Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 10 tsamba 13
  • Kusinthasintha Mawu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusinthasintha Mawu
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Kusinthasintha Mawu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kugogomeza Ganizo ndi Kusinthasintha Mawu
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Mphamvu ya Mawu Yoyenerera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kulankhula ndi Mtima Wonse
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 10 tsamba 13

PHUNZIRO 10

Kusinthasintha Mawu

Lemba

Miyambo 8:4, 7

MFUNDO YAIKULU: Muzilankhula momveka bwino ndipo muzisinthasintha mawu, pena kukweza pena kutsitsa, pena kulankhula mofulumira pena pang’onopang’ono.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Pena muzikweza mawu pena kuwatsitsa. Mungakweze mawu kuti mutsindike mfundo yofunika kapena kuti mulimbikitse anthu kuchita zinazake. Mungachitenso zomwezo powerenga uthenga wachiweruzo wa m’Baibulo. Mungatsitse mawu pothandiza anthu kuyembekezera kumva mfundo inayake kapena pofotokoza zinthu zochititsa mantha kapena zodetsa nkhawa.

    Mfundo yothandiza

    Koma sikuti muzingokwezakweza mawu mpaka kufika pokhala ngati mukukalipira anthu. Muzipewa kuchita zinthu mokokomeza kapena mofuna kuti anthu akutameni.

  • Pena muzilankhula mawu aakulu pena aang’ono. Ngati n’zololeka m’chilankhulo chanu, muzisintha mawu potsindika mfundo, ponena zinthu zazikulu kapena pofotokoza zinthu zimene zili patali. Muzisinthanso mawu ponena zinthu zomvetsa chisoni kapena zodetsa nkhawa.

  • Pena muzilankhula mofulumira pena pang’onopang’ono. Muzilankhula mofulumira posonyeza kusangalala koma pang’onopang’ono mukamatchula mfundo yofunika kwambiri.

    Mfundo yothandiza

    Kuti mawu anu asachite kudabwitsa anthu musamasinthe mwadzidzidzi. Musamalankhule mofulumira kwambiri kufika poti anthu azilephera kukutsatirani.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena