Mawu Oyamba Gawo 11
M’chigawochi muli nkhani zochokera m’Malemba a Chigiriki. Yesu anabadwira m’banja losauka lomwe linkakhala m’katauni kenakake. Iye ankagwira ntchito ya ukalipentala limodzi ndi bambo ake. Koma Yesu anapatsidwa udindo wopulumutsa anthu. Yehova anamusankha kuti akhale Mfumu ya Ufumu wakumwamba. Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanuyo kudziwa kuti Yehova anasankha mwanzeru banja komanso malo oti Yesu abadwire ndiponso akulire. Muthandizeni kudziwa zimene Yehova anachita poteteza Yesu kuti asaphedwe ndi Herode. M’chigawochi tiona umboni wakuti palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa cholinga chake. Tionanso kuti Yehova anatuma Yohane kuti akonzere Yesu njira. Pokambirana, tsindikani umboni wosonyeza kuti Yesu ankatsatira mfundo za Yehova kuyambira ali mwana ndipo ankazikonda kwambiri.