Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • dg gawo 7 tsamba 14-17
  • Kodi N’chiyani Chakhala Chotulukapo Chachipanduko?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi N’chiyani Chakhala Chotulukapo Chachipanduko?
  • Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mkhalidwewo Lerolino
  • Chimene Nthaŵiyo Yasonyeza
  • Lingaliro Lowona Patali la Mulungu
  • Chifukwa Chimene Mulungu Analola Kuvutika
    Galamukani!—1990
  • Nthaŵi Yomwe Mulungu Walola Anthu Kuvutika Ili Pafupi Kutha
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kodi Nchifukwa Ninji Kuvutika ndi Chisalungamo Zili Zochuluka Motero?
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa
    Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa
Onani Zambiri
Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
dg gawo 7 tsamba 14-17

Chigawo 7

Kodi N’chiyani Chakhala Chotulukapo Chachipanduko?

1-3. Kodi nthaŵi yatsimikizira motani Yehova kukhala wolondola?

PONENA za nkhani ya kuyenera kwa Mulungu kwa kulamulira, kodi chotulukapo chakhala chiyani kwa zaka mazana onse amenewa a ulamuliro wa anthu wosaphatikizapo Mulungu? Kodi anthu atsimikizira kukhala olamulira abwino kwambiri kuposa Mulungu? Ngati titsimikizira mwa cholembedwa cha nkhalwe ya munthu kwa munthu mnzake, sanaterodi.

2 Pamene makolo athu oyamba anakana ulamuliro wa Mulungu, tsoka linatsatirapo. Iwo anabweretsa kuvutika kwa iwo eni ndi pabanja lonse la anthu limene linachokera mwa iwo. Ndipo iwo sakanaimba mlandu munthu aliyense kusiyapo iwo eni. Mawu a Mulungu amati: “Anamchitira zovunda sindiwo ana ake koma chilema n’chawo.”—Deuteronomo 32:5.

3 Mbiri yasonyeza kulondola kwa chenjezo la Mulungu kwa Adamu ndi Hava lakuti ngati iwo akachoka pa makonzedwe a Mulungu, iwo akanyonyotsoka ndipo potsirizira pake kufa. (Genesis 2:17; 3:19) Iwo anachoka mu ulamuliro wa Mulungu, ndipo m’nthaŵi yokwanira iwo ananyonyotsoka nafa.

4. Kodi n’chifukwa ninji tonsefe tabadwira m’kupanda ungwiro, okhoterera kukudwala ndi imfa?

4 Chimene chinachitika pambuyo pake kwa mbadwa zawo zonse chili monga momwe Aroma 5:12 akufotokozera kuti: “Uchimo unalowa m’dziko lapansi ndi munthu mmodzi [Adamu, mutu wabanja la anthu onse], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse.” Chotero pamene makolo athu oyamba anapandukira uyang’aniro wa Mulungu, anakhala ochimwa a chirema. Mogwirizana ndi malamulo a choloŵa, chotulukapo chakupanda ungwiro chinali kokha chimene iwo akanachipatsa mbadwa zawo. Ndicho chifukwa chake tonsefe tabadwa ndi chilema, okhoterera ku matenda ndi imfa.

5, 6. Kodi mbiri yasonyezanji ponena za zoyesayesa za anthu zakudzetsa mtendere wowona ndi kulemerera?

5 Zaka mazana ambiri zapita. Maulamuliro afika ndi kupita. Mtundu uliwonse wolingaliridwa wa boma wayesedwa. Komabe, zinthu zochititsa mantha zachitika mobwerezabwereza kubanja laumunthu. Pambuyo pa zaka zikwi zisanu ndi chimodzi, munthu akalingalira kuti anthu anayenera kukhala atapita patsogolo mpaka kufika pakukhazikitsa mtendere, chilungamo, ndi kulemelera padziko lonse lapansi ndi kuti podzafika panopa anayenera kukhala atazoloŵera mikhalidwe yabwinoyo ya kukoma mtima, chifundo, ndi kugwirizanika.

6 Komabe, chowonadi n’chakuti siziridi choncho. Palibe mtundu waboma la anthu umene udalinganizidwa umene wabweretsa mtendere wowona ndi ulemerero kwa onse. M’zaka za zana la 20 zino zokha, tawona kuphedwa mwambanda kolinganizidwa kwa mamiliyoni ambiri mkati mwa Chipiyoyo ndi kuphedwa kwa oposa mamiliyoni 100 m’nkhondo. M’nthaŵi yathu ziŵerengero zosaŵerengeka za anthu zazunzidwa, zaphedwa mwambanda, ndi kuikidwa m’ndende chifukwa cha mtopola ndi kusiyana kwa ndale zadziko.

Mkhalidwewo Lerolino

7. Kodi mkhalidwe wabanja laumunthu lerolino ungalongosoledwe motani?

7 Ndiponso, talingalirani mkhalidwe wonse wa banja laumunthu lerolino. Upandu ndi chiwawa zawanda. Kugwiritsira ntchito kolakwa anamgoneka kwafikira kukhala mliri. Nthenda zopatsirana mwakugonana zafikira kukhala chawola. Nthenda yochititsa mantha ya AIDS ikuyambukira anthu mamiliyoni ambiri. Anthu mamiliyoni makumi ambiri akufa ndi njala kapena ndi matenda chaka chilichonse, pamene chiŵerengero chochepa chili chokhuphuka kwambiri. Anthu akuipitsa ndi kusakaza dziko lapansi. Moyo wabanja ndi makhalidwe abwino zawonongeka kulikonse. Ndithudi, moyo lerolino umasonyeza ulamuliro woipa wa ‘mulungu wa nthaŵi yapansi pano,’ Satana. Dziko limene iye ali mbuye n’lopanda chikondi, n’lankhalwe, ndi lopanda chilungamo kotheratu.—2 Akorinto 4:4.

8. Kodi n’chifukwa ninji sitingatche zipambano za anthu kukhala kupita patsogolo kowona?

8 Mulungu walola nthaŵi yokwanira yoti anthu afike pachimake pakupita patsogolo kwawo kwa sayansi ndi m’zinthu zakuthupi. Koma kodi ndikupita patsogolo kowona pamene uta ndi muvi zalowedwa mmalo ndi mfuti za makina, akasinja, ndege zoponya mabomba, ndi zida zoponyedwa zanyukiliya? Kodi ndikupita patsogolo pamene anthu angathe kuyenda ulendo kutali m’mlengalenga koma sangathe kukhalira limodzi mumtendere padziko lapansi? Kodi ndikupita patsogolo pamene anthu akuwopa kuyenda m’makwalala pausiku kapena ngakhale masana mmalo ena?

Chimene Nthaŵiyo Yasonyeza

9, 10. (a) Kodi nthaŵi yokwanira zaka mazana ambiri zapitazo yasonyeza chiyani kwenikweni? (b) Kodi n’chifukwa ninji Mulungu sadzachotsa ufulu wakudzisankhira?

9 Chimene chiyeso cha nthaŵi ya zaka mazaka ambiri chasonyeza chili chakuti sikuli kotheka kwa anthu kutsogoza mapazi awo mwachipambano popanda ulamuliro wa Mulungu. Kuli kosatheka monga momwedi kulili kosatheka kwa iwo kukhala moyo popanda kudya, kumwa, ndi kupuma. Umboniwo n’ngwachiwonekere kuti: Tinalinganizidwira kukhala odalira pa chitsogozo cha Mlengi wathu monga momwedi tinalengedwera kudalira pachakudya, madzi, ndi mpweya.

10 Mwakulola kuipa, Mulungu wasonyeza kotheratu zotulukapo zomvetsa chisoni za kugwilitsira ntchito molakwa ufulu wakudzisankhira. Ndipo ufulu wakudzisankhira ulidi mphatso ya mtengo wapatali kotero kuti mmalo mwakuuchotsa pa anthu, Mulungu wawalola kuwona chimene kugwiritsiridwa ntchito kwake molakwa kumatanthauza. Mawu a Mulungu amalankhula chowonadi pamene amati: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” N’ngowonanso pamene amati: “Wina apweteka mnzake pomlamulira.”—Yeremiya 10:23; Mlaliki 8:9.

11. Kodi mpangidwe uliwonse wa ulamuliro waumunthu wachotsa kuvutika?

11 Chilolezo cha Mulungu cha ulamuliro wa anthu kwa zaka zikwi zisanu ndi chimodzi chikusonyeza mwamphamvu kuti munthu sali wokhoza kuthetsa kuvutika. Iye sanatero kalelonse. Mwachitsanzo, m’tsiku lake Mfumu Solomo ya Israyeli, ndi nzeru zake zonse, chuma, ndi ulamuliro, sakanatha kulungamitsa chisoni chochokera muulamuliro wa anthu. (Mlaliki 4:1-3) Mofananamo, m’tsiku lathu, atsogoleri adziko, ngakhale ali ndi maluso azopangapanga zamakono zapamwamba, sali okhoza kuthetsa kuvutika. Zoipa kuposa izi, mbiri yasonyeza kuti kusadalira kwa anthu pa Mulungu kwawonjezera kuvutika mmalo mwakukuthetsa.

Lingaliro Lowona Patali la Mulungu

12-14. Kodi ndi mapindu okhalitsa otani amene akuchokera m’chilolezo cha Mulungu cha kuvutika?

12 Chilolezo cha Mulungu cha kuvutika chakhala chopweteka pa ife. Koma iye wakhala ali ndi lingaliro lowona patali, akumadziŵa zotulukapo zabwino zimene zikakhalapo potsirizira pake. Lingaliro la Mulungu lidzapindulitsa zolengedwa, osati kokha kwa zaka zoŵerengeka kapena zikwi zoŵerengeka, koma zaka mamiliyoni ambiri, inde, kwamuyaya.

13 Ngati mtsogolomu mkhalidwe ukabuka pa nthaŵi iliyonse mu umene munthu wina akagwiritsira ntchito molakwa ufulu wakudzisankhira akumakayikira njira ya Mulungu yakuchita zinthu, sikukakhala kofunikira kumpatsa nthaŵi yakuyesa kutsimikizira malingaliro akewo. Pokhala atalola kale opandukawo zaka zikwi zambiri, Mulungu wakhazikitsa chitsanzo cha lamulo chimene chingagwiritsiridwe ntchito kwamuyaya wonse kulikonse m’chilengedwe chonse.

14 Chifukwa chakuti Yehova walola kuipa ndi kuvutika panthaŵi ino, kudzakhala kutatsimikiziridwa mokwanira kale kuti palibe chilichonse chosagwirizana naye chingapambane. Kudzakhala kutasonyeza popanda chikayikiro chilichonse kuti palibe lingaliro lodzigangira la anthu kapena zolengedwa zauzimu limene lingabweretse mapindu osatha. Chifukwa chake, pamenepo Mulungu adzalungamitsidwa kuphwanya mofulumira wopanduka aliyense. “Oipa onse adzawawononga.”—Salmo 145:20; Aroma 3:4.

[Chithunzi patsamba 15]

Makolo athu oyamba atasankha kudziimira kuchokera kwa Mulungu, iwo potsirizira pake anakalamba nafa

[Chithunzi patsamba 16]

Ulamuliro wa anthu wosaphatikizapo Mulungu watsimikizira kukhala wobweretsa tsoka

[Mawu a Chithunzi]

U.S. Coast Guard photo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena