Ripoti Lolongosoka la Mboni Yowona ndi Maso!
Lemba lofalitsidwa posachedwapa la chiUgaritic (KTU 1.161) likutsimikizira kudalirika kwa 2 Mafumu 10:19, 20. Kuti awononge alambiri a Baala, Mfumu Yehu analamula kuti: “Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala.” (Mulungu wonyenga, mothekera woimiridwa ndi kafano koumbidwa kulamanzere.) Mogwirizana ndi Vetus Testamentum, magazini yofalitsidwa mu Netherlands, kalongosoledweka kali “mKanani weniweni” ndipo kamatanthauza “ ‘zungulire wotsekedwa’: wakunja aliyense akanakhoza kulangidwa ndi temberero.” “Tsopano tikuzindikira kuti mkonzi wa ndimeyo mu 2 Mafumu mwachiwonekere akusonyeza chidziŵitso chabwino cha kugwiritsira ntchito mawu kwa chipembedzo kwa Chikanani,” yachitira ndemanga tero Vetus Testamentum.
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Louvre Museum, Paris