PHUNZIRO 38
Mawu Oyamba Okopa Chidwi
MAWU oyamba ndi mbali yofunika kwambiri ya nkhani iliyonse. Ngati mukopadi chidwi cha omvera anu, amatchera khutu mwakhama kuti amve zotsatira. Mu utumiki wa kumunda, ngati mawu anu oyamba sakopa chidwi, mungalephere kupitiriza ulaliki wanu. Pamene mukamba nkhani mu Nyumba ya Ufumu, sikuti anthu angatuluke mukapanda kuwakopa chidwi, koma angayambe kuganizira zinthu zina.
Pokonzekera mawu anu oyamba, khalani ndi zolinga izi: (1) kukopa chidwi cha omvera anu, (2) kudziŵikitsa nkhani yanu momveka bwino, ndi (3) kusonyeza chifukwa chake nkhaniyo ili yofunika kwa omvera anu. Nthaŵi zina, zolinga zitatuzi zingakwaniritsidwe pamodzi. Nthaŵi zina, ziyenera kufotokozedwa chimodzichimodzi, koma dongosolo la kutsatizana kwake lingasinthe.
Mmene Mungakopere Maganizo a Omvera Anu. Kungoti anthu asonkhana kuti amve nkhani sikutanthauza kuti akonzeka kuika maganizo onse pa nkhaniyo. Chifukwa chiyani? Amakhala ndi zinthu zambiri pamoyo zimene zimafika m’maganizo mwawo. Angakhale ndi nkhaŵa chifukwa cha vuto lina kunyumba kapena nkhaŵa zina za moyo. Ndi udindo wanu monga wolankhula kukopa maganizo a omvera anu kuti asayendeyende. Pali njira zingapo zochitira zimenezo.
Imodzi ya nkhani zotchuka koposa pa nkhani zokambidwapo inali Ulaliki wa pa Phiri. Kodi unayamba motani? Malinga ndi kunena kwa nkhani ya Luka, Yesu anayamba ndi mawu akuti: “Odala osauka inu; . . . Odala inu akumva njala tsopano; . . . Odala inu akulira tsopano; . . . Odala inu, pamene anthu adzada inu.” (Luka 6:20-22) Kodi mawuwo anakopa chidwi chifukwa chiyani? Mwachidule, Yesu anazindikira mavuto ena aakulu amene omvera ake anali kukumana nawo. Ndiyeno, m’malo moyamba kukambirana nawo za mavutowo, anawauza kuti anthu okhala ndi mavuto otero akhoza kukhalabe achimwemwe, ndipo anawauza mwa njira imene inapatsa omverawo chidwi chofuna kumva zambiri.
Tikhoza kukopa chidwi ndi mafunso, koma akhale oyenerera. Ngati mafunso anu aonetsa kuti zimene mulankhule ndi zinthu zimene omvera anu anazimvapo kale, chidwi chawo chimangozilala nthaŵi yomweyo. Musafunse mafunso ochititsa manyazi omvera anu kapena owanyoza. M’malo mwake, yesetsani kupereka mafunso owalimbikitsa kuganiza. Mukafunsa funso, imani kaye pang’ono kuti mupatse mpata omvera anu kupeza mayankho m’maganizo mwawo. Ngati aona kuti akuyendera nanu limodzi, maganizo awo amakhala pa inu.
Njira ina yokopera chidwi ndiyo kufotokoza chochitika chenicheni. Koma kusimba chochitika chonyazitsa wina m’gulu kungawononge cholinga chanu. Ngati omvera anu adzakumbukira chochitikacho koma osati phunziro lake, ndiye kuti simunakwaniritse cholinga chanu. Ngati musimba chochitika china m’mawu anu oyamba, chiyenera kukhala maziko a mfundo yofunika ya nkhani yanu. Ngakhale kuti mbali zina zokhudza chochitikacho zingafunikire kuti chochitikacho chisimbike bwino, samalani kuti musasimbe chochitika chachitali kwambiri.
Okamba nkhani ena amayamba ndi nkhani yomwe yamveka panyuzi, mawu otengedwa m’nyuzipepala, kapena mawu a munthu wina wolemekezeka. Zimenezinso zimakopa chidwi ngati zikhala zoyenereradi nkhaniyo ndi omverawo.
Ngati nkhani yanu ndi yosiyirana kapena ndi ya pa Msonkhano wa Utumiki, mungachite bwino kwambiri kunena mawu oyamba achidule ndi olunjika. Ngati mukukamba nkhani ya onse, samalani nthaŵi yosonyezedwa ya mawu oyamba. Thunthu la nkhani ndi limene limapereka mfundo zofunikira kwambiri kwa omvera anu.
Nthaŵi zina mungamalankhule kwa anthu okayikira zimene mukunena kapena otsutsa kumene. Kodi mungatani kuti akumvetsereni? Stefano, Mkristu wakale uja amene anali “wodzala ndi mzimu ndi nzeru,” anatengedwa mwamphamvu kukaonekera pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. Atafika kumeneko analankhula bwino kwambiri potchinjiriza Chikristu. Kodi anayamba motani? Mwaulemu, anayamba ndi mfundo yovomerezeka kwa onse. “Amuna, inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu.” (Mac. 6:3; 7:2) Ku Areopagi ku Atene, mtumwi Paulo anasankha mawu ake oyamba ogwirizana ndi omvera osiyana kwambiri ndi enawo, akumati: “Amuna inu a Atene, m’zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa.” (Mac. 17:22) Chifukwa cha mawu oyamba okopawo, magulu omvera aŵiriwo anafunitsitsa kumva zambiri.
Pamene muli mu utumiki wa kumunda, inunso muyenera kukopa chidwi cha anthu. Ngati ulendo wanu sunali wopangana, mwininyumba angakhale wotanganidwa ndi zinthu zina. M’mbali zina za dziko, alendo osawadziŵa ayenera kunena msanga chimene ayendera. M’mbali zina, chikhalidwe chimafuna kuti musonyeze ulemu wakutiwakuti musananene chimene mwayendera.—Luka 10:5.
Mulimonsemo, mzimu waubwenzi ungachititse kuti pakhale makambirano abwino. Kaŵirikaŵiri zimakhala bwino kuyamba ndi nkhani yokhudza zimene mwininyumba ali nazo m’maganizo. Nanga mungadziŵe bwanji zimene muyenera kunena? Eya, kodi munthuyo mwam’peza akuchita ntchito inayake? Kapena akulima, kukonzakonza pakhomo, kukonza galimoto, kuphika, kuchapa, kapena kusamalira ana? Kodi anali kuyang’ana kanthu kena—nyuzipepala kapena chochitika china mumsewu? Kodi pakhomopo pali zinthu zoonetsa kuti amakonda kuŵedza kapena kupha nsomba, maseŵero, kuimba, kuyenda maulendo, makompyuta, kapena zinthu zina? Kaŵirikaŵiri anthu amakhudzidwa ndi zimene zamveka pawailesi kapena pawailesi yakanema. Kuperekapo funso kapena ndemanga yachidule pa iliyonse ya nkhanizo kungayambitse makambirano abwino.
Kucheza kwa Yesu ndi mkazi wachisamariya pachitsime paja, pafupi ndi mudzi wa Sukari, kunali chitsanzo chabwino kwambiri cha mmene mungayambire makambirano, ndi cholinga chochitira umboni.—Yoh. 4:5-26.
Konzekerani mawu anu oyamba mosamala, makamaka ngati mpingo wanu umagwirira ntchito m’gawo lofoledwa kaŵirikaŵiri. Kupanda kutero, simungathe kuchitira umboni.
Tchulani Nkhani Yanu. Mumpingo wachikristu, tcheyamani kapena munthu wina amene mukum’tsatira papulatifomu kaŵirikaŵiri amalengeza mutu wa nkhani yanu kenako amakuitanani. Komabe, zimachita bwino ngati inunso mukumbutsa omvera anu mutu wa nkhaniyo m’mawu anu oyamba. Musatchule mutuwo mmene ulili, koma mukhoza kunena mawu ena osonyeza nkhaniyo. Mulimonsemo, mutu wake uyenera kuonekera pamene nkhaniyo ikutambasuka. Koma m’mawu anu oyamba muyenera kuunika nkhaniyo.
Pamene Yesu anali kutumiza ophunzira ake, anasonyeza bwino lomwe uthenga umene amakalalikira. Iye anati: “Pamene mulikupita lalikani kuti, Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mat. 10:7) Ponena za tsiku lathu, Yesu anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa.” (Mat. 24:14) Tiyeni ‘tilalikire mawuwo,’ timamatire ku Baibulo pochitira umboni. (2 Tim. 4:2) Komabe, tisanatsegule Baibulo kapena tisanauze munthu za Ufumu, m’pofunika nthaŵi zonse kutchulapo nkhani imene ikudetsa nkhaŵa anthu panthaŵiyo. Mungatchule za upandu, ulova, kusoŵeka kwa chilungamo, nkhondo, njira zothandizira achinyamata, matenda, kapena imfa. Koma musatenge nthaŵi yochuluka mukulankhula nkhani zosasangalatsa; uthenga wanu ndi uthenga wolimbikitsa. Sinthirani makambiranowo ku Mawu a Mulungu ndi chiyembekezo cha Ufumu.
Sonyezani Chifukwa Chake Nkhaniyo Ili Yofunika kwa Omvera Anu. Ngati mukakamba nkhani ku mpingo, mungatsimikize kuti omvera anu adzakhala ndi chidwi chofuna kumva nkhani yanu. Koma kodi azikamvetsera, muja amachitira munthu amene akuphunzira nkhani imene imam’khudza kwambiri? Kodi adzatchera khutu chifukwa chakuti zimene akamvazo zikakhudza moyo wawo ndiponso mukawalimbikitsa kuchitapo kanthu? Zimenezo zingatheke pokhapokha mukaganizira omvera anu mosamala—mikhalidwe yawo, nkhaŵa zawo, ndi maganizo awo—pokonzekera nkhani yanu. Ngati mutero, sonyezani zimenezo m’mawu anu oyamba.
Kaya mukulankhulira papulatifomu kapena mukulalikira munthu mmodzi, imodzi mwa njira zabwino koposa zokopera chidwi ndiyo kuloŵetsa omvera anu m’nkhaniyo. Sonyezani mmene nkhani yanuyo ikukhudzira mavuto awo, zosoŵa zawo, kapena mafunso awo. Ngati mukasonyeza kuti muperekanso mayankho pankhani zowakhudza, adzamvetsera mwachidwi. Kuti mukachite zimenezo, muyenera kukonzekera bwino.
Mmene Munganenere Mawu Oyamba. Zimene munena m’mawu anu oyamba zimakhala zofunika kwambiri, koma chimene chimakopa chidwi ndi mmene mumazinenera. Pachifukwa chimenechi, musangokonzekera zimene mukanene komanso mmene mukazinenere.
Kukwaniritsa cholinga chanu kudzadalira kusankha mawu oyenerera, choncho ndi bwino kukonzekera masentensi aŵiri kapena atatu oyambirira mosamala kwambiri. Kaŵirikaŵiri, masentensi aafupi komanso osavuta amakhala bwino kwambiri. Ngati ili nkhani mumpingo, mungalembe masentensiwo pa manotsi anu kapena mungawaloŵeze pamtima kotero kuti mawu anu oyamba mukawalankhule ndi mphamvu yake yoyenerera. Kulankhula mofatsa mawu oyamba okopa chidwi kungakuthandizeni kukhazikitsa maganizo anu kuti mulankhule nkhani yonseyo.
Pamene Muyenera Kukonzekera Mawu Oyamba. Pali maganizo osiyanasiyana pamfundoyi. Okamba nkhani ena aluso amakhulupirira kuti pokonza nkhani ndi bwino kukonza kaye mawu oyamba. Ena amene anachita maphunziro a zakulankhula pamaso pa anthu amanena kuti mawu oyamba ayenera kukonzedwa pambuyo pokonzekera thunthu la nkhani.
Koma muyenera kuidziŵiratu nkhani yanu ndi mfundo zazikulu zimene mudzafotokoza musanakonze mawu oyamba oyenerera. Bwanji ngati mukukonza nkhani kuchokera pa autilaini yofalitsidwa kale? Mutaŵerenga autilainiyo, ndi kuganizira mawu oyamba abwino, palibe choletsa kuwalemba mawuwo. Kumbukiraninso, kuti mawu anu oyamba akhale okopa chidwi, muyenera kuganizira omvera anu komanso mfundo za pa autilaini yanuyo.