zinenero zoterozo, zilipo zinthu zimene munthu angachite kuti akometse malankhulidwe ake. Akhoza kuyesetsa kumveketsa bwinobwino mawu ake. Akhozanso kukweza mawu ndi kuwatsitsa moyenerera.
M’zinenero zinanso, kusintha mamvekedwe a mawu kungapereke malingaliro osiyanasiyana. Mwachitsanzo, pofuna kutsindika mawu, angakweze mawu pang’ono ndi kuwonjezera mphamvu ya mawu. Kapena angachite zimenezo pofuna kusonyeza ukulu wa chinthu kapena mtunda. Kukweza mawu kumapeto kwa sentensi kungasonyeze kuti ndi funso. M’zinenero zina amafunsa mwa kutsitsa mawu kumapeto kwa sentensi.
Pofuna kusonyeza chisangalalo ndi kukondwa, timakweza mawu. (M’zinenero zina, amasinthasintha mawu.) Posonyeza chisoni ndi nkhaŵa timatsitsa mawu. (M’zinenero zina, amachepetsa mawu.) Makhalidwe okhudza mtima otchulidwa pano ndi amene amathandiza munthu kuwafika pamtima ena. Pofuna kuwasonyeza, musangotchula mawu. Gwiritsani ntchito mawu anu m’njira yosonyeza kuti inunso mukumva chimodzimodzi.
Kuyala Maziko. Nanga mungayambire pati kusinthasintha mawu kumeneko? Mungayambire posankha mfundo za nkhani yanu. Ngati musankha zifukwa zogomeka zokhazokha, kapena zilimbikitso zokhazokha, simukhala ndi mwayi waukulu wosinthasintha mawu. Choncho, pendani bwino nkhani yanuyo, ndipo onetsetsani kuti muli mbali zosiyanasiyana zochititsa nkhani kukhala yokoma, ndi yopatsa chidziŵitso.
Yerekezani kuti pamene muli m’kati mokamba nkhani yanu, mukuona kuti mufunikira kusinthasintha mawu chifukwa siikukoma. Muyenera kutani pamenepo? Sinthani kalankhulidwe ka nkhani yanu. Motani? Nayi njira imodzi: Tsegulani Baibulo lanu, kenako pemphani omvera anu kutsegula awo, ndiyeno ŵerengani lemba m’malo mongolankhula. Kapena sinthani ndemanga zina zikhale mafunso, mukumapumira pofuna kutsindika. Ponyanimo kachitsanzo kakafupi. Aŵa ndiwo maluso amene akatswiri okamba nkhani amagwiritsa ntchito. Koma mosalingalira zakuti ndinu chiyambakale kapena watsopano, mutha kugwiritsa ntchito maganizo amodzimodziwo pokonzekera nkhani yanu.
Tingatero kuti kusinthasintha mawu ndizo nsinjiro za nkhani. Mukathiramo mlingo woyenerera ndipo zasakanikirana bwinobwino m’nkhanimo, kukoma konse kwa nkhani yanu kudzangoloŵerera mwa omvera anu.