Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 6/1 tsamba 7
  • Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo ndi Uminisitala za Yesu
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Nkhani Zothandiza mu Utumiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Zatsopano Zimene Zizipezeka mu Nsanja ya Olonda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Kodi Mumagwiritsa Ntchito Nkhani Zonse za M’magazini Yogawira?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Zatsopano Zoyambitsira Maphunziro A Baibulo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 6/1 tsamba 7

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

NKHANI yakuti “Yesu Amaliza Zonse Zimene Mulungu Afuna,” pamasamba otsatira, ndiyo chigawo chothera cha mpambo wathu wautali wa “Moyo ndi Uminisitala za Yesu.” Mbali imeneyi yawonekera mu Nsanja ya Olonda kwazaka zoposa zisanu ndi chimodzi, m’makope otsatizana 149, kuyambira ndi kope la April 1, 1985.

Tikhulupirira kuti mpambo umenewu m’Nsanja ya Olonda wakuthandizani kutsatira chenjezo la mtumwi Paulo la ‘kuyang’anitsitsa dwii pa Yesu’ ndi kulabadira lamulo la Mulungu la ‘kumvera iye.’ (Ahebri 12:2, 3, NW; Mateyu 17:5) Mkati mwa zakazi, anthu ambiri alemba makalata onena kuti iwo athandizidwa kuchita zimenezi. “Kuli monga ngati kuti ndinaliko kumeneko ndikumvetsera kwa iye ndi kuwona zimene akuchita,” analemba motero woŵerenga wina. “Ndafikira pakumkonda kwambiri chifukwa cha nkhani zimenezi.”

Woŵerenga wina analemba kuti: “Kope lirilonse liwonekera kukhala ndi mfundo yomwe ndinaphonya poŵerenga cholembedwa cha Baibulo. Ndasangalala ndi kudziŵa zochitika zosiyanasiyana m’moyo wa Yesu m’dongosolo lotsatizana bwino mwakuŵerenga nkhani iriyonse.” Anthu ambiri afotokoza kuyamikira kofananako kaamba ka kuphunzira pamene ndi kumene Yesu anaphunzitsira ndi kuchita zinthu mkati mwa uminisitala wake.

Mkazi wina ku Spanya anati: “Ndasunga nkhani zonse kuyambira pachiyambi. Izo nzoperekadi chilangizo kwa akulu ndi ana. Ndiri ndi zaka zakubadwa 44, ndipo ndimasangalala pamene ndiŵerenga nkhani zimenezi. Kumakhala ngati kuti ndinaliko pachochitika chirichonse chambiri yakale.”

Nakubala wina ku United States analemba kuti: “Chifukwa chakuti nkhanizo zimatchula zinthu mwachidule ndi kuzilongosola mokhweka, mwamuna wanga wagwirizana nafe m’phunziro lathu labanja. Mwana wanga wamwamuna wa zaka zakubadwa zisanu ndi zitatu anandipempha kukulemberani kukuyamikirani kuti atate ake tsopano amaphunzira Baibulo. Iye akupempha kuti tsiku lina mpambowu utatha, nkhanizi zikafalitsidwe m’bukhu kotero kuti iye angagaŵireko anzake akusukulu.”

Mwinamwake inuyo mukuvomereza malingaliro a woŵerenga yemwe posachedwapa anadandaula kuti: “Ndimadzimva woipidwa pang’ono kulingalira kuti mpambowu udzatha posachedwapa pamene masiku omalizira a moyo wa Kristu akufotokozedwa. Ndidzawalakalakadi malo ake m’Nsanja ya Olonda.” Tikhulupirira kuti mudzasangalala ndi mbali yomalizirayi ya mpambo wathu wakuti, “Moyo ndi Uminisitala za Yesu.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena