Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 3/1 tsamba 24-29
  • Chilungamo Posachedwapa Kaamba ka Mitundu Yonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilungamo Posachedwapa Kaamba ka Mitundu Yonse
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mthunzi wa Zokoma Zirinkudza
  • Chilungamo Chilinganizidwa Ndi Chifundo
  • Chilungamo Kaamba ka Mitundu Yonse
  • Kodi Mukuvomereza ku Njira Zolungama za Mulungu?
  • Mulungu Wachilungamo Adzachitapo Kanthu Mofulumira
  • “Kondwerani, Amitundu Inu, Ndi Anthu Ake”
  • Yehova—Gwero la Chilungamo Chenicheni
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Tsanzirani Yehova—Chitani Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—1998
  • “Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”
    Yandikirani Yehova
  • Yehova Wokonda Chilungamo ndi Chiweruzo
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 3/1 tsamba 24-29

Chilungamo Posachedwapa Kaamba ka Mitundu Yonse

“Chilungamo, chilungamo ndicho mudzichitsata, kuti mukhale ndi moyo ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.”​—DEUTERONOMO 16:20.

1. Nchiyani chomwe chinali chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba ka munthu, ndipo ndimotani kokha mmene iye akadakwaniritsira icho?

CHIFUNO cha Yehova Mulungu m’kulenga mwamuna ndi mkazi chinali cha kukhala ndi dziko lapansi litadzazidwa ndi zolengedwa zangwiro. Onsewo akamtamanda iye ndi kuchita mbali yawo m’kugonjetsa dziko lapansi. (Genesis 1:26-28) Popeza kuti munthu anapangidwa m’chifanizo ndi m’chifanefane cha Mulungu, iye anapatsidwa mikhalidwe ya nzeru, chilungamo, chikondi, ndi mphamvu. Kokha ndi kuchita kolinganizika kwa mikhalidwe imeneyi ndi pamene munthu akakwaniritsa chifuno cha Mpangi wake kaamba ka iye.

2. Kodi kulondola chilungamo kwa ana a Israyeli kunali kofunika motani?

2 Monga momwe chawonedwera m’nkhani yapitayo, munthu anapanduka motsutsana ndi njira ya Mulungu ya kuchitira zinthu ndipo anaweruzidwa ku imfa. Tsopano, chifukwa cha kupanda ungwiro, chinali chosatheka kaamba ka iye kuchita chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu. Kusatha kwa munthu kusonyeza chilungamo changwiro kwakhala mbali yowonekera m’kulephera kumeneku. Nchosadabwitsa, chotero, kuti Mose anakumbutsa ana a Israyeli kuti: “Chilungamo, chilungamo ndicho mudzichitsata”! Miyoyo yawo ndi kuthekera kwa kulowa m’Dziko Lolonjezedwa kunali kodalira pa kutsata kwawo chilungamo.​—Deuteronomo 16:20.

Mthunzi wa Zokoma Zirinkudza

3. Nchifukwa ninji kusanthula kwa njira za Yehova ndi Israyeli kuli kofunika kwambiri kwa ife lerolino?

3 Zochita za Yehova ndi mtundu wa Israyeli zimalimbikitsa chidaliro chathu kuti iye ndithudi adzapanga chilungamo chake kuwonekera ku mitundu yonse kupyolera mwa Mtumiki wake wosankhidwa, Yesu Kristu. Mtumwi Paulo akulongosola nkhaniyo m’njirayi: “Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha Malembo, tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Popeza kuti Mulungu “ndiye wa kukonda chilunjiko ndi chilungamo,” iye anafuna kuti Aisrayeli atsanzire iye m’zochita zawo zonse wina ndi mnzake. (Salmo 33:5, NW) Ichi chingawonedwe bwino mwa kusanthula oŵerengeka a malamulo 600 operekedwa kwa Israyeli.

4. Kodi mavuto a kuyenera kwa lamulo anasamaliridwa motani pansi pa Chilamulo cha Mose?

4 Mavuto a kuyenera kwa nzika sanaliko pamene Chilamulo cha Mose chinatsatiridwa. Kumatenga nkhani ya wosakhala m’Israyeli yemwe anabwera kudzakhala m’dzikolo, Levitiko 19:34 ikulongosola kuti: “Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha.” Ndi kakonzedwe kolungama ndi kachikondi chotani nanga! Mowonjezerapo, oweruza ndi mboni mofananamo anachenjezedwa kuti: “Usachite umboni ku mlandu, ndi kupatukira kutsata unyinji ndi kukhotetsa mlandu; kapena usakometsera munthu wosauka pa mlandu wake.” (Eksodo 23:2, 3) Tangolingalirani za chimenecho​—chilungamo chikumaperekedwa kwa olemera ndi osauka mofanana!

5. Yerekezani malamulo aupandu pansi pa Chilamulo cha Mose ndi awo a lerolino.

5 Pansi pa ndandanda ya malamulo ya Chilamulo cha Mose, malamulo a upandu anali apamwamba kwenikweni kuposa malamulo a m’mabukhu amalamulo a mitundu lerolino. Mwachitsanzo, wakuba sanali kuikidwa m’ndende kotero kuti aike thayo pa anthu ogwira ntchito zolimba omwe anamvera Chilamulo. Iye anayenera kugwira ntchito ndi kulipira kuwirikiza kaŵiri kapena kuposerapo kaamba ka chimene iye anaba. Chotero mnkholeyo sanavutike ndi kutayikiridwa. Bwanji ngati wakubayo anakana kugwira ntchito ndi kulipira. M’nkhani imeneyo, iye ankagulitsidwa mu ukapolo kufikira kubwezeranso kunapangidwa. Ngati iye anapitiriza kusonyeza mkhalidwe wowuma mutu, iye anayenera kuphedwa. Mwa njira imeneyi chilungamo chinachitidwa kwa mnkholeyo, ndipo ichi chinali chiletso champhamvu kaamba ka ena omwe angakhale anali okhoterera ku kuba. (Eksodo 22:1, 3, 4, 7; Deuteronomo 17:12) M’kuwonjezerapo, popeza kuti moyo uli wopatulika m’maso mwa Mulungu, wakupha munthu aliyense anaphedwa. Ichi chinachotsa woipa, munthu wakupha kuchoka mu mtunduwo. Mosasamala kanthu za chimenecho, chifundo chinasonyezedwa kwa akupha anthu mosadziŵa.​—Numeri 35:9-15, 22-29, 33.

6. Ndi kumapeto otani kumene kusanthula kwa malamulo a Israyeli kumatitsogolera ife?

6 Ndani angakane, chotero, kuti chilungamo chinazindikiritsa zonse za zochita zachiweruzo za Mulungu ndi mtundu wa Israyeli? Chotero, ndi chitonthozo chotani, ndi chiyembekezo chotani nanga, chomwe timadzazidwa nacho pamene tilingalira mmene lonjezo la Mulungu pa Yesaya 42:1 lidzagwirira ntchito kupyolera mwa Kristu Yesu! Pamenepo ife tikupatsidwa chitsimikiziro ichi: “Iye adzatulutsira amitundu [chilungamo,NW].”

Chilungamo Chilinganizidwa Ndi Chifundo

7. Longosolani zochita zachifundo za Yehova ndi Israyeli.

7 Chilungamo cha Mulungu chiri cholinganizidwa ndi chifundo. Ichi chinasonyezedwa mowonekera bwino pamene Aisrayeli anayamba kupanduka motsutsana ndi njira zolungama za Mulungu. Mvetserani ku kulongosola kwa Mose kwa chisamaliro chachifundo cha Yehova kaamba ka iwo mkati mwa zaka zawo 40 m’chipululu: “Anampeza m’dziko la mabwinja, ndi m’chipululu cholira chopanda kanthu; Anamzinga, anamlangiza, Anamsunga ngati kamwana ka m’diso; Monga mphungu ikasula chisa chake, Nikapakapa pa ana ake, Iye anayala mapiko ake, nawalandira, Nawanyamula pa mapiko ake; Yehova Yekha anamtsogolera.” (Deuteronomo 32:10-12) Pambuyo pake, pamene mtunduwo unatembenukira ku mpatuko, Yehova anachonderera kuti: “Bwereranitu kuleka njira zanu zoipa, ndi machitidwe anu oipa.”​—Zekariaya 1:4a.

8, 9. (a) Ndi ku mlingo wotani kumene Mulungu anasonyeza chilungamo chake chachifundo kwa Ayuda? (b) Ndi tsoka lomalizira lotani lomwe linalaka iwo, koma nchiyani chomwe chinganenedwe ponena za njira mu imene Mulungu anachitira nawo?

8 Chopereka cha Yehova cha chifundo chinafika pa makutu ogontha. Kupyolera mwa mneneri Zekariya, Mulungu ananena kuti: “Sanamva, kapena kumvera Ine.” (Zekariya 1:4b) Chotero chilungamo cha chifundo cha Mulungu chinamfulumiza iye kutumiza Mwana wake wobadwa yekha kukawathandiza iwo kubwerera kwa Iye. Yohane Mbatizi anadziŵikitsa Mwana wa Mulungu mwa kunena kuti: “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa chimo lake la dziko lapansi!” (Yohane 1:29) Kwa zaka zingapo, Yesu mosatopa anaphunzitsa Ayuda njira zolondola za Mulungu, kuchita zozizwitsa zosaŵerengeka ndipo motero kutsimikizira kuti iye anali Mpulumutsi wonenedweratuyo. (Luka 24:27; Yohane 5:36) Koma anthuwo sanamvetsre kapena kukhulupirira. Chotero, Yesu anasonkhezeredwa kufuula kuti: “Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi! Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.”​—Mateyu 23:37, 38.

9 Mulungu analekerera kupereka chiweruzo chake chowopsya kwa zaka 37 zina, kufikira 70 C.E. Kenaka iye analola Aroma kuwononga Yerusalemu ndi kutenga zikwi za Ayuda mu ukapolo. Pamene tilingalira kupirira ndi kuleza mtima kwa Yehova pa nyengo ya zaka mazana ambiri, ndani yemwe angalephere kuwona chizindikiro cha chilungamo m’zochita zake zonse ndi nyumba ya Israyeli?

Chilungamo Kaamba ka Mitundu Yonse

10. Ndimotani mmene chilungamo cha Mulungu chinafutukulidwira ku mitundu yonse?

10 Kutsatira kukana Yesu kwa Aisrayeli, Yakobo ananena kuti: “Poyamba Mulungu anayang’anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.” (Machitidwe 15:14) “Anthu” amenewa, kuphatikizapo Ayuda oŵerengeka amenewo omwe analandira Yesu monga Mesiya, mosonkhanitsidwa anapanga “Israyeli [wauzimu] wa Mulungu” ndipo ali wopangidwa ndi otsatira a Kristu Yesu odzozedwa ndi mzimu a 144,000. (Agalatiya 6:16; Chibvumbulutso 7:1-8; 14:1-5) Wokhulupirira woyamba Wachikunja wosadulidwa anali Korneliyo. Pamene Korneliyo ndi banja lake analandira njira ya Mulungu ya chipulumutso, Petro ananena kuti: “Zowona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa Iye ndi wakuchita [chilunjiko, NW] alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Paulo akukulitsa pa kulungama kwa kupanda tsankho kwa Yehova pamene iye akunena kuti: “Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu. Koma ngati muli a Kristu, muli mbewu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano.”​—Agalatiya 3:28, 29.

11. Ndi lonjezo lotani lomwe linaperekedwa kwa Abrahamu, ndipo ndimotani mmene ilo lidzakwaniritsidwira?

11 Pano tikukumbutsidwa za lonjezo losangalatsa limene Yehova anapereka kwa Abrahamu. Lozikidwa pa kufunitsitsa kwa kholo limenelo kupereka nsembe mwana wake wokondedwa Isake, Mulungu anamuwuza iye kuti: “Popeza wachita ichi, sunandikaniza mwana wako wa yekha, kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, . . . M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.” (Genesis 22:16-18) Ndimotani mmen lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwira? “Mbewu ya Abrahamu,” yopangidwa ndi Yesu Kristu ndi otsatira ake odzozedwa 144,000 omwe atsimikizira kukhala okhulupirika kufikira imfa, idzalamulira mtundu wa anthu kochokera kumwamba kwa zaka chikwi. (Chibvumbulutso 2:10, 26; 20:6) Ponena za nthaŵi yodalitsidwa imeneyo, Yehova akutitsimikizira ife kuti: “Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “ulamuliro” wa Ufumu wa Umesiya umenewu ‘udzachirikizidwa ndi [chilungamo ndi chilunjiko, NW] kunkabe nthaŵi zonse.’​—Yesaya 9:7.

12. Ndi ku mlingo wotani kumene madalitso a pangano la Abrahamu akukumanizidwira kale?

12 Koma palibe chifukwa cha kudikirira kufikira Zaka Chikwi za Kulamulira kwa Yesu Kristu kuyamba ndi cholinga chofuna kusangalala ndi madalitso a pangano la Abrahamu. Madalitso amenewa akukumanizidwa kale ndi “khamu lalikulu” la anthu “ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” Mophiphiritsira mwa ‘kutsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa,’ Yesu Kristu, iwo afikira pa kukhala ndi kaimidwe kolungama pamaso pa Yehova. Mofanana ndi Abrahamu, iwo akhala mabwenzi a Yehova! Chilungamo chikuzindikiritsadi njira ya chipulumutso ya Yehova kaamba ka mamiliyoni ochokera m’mitundu yonse.​—Chibvumbulutso 7:9, 14.

Kodi Mukuvomereza ku Njira Zolungama za Mulungu?

13, 14. (a) Ndi kudzisanthula kwa mtima kotani kumene tonsefe tiyenera kupanga? (b) Ndimotani mmene chiyamikiro chathu kwa Yehova chiyenera kusonyezedwera?

13 Kodi mtima wanu wakhudzidwa ndi kufulumizidwa mozama ndi njira ya chilungamo ya Mulungu ndi chikondi ‘kupereka Mwana wake wobadwa yekha monga dipo kaamba ka inu? Tangolingalirani kudzimva kwa Abrahamu pamene Yehova anamfunsa iye kupereka nsembe mwana wake, amene anamkona koposa! Koma kudzimva kwa Mulungu kumapita mozamirapo. Lingalirani za kudzimva kwake pamene Mwana wake wokondedwa anali kuvutitsidwa ndi mitonzo, mawu otonza a odutsa, kupweteka kowawitsa kwa mtengo wozunzirapo. Tangolingalirani kudzimva kwa Yehova ku kulira kwa Yesu: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?” (Mateyu 27:39, 46) Mosasamala kanthu za chimenecho, chilungamo chinafuna kuti Yehova Mulungu alole Mwana wake kufa m’njira yoteroyo kotero kuti atsimikizire umphumphu wake m’kulemekeza kulunjika kwa Mulungu. M’kuwonjezerapo, mwa kulola Mwana wake kufa, Yehova anatsegula njira ya chipulumutso kwa ife.

14 Chotero, ndithudi, chiyamikiro chathu kwa Yehova ndi kwa Mwana wake chiyenera kutifulumiza ife kuvomereza mwapoyera kuti: “Chipulumutso kwa Mulungu wathu . . . ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chibvumbulutso 7:10) Mwa kuvomereza kwathu mwachiyanjo m’njira imeneyi, timasonyeza kuti timakhulupirira m’mawu a Mose akuti: “Njira za [Yehova] zonse ndi chilungamo.” (Deuteronomo 32:4) Ndi chimwemwe chotani nanga chimene tingabweretse ku mitima ya Yehova ndi Mwana wake pamene tikuvomereza ndipo kenaka kulondola njira zolungama za Mulungu kaamba ka chipulumutso cha anthu!

15. Kodi mawu a Yesu kwa Nikodemo ali ofunika motani kwa ife?

15 Kodi sitiri achimwemwe kuti akhulupiriri anzathu mu ma 1870 anatenga kaimidwe kolimba pa nkhani ya nsembe ya dipo? Kodi sitiri osangalala kuti ife lerolino tiri mbali ya gulu lomwe liri kokha logamulapo kusungirira njira yolungama ndi yachikondi ya Mulungu kaamba ka chipulumutso cha munthu? Ngati tiri tero, chotero tiyenera kupereka chisamaliro chapadera ku chimene Yesu anawuza Nikodemo: “Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, . . . kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye. Wokhulupirira Iye saweruzidwa; koma wochita chowonadi adza kukuwunika, kuti ntchito zake ziwonekere kuti zinachitidwa ndi Mulungu.” Kuti tipulumuke chiweruzo chowopsya cha Mulungu, tiyenera kutsimikizira chihulupiriro chathu mwa Mwana mwa kuchita ‘ntchito zochitidwa ndi Mulungu.’​—Yohane 3:17, 18, 21.

16. Ndimotani mmene ophunzira a Yesu angalemekezere Atate wakumwamba?

16 Yesu ananena kuti: “Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga. Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m’chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m’chikondi chake.” (Yohane 15:8, 10) Ndi ati omwe ali ena a malamulo amenewa? Limodzi likupezeka pa Yohane 13:34, 35, pamene Yesu anawuza ophunzira ake kuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; . . . Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” Chipatso cha chikondi chiri chowonekera pakati pa Mboni za Yehova. Yesu analamulanso kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Kodi inu mwaumwini mukuchita ‘ntchito zochitidwa ndi Mulungu’ zimenezi?

17. Ndi chotulukapo chotani chimene chimasonyeza kuti ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira iri chisonyezero cha chilungamo cha Yehova?

17 Kulungama kwa njira ya Yehova m’kulola otsatira a Yesu kuchita ntchito zimenezi za kulalikira ndi kuphunzitsa kumakhala kowonekera pamene tilingalira chomwe chinakwaniritsidwa ndi Mboni za Yehova m’kokha chaka chimodzi. Mkati mwa 1988, panali ophunzira atsopano 239,268 obatizidwa! Kodi ichi sichimabweretsa chimwemwe ku mtima wanu?

Mulungu Wachilungamo Adzachitapo Kanthu Mofulumira

18. Ndi mafunso otani omwe angadzutsidwe m’chiyang’aniro cha chizunzo cha anthu a Yehova?

18 Ntchito yochitira umboni siinachitidwe popanda chitsutso. Yesu anawuza ophunzira ake kuti: “Ngati iwo andizunza, iwo adzakuzunzaninso.” (Yohane 15:20, NW) Mbiri yamakono ya Mboni za Yehova ikutsimikizira ku kuwona kwa ndemanga imeneyo. Ziletso, kuikidwa m’ndende, kumenyedwa, ndipo ngakhale kuzunzidwa kwakumanizidwa ndi Mboni m’dziko limodzi pambuyo pa linzake. Mawu a ulosi a Habakuku kachiŵirinso amabwera ku maganizo athu: “Chilamulo chalekeka, [chilungamo, NW] sichitulukira konse.” Chotero, pa nthaŵi zina, ngakhale anthu a Yehova angadzimve kukhala ofuna kufunsa kuti: ‘Nchifukwa ninji Yehova akupenyerera iwo akuchita mochenjerera? Nchifukwa ninji Iye akhala chete pamene woipa ammeza munthu [wolunjika, NW] woposa iyemwini?’​—Habakuku 1:4, 13.

19. Kodi ndi fanizo lotani limene Yesu anapereka kutithandiza ife kumvetsetsa zinthu kuchokera ku lingaliro la Mulungu?

19 Yesu anapereka fanizo lomwe likuthandiza kuyankha mafunso oterowo ndi kutitheketsa ife kuwona zinthu kuchokera ku kawonedwe ka Mulungu. Pa Luka 17:22-37, Yesu analongosola mkhalidwe wa chiwawa womwe ukazindikiritsa mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu. Iye ananena kuti ikakhala yofanana ndi ija yomwe inalipo chisanachitike Chigumula cha tsiku la Nowa ndi chiwonongeko cha Sodomu ndi Gomora m’masiku a Loti. Kenaka, monga momwe kwalongosoledwera pa Luka 18:1-5, NW, Yesu anatembenukira kwa ophunzira ake ndipo “anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthaŵi zonse osafoka mtima.” Yesu anasimba za mkazi wamasiye yemwe anali m’kusowa kwakukulu ndi za “woweruza” wokhala mu mkhalidwe wa kukhutiritsa zosowa zake. Mkazi wamasiyeyo anapitiriza kupempha: “Onani kuti ndipeze chilungamo kuchokera kwa adani anga pa lamulo.” Chifukwa cha kuwumirira kwake, woweruzayo pomalizira pake ‘anawona kuti mkaziyo anapeza chilungamo.’

20. Ndi phunziro lotani limene fanizo la Yesu liri nalo kaamba ka ife?

20 Nchiyani chomwe chiri phunziro kwa ife lerolino? Kusiyanitsa woweruza wopanda chilunjiko ameneyo ndi Yehova, Yesu ananena kuti: “Tamverani chonena woweruza [wosalunjikayo, NW]. Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nawo mtima? Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa.”​—Luka 18:6-8a.

21. Ndimotani mmene tiyenera kuwonera ndi kusamalira mavuto athu aumwini?

21 Nthaŵi zonse kumbukirani kuti pamene chibwera ku mavuto athu aumwini, komwe kumawoneka kukhala kuchedwa kulikonse m’kuyankha ku mapembedzero athu sikuli chifukwa cha kusafunitsitsa ku mbale ya Mulungu. (2 Petro 3:9) Ngati tikuvutika ndi mtundu winawake wa chizunzo kapena kupanda chilungamo konga kuja kwa mkazi wamasiyeyo, tingakhale ndi chikhulupiriro kuti Mulungu adzawona kuti chilungamo chachitidwa potsirizira pake. Ndimotani mmene tingasonyezere chikhulupiriro choterocho? Mwa kupemphera mwakhama ndi kuchirikiza mapemphero athu mwa kusungirira njira yokhulupirika ya kachitidwe. (Mateyu 10:22; 1 Atesalonika 5:17) Ndi kukhulupirika kwathu, tidzatsimikizira kuti pali chikhulupiriro pa dziko lapansi, kuti pali okonda chilungamo owona, ndipo kuti tiri pakati pawo.​—Luka 18:8b.

“Kondwerani, Amitundu Inu, Ndi Anthu Ake”

22. Ndi pa chidziŵitso chotani cha chipambano pamene Mose akumaliza nyimbo yake?

22 Mazana ambiri apitawo, Mose anamaliza nyimbo yake pa chidziŵitso cha chipambano ichi: “Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake; Adzalipsyira mwazi wa atumiki ake, Adzabwezera chilango akumuwukira, Nadzafafanizira zoipa dziko lake ndi anthu ake.” (Deuteronomo 32:43) Tsiku la kubwezera la Yehova lakhala likuyandikira pafupi nthaŵi zonse. Tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga kuti iye adakasonyezabe kuleza mtima limodzi ndi chilungamo!

23. Ndi chotulukapo chosangalatsa chotani chomwe chikuyembekezera awo omwe akugawanamo m’chikondwerero cha anthu a Mulungu?

23 Njira idakali yotseguka kaamba ka awo mu mitundu yonse “kufika ku kulapa,” koma palibe nthaŵi yofunika kuitaya. Petro anachenjeza kuti: “Tsiku la [Yehova, NW] lidzadza ngati mbala.” (2a Petro 3:9, 10) Chilungamo cha Mulungu chimafuna kuti dongosolo la kachitidwe koipa iri liwonongedwa posachedwapa. Pamene litero, lolani kuti tidzapezedwe pakati pa awo omwe avomereza ku chiitano chosangalatsa chakuti: “Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake.” Inde, lolani kuti tikhale pakati pa achimwemwewo omwe awona kuti chilungamo chimazindikiritsa njira zonse za Mulungu!

Kodi Mukayankha Motani?

◻ Nchifukwa ninji Chilamulo cha Mose chiyenera kulimbikitsa chikhulupiriro chathu m’chilungamo cha Mulungu?

◻ Nchiyani chomwe chifunikira kutisonkhezera ife kuvomereza ku njira zolungama za Mulungu?

◻ Ndimotani mmene Yehova angalemekezedwere?

◻ Lerolino, nkuti kokha kumene chikondwerero chowona chingapezedwe?

[Chithunzi patsamba 25]

“Zowona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa lye ndi wakuchita [chilunjiko, “NW”] alandiridwa naye.”​—Machitidwe 10:34, 35

[Chithunzi patsamba 28]

Mulungu adzapangitsa chilungamo kuchitidwa kwa osankhidwa ake omwe akufuula kwa iye

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena