Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 32 tsamba 158-163
  • Kugogomeza Ganizo ndi Kusinthasintha Mawu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugogomeza Ganizo ndi Kusinthasintha Mawu
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • **********
  • Kusinthasintha Mawu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kutsindika Ganizo Moyenerera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kusinthasintha Mawu
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Uphungu Umalimbikitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 32 tsamba 158-163

Phunziro 32

Kugogomeza Ganizo ndi Kusinthasintha Mawu

1, 2. Kodi kugogomeza ganizo kuli ndi ntchito yanji m’nkhani?

1 Kugogomeza ganizo ndi kusinthasintha mawu zimagwirizana popangitsa nkhani kukhala yatanthauzo ndi yokoma. Popanda ziŵirizo, malingaliro samatuluka bwino ndipo nkhani imazizira. Pakuti kugogomeza ganizo nthaŵi zambiri kumakhala kosavuta paziŵirizo, tiyambe ndi mbali imeneyo.

2 Musaiŵale cholinga chogogomezera ganizo. Ndicho kugogomeza mawu kapena malingaliro m’njira yopereka tanthauzo lolondola ndi kusonyeza omvetsera anu kufunika kwake. Nthaŵi zina pamafunika kugogomeza kotsindika mawu kapena kopepukirapo, komanso nthaŵi zina kumangofunika pang’ono chabe.

3-7. Fotokozani mmene munthu angadziŵire kugogomeza ganizo kwabwino.

3 Kugogomeza mawu opereka ganizo m’masentensi. M’pofunika kugogomeza mawu oyenerera. Kumatheka mwa kuzindikira mawu opereka lingaliro lofunika, ndipo mwa chigogomezo kapena kunena motsindika mawu koyenerera, mumawapangitsa kuonekera kwambiri kuposa mawu ena ozungulira. Ngati mugogomeza mawu osapereka ganizo lofunikira, tanthauzo lake limaphimbika kapena kusokonekera kumene.

4 Anthu ambiri amafuna kumveketsa bwino zimene akunena m’kalankhulidwe kawo ka tsiku ndi tsiku. Mbali imeneyi siiyenera kukhala vuto kwa inu, kupatulapo ngati muli ndi chizoloŵezi choipa, monga kugogomeza mawu otchedwa aperekezi monga, pa, ku, ndi mu. Nthaŵi zonse kutsindika mawu olakwika kumachitika chifukwa cha vuto limenelo. Ngati inunso muli nalo, limbikirani kuliwongolera. Chizoloŵezi choterocho sichingathe ndi nkhani imodzi kapena ziŵiri zokha. Choncho phungu wanu adzakulolani kupitiriza ndi luso lotsatira la kulankhula ngati kugogomeza kwanu mawu osafunikira sikusokoneza tanthauzo la mawu ake. Koma kuti nkhani zanu zikakhale zamphamvu ndi zogwira mtima, limbikirani mfundo imeneyo kufikira mutazoloŵera kugogomeza mawu oyenera.

5 Nthaŵi zambiri m’pofunika kulingalira za kugogomeza ganizo pokonzekera kuŵerenga kwapoyera kuposa ndi polankhula kuchokera m’maganizo. Zili choncho makamaka poŵerenga malemba m’nkhani, monganso poŵerenga ndime paphunziro la Nsanja ya Olonda pampingo. Chifukwa chake chosamalira kwambiri za kugogomeza ganizo poŵerenga n’chakuti nkhani imene timaŵerenga imakhala italembedwa ndi munthu wina. Choncho tifunikira kuiphunzira bwino, tikumapenda malingaliro ake ndi kumabwerera m’mawuwo kufikira titawazoloŵera.

6 Kodi kugogomeza kapena kutsindika ganizo kumachitidwa motani? Pali njira zosiyanasiyana, ndipo nthaŵi zambiri zimagwiritsidwa ntchito pamodzi: mwa mphamvu ya mawu, mwa kutchula ndi mzimu wake, mwa kutsitsa mawu, mwa kukweza mawu, mwa kutchula mawu pang’onopang’ono, mwa kuwonjeza liŵiro, mwa kupuma kaye pofuna kutchula mawu kapena pambuyo potchula mawu (kapena zonse ziŵiri), mwa kugwiritsa ntchito manja ndi nkhope.

7 Choyamba onetsetsani kuti mukugogomeza mawu oyenerera komanso mokwanira kuti mawu ofunikawo aonekere. Chotero, posanja mfundo zanu, lembani mzera pansi pa mawu ofunika ngati mudzakhala mukuŵerenga. Ngati mukulankhula kuchokera m’maganizo, pangitsani mfundozo kukhala zoonekera bwino m’maganizo mwanu. Gwiritsani ntchito mawu ofunika kwambiri m’notsi zanu ndipo agogomezeni mawuwo.

8, 9. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kugogomeza mfundo zazikulu?

8 Kugogomeza mfundo zazikulu m’nkhani. Iyi ndiyo mbali ya kugogomeza ganizo imene imasoŵeka kwambiri. Zikatero nkhaniyo siikhala ndi mokwera mulimonse. Palibe chilichonse chimene chimaoneka kukhala chapadera. Pamene nkhani yoteroyo imalizidwa kaŵirikaŵiri sikutheka kukumbukira mfundo iliyonse kukhala yapadera. Ngakhale ngati mfundo zazikulu zakonzedwa bwino lomwe kuti zikaonekere, kulephera kugogomeza moyenerera poikamba nkhaniyo kungafooketse kwambiri mfundozo moti mwina osaonekanso.

9 Kuti mugonjetse vuto limenelo, choyamba muyenera kupenda nkhani yanu mosamalitsa. Kodi mfundo yaikulu kwambiri m’nkhani yanu ndi iti? Nanga yotsatira yake ndi iti? Ngati mungafunsidwe kutchula mfundo yaikulu ya nkhani yanu mwa sentensi imodzi kapena aŵiri mungati chiyani? Imeneyo ndi imodzi mwa njira zabwino kwambiri zimene mungadziŵire mfundo zazikulu. Mutazidziŵa, zilembeni mzera kunsi kwake m’notsi zanu kapena m’nkhani yanu yoŵerenga. M’mfundo zazikulu zimenezi tsopano mutha kuikamo mokwera mwake. Ndimo mokwera mwa nkhani yanu, ndipo ngati mfundo zanu mwazikonza bwino ndipo muzifotokoza ndi chigogomezo choyenerera, mfundo zazikulu zidzakumbukika. Ndicho cholinga chanu pokamba nkhani.

**********

10-12. Fotokozani zimene kusinthasintha mawu kumatanthauza.

10 Kugogomeza ganizo pang’ono kumatheketsa omvetsera kumvetsa zimene mukunena, koma kusinthasintha m’kagogomezedwe kungapangitse nkhaniyo kukhala yosangalatsa kwa iwo poimvetsera. Kodi mumayesa kusinthasintha mawu mu utumiki wanu wakumunda ndi m’nkhani zimene mumalankhula mu mpingo?

11 Kusinthasintha mawu ndiko kusinthasintha ukulu wa mawu, liŵiro ndi mphamvu yake pofuna kukopa chidwi ndi kumveketsa malingaliro amene mukuwafotokoza ndi mzimu wake monga mlankhuli. Kuti zikuyendereni bwino, kusinthasintha mawu kuyenera kuyendera m’mbali zake zonse zitatu zimene nkhani iliyonse ingalole. Mukasinthira pambali yapamwamba, mukumatsika pang’onopang’ono, muyenera kulankhula mwaumoyo, mwansangala ndi motengeka maganizo. Mukasinthira pambali yapakati, mumalankhula modekherapo, ndipo mukasinthira pambali yapansi mumalankhula mofatsa ndi mwaulemu.

12 Peŵani kulankhula ngati m’seŵero ndi mawu okwera mowonjezera kapena achisoni chopitirira. Kulankhula kwathu kuyenera kukhala kokoma, osati komveka ngati kopatulika kochititsa nthumanzi monga amachitira abusa a zipembedzo zosungitsa mwambo wachikale, kapena kwaphokoso monga amachitira alaliki ena osonkhana m’mahema. Ulemu wathu woyenera uthenga wa Ufumu sumatilola kudzionetsera mwa njira zimenezo zosemphana ndi Chikristu.

13, 14. Kodi kusinthasintha mphamvu ya mawu n’chiyani?

13 Kusinthasintha mphamvu ya mawu. Mwina njira yosavuta kwambiri yosinthasinthira mawu ndiyo kusinthasintha mphamvu ya mawu anu. Imeneyo ndi njira imodzi yofikira mokwera muja ndi kugogomeza mfundo zazikulu za nkhani yanu. Komabe, kungowonjezera mphamvu ya mawu anu nthaŵi zina sikungapangitse mfundo kuonekera. Nthaŵi zina kungazipangitse kuonekera, koma mphamvuyo ikakulitsa kwambiri imawononga cholinga chanu. Mwina mfundo zanu zingofuna mawu aubwenzi ndi achifundo m’malo mwa ofuula. Pamenepo tsitsani mawu anu koma wonjezerani ukulu wake. N’chimodzimodzi ngati mukufotokoza chinthu china chodetsa nkhaŵa kapena chochititsa mantha.

14 Ngakhale kuti kusinthasintha mphamvu ya mawu n’kofunika pofuna kusinthasintha mawu, samalani kuti musalankhule mofeŵa kwambiri moti ena n’kulephera kumva. Ndiponso musakweze mawu kwambiri mpaka kusokosera ena.

15-17. Kodi kusinthasintha liŵiro kumakometsa nkhani motani?

15 Kusinthasintha liŵiro polankhula. Alipo okamba nkhani angapo atsopano amene amatha kusinthasintha liŵiro lawo papulatifomu. Timachita zimenezo nthaŵi zonse m’kulankhula kwathu kwa tsiku ndi tsiku chifukwa mawu athu amatuluka mwachibadwa tikangowaganizira kapena tikawafuna. Koma nthaŵi zambiri mlankhuli watsopano samachita zimenezo papulatifomu. Amakonzekera mawu ake ndi malankhulidwe ake mosamalitsa kwambiri, kwakuti mawu onse amatuluka paliŵiro limodzi. Kulankhula kuchokera pa autilaini kungathandize kuwongolera chofooka chimenecho.

16 Mbali yaikulu ya nkhani yanu iyenera kukhala paliŵiro lachikatikati. Mfundo zazing’ono, kusimba chochitika, ambiri a mafanizo, ndi zina zotero, zimakulolani kufulumirako. Mutafika pambali zofunikira kwambiri, komanso mokwera mwake ndiponso pamfundo zazikulu, kaŵirikaŵiri n’kofunika kulankhula modekha. Nthaŵi zina, pofuna kugogomeza kwambiri, mungalankhule pang’onopang’ono koma motsindika mawu. Nthaŵi zina mukhoza kuima kumene, kanthaŵi pang’ono, kumene kumakhala kusinthiratu liŵiro.

17 Naŵa mawu ochenjeza pang’ono. Musalankhule mofulumira kwambiri kwakuti mawu anu n’kusamveka bwino. Njira yabwino koposa yopangira pulakatisi ndiyo kuyesa kuŵerenga panokha mofuula koma mofulumira kwambiri popanda kukhumudwa. Ŵerenganinso ndime imodzimodziyo mobwerezabwereza, mukumawonjezera liŵiro lanu popanda kupunthwa kapena kusatchula bwino mawu. Ndiyeno yesani kuŵerenga pang’onopang’ono kwambiri, mu-ku-ma-ko-ke-ra ma-va-we-lo m’malo modulira mawu. Ndiyeno fulumirani, kenako pang’onopang’ono, mukumasinthasintha motero kufikira mawu anu atazoloŵera kusinthasintha moti mutha kulankhula mmene mungafunire. Tsopano pamene mulankhula, liŵiro lanu lizisintha lokha, molingana ndi ganizo la chimene mukunena.

18-20. Fotokozani mmene munthu angadziŵire kusinthasintha ukulu wa mawu.

18 Kusinthasintha ukulu wa mawu. Kusinthasintha ukulu wa mawu mwina ndiko njira yovuta kwambiri yosinthasinthira mawu, ndipo ndi pambali iliyonse. Inde, timagogomeza mawu nthaŵi zonse mwa kukweza pang’ono ukulu wa mawu, komanso mwa kuwonjezera mphamvu yake pang’ono. Timachita ngati kuwagunda mawuwo.

19 Koma kusinthasintha kwina kwa ukulu wa mawu koposa kumeneku kumafunika ngati mufuna kupeza phindu lalikulu pambali imeneyi yosinthasintha mawu. Yesani kuŵerenga mofuula Genesis 18:3-8 ndi 19:6-9. Onani kusinthasintha kosiyanasiyana kwa liŵiro ndi ukulu wa mawu kofunikira m’mavesi ameneŵa. Kulankhula mwaumoyo ndi mwansangala nthaŵi zonse kumafuna kukweza mawu mosiyana ndi polankhula mwachisoni kapena mwankhaŵa. Pamene mikhalidwe imeneyi ipezeka m’nkhani yanu, isonyezeni molingana ndi mzimu wake.

20 China cholepheretsa m’mbali imeneyi ya kulankhula ndicho kulephera kusinthasintha mawu. Ngati limenelo ndilo vuto lanu, yesetsani kuliwongolera. Yesani pulakatisi yofanana ndi imene tatchula ija m’nkhani ino. Komabe, pambali imeneyi, limbikirani kukweza ndi kutsitsa mawu m’malo mwa kusinthasintha liŵiro.

21-24. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti kusinthasintha mawu kuyenerane ndi ganizo kapena mzimu wake wa mawuwo?

21 Kusinthasintha mawu koyenerana ndi ganizo kapena mzimu wake. Mwa zimene tafotokoza pa luso limeneli mpaka pano, n’koonekeratu kuti sitimangosinthasintha mawu mulimonse mmene tingafunire. Mawu anu ayenera kuyenerana ndi mzimu wake wa zimene mukunena. Nangano kusinthasintha mawu kumayambira pati? Mwachionekere, kumayamba ndi nkhani imene mwakonzekera kukailankhula. Ngati nkhani yanu ndi yopereka zifukwa basi kapena kulimbikitsa kokhakokha, kulankhula kwanu sikudzasinthasintha kwambiri. Choncho pendani autilaini yanu mutaitsiriza ndipo onetsetsani kuti ili ndi mbali zonse zosiyanasiyana kuti ikhale yosangalatsa ndi yatanthauzo.

22 Nthaŵi zina zimachitika kuti pamene muli m’kati mwa nkhani yanu mukuona kuti m’pofunika kuti musinthe liŵiro lanu. Mumaona kuti nkhani yanu siikukoka. Pamenepo muyenera kuchitanji? Apanso kulankhula kochokera m’maganizo kumakhala kothandiza. Mukhoza kusintha mtundu wa mfundo zanu pamene muli m’kati molankhula. Motani? Njira imodzi ndiyo mwa kuleka kulankhula ndi kuyamba kuŵerenga lemba m’Baibulo. Kapena mutha kusintha mawu ena kuwapanga funso, ndi kupuma pang’ono pofuna kugogomeza. Mwinanso mukhoza kuphatikizapo fanizo, monga poloŵetsera mfundo ina m’nkhani yanu.

23 Komabe, maluso ameneŵa n’ngofunika kugwiritsa ntchito alankhuli ozoloŵera. Koma mutha kugwiritsa ntchito maganizo amodzimodziwo pokonzekera nkhani yanu nthaŵi idakalipo.

24 Pali mawu akuti kusinthasintha mawu ndiwo mchere wa nkhani. Ngati muthiramo mtundu woyenera komanso mlingo wake, nkhani yanu idzakoma kwabasi ndipo idzasangalatsa omvetsera anu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena