Mutu 6
Kodi Mulungu Wakhala Akuchitanji?
1. Kodi nchiyani chimene anthu ochuluka lerolino amakhulupirira ponena za Mulungu, koma kodi nzowona?
ANTHU ambiri lerolino amakhulupirira kuti Mulungu saali wokondweretsedwa kwambiri ndi dziko lapansi kapena kuti sali kuchita kanthu kalikonse ndi mavuto ovutitsa anthu. Koma chowonadi ndichakuti Mulungu amasamala kwambiri. Zowona, iye angakhale asanachite zimene anthu anamuyembekezera kuchita. Koma chimenechi sichitanthuza kuti iye sanachite kanthu. Kwenikweni, iye wakhala akuchita zinthu kuthandiza anthu kuyambira pachiyambi cha mbiri ya anthu kufikira lerolino.
2. Kodi ndimotani mmene kufupika kwa utali wa moyo wawo kungayambukirire kulingalira kwa anthu pankhaniyi?
2 Chifukwa chimodzi chimene anthu ena amanenera kuti Mulungu sakuchita kanthu kalikonse ndicho kufupika kwautali wa nthawi ya moyo wawo. Kumeneku kumawapangitsa kukhala otekeseka maganizo kuchititsa zinthu kuti zichitidwe m’nthawi yaifupi imene moyo wawo umalola. Chotero chikhumbo cha kuwona masinthidwe mkati mwa nthawi ya moyo wawo chimalamulira kuganiza kwawo. Pamenepa, chikhoterero chawo, ndicho kuweruza Mulungu pamaziko a chidziwitso chotero chaumunthu, limodzi ndi zoperewera zake zonse.
3. Kodi ndimotani mmene utali wa moyo wa Yehova umayambukirira kukhoza kwake kuchita ndi mikhalidwe panthawi yoyenelera yabwino kopambana?
3 Kumbali ina, Yehova amakhala ndi moyo kosatha. (Salmo 90:2, 4; Yesaya 44:6) Mwalingaliro lake iye angathe kuwona bwino lomwe pamene m’kupita kwa nthawi machitidwe ake adzachitira zabwino kopambana aliyense woloŵetsedwamo kudzanso kuchitika kogwira mtima kwa chifuniro chake. (Yesaya 40:22; 2 Petro 3:8, 9) Chimenechi ndicho chimenedi Mulungu wakhala akuchita.
Mmene Mulungu Wadzivumbulira
4. Kodi nchiyani chimene Yehova walengeza kukhala chifuno chake, ndipo chotero kodi iye wapatsa anthu chidziŵitso chotani?
4 Chifuno cha Yehova ndicho kupereka boma lolungama kaamba ka cholengedwa chonse, iro limene lidzagwirizanitsa anthu m’mtendere ndi umodzi, akumakhala ndi chisungiko chokwanira. (Aefeso 1:9, 10; Miyambo 1:33) Komabe, Mulungu samaumiriza munthu aliyense kulamulidwa ndi boma lake. Awo okha amene amamtumikira ndi amene amakonda kalamuliridwe kake amalandiridwa. Ali ndi cholinga cha kukhazikitsa dziko lathunthu limene likakhala ndi moyo mogwirizana ndi miyeso yolungama ya boma lake, Mulungu wapatsa anthu chidziŵitso cha miyezo imeneyo ndi mmene boma lake limagwirira ntchito. Panthawi imodzimodziyo Mulungu wakhala akutheketsa anthu kupeza chidziwitso chofunika chonena za iyemwini ndi mikhalidwe yake.—Yohane 17:3.
5. Kuchokera m’ntchito zachilengedwe, kodi tingaphunzirenji ponena za Mulungu?
5 Ndithudi, pokhala mzimu, Yehova ali wosawoneka kwa anthu. Chotero, kodi ndimotani mmene iye akapangitsira anthu athupi ndi mwazi kuzindikira zinthu zimenezi? Choyamba, zochuluka zingathe kuphunziridwa ponena za mikhalidwe ya Mlengi kuchokera kuntchito za manja ake. (Aroma 1:20) Kugwirizana kodabwitsa pakati pa zinthu za moyo ndi malamulo a chilengedwe amene amalamulira zinthu zonse kumachitira umboni nzeru zake. Mphamvu yaikulu kwambiri yosonyezedwa m’nyanja za mchere, m’mphepo, ndi m’nyonga za nyenyezi zimapereka umboni wa kukhala kwake wamphamvuyonse. (Yobu 38:8-11, 22-33; 40:2) Ndipo mitundu yosiyanasiyana ya zakudya zokoma, kukongola kwa maluŵa, mbalame, kutuluka kwa dzuŵa ndi kuloŵa kwa dzuŵa, ndi mikhalidwe yodabwitsa ya maseŵera ya zinyama—zonsezo zimasonyeza kukonda anthu kwa Mlengi ndi chikhumbo chake chakuti tipeze chisangalalo m’moyo. Komabe kudzivumbula kwa Mulungu sikumathera pa zinthu zimenezi.
6. (a) Kodi ndimwanjira yotani imene Mulungu waperekera zivumbulutso zotsimikizirika za chifuniro chake? (b) Kodi ndinjira zina zotani zimene Mulungu wavumbulira njira zake ndi mikhalidwe kwa anthu?
6 Panthawi zosiyanasiyana iye walankhulanso ali kumwamba. Nthawi zina anachita izi mwachindunji. M’nthawi zina analankhula kupyolera mwa angelo, monga pa Phiri la Sinai pa Ndomo ya Arabiya, pamene anapereka chilamulo chake kwa Aisrayeli mamaliyoni ambiri. (Eksodo 20:22; Ahebri 2:2) Ndiyeno, kupyolera mwa aneneri ake iye analankhula ndi anthu mkati mwa nyengo ya zaka mazana ambiri, ndipo iye anawachititsa kulembedwa kwa zovumbulutsidwa za chifuniro chake. (2 Petro 1:21) Motero, mwapang’ono pang’ono, Yehova wadziŵitsa anthu miyezo Yake yolungama ndi chifuniro Chake. Mbali yofunika ya ichi ndiyo njira imene wavumbulira nayo malamulo ake a makhalidwe abwino ndi mikhalidwe mwanjira ya zochita zake ndi anthu. Izi zawonjezera kukondweretsa kwambiri kwa chidziŵitso cha anthu cha Mawu ake olembedwa. Ha ndikolimbikitsa kwambiri ndi kokhutiritsa maganizo chotani nanga osati kokha kumva ndi kuŵerenga zilengezo za Mulungu za zifuno, komanso kukhala ndi zitsanzo za moyo zolembedwa m’Baibulo zimene zimatithandiza kuzindikira bwino kwambiri chifuniro chake! (1 Akorinto 10:11) Ndipo kodi cholembedwa chimenecho chikuvumbulanji?
7. (a) Kodi Mulungu wasonyeza motani kuti samalekerera kosatha kuipa? (b) Titadziŵa mmene Mulungu amawonera khalidwe loterolo, kodi tiyenera kuchitanji?
7 Chimapereka umboni wakuti Mulungu samalekerera chisalungamo kosatha. Nzowona, iye analola ana a Adamu ndi Hava kuchita monga momwe anafunira, akumapanga mbiri yotsimikizirika ya kusakhoza kwa munthu kudzilamulira mwachipambano. Koma Mulungu sanasiye anthu ali opanda umboni wa chiweruzo Chake panjira zawo zosalungama. Motero iye anadzetsa chigumula m’tsiku la Nowa chifukwa chakuti ‘dziko lapansi linadzala ndi chiwawa.’ (Genesis 6:11-13) Iye anawononga mizinda yoipa mwamakhalidwe ya Sodomu ndi Gomora. (Genesis 19:24, 25; Yuda 7) Iye analola mtundu wa Israyeli, umene unadzinenera kukhala ukumtumikira, kuloŵa muukapolo chifukwa cha kugwiritsira ntchito chipembedzo chonyenga. (Yeremiya 13:19, 25) Titaphunzira mmene Mulungu amawonera khalidwe lotero, ife tiri ndi mwaŵi wa kupanga masinthidwe m’miyoyo yathu kusonyeza kukonda kwathu chilungamo. Kodi tidzatero?
8. Pamene Mulungu adzetsa chiwonongeko, kodi pali opulumuka alionse? Fotokozani mwafanizo.
8 Cholembedwa Chabaibulo chimavumbulanso kuti Mulungu amasiyanitsa pakati pa olungama ndi oipa. M’Chigumula chapadziko lonse lapansi, Mulungu sanawononge Nowa, amene anali “mlaliki wa chilungamo,” koma anampulumutsa ndi ena asanu ndi awiri. (2 Petro 2:5) Ndipo, moto ndi sulfure zisanavumbire pa Sodomu, kupulumuka kunapangitsidwa kukhala kothekera kwa Loti wolungamayo ndi banja lake.—Genesis 19:15-17; 2 Petro 2:7.
9. Kodi timaphunziranji kuchokera kunjira imene Yehova anachitira ndi Israyeli wakale?
9 Pamene anthu a Israyeli, amene anali atalumbira kutumikira Mulungu, anatsimikizira kukhala osakhulupirika iye sanawataye panthawi yomweyo. Monga mowe iye anawauzira kuti: “Ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamaŵa ndi kuwatumiza iwo.” Koma iwo sanamvere. (Yeremiya 7:25, 26) Ngakhale pamene nthawi ya kuwonongedwa kwa Yerusalemu inayandikira, Yehova anati: “Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa . . . sindiko kuti abwerere kuleka njira yake, ndi kukhala ndi moyo? . . . Chifukwa chake bwererani, nimukhale ndi moyo.”—Ezekieli 18:23, 32.
10. Kuphatikiza pa kukhala kwake wodekha, kodi zolembedwa zimenezi zimatiphunzitsanso chiyani ponena za Mulungu?
10 Pamenepa, kodi tikuwonanji? Kuti m’mkhalidwe umene umakhudza kwambiri mtima wa anthu okonda chilungamo, Yehova wasonyeza bwino lomwe kudekha kwake kwakukulu ndi anthu. Panthawi imodzimodziyo, machitidwe akewo amagogomezeranso mwamphamvu pa ife kukonda kwake chilungamo ndi kufunika kwa kukhala kwathu ndi moyo mogwirizana ndi zofunika zake.
11. (a) Kodi ndimawu otani okhala ndi chifuno amene Yehova ananena mu Edene? (b) Kodi Mulungu wakhala akuchitanji kuyambira pamenepo?
11 Kanthu kenanso, kakakulu kwambiri, kakuwonekera. Kuyambira pa chiyambi, kukukhala kowonekera bwino kuti Mulungu wakhala ndi chifuno chotsimikizirika m’chirichonse chimene iye wachita. Ndipo iye sanalephere konse kuchitapo kanthu pamene kukwaniritsidwa kwa chifuniro chake kunafunikira kuchitapo kanthu. Chifuno chachikulu ichi chinalongosoledwa mu Edene mwenimwenimo. Popereka chiweruzo pa Satana, Yehova ananeneratu kuti Satana akakakhala ndi mwaŵi wa kutulutsa “mbewu,” awo amene akasonyeza mikhalidwe yake ndi kum’chirikiza. Iye ananeneratunso kutulutsidwa kwa “mbewu,” ina, wolanditsa wolungama. Ameneyu akakantha “njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana” ndi nkhonya yakupha motero kumasula anthu ku ulamuliro wake woipa. (Genesis 3:15; Chivumbulutso 12:9) Atanena mawu okhala ndi chifuno amenewa Yehova anapitiriza kupanga makonzedwe otsimikizirika a boma limene potsirizira pake likayendetsa zinthu za padziko lapansi pansi pa “mbewu” yolonjezedwa. Ntchito yokonzekera imeneyi ikatenga nthawi, monga momwe tidzawonera.
Chifukwa Chake Iye Anachita Mwachindunji ndi Israyeli Wakale
12, 13. (a) Kodi nchifukwa ninji Mulungu anasankha Israyeli ndi kupereka malamulo ake kwa mtundu umodzi wokhawo? (b) Chotero, kodi tingaphunzirenji m’mbiri ya Israyeli ndi ija ya mitundu inayo?
12 Kalekale mitundu yalerolinoyi isanakhaleko, Mulungu anasankha mtundu umodzi umene anagwiritsira ntchito kwa zaka mazana ambiri monga anthu ake. Chifukwa ninji? Kuti apereke chitsanzo chamoyo cha kugwira ntchito kwa malamulo ake a makhalidwe abwino olungama. Mtundu umenewu, Israyeli wakale, unapangidwa ndi mbadwa za Abrahamu, munthu amene anasonyeza chikhulupiriro chachikulu mwa Mlengi. Kwa iwo Yehova anati: “Sichinali chifukwa cha kukhala kwanu ochuluka kwambiri mwa mitundu yonse kuti Yehova anakukondani kotero kuti anakusankhani, pakuti inu munali apang’ono kwambiri mwa mitundu yonse. Koma chinali chifukwa cha kukukondani kwa Yehova, ndi chifukwa cha kusunga kwake lumbiro limene iye analumbirira makolo anu.”—Deuteronomo 7:7, 8, NW; 2 Mafumu 13:23.
13 Atawalanditsa kuukapolo mu Igupto, Yehova anawalonjeza kuwalowetsa mu unansi wapadera ndi iye, ndipo iwo anayankha kuti: “Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita.” (Eksodo 19:8) Pamenepo Yehova anawapatsa maweruzo ake, mwakutero anawasiyanitsa ndi mitundu ina yonse ndipo anapereka chidziwitso chatsatanetsatane chonena za miyezo yake yolungama. (Deuteronomo 4:5-8) Chotero, mbiri ya Israyeli wakale imapereka cholembedwa chonena za chimene chimachitika pamene malamulo olungama a Mulungu amveredwa kapena kusamveredwa. Panthawi imodzimodziyo, mbiri ya mitundu ina imavumbula chotulukapo kwa awo amene amakhala ndi moyo popanda lamulo la Mulungu.
14. (a) Kodi Mulungu analakwila mitundu yosakhala Yachiisrayeli mwa kusalowerera m’zochitika zawo? (b) Komabe, kodi inapindula motani ndi kukoma mtima kwapadera kwa Mulungu?
14 Bwanji nanga ponena za mitundu ina imeneyo? Inachita monga momwe inafunira, ikumasankha mipangidwe yawoyawo ya boma. Anthu awo sanali opandiratu ubwino wonse m’miyoyo yawo. Iwo anali chikhalirebe ndi mphamvu ya chikumbumtima, ndipo chimenechi nthawi zina chinawachititsa kuchitira mwachifundo anthu anzawo. (Aroma 2:14; Machitidwe 28:1, 2) Koma uchimo wawo wacholoŵa ndi kukana kwawo chitsogozo cha Mulungu zinawachititsa kutsatira kulondola njira yofuna zawo zokha imene inatsogolera kunkhondo zankhanza ndi machitachita oipa. (Aefeso 4:17-19) Ndithudi Mulungu sakanapatsidwa thayo la masoka amene anadza mwanjira ya moyo imene anadzisankhira iwo eni. Nthawi zokha zimene Mulungu anadodometsa zinali pamene machititidwe a anthu anali kuwombana ndi kuchitika kwa zifuno zake. Panthawi imodzimodziyo, Mulungu mwachifundo anawalola kukhala ndi mbali m’chisangalalo cha kukhala ndi moyo, zokongola zachilengedwe ndi zipatso za dziko lapansi.—Machitidwe 14:16, 17.
15. Kodi ndimakonzedwe otani amene Mulungu anali kulinganiza kaamba ka kudalitsa anthu a mitundu imeneyi potsirizira pake?
15 Ndiponso Yehova sanapatule anthu a mitundu imeneyi kuti potsirizira pake asalandire mapindu olonjezedwa kupyolera mwa “mbewu” ya Abrahamu. Yehova anati ponena za “mbewu” yake imene inayenera kudza kupyolera m’mzera wabanja la Abrahamu kuti: “Mwanjira ya mbewu yako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadzidalitsadi chifukwa chakuti wamvera mawu anga.” (Genesis 22:18, NW) Chotero ngakhale kuli kwakuti Yehova anali kuchita mwapadera ndi Israyeli, iye mopanda tsankho anali kulinganiza chifuno chake cha kudalitsa mitundu ina pambuyo pake, ngakhale kuli kwakuti iyo inali yosadziŵa za ichi.—Machitidwe 10:34, 35.
16. (a) Mkati mwa nthawi yonseyi, kodi Mulungu anali kuchitanji mogwirizana ndi lonjezo lonena za Mbewu? (b) Kodi ndani amene anadzatsimikizira kukhala Mbewu ya lonjezo imeneyo?
16 Mkati mwa nthawi imene Yehova anali kuchita ndi Israyeli wakale, anapereka maulosi ambiri amene anakwaniritsa chosowa chofunika kwambiri kaamba ka anthu a chikhulupiriro—mmene akadziŵira Mbewu yolonjezedwa ya Abrahamu pamene iyo potsirizira pake inafika. Ngakhale mzera wabanja lake, kupyolera mwa fuko la Yuda ndi nyumba ya Davide, zinatchulidwa mwachindunji. (Genesis 49:10; Salmo 89:35, 36) Malo ake obadwira, Betelehemu, anatchulidwa. (Mika 5:2) Zaka mazana ambiri pasadakhale, chaka chenicheni chimene iye akadzozedwa monga Mesiya chinatchulidwa. (Danieli 9:24-27) Mautumiki ake aunsembe otumikira anthu anaphiphiritsiridwa. Chimodzimodzi ndi nsembe ya iye mwini inatsegula mwaŵi wa moyo wamuyaya kaamba ka mitundu yonse. (Ahebri 9:23-28) Motero, pamene nthawi yoikidwiratuyo inafika, chinthu chirichonse mosalakwika chinasonyeza Yesu Kristu kukhala Mbewu yolonjezedwa mwa imene potsirizira pake madalitso akadzera kwa anthu.—Agalatiya 3:16, 24; 2 Akorinto 1:19, 20.
Kukonzekeretsedwa kwa Olamulira a Anthu
17. Kupyolera mwa Yesu, kodi Mulungu akadzetsa chiyani, ndipo ndimotani mmene chimenechi chinagogomezedwera panthawi ya kubadwa kwake?
17 Kubadwa kwa Yesu kusanachitike mayi wake Mariya anali atauzidwa ndi mngelo kuti mwana wake akapatsidwa ufumu wosatha. Abusa okhala pafupi ndi Betelehemu anauzidwa za kubadwa kwake, ndiyeno iwo anamva khamu la magulu akumwamba likutamanda Mulungu ndi kunena kuti: “Ulemerero kumwambamwamba kwa Mulungu, ndi padziko lapansi, mtendere pakati pa anthu oyanjidwa.”—Luka 1:31-33; 2:10-14, NW.
18. (a) Kodi zokumana nazo zake pa dziko lapansi zinamkonzekeretsa m’njira yotani kaamba ka malo antchito a mfumu ndi wansembe? (b) Kodi imfa yake inali ndi chiyambukiro chotani pa kupezedwa kwa mtendere?
18 Talingalirani mapindu akukhala kwa mfumu yamtsogolo yakumwamba imeneyi ndi moyo padziko lapansi. Monga munthu anafikira pa kudziŵa ndi kuzindikira mavuto a anthu. Iye anakhala ndi kugwira ntchito limodzi nawo, akumamva chisoni limodzi nawo, ndi kukumana ndi mavuto iyemwini. Pansi pa ziyeso zoŵaŵa kopambana iye anasonyeza kukhulupirika kwake kwa Yehova ndi kukonda kwake chilungamo. Mwanjirayi Mulungu anali kukonzekeretsa Yesu kukhala Mfumu yomvetsetsa kudzanso Mkulu wa Ansembe wooti apereke mapindu opatsa moyo kwa anthu. (Ahebri 1:9; 4:15; 5:8-10) Ndiponso, mwakupereka nsembe moyo wake, Yesu Kristu anatsegula njira kaamba ka anthu kupezanso maunansi amtendere ndi Mulungu.—1 Petro 3:18.
19. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu anaukitsidwa ndi kukwera kumwamba? (b) Ponena za ufumu wake, kodi anachitanji atakwera kumwamba?
19 Pambuyo pa imfa ya Yesu Mulungu anamuukitsira kumoyo kachiŵirinso, ndipo anawonedwa ndi mboni zaumunthu zoposa 500 zimene zikanachitira umboni kuti chiukirirocho chinali chitachitikadi. (1 Akorinto 15:3-8) Masiku makumi anai pambuyo pa kuukitsidwa kwa Yesu, iye anakwera kumka kumwamba nazimiririka kumaso kwa ophunzira ake owonererawo. (Machitidwe 1:9) Iye ali kumwamba anapitirizabe kusonyeza ufumu wake kwa otsatira ake okhulupirika, ndipo mapindu a ulamuliro wake anawapangitsa kukhala apadera mosiyana ndi anthu ena onse. Koma kodi tsopano inali nthawi yokwanira kwa iye kuyamba kulamulira amitundu? Ayi, pakuti zinthu zina m’programu yaikulu ya Mulungu zinafunikira chisamaliro.—Ahebri 10:12, 13.
20. Kodi ndintchito yatsopano yotani imene Yesu anambulira njira ophunzira ake padziko lapansi?
20 Ntchito yaikulu inayenera kuchitidwabe padziko lonse lapansi. Imfa ndi chiukiriro cha Yesu zisanachitike palibe Aisrayeli amene anapita monga alaliki kukatembenuza anthu amitundu ina. Komabe nthawi zonse alionse amene anafuna kulambira Yehova akanatha kulandira madalitso limodzi ndi Israyeli. (1 Mafumu 8:41-43) Komabe, kuyambika kwa Chikristu kunatsegula ntchito yaikulu yatsopano. Yesu Kristu mwiniyo anapereka chitsanzo naisiya monga mphatso kwa ophunzira ake, akumawauza asanakwere kumwamba kuti: “Mudzakhala mboni zanga ponse paŵiri m’Yerusalemu ndi m’Yudeya monse ndi m’Samariya ndi kumalekezero a dziko lapansi.”—Machitidwe 1:8, NW.
21. Mmalo mwa kutembenuzidwa kwa dziko lonse, kodi Mulungu anali kuchitanji mwanjira ya kuchitira umboni kumeneko?
21 Kodi cholinga chinali kutembenuzidwa kwa dziko lonse? Ayi. Mmalo mwake, Yesu anasonyeza kuti mkati mwa nyengo yonse kufikira mu “mapeto adongosolo lazinthu” pakakhala kusonkhanitsidwa pamodzi kwakukulukulu kwa “ana aufumuwo.” Inde, ziwalo zina za boma la Ufumu lirinkudza zinafunikira kusankhidwa. (Mateyu 13:24-30, 36-43) Aliyense woŵerenga Malemba Achikristu Achigiriki angathe kuwona mosavuta kuti kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., ena anali kuitanidwa kukhala ndi phande limodzi ndi Yesu Kristu mu ulamuliro wake Waufumu kumwamba.—2 Timoteo 2:12; Ahebri 3:1; 1 Petro 1:3, 4.
22. (a) Kodi Mulungu anafuna mikhalidwe yotani mwa oyembekezera kukhala oloŵa nyumba a Ufumu wakumwamba amenewa? (b) Chotero, kodi kusankhako kunachitidwa mwandithendithe?
22 Kusankha olamulira anzake pa mtundu wa anthu amtsogolo amenewa kukatenga nthawi. Chifukwa ninji? Choyamba, mwaŵi umenewo unafunikira kuperekedwa kwa anthu amitundu yonse. Ndipo, pamene kuli kwakuti ochuluka anadzinenera kukhala ataugwira, owerengeka anatsimikiziradi kukhala otsatira okhulupirika a Mwana wa Mulungu. (Mateyu 22:14) Miyezo yapamwamba inayenera kufikiridwa. Ngakhale kuti Akristu sanakhale ndi moyo monga gulu lolekana lamtundu mofanana ndi Israyeli wakale, iwo awonedwa kukhala ngati alendo, ochirikiza njira ina ya moyo. (1 Petro 2:11, 12) Iwo ayenera kudzisunga ali oyera ku machitachita achisembwere ndi oipa a dziko lowazinga. (1 Akorinto 6:9, 10) Kuti akhaledi “ana a Mulungu,” ayenera kudzitsimikizira kukhala ‘amtendere,’ osalowa m’nkhondo za amitundu ndi kusabwezera pozunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. (Mateyu 5:9; 26:52; Aroma 12:18, 19) Ayenera kusonyeza kukhulupirika ku ulamuliro wa Mulungu mwa kukana kuchirikiza maboma andale zadziko, ophiphiritsiridwa m’Baibulo kukhala ‘zirombo.’ (Chivumbulutso 20:4, 6) Chifukwa cha zonsezi ndi chifukwa chakuti iwo amamatira ku dzina la Yesu Kristu pantchito yake monga Mfumu yodzozedwa ya Mulungu, iwo akhala ‘odedwa ndi mitundu yonse.’ (Mateyu 24:9) Chotero awo amene ayenera kukhala olamulira akumwamba a anthu limodzi ndi Kristu sanasankhidwe mofulumira.
23. (a) Kodi ndiangati amene ayenera kukhala m’bungwe lolamulira lakumwamba limenelo limodzi ndi Kristu? (b) Kodi iwo asankhidwa kuchokera mwa ayani, ndipo chifukwa ninji?
23 Utali wanthawi yotengedwayo suunali chifukwa chakuti chiŵerengero chosankhidwacho chinayenera kukhala chachikulu. Malinga ndi kunena kwa Malemba, Mulungu anaika malire a chiŵerengero cha bungwe lolamulira losankhidwa lokhala pansi pa Yesu Kristu limeneli kukhala anthu 144 000 okha. (Chivumbulutso 14:1-3) Koma Mulungu wawasankha mosamalitsa. Iwo atengedwa mwa “mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse.” (Chivumbulutso 5:9, 10) Pakati pawo pali anthu ochokera m’mikhalidwe yonse ya moyo, amuna ndi akazi, anthu amene akumana ndi mavuto osiyanasiyana amtundu wa anthu. Mkati mwakuvala kwawo umunthu watsopano Wachikristu, palibiretu vuto limene ena a iwo sanakumane nalo ndi kulilaka. (Aefeso 4:22-24; 1 Akorinto 10:13) Ha ndiachimwemwe chotani nanga mmene tingakhalire kaamba ka chimenechi! Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti chimatipatsa chitsimikiziritso chakuti iwo adzakhala mafumu ndi ansembe omvera chisoni ndi achifundo, okhoza kuthandiza amuna ndi akazi amitundu yonse kupindula kuchokera ku makonzedwe a Mulungu a moyo wamuyaya.
24. Bwanji ponena za anthu ena mamiliyoni ambiri amene anakhala ndi moyo ndi kufa mkati mwa nthawi imeneyo, ambiri a iwo osadziŵa Baibulo?
24 Bwanji ponena za anthu kunja kwa kakonzedwe aka? Mkati mwa nthawi yonseyi Mulungu sanadodometse maboma osiyanasiyanawo. Iye analola anthu kuyenda m’njira imene iwo anasankha. Ndithudi, anthu mamiliyoni ambiri anakhala ndi moyo ndi kufa, ambiri a iwo sanamve konse za Baibulo kapena Ufumu wa Mulungu. Komabe Mulungu sanawaiwale. Anali kukonzekera nthawi imene mtumwi Paulo anainena kuti: “Ndiri ndi chiyembekezo kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala chiwukiriro cha olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15, NW) Ndiyeno, pansi pa mikhalidwe yabwino kopambana, m’Dongosolo Latsopano la Mulungu, iwo adzapatsidwa mwaŵi wokwanira wa kuphunzira njira za Yehova. Pamaziko a izi iwo akatha kutenga kaimidwe kawo pankhani ya ulamuliro wachilengedwe chonse. Awo amene akonda chilungamo akapeza mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha.
Pamene “Mapeto” Akuyandikira
25, 26. (a) M’nthawi yokwanira, kodi ndiulamuliro wowonjezereka wotani umene Kristu akapatsidwa, ndipo iye akachitapo kanthu motsutsana ndi ayani? (b) Kodi chimenechi chikayambukira motani mikhalidwe pa dziko lapansi?
25 Dongosolo latsopano limenelo lisanadze, zochitika zokondweretsa ziyenera kuchitika. Baibulo linaneneratu kusintha kwakukulu m’zochitika za dziko. Pamenepo Yesu Kristu akakhazikitsidwa pampando wachifumu monga Mfumu osati kungolamulira pa ophunzira ake okha koma wokhala ndi ulamuliro wakuchitapo kanthu kudziko lonse. Chilengezo chikaperekedwa kumwamba chakuti: “Ufumu wa dziko unakhaladi ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Kristu wake, ndipo adzalamulira monga mfumu kunthawi zanthawi.” (Chivumbulutso 11:15, NW) Chochita choyamba cha Mfumuyo chikakhala kuukira “wolamulira wa dziko” mwiniyo, Satana Mdyerekezi, ndi ziwanda zake. (Yohane 14:30, NW) Makamu oipa amenewa akaponyedwa pansi kuchokera kumwamba ndi kubindikiritsidwa pafupi ndi dziko lapansi. Nchotulukapo chotani?
26 Kulongosoledwa kolosera kukusimba mawu ochokera kumwamba kukhala akuti: “Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.” (Chivumbulutso 12:12) Chipwirikiti chosafanana ndi china chirichonse chikachitika pakati pa mitundu, koma mapeto sakafika panthawi yomweyo.
27. (a) Pamene “mapeto” akayandikira, kodi ndintchito yaikulu yolekanitsa yotani imene ikachitika, ndipo motani? (b) Kodi chiwonongeko cha padziko lonse chonenedweratucho chikakhala chachikulu motani?
27 Imeneyi ikakhala nthawi yantchito yaikulu yolekanitsa. Motsogozedwa ndi Yesu Kristu wokhazikitsidwa pa mpando wachifumu, otsatira ake okhulupirika akalowetsa kulalikidwa kwa “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu” m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba umboni kumitundu yonse. Anthu kulikonse akapatsidwa mwaŵi wa kusonyeza mkhalidwe wawo kulinga kuulamuliro wa Mulungu. (Mateyu 24:14, NW; 25:31-33) Chimenechi chitachitidwa, monga momwe Yesu analongosolera, “pomwepo mapeto adzafika.” Chidzakhala “chisautso chachikulu chimene sichinachitike chiyambire chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde, ndipo sichidzachitikanso.” (Mateyu 24:21, NW) Anthu sadzafunsanso kuti, Kodi Mulungu wakhala akuchitanji? Okha amene adzapulumuka adzakhala awo amene anafuna kwambiri kudziŵa chimene iye anali kuchita ndi kugwirizanitsa miyoyo yawo ndi zofuna zake chiwonongeko cha dziko chisanadze.
28. (a) Kodi ndiliti pamene kulongedwa ufumu kwa Kristu ndi kulekanitsidwa kwa anthu a mitundu yonse kukuchitika? (b) Chotero, kodi nchiyani chimene chiri chofulumira choti inu aliyense payekha muchite?
28 Koma kodi zinthu zonsezi zidzachitika liti? Kodi ndiliti pamene Kristu akupatsidwa mphamvu ya kulamulira monga Mfumu ndi kupitirizabe ndi ntchito yolekanitsa anthu a mitundu yonse? Maumboni akusonyeza kuti Mulungu wakhala akuchita zinthu zimenezi m’zaka za zana la20 zino. Kristu ali kale pampando wake wachifumu wakumwamba, ndipo ntchito yolekanitsa tsopano yatsala pang’ono kutha. Nthawi imene yatsala kuti mudzisonyeze kukhala muli kumbali ya Yehova ya mkangano wa ufumu wa m’chilengedwe chaponseponse njaifupi kwambiri. “Chisautso chachikulu” chayandikira! Kupendedwa kosamalitsa kwa ulosi Wabaibulo mothandizidwa ndi mbiri yaposachedwapa kukutsimikizira zimenezi kukhala zowona. Tikukulimbikitsani kuzilingalira mosamalitsa.
[Chithunzi patsamba 62]
Mwakukhala ndi moyo pakati pa a anthu, wolamulira watsopano wa dziko lapansi anafikira pakuzindikira anthu bwino kwambiri