Mawu Oyamba Gawo 13
Yesu anabwera padzikoli kudzafera anthu ochimwa. Ngakhale kuti anafa, iye anagonjetsa dziko. Yehova anachita zinthu mokhulupirika ndipo anaukitsa Mwana wakeyu. Nthawi yonse imene Yesu anali padzikoli, anali wodzichepetsa, ankatumikira anthu ndipo anthuwo akalakwitsa ankawakhululukira. Yesu ataukitsidwa anapita kukaonana ndi ophunzira ake. Iye anawaphunzitsa mmene angagwirire ntchito yofunika kwambiri imene anawapatsa. Ngati ndinu kholo thandizani mwana wanu kudziwa kuti nafenso tiyenera kugwira ntchito imeneyi.