Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 24 tsamba 122-126
  • Kulozera Maganizo a Omvetsera ku Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulozera Maganizo a Omvetsera ku Baibulo
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • **********
  • Kutchula Malemba Moyenerera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kulimbikitsa Omvera Kuŵerenga Baibulo
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kuŵerenga Malemba ndi Kuwatanthauzira
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Mawu Oyamba Okopa Chidwi
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 24 tsamba 122-126

Phunziro 24

Kulozera Maganizo a Omvetsera ku Baibulo

1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kukopera omvetsera ku Baibulo?

1 Cholinga chathu pamene tili mu utumiki ndicho kulozera maganizo a munthu aliyense ku Mawu a Mulungu, Baibulo. Ilo lili ndi uthenga umene timalalikira, ndipo timafuna kuti anthu adziŵe kuti zimene timanena sizochokera m’maganizo mwathu ayi koma kwa Mulungu. Anthu okonda Mulungu amalidalira Baibulo. Pamene tiliŵerenga kwa iwo, amamvetsera nalabadira uphungu wake. Koma pamene atulutsa Baibulo lawo ndi kudziŵerengera okha, zimawakhudza mtima kwambiri. Choncho, pamene tili mu utumiki wakumunda, ndipo ngati mikhalidwe ilola, n’kwanzeru kulimbikitsa mwininyumba kuti atenge Baibulo lake ndi kuŵerenga nanu malembawo. Chimodzimodzinso pamisonkhano ya mpingo, ngati onse alimbikitsidwa kuŵerenga Baibulo lawo, anthu atsopano adzalizindikira msanga kuti ndilo gwero la zimene timakhulupirira, ndipo onse adzapindula kwambiri mwa kudzionera okha ndi maso awo.

2 Mukatero mudzakwaniritsa cholinga chanu polankhula, ngati omvetserawo atsatira kuŵerenga kwanu m’ma Baibulo awo ngati n’kotheka. Kuti iwonso aŵerenge zidzadalira inuyo kuwapatsa chilimbikitso choyenera. Ichi n’chimene pasilipi lanu la Uphungu wa Kulankhula chikutchedwa “Kulimbikitsa Omvetsera Kuŵerenga Baibulo.”

3, 4. Nanga ndi motani mmene tingachitire zimenezo mogwira mtima?

3 Mwa kungotchula lemba. Imodzi ya njira zabwino kwambiri ndiyo kupempha mwachindunji omvetserawo kuti aŵerenge Baibulo; njira imeneyi imagwiritsidwa ntchito kaŵirikaŵiri. Nthaŵi zina tingangotchula lemba limene mawu akupezekapo tisanawaŵerenge; mwina mwa kunena kuti: “Tsopano pamene tiŵerenga 2 Timoteo 3:1-5, ganizirani za mikhalidwe ya kuno kwathu.” Ndiyeno pamene mutsegula lembalo, yang’anani uku ndi uku kuona ngati omvetserawo akulabadira. Nthaŵi zambiri mudzaona kuti iwonso akufunafuna lembalo.

4 Zili kwa mlankhuliyo kusankha ndi malemba ati amene akufuna kugogomeza, mwa kuuza omvetsera kuti awatsegule. Yang’anani omvetsera anu. Khalani ndi chidwi choona ngati akukutsatirani. Ngakhale ngati pazifukwa zina mufunikira kulankhula nkhani yoŵerenga (manuscript), mukhoza kuŵerenga malemba ofunikira kwambiri mwanjira yolola kuti omvetsera akutsatireni m’ma Baibulo awo.

5, 6. Fotokozani chifukwa chake kuli kopindulitsa kulola nthaŵi yakuti omvetsera apeze malemba oti tiŵerenge.

5 Mwa kulola nthaŵi kuti apeze lembalo. Kungotchula lemba sikokwanira. Ngati mungoŵerenga lemba kenako n’kupita ku lina omvetserawo asanalipeze, potsirizira pake adzagwa mphwayi ndi kuleka. Yang’anani omvetsera anu, ndipo mutaona kuti ochuluka alipeza lembalo, ŵerengani.

6 Kaŵirikaŵiri ndi bwino kutchula lemba kanthaŵi kadakalipo musaliŵerenge kuti nthaŵi yofunikayo isangowonongeka mwa kukhala chete nthaŵi yaitali poyembekeza kuti omvetseranso alipeze, kapena polankhula izi ndi izi zongoyembekezera chabe. Komabe kupuma koyenera panopo n’kofunika. Ndiponso, ngati mwatchula msanga lemba musanaliŵerenge, muyenera kukumbukira kuti zina mwa zinthu zimene mukunena sizidzatsatiridwa kwenikweni. Choncho m’pofunika kuti zinthu zofunika kwambirizo pamfundo imene mukufuna kufotokoza muzineneretu musanatchule lembalo.

**********

7-18. Ndi njira ziti zimene tingagwiritse ntchito kuti titchule Malemba mogwira mtima?

7 Malemba amene amaŵerengedwa m’nkhani kaŵirikaŵiri amakhala mfundo zazikulu za nkhaniyo. Nkhani yonse imagona pamalembawo. Kuti iwo adzamveketsa nkhani motani, zimadalira mmene muti muwaŵerengere mogwira mtima. Choncho mfundo yakuti “Kutulutsa malemba koyenera,” imene ili pasilipi lanu la Uphungu wa Kulankhula, n’njofunika kuipenda bwino.

8 Pali njira zambiri zosiyanasiyana zimene tingatulutsire Malemba, kuwaŵerenga ndi kuwatanthauzira. Mwachitsanzo, nthaŵi zina, mawu amene tinganene otsogolera ku lemba angaperekenso kutanthauzira kwake, kotero kuti kuŵerenga kwenikweniko kumagogomeza kapena kukhomereza mfundoyo. Komanso nthaŵi zina malemba ena amakhala ogwira mtima kwambiri pamene angoŵerengedwa popanda kuwatsogolera ndi mawu ena alionse, monga pachiyambi penipeni pa nkhani.

9 Kuti muphunzire katulutsidwe ka malemba kogwira mtima, onetsetsani zimene alankhuli a nkhani ozoloŵera amachita. Yesani kusiyanitsa njira zosiyanasiyana zimene amatulutsira malemba. Lingalirani kugwira mtima kwake. Pokonza nkhani zanu ganizirani kaye cholinga choŵerengera lemba, makamaka ngati ndi lemba lofunika kwambiri pamfundo yaikulu. Ganizirani mosamalitsa mmene mutulutsire lembalo kotero kuti likhale logwira mtima kwambiri. Nazi njira zingapo:

10 Mwa funso. Mafunso amafuna mayankho. Ndipo amachititsa kulingalira. Lolani kuti lembalo ndi kulitanthauzira kwake zipereke yankho lofunikalo. Mwachitsanzo, pofotokoza zothira magazi m’thupi, mungafune kutulutsa Machitidwe 15:28, 29, mutalongosola chiletsocho malinga ndi kunena kwa Malemba Achihebri. Mungatulutse lembalo mwa kufunsa kuti, “Koma kodi chiletso chimenechi chikugwirabe ntchito pa Akristufe? Tamverani mmene bungwe lolamulira la mpingo woyambirira linalangizira mwamphamvu pothandizidwa ndi mzimu woyera.”

11 Mwa ndemanga kapena mfundo yoti ichirikizidwe ndi lembalo. Mwachitsanzo, polankhula nkhani yonena za kupulupudza munganene kuti: “Ngakhale kasankhidwe kathu ka mabwenzi n’kofunika kwambiri poonetsa maganizo athu kulinga ku chabwino ndi choipa.” Ndiyeno mungaŵerenge mawu a Paulo pa 1 Akorinto 15:33 kuti achirikize zimene mwanenazo.

12 Mwa kusonyeza Baibulo monga maziko a zimene munena. Makamaka potulutsa malemba othandizira ongoperekera umboni munganene kuti: “Onani zimene Mawu a Mulungu amanena pamfundo imeneyi.” Zimenezi n’zokwanira kuwapatsa chidwi choti amve zimene lembalo likunena ndipo zimapereka chifukwa chomveka bwino choŵerengera lembalo.

13 Mwa kusonyeza chothetsa nzeru. M’nkhani yonena za “helo” munganene kuti: “Ngati munthu amakazunzika kwamuyaya m’malaŵi amoto, zimenezo zingatanthauze kuti amakhalabe akuzindikira zinthu atamwalira. Koma tamverani zimene Mlaliki 9:5, 10 akunena.”

14 Mwa kupereka mayankho osiyanasiyana. Ngati funso lachindunji kapena chothetsa nzeru chingakhale chovuta kwa omvetserawo kuti atsatire, perekani mayankho osiyanasiyana kenako lolani kuti lembalo ndi kutanthauzira kwake kupereke yankho lolondola. Pokambirana ndi Mkatolika mungafune kugwiritsa ntchito Mateyu 6:9 pofuna kum’sonyeza uyo amene tiyenera kulunjikitsako mapemphero athu. Funso lachindunji kapena chothetsa nzeru chingasocheze maganizo a mwininyumba, choncho munganene kuti: “Pali maganizo osiyanasiyana ponena za amene tiyenera kupempherako. Ena amati tiyenera kupemphera kwa Mariya, ena amati kwa mmodzi wa ‘oyera mtima,’ komanso ena amati kwa Mulungu yekha. Koma tamverani zimene Yesu ananena.”

15 Mwa chochitika cha m’mbiri yakale. Ngati mufuna kugwiritsa ntchito Ahebri 9:12 m’nkhani yonena za dipo posonyeza kuti Yesu, ‘analandira chiwombolo chosatha’ kaamba ka ife, mwa kupereka nsembe ya magazi ake, mungakuone kukhala kofunika musanaŵerenge lembalo, kuyamba mwafotokozapo mwachidule za “malo opatulika” m’chihema, amene Paulo akusonyeza kuti anaimira malo amene Yesu analoŵako.

16 Mwa mfundo zina zozungulira. Nthaŵi zina kusonyeza mgwirizano wa vesilo ndi mavesi ena ozungulira kumathandiza potulutsa lemba. Mwachitsanzo, pogwiritsa ntchito lemba la Luka 20:25 kusonyeza tanthauzo la ‘kupereka kwa Kaisara zake za Kaisara,’ kungakhale kothandiza kufotokoza chifukwa chake Yesu anagwiritsa ntchito ndalama yokhala ndi chithunzi cha Kaisara, pakuti mfundozo n’zogwirizana m’nkhaniyo.

17 Mwa kuphatikiza njira zosiyanasiyana. Inde, nthaŵi zambiri kuphatikiza njira zimenezi kulinso kotheka ndipo kopindulitsa.

18 Mawu otchulira lemba ayenera kudzutsa chidwi chokopa maganizo pamene lembalo likuŵerengedwa ndipo ayenera kusonyeza chifukwa chimene mukuliŵerengera.

19, 20. Kodi tingadziŵe bwanji kuti tadzutsa chidwi palemba limene tatchula?

19 Kudzutsa chidwi pa malemba. Kodi mungadziŵe motani kuti mwadzutsa chidwi pa lemba? Choyamba mwa kuona mmene omvetserawo akuchitira, komanso mwa njira imene mwatulutsira lembalo. Ngati omvetsera atsala m’malere chifukwa simunaŵerenge lemba limene mwalitchulalo, kapena ngati mwasiya funso losayankhidwa m’mawu anu otchulira lemba, pamenepo tsimikizani kuti mwadzutsa chidwi palembalo. Komabe, mawu otchulira lemba ayenera kugwirizana ndi nkhaniyo komanso ndi lemba loti mulitchule. Ndipo lemba lenilenilo kapena kutanthauzira kwake kuyenera kuyankhe funso limene mwadzutsa m’mawu otchulira lemba.

20 Mawu otchulira lemba angafanizidwe ndi kulira kwa lipenga kumene kumatsogolera chilengezo. Woliza lipengayo samaimba nyimbo yonse ayi. M’malo mwake, maliridwe odzutsa chidwi a lipenga lake amakopera maganizo onse ku chilengezocho. Ngati lemba limene mwasankha mulitchula mwa njira imeneyo, adzalimvetsera mosangalala komanso adzapindula nalo.

21. N’chifukwa chiyani tiyenera kusumika maganizo pa chifukwa chimene taŵerengera lemba?

21 Kutchula chifukwa choŵerengera lemba. Pamene kuli kwakuti mawu otchulira lemba angasiye funso losayankhidwa, ayenerabe kupereka chifukwa chosonyeza kuti lembalo n’lofunika ndipo n’kofunika kulitchera khutu. Mwachitsanzo, m’nkhani yosonyeza kuti dziko lapansi ndilo mudzi wachikhalire wa anthu mungakonzekere kuŵerenga Chivumbulutso 21:3, 4. Limodzi ndi zifukwa zimene mwapereka poyamba munganene kuti: “Tsopano m’lemba lotsatirali, Chivumbulutso 21:3, 4, yesani kupeza malo kumene kudzakhale chihema cha Mulungu kuvutika ndi imfa zitachotsedwa.” Simunangodzutsa chidwi mwa kusiya kanthu kena kuti lemba likavumbule, komanso mwasumika maganizo pambali yofunika ya lemba lanu, imene mungaitanthauzire mosavuta mutaŵerenga lembalo. Choncho mwa kukopera chidwi ku mfundo yaikulu ya lembalo, mumagogomeza kufunika kwa Mawu a Mulungu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena