Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/00 tsamba 3
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Mfundo Zopatsa Chidziŵitso, Zofotokozedwa Momveka Bwino
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kulimbikitsa Omvera Kuŵerenga Baibulo
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kuyendera Limodzi ndi Omvetsera ndi Ntchito ya Notsi
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 9/00 tsamba 3

Bokosi la Mafunso

◼ N’chifukwa chiyani kuli kopindulitsa kuti omvetsera aziŵerenga malemba pamene wokamba nkhani wawapempha kutero?

Zinthu ngati mtundu wa nkhani yomwe ikukambidwayo ndiponso kaya ngati nkhaniyo ikupenda vesi ndi vesi la mbali inayake ya Mawu a Mulungu ndizo zidzanena kuchuluka kwa malemba amene omvetsera adzapemphedwa kuŵerenga.

N’kofunika kukumbukira kuti chifukwa china chimene timaŵerengera malemba ndicho kufuna kutsimikizira kuti zimene zikunenedwazo n’zochokera m’Baibulo. (Mac. 17:11) Cholinga china ndicho kusanthula umboni wa m’Malemba wochirikiza zimene zikunenedwazo n’cholinga cholimbitsa chikhulupiriro cha onse. Kuona zenizeni zimene Baibulo likunena pamene lemba lomwe lili ndi mfundo yofunika likuŵerengedwa kudzachititsa mfundoyo kukhazikika m’maganizo. Kuphatikiza pa kuŵerenga malemba, kulemba notsi ndiponso kutsatira bwino mfundo zimene zikunenedwa n’kopindulitsa.

Ngakhale kuti autilaini ya Sosaite imakhala ndi Malemba ambiri ofotokoza nkhaniyo, malemba ameneŵa amaperekedwa n’cholinga chothandiza wokamba nkhani, pamene akukonzekera nkhaniyo. Malembawo angapereke chithunzi cha mmene nkhaniyo ilili kapenanso kum’thandiza kuti amvetse mfundo zazikulu zachikhalidwe za m’Malemba ndiponso kumvetsetsa mmene angakambire nkhaniyo. Wokamba nkhani amaona malemba amene ali ofunika pomveketsa nkhaniyo ndiyeno amauza omvetsera kutsagana naye pamene akuŵerenga ndi kufotokozera malembawo. Malemba ena ochirikiza nkhaniyo angatchulidwe n’kuwafotokoza mwachidule zimene amanena, koma omvetsera safunikira kuti achite kuwaŵerenga.

Wokamba nkhani akamaŵerenga malemba, amaŵerenga kuchokera m’Baibulo mwenimweni osati kuchokera pamapepala olembedwa pa kompyuta. Wokamba nkhani akapempha omvetsera kuŵerenga naye pamodzi malemba, amatchula momveka bwino buku la Baibulo, chaputala, ndi vesi (mavesi). Mwa kuima pang’ono kuti afunse funso kapena kugogomezera mwachidule chifukwa chake akuŵerenga lembalo, amapereka mpata kwa omvetsera kupeza lembalo. Kubwereza kutchula lembalo kumathandizanso omvetsera kulikumbukira. Komabe, sikovomerezeka kutchula nambala ya tsamba pamene lembalo likupezeka, chifukwa chakuti manambala amasamba amasiyanasiyana malinga ndi mtundu wa Baibulo limene omvetsera akugwiritsa ntchito. Kuŵerenga malemba pamene tapemphedwa kutero kumathandiza omvetsera kupindula ndi mphamvu ya Mawu a Mulungu monga afotokozedwera m’nkhaniyo.—Aheb. 4:12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena