Mbali 6
Kodi Nchifukwa Ninji Kuvutika ndi Chisalungamo Zili Zochuluka Motero?
1 Komabe, ngati Wokhalako Wamkuluyo anafuna kuti anthu angwiro akhale kosatha padziko lapansi m’mikhalidwe yaparadaiso ndipo ngati chimenecho chidakali chifuno chake, nchifukwa ninji palibe paradaiso tsopano? M’malomwake, nchifukwa ninji anthu akumana ndi kuvutika ndi chisalungamo kwa zaka mazana ambiri?
2 Mosakayikira, mbiri ya anthu yadzaza ndi chisoni chochititsidwa ndi nkhondo, kugonjetsa kwa atsamunda, kudyerana masuku pamutu, chisalungamo, umphaŵi, masoka, matenda, ndi imfa. Kodi nchifukwa ninji zinthu zoipa zambiri zachitikira anthu ambiri opanda liŵongo? Ngati Mulungu ali wamphamvuyonse, nchifukwa ninji walola kuvutika kwakukulu kumeneku kuchitika kwa zaka zikwi zambiri? Popeza kuti Mulungu analinganiza ndi kupanga bwino kwambiri chilengedwe, nchifukwa ninji walola chisokonezo ndi chiwonongeko padziko lapansi?
Chitsanzo
3 Tiyeni tigwiritsire ntchito chitsanzo kusonyeza chifukwa chake Mulungu wa dongosolo walola chisokonezo padziko lapansi. Tayerekezerani chonde, mukuyenda m’nkhalango ndiyeno nkutulukira pa nyumba. Pamene muunguza nyumbayo, muwona kuti njosalongosoka. Mazenera ngosweka, denga nlowonongeka kwambiri, likole lamatabwa nlodzaza ndi ziboo, chitseko nchogweluka mbali imodzi, ndipo mipopi yamadzi sigwira ntchito.
4 Powona zowonongeka zonsezo, kodi munganene kuti palibe wolinganiza waluntha amene anamanga nyumbayo? Kodi kuwonongekako kungakukhutiritseni maganizo kuti nyumbayo inangokhalako yokha? Kapena ngati munena kuti pali munthu wina amene anailinganiza ndi kuimanga, kodi mungalingalire kuti munthuyo anali wopanda luso ndi wosalingalira?
5 Mutayang’anitsitsa nyumbayo, muwona kuti inali yomangidwa bwino ndipo ikupereka umboni wa kulingalira kosamalitsa. Koma yakhalitsa tsopano ndipo ikuwonongeka. Kodi zowonongekazo ndi mavutowo akasonyeza chiyani? Akasonyeza kuti (1) mwini wake anafa; (2) ndi mmisiri womanga waluntha koma sakuifunanso nyumbayo; kapena (3) anabwereketsa nyumbayo kwa anthu osasamala. Mfundo yomalizayi njofanana ndi mkhalidwe wa dziko lapansili.
Chimene Chinalakwika
6 Kuchokera m’cholembedwa cha Baibulo choyambirira, timawona kuti sichinali chifuno cha Mulungu kuti anthu adzivutika kapena kufa. Makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anafa kokha chifukwa chakuti sanamvere Mulungu. (Genesis, machaputala 2 ndi 3) Pamene anapanduka, iwo analeka kuchita chifuniro cha Mulungu. Anachoka m’chisamaliro cha Mulungu. Kwenikweni, anadzichotsa kwa Mulungu, “chitsime cha moyo.”—Salmo 36:9.
7 Mofanana ndi makina amene pang’onopang’ono amaleka kugwira ntchito ndi kuima pamene achotsedwa ku mphamvu yake yamagetsi, matupi ndi maganizo awo anafooka. Chotsatirapo nchakuti Adamu ndi Hava anayamba kufooka, anakalamba, ndipo pomalizira pake anafa. Ndiyeno chinachitika nchiyani? Iwo anabwerera kumene anachokera: “Ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” Mulungu anali atawachenjeza kuti imfa ikakhala chotsatirapo cha kusamvera malamulo ake: “Udzafa ndithu.”—Genesis 2:17; 3:19.
8 Makolo athu oyamba sanangomwalira kokha koma ana awo onse, fuko lonse la anthu, laweruzidwiranso ku imfa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti malinga ndi malamulo a majini, ana amabadwa ndi choloŵa cha mikhalidwe ya makolo awo. Ndipo zimene ana onse a makolo athu oyamba anabadwa nazo monga choloŵa ndizo kupanda ungwiro ndi imfa. Lemba la Aroma 5:12 limatiuza kuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu, kholo la anthu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa [mwakubadwa ndi choloŵa cha kupanda ungwiro, ndiko, zikhoterero zauchimo].” Ndipo popeza kuti tchimo, kupanda ungwiro, ndi imfa ndizo zinthu zokha zimene anthu amadziŵa, ena amaziwona kukhala zachibadwa ndi zosapeŵeka. Komabe, anthu oyambirirawo analengedwa ndi kuthekera ndi chikhumbo chakukhala ndi moyo kosatha. Nchifukwa chake anthu ambiri amakupeza kukhala kolefula kulingalira kuti moyo wawo udzatha ndi imfa.
Chifukwa Ninji kwa Nthaŵi Yaitali Motero?
9 Kodi nchifukwa ninji Mulungu walola anthu kutsatira njira yawo kwa nthaŵi yaitali motere? Nchifukwa ninji walola kuvutika kukhalapo kwa zaka mazana ambiri onsewa? Chifukwa chachikulu nchakuti nkhani yaikulu inadzutsidwa: Kodi ndani ali ndi kuyenera kwa kulamulira? Kodi Mulungu ayenera kukhala Wolamulira wa anthu, kapena kodi iwo akhoza kudzilamulira okha mwachipambano popanda iye?
10 Anthu analengedwa ndi ufulu wakusankha, ndiko kuti, kukhoza kwa kusankha. Iwo sanapangidwe monga maroboti kapena nyama, zimene zimatsogozedwa ndi luntha lobadwa nalo. Chotero anthu akhoza kusankha amene adzatumikira. (Deuteronomo 30:19; 2 Akorinto 3:17) Motero, Mawu a Mulungu amapereka uphungu wakuti: “[Khalani] monga mfulu, koma osakhala nawo ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu.” (1 Petro 2:16) Komabe, ngakhale kuti anthu ali ndimphatso yabwino koposa ya ufulu wakusankha, ayenera kulandira zotulukapo za chimene asankha kuchita.
11 Makolo athu oyamba anapanga chosankha cholakwa. Iwo anasankha kusadalira Mulungu. Zowona, Mulungu akanakhoza kupha opanduka aŵiriwo panthaŵi yomweyo pamene anagwiritsira ntchito molakwa ufulu wawo. Koma zimenezo sizikanayankha funso lonena za kuyenera kwa Mulungu kulamulira anthu. Popeza kuti aŵiri oyambawo anafuna kusadalira Mulungu, funsoli liyenera kuyankhidwa: Kodi kachitidwe kameneko kakachititsa moyo wachimwemwe, wachipambano? Njira yokha yopezera yankho inali kulola makolo athu oyambawo ndi ana awo kutsatira njira yawo, popeza kuti ndicho chinali chosankha chawo. Kupita kwa nthaŵi kukasonyeza ngati anthu analengedwa kuti akhale achipambano m’kudzilamulira okha popanda kudalira Mlengi wawo.
12 Wolemba Baibulo Yeremiya anadziŵa kuti zotulukapo zikakhala zotani. Motsogozedwa ndi mzimu woyera wamphamvu, kapena mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, iye analemba mowonadi kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. Yehova, mundilangize.” (Yeremiya 10:23, 24) Iye anadziŵa kuti anthu ayenera kutsogozedwa ndi nzeru yakumwamba ya Mulungu. Chifukwa? Chifukwa chakuti Mulungu sanalenge anthu kuti akhale achipambano popanda chitsogozo chake basi.
13 Zotulukapo za kulamulira kwa anthu kwa zaka zikwi zambiri zasonyeza mosakayikira konse kuti sikuli kwa anthu kutsogoza zochita zawo popanda Mlengi wawo. Pokhala kuti ayesa zimenezo, mlandu uli wawo wa zotsatirapo zatsokazo. Baibulo linamveketsa mfundoyi motere: “Thanthwe [Mulungu], ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika. Anamchitira zovunda sindiwo ana ake, chirema nchawo; iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.”—Deuteronomo 32:4, 5.
Mulungu Adzaloŵererapo Posachedwapa
14 Popeza kuti walola ulamuliro wa anthu kwa nyengo ya zaka mazana ambiri kusonyeza kulephera kwawo, Mulungu tsopano angaloŵerere m’zochita za anthu ndi kuthetsa kuvutika, chisoni, matenda, ndi imfa. Popeza kuti walola anthu kufika pachimake cha zipambano zawo za sayansi, za maindasitale, mankhwala, ndi mbali zina, palibenso chifukwa chakuti Mulungu alole zaka mazana owonjezereka kuti awone ngati anthu osadalira pa Mlengi wawo angabweretse dziko lamtendere, laparadaiso. Iwo alephera ndipo sangathe. Kusadalira pa Mulungu kwachititsa dziko kukhala loipa, laudani, lakupha.
15 Pamene kuli kwakuti pakhala olamulira owona mtima amene afuna kuthandiza anthu, zoyesayesa zawo zalephera. Kulikonse lerolino kuli umboni wakusweka kwa ulamuliro wa anthu. Nchifukwa chake Baibulo limapereka uphungu wakuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.”—Salmo 146:3.
[Study Questions]
1, 2. Polingalira za zimene anthu akumana nazo, kodi ndimafunso otani amene angafunsidwe?
3-5. (a) Kodi nchitsanzo chotani chimene chingatithandize kumvetsetsa chifukwa chake Mulungu wa dongosolo walola chisokonezo padziko lapansi? (b) Kodi ndimkhalidwe uti mwa yotchulidwayo umene umayenerera mkhalidwe wonena za dziko lapansi?
6, 7. Kodi chinachitika nchiyani kwa Adamu ndi Hava pamene anaswa lamulo la Mulungu?
8. Kodi tchimo la makolo athu oyamba linayambukira bwanji mtundu wa anthu?
9. Kodi nchifukwa ninji Mulungu walola kuvutika kupitiriza kwa nthaŵi yaitali motere?
10. Kodi anthu anapatsidwa kukhoza kotani, limodzi ndi thayo lotani?
11. Kodi ndinjira imodzi yokha yotani imene ingakhalepo yodziŵira ngati njira ya kusadalira pa Mulungu ingakhale yachipambano?
12. Kodi Yeremiya anapenda motani ulamuliro wa anthu, ndipo nchifukwa ninji?
13. Kodi zotulukapo za zaka zikwi zambiri za kulamulira kwa anthu zasonyeza chiyani mosakayikira?
14. Kodi nchifukwa ninji Mulungu sadzachedwanso kuloŵerera m’zochita za anthu?
15. Kodi ndiuphungu wa Baibulo uti umene tiyenera kulabadira?
[Picture on page 24, 25]
Ngakhale olamulira dziko owona mtima sanakhoze kubweretsa dziko lamtendere, laparadaiso