Bwerani ndi Kudzamva Nkhani ya Baibulo:
Chilungamo kaamba ka Onse ndi Woweruza Woikidwa ndi Mulungu
Maboma ayesera kwa nthaŵi yaitali kufikira ‘Chilungamo kaamba ka Onse,’ monga mmene anachitira Agriki akale amene oŵeruza awo anamvetsera ku nkhani za lamulo zovuta pa Areopagi, kapena Phiri la Mars. Pa khoti limeneli la chilungamo zoposa zaka 1,900 zapitazo, munthu anasonyeza mmene chilungamo chowona kaamba ka onse chidzazindikiridwa. Ndemanga zake zidzasanthulidwa mosamalitsa m’nkhani yaikulu ya chirimwe chino, ya Msonkhano Wachigawo wa “Chilungamo Chaumulungu” wa Mboni za Yehova.
Mungamvetsere nkhaniyi pa imodzi iriyonse ya misonkhano yoposa pa zana limodzi yochitidwa mu Zambia, United States, British Isles, ndi Canada. Programu ya msonkhano imaperekanso kukambitsirana kwa m’Baibulo kothandiza pa nkhani zogwira ntchito za moyo, ndi zitsanzo ziŵiri zolangiza za m’Baibulo.
Fikirani Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya kumaloko kaamba ka malo a msonkhano womwe uli kufupi kwambiri ndi inu, kapena lemberani ofalitsa a magazini ino. Mu Zambia, nkhaniyo idzaperekedwa pa Sande pa 2:10 p.m.