Dziko Latsopano—Liri Pafupi Kwambiri!
DZIKO iriliri m’zowawa zake za imfa! Kodi chimenecho chingakhaledi chowona? Chabwino, lingalirani mikhalidwe ya dziko mosamalitsa.
Pali zida za nyukliya zokwanira kuwononga chiŵerengero chonse cha anthu pa dziko lapansi nthaŵi zambiri mobwerezabwereza. Nkhondo ya chiweniweni ikumenyedwa m’maiko ambiri, monga ngati Angola ndi Mozambique. Pali kukanthana kwa magulu a anthu mu South Africa, Sri Lanka, ndi maiko ena. Uchigawenga ndi njala nazonso zikutenga chiŵerengero chokulira cha miyoyo ya anthu.
Bwanji ponena za mliri wa AIDS? Sunday Times ya ku South Africa ya pa October 25, 1987, inaitcha iyo “imfa yakuda yatsopano” ndipo inanena kuti: “Tsopano kuwopsya kokwanira kwa Aids ya ku Africa kwavumbulidwa: M’maiko ena anthu asanu ndi mmodzi mwa khumi aliwonse ali otsimikizirika kufa pofika 1994.”
Mantha akufalikira chifukwa cha mikhalidwe yoteroyo. Monga mmene wopeza mphoto Yapamwamba ya pa Chaka Harold C. Urey ananenera zaka zingapo zapitazo kuti: “Tidzadya mantha, kugona m’mantha, kukhala m’mantha ndi kufa m’mantha.” Motsimikizirika, Yesu Kristu, mneneri wamkulu koposa yemwe anakhala pa dziko lapansi, ananeneratu kuti m’masiku otsiriza a dziko iri, anthu adzakhala “akukomoka ndi mantha ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza pa dziko.”—Luka 21:26.
Koma ambiri sali ndi mantha. M’malomwake, iwo akusangalala. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti akudziŵa kuti dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu ka dziko (osati pulaneti ya Dziko Lapansi) liri pafupi ndi mapeto ake, koma dziko latsopano liri pafupi kwenikweni. Kodi ndimotani mene angakhalire otsimikiza chotero? Chifukwa cha kukwaniritsidwa kwa maulosi ambiri a Baibulo.
Mwachitsanzo, pamene Yesu Kristu anafunsidwa chomwe chidzakhala chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi mapeto a dziko, iye ananena kuti: “Mtundu umodzi wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina ndipo ufumu ndi ufumu wina.” Mu 1914, Nkhondo ya Dziko ya I inaphulika. Iyo inapangitsa kutaika kokulira koposa kwa moyo kuchokera ku khondo kufika ku nthaŵi imeneyo. Mtengo wa omenyanawo? 9,000,000 ena anafa, pambali pa mamiliyoni a anthu wamba! Koma Nkhondo ya Dziko ya II inali yosakaza koposa, ikumatenga miyoyo ina 55,000,000! Yesu analozeratu kuti zonsezi zikatsagana ndi kuperewera kwa zakudya, zivomezi, miliri, ndi kusayeruzika.—Mateyu 24:7-13; Luka 21:10, 11.
Mtumwi Wachikristu Paulo nayenso molondola ananeneratu mikhalidwe ya dziko iripoyi. Iye analemba kuti: “M’masiku otsiriza nthaŵi zovuta kuchita nazo [zidzakhala pano, NW]. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, a mwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi cha chibadidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliwuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu osati okonda Mulungu, akukhala nawo mawonekedwe a chipembedzo koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.” (2 Timoteo 3:1-5) Paulo anakhoza kuneneratu molongosoka mikhalidwe ya lerolino chifukwa Mulungu anamuuzira iye kulemba mawu amenewo.
Ponena za mawu ake m’chigwirizano ndi nthaŵi ya mapeto, Yesu ananena kuti: “Pamene muwona zinthu izi ziri kuchitika, dziŵani kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.” (Luka 21:31) Mamiliyoni amagwiritsira ntchito pemphero la chitsanzo la Yesu ndi kupempha kaamba ka Ufumu wa Mulungu kudza. (Mateyu 6:9, 10) Koma pamene afunsidwa kuti, “Kodi nchiyani chimene Ufumu umenewu kwenikweni udzachita?” iwo alibe yankho. Mosiyanako, mamiliyoni omwe amaphunzira Baibulo mwakhama aphunzira kuti Ufumuwo udzabweretsa kumapeto dziko lakale iri ndipo kukhazikitsa zolimba dziko latsopano limene lidzabweretsa madalitso osaŵerengeka kwa mtundu wa anthu. Koma motani? Liti?