PHUNZIRO 19
Kulimbikitsa Omvera Kuŵerenga Baibulo
CHOLINGA chathu ndicho kulimbikitsa aliyense kuŵerenga Mawu a Mulungu, Baibulo. Buku lopatulika limenelo ndilo gwero la uthenga womwe timalalikira, ndipo tikufuna anthu azindikire kuti zimene timanena si zochokera mwa ife tokha, koma kwa Mulungu. Timafuna kuti anthu akhale olidalira Baibulo.
Mu Utumiki wa Kumunda. Pokonzekera utumiki wa kumunda, nthaŵi zonse sankhani lemba limodzi kapena aŵiri okakambirana ndi anthu ofuna kumvetsera. Ngakhale mutakonzekera ulaliki wachidule wogaŵira buku lophunzirira Baibulo, kumakhala kopindulitsa kuŵerengapo Lemba loyenerera. Baibulo lili ndi mphamvu yopambana pakutsogolera anthu onga nkhosa kuposa chilichonse chimene tinganene mwa ife tokha. Ngati n’zosatheka kuŵerenga m’Baibulo, ingonenani zimene limanena. M’zaka 100 zoyambirira, si ambiri anali ndi mipukutu ya Malemba. Komabe, Yesu ndi atumwi ake anagwira mawu kaŵirikaŵiri ochokera m’Malemba. Ifenso tikhale ndi khama loloŵeza pamtima malemba oti tiziŵerenga mu utumiki wa kumunda, ndipo nthaŵi zina tizingowagwira mawu.
Poŵerenga m’Baibulo, ligwireni moti mwininyumbayo athe kutsatira pamene mukuŵerenga. Mwininyumba akamatsatira m’Baibulo lake, amatha kulabadira mosavuta zimene waŵerenga.
Komabe, dziŵani kuti omasulira Baibulo ena atsatira maganizo awoawo pomasulira Mawu a Mulungu. Mbali zina zimene amasulira sizigwirizana kwenikweni ndi zimene zinali m’zinenero zoyambirira zimene analembera Baibulo. Mabaibulo atsopano ochulukirapo achotsa dzina lenileni la Mulungu, abisa zimene malemba a m’zinenero zoyambirira amanena za anthu akufa, ndiponso aphimba zimene Baibulo limanena pa chifuniro cha Mulungu cha dziko lapansi. Pofuna kuonetsa munthu wina zimene achita anthu amenewo, yerekezani malemba ofunika kwambiri m’mabaibulo osiyanasiyana kapena m’mabaibulo akalepo m’chinenero chimodzi. Pankhani zosiyanasiyana, buku la Kukambitsirana za m’Malemba limasonyeza mmene mabaibulo osiyanasiyana amasulira mawu ofunika m’mavesi ogwiritsidwa ntchito kaŵirikaŵiri. Aliyense wokonda choonadi adzasangalala kudziŵa zimenezi.
Pamisonkhano ya Mpingo. Tiyenera kulimbikitsa onse kuti aziŵerenga Baibulo pamisonkhano yampingo. Kuŵerenga Baibulo kumathandiza omvera m’njira zambiri. Kumawathandiza kuika maganizo pa zimene zikulankhulidwa. Kumawapatsa zithunzi za m’maganizo kuwonjezera pa malangizo omwe akuperekedwa ndi wokamba nkhani. Ndipo kumakhomereza m’maganizo mwa okondwerera atsopano mfundo yakuti Baibulo lilidi gwero la zimene timakhulupirira.
Kuti omvera anu akutsatireni m’mabaibulo awo pamene mukuŵerenga Malemba zimadalira inuyo kuwalimbikitsa. Imodzi mwa njira zabwino koposa zowalimbikitsira ndiyo kuwapempha mwachindunji.
Zili kwa inu wokamba nkhani kusankha malemba omwe mukufuna kuwamveketsa bwino oti omvera anu awaŵerenge. Ndi bwino kwambiri kuŵerenga malemba omwe angakuthandizeni kufotokoza mfundo zanu zazikulu. Ndiyeno, malinga ndi nthaŵi, wonjezerani malemba ena ochepa otsimikizira mfundo yanu.
Komabe, kungotchula lemba kapena kungopempha omvera kuti aŵerenge nanu lemba si kokwanira. Ngati muŵerenga lemba ili kenako n’kupita ku lina, omvera anu asanapeze loyamba lija, amagwa mphwayi ndipo sayesanso kukutsatirani m’Baibulo. Choncho, khalani maso. Mukaona kuti ambiri alipeza lembalo, ŵerengani.
Lingalirani pasadakhale. Tchulani lemba m’nthaŵi yabwino musanafike poliŵerenga. Zimenezi zidzasungitsa nthaŵi imene imatayika poyembekezera omvera kuti apeze lembalo. Ngakhale kuti kupatsa omvera mpata wopeza malemba kumatenga nthaŵi imene mukanafotokozera mfundo zina, mapindu ake ndi aakulu.