Kodi Tingambwezere Motani Yehova?
YEHOVA MULUNGU amapereka chitsanzo chabwino koposa cha kupatsa. Iye anapatsa anthu onse “moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25) Mulungu amawalitsira dzuŵa lake pa anthu oipa ndi olungama omwe. (Mateyu 5:45) Ndithudi, ‘Yehova amatipatsa mvula yochokera kumwamba ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yathu ndi chakudya ndi chikondwero.’ (Machitidwe 14:15-17) Eya, ‘mphatso iriyonse yabwino, ndi chininkho chirichonse changwiro zichokera kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko’!—Yakobo 1:17.
Pambali pa mphatso zonse zakuthupi za Mulungu, iye amatumiza kuunika kwauzimu ndi chowonadi. (Salmo 43:3) Atumiki okhulupirika a Yehova adalitsidwa molemera ndi chakudya chauzimu chimene amapereka panthaŵi yake kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Tikhoza kupindula ndi zopereka zauzimu za Mulungu chifukwa chakuti wakupanga kukhala kotheka kwa anthu ochimwa, omafa kuyanjanitsidwa ndi iye. Motani? Kupyolera mu imfa ya Mwana wake, Yesu Kristu, amene anapereka moyo wake monga dipo la ambiri. (Mateyu 20:28; Aroma 5:8-12) Ha, ndimphatso yotani nanga kuchokera kwa Mulungu wachikondi, Yehova!—Yohane 3:16.
Kodi Pali Malipiro Alionse Amene Ali Othekera?
Zaka mazana ambiri dipo lisanaperekedwe, wamasalmo wouziridwa anayamikira mwakuya chifundo, chilanditso, ndi chithandizo zoperekedwa ndi Mulungu, kotero kuti ananena kuti: ‘Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira? Ndidzanyamula chikho cha chipulumutso, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova. Ndidzachita zoŵinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse.’—Salmo 116:12-14.
Ngati ndife odzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova, timaitanira pa dzina lake ndi chikhulupiriro ndikukwaniritsa zoŵinda zathu kwa iye. Monga Mboni za Yehova, tingadalitse Mulungu mwakulankhula zabwino za iye panthaŵi zonse ndi kulengeza uthenga wa Ufumu wake. (Salmo 145:1, 2, 10-13; Mateyu 24:14) Koma sitingamlemeretse Yehova, yemwe ali mwini zinthu zonse, kapena kumbwezera kaamba ka zabwino zake zonse za kwa ife.—1 Mbiri 29:14-17.
Kupereka zinthu zopititsira patsogolo zabwino za Ufumu sinjira yobwezera kapena kulemeretsa Yehova. Komabe, kupereka koteroko kumatipatsa mwaŵi wakusonyeza kukonda kwathu Mulungu. Zopereka zopatsidwa, osati ndi cholinga chadyera kapena kutchuka ndi chitamando, koma ndi mzimu wooloŵa manja ndi cholinga chopititsa patsogolo kulambira kowona, zimabweretsera woperekayo chimwemwe ndi dalitso la Yehova. (Mateyu 6:1-4; Machitidwe 20:35) Munthu angakhaledi ndi phande m’kupatsa koteroko ndi chimwemwe chotulukapo mwakuika pambali mosalekeza chinthu chinachake chakuthupi chochilikiza kulambira kowona ndi kuthandiza oyenera. (1 Akorinto 16:1, 2) Kodi zimenezi ziyenera kuchitidwa mwakupereka chachikhumi?
Kodi Muyenera Kupereka Chachikhumi?
Yehova ananena motere kupyolera mwa mneneri wake Malaki: ‘Mubwere nalo limodzi limodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, . . . ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoŵeka malo akuulandira.’ (Malaki 3:10) Matembenuzidwe ena amati: “Bweretsani chachikhumi chonse m’nyumba yosungiramo.”—An American Translation.
Chachikhumi ndi gawo limodzi mwa khumi la chinthu chinachake. Ndicho 10 peresenti yoperekedwa kapena kulipiridwa monga msonkho. Kupereka chachikhumi kumachitidwa makamaka kaamba ka zifuno zachipembedzo. Kumatanthauza kupereka gawo limodzi mwa khumi la malipiro a munthuwe kupititsira patsogolo kulambira.
Kholo Abrahamu (Abramu) anapatsa Melikizedeke mfumu ndi wansembe wa ku Salemu gawo limodzi mwa khumi la zofunkha za chilakiko chake pa Kedorelaomere ndi amene anali naye. (Genesis 14:18-20; Ahebri 7:4-10) Pambuyo pake, Yakobo anawinda kupereka gawo limodzi la magawo khumi a zinthu zake kwa Mulungu. (Genesis 28:20-22) M’chochitika chirichonse, kupereka chachikhumiko kunali kodzifunira, popeza kuti Ahebri oyambirirawo analibe malamulo owakakamiza kupereka chachikhumi.
Kupereka Chachikhumi Pansi pa Chilamulo
Monga anthu a Yehova, Aisrayeli analandira malamulo pakupereka chachikhumi. Mwachiwonekere iwo anaphatikizapo kugwiritsira ntchito magawo aŵiri mwa khumi a malipiro apachaka, ngakhale kuti akatswiri ena amaganiza kuti panali chachikhumi chapachaka chimodzi chokha. Palibe chachikhumi chimene chinaperekedwa m’chaka cha Sabata, popeza kuti panalibe malipiro omwe anali kuyembekezeredwa panthaŵiyo. (Levitiko 25:1-12) Zachikhumi zinali kuperekedwa kuwonjezera pa zoyamba kucha zoperekedwa kwa Mulungu.—Eksodo 23:19.
Gawo limodzi mwa khumi la zokolola za dziko ndi mitengo yazipatso ndipo mwachiwonekere la unyinji wa ng’ombe ndi nkhosa linaperekedwa kukachisi ndi kuperekedwa kwa Alevi, amene sanalandire choloŵa m’dzikolo. Nawonso, anapereka gawo limodzi mwa khumi la zimene analandira kuchirikiza ansembe a Aroni. Mwachiwonekere, mbewuzo zinapunthidwa ndipo zipatso za mpesa ndi azitona zinapangidwa vinyo ndi mafuta zisanaperekedwe monga chachikhumi. Ngati Mwiisrayeli anafuna kupereka ndalama m’malo mwa zokolola, iye akadatero, malinga ngati anawonjezerapo gawo limodzi mwa asanu pa mtengo wake.—Levitiko 27:30-33; Numeri 18:21-30.
Kukuwonekanso kuti chachikhumi china chinaikidwa pambali. Mwanthaŵi zonse, chinagwiritsiridwa ntchito ndi banja pamene anthu anasonkhana kaamba ka mapwando. Koma bwanji ngati mtunda wopita ku Yerusalemu unali wautali kwakuti kunali kovuta kutumiza chachikhumichi? Pamenepo dzinthuzo, vinyo watsopano, mafuta, ndi nyamazo zinasinthidwa kukhala ndalama kotero kuti zinyamulike mopepuka. (Deuteronomo 12:4-18; 14:22-27) Pamapeto pa chaka chirichonse chachitatu ndi chachisanu ndi chimodzi cha sabata ya zaka zisanu ndi ziŵiri, chachikhumi chinaikidwa pambali kaamba ka Alevi, alendo, akazi amasiye, ndi ana amasiye.—Deuteronomo 14:28, 29; 26:12.
Pansi pa Chilamulo, panalibe chilango kwa olephera kupereka chachikhumi. M’malo mwake, Yehova anaika anthuwo pansi pa thayo lamphamvu la makhalidwe abwino lakupereka chachikhumi. Nthaŵi zina iwo anafunikira kulengeza kwa iye kuti chachikhumicho chaperekedwa mokwanira. (Deuteronomo 26:13-15) Chirichonse chosungidwa mosayenerera chinawonedwa kukhala chobedwa kwa Mulungu.—Malaki 3:7-9.
Kupereka chachikhumi sikunali kakonzedwe kolemetsa. Kwenikwenidi, pamene Aisrayeli anasunga malamulo ameneŵa, anakhupuka kwambiri. Kupereka chachikhumi kunapititsa patsogolo kulambira kowona popanda kuika chigogomezero chopambanitsa pa mmene tingaperekere zinthu zakuthupi. Chotero, kakonzedwe ka chachikhumi kanali kabwino kwa onse mu Israyeli. Koma kodi Akristu ayenera kupereka chachikhumi?
Kodi Akristu Ayenera Kupereka Chachikhumi?
Kwa nthaŵi yaitali, kupereka chachikhumi kunali kofala m’Chikristu Chadziko. The Encyclopedia Americana ikufotokoza kuti: “. . . Mwapang’onopang’ono kunakhala kofala pofika m’zaka za zana la 6. Msonkhano wa ku Tours mu 567 ndi Msonkhano wachiŵiri wa Macon mu 585 unachirikiza kupereka chachikhumi. . . . Zinyengo zinakhala zofala, makamaka pamene kuyenera kwakusonkhanitsa chachikhumi kunaperekedwa kapena kugulitsidwa kwa anthu wamba. Kuyambira ndi Papa Gregory VII kachitidwe kameneka kanalengezedwa kukhala kopanda lamulo. Anthu wamba ambiri anapereka kuyenera kwawo kwa kupereka chachikhumi ku malo achipembedzo ndi gulu la mamembala a tchalitchi. Kukonzanso sikunathetse kupereka chachikhumi, ndipo kachitidweko kanapitirizidwa m’Tchalitchi cha Roma Katolika ndi m’maiko Achiprotesitanti.” Kupereka chachikhumi kunathetsedwa kapena kuloŵedwa m’malo mwapang’onopang’ono m’maiko osiyanasiyana, ndipo zipembedzo zoŵerengeka ndizo zimakuchita tsopano.
Pamenepo, kodi Akristu amafunikira kupereka chachikhumi? M’bukhu lake la ndondomeko ya Baibulo, Alexander Cruden anati: “Ngakhale Mpulumutsi wathu, kapena atumwi ake sanalamule chirichonse chokhudza kupereka chachikhumi.” Ndithudi, Akristu sakulamulidwa kupereka chachikhumi. Mulungu iyemwini anathetsa Chilamulo cha Mose, limodzi ndi makonzedwe ake akupereka chachikhumi, kuchikhomera pamtengo wozunzirapo wa Yesu. (Aroma 6:14; Akolose 2:13, 14) Chotero, m’malo mofunsidwa kupereka unyinji wakutiwakuti wochepetsera zowonongedwa za mpingo, Akristu amapanga zopereka zodzifunira mwaufulu.
Lemekeza Yehova ndi Chuma Chako
Ndithudi, sipangakhale chiletso Chamalemba chirichonse cha zopereka zoterozo ngati Mkristu asankha modzifunira kupereka gawo limodzi la khumi la malipiro ake ku kulambira kowona. M’kalata yotsagana ndi chopereka chake, mnyamata wazaka 15 zakubadwa wa ku Papua New Guinea analemba kuti: “Pamene ndinali wamng’ono, bambo ŵanga ankandiuza kuti, ‘Ukadzayamba kugwira ntchito, uyenera kumpatsa Yehova zipatso zoyamba kucha.’ Ndimakumbukira mawu a Miyambo 3:1, 9, amene amati tiyenera kumpatsa Yehova zipatso zoyamba kucha kuti timlemekeze. Chotero ndinalonjeza kuchita zimenezo, ndipo tsopano ndiyenera kukwaniritsa lonjezo langa. Ndine wachimwemwe kwambiri kutumiza ndalama izi kuthandiza m’ntchito Yaufumu.” Baibulo silimauza Akristu kupanga lonjezo loterolo. Komabe, kupereka kooloŵa manja kuli njira yabwino yosonyezera chikondwerero chenicheni m’kupititsa patsogolo kulambira kowona.
Mkristu angasankhe kusaika pambali unyinji wakutiwakuti wa zopereka zimene amapereka kupititsira patsogolo kulambiridwa kwa Yehova Mulungu. Kufotokoza mwafanizo: Pamene anali pamsonkhano wa Mboni za Yehova, alongo aŵiri okalamba anali kukambitsirana za zopereka zimene zingaperekedwe ku ntchito Yaufumu. Ponena za chakudya cha pamsonkhano, mmodzi wa alongowo, yemwe ali ndi zaka 87 zakubadwa, anafunsa ndalama zomwe zikatenga kuti apereke unyinji umenewo. Mlongo winayo, yemwe ali ndi zaka 90, anati: ‘Tangopereka zimene ukulingalira kuti ndiwo ungakhale mtengo wake—ndikuwonjezapo pang’ono.’ Ha, mlongo wachikulireyu anasonyeza mkhalidwe wabwino chotani nanga!
Popeza kuti anthu a Yehova anadzipereka iwo eni kwa iye, mwachimwemwe amapereka zopereka za ndalama ndi zopereka zina zochilikizira kulambira kowona. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 8:12.) Kwenikwenidi, kupereka Kwachikristu kumapereka mwaŵi wakusonyeza chiyamikiro chakuya kaamba ka kulambiridwa kwa Yehova. Kupereka koteroko sikumakhala chachikhumi chokha, kapena gawo limodzi mwa khumi, ndipo pangakhale mikhalidwe imene munthu amasonkhezeredwa kupereka zowonjezereka kupititsa patsogolo zabwino Zaufumu.—Mateyu 6:33.
Mtumwi Paulo anati: ‘Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.’ (2 Akorinto 9:7) Ngati mupereka mokondwera ndi mooloŵa manja kuchirikiza kulambira kowona, mudzakhala bwino, popeza mwambi wanzeru umati: ‘Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha; motero nkhokwe zako zidzangoti the, mbiya zako zidzasefuka vinyo.’—Miyambo 3:9, 10.
Sitingamlemeretse Wam’mwambamwambayo. Iye ndiye mwini golidi yense ndi siliva, zinyama za pamapiri zikwi, ndi zinthu zamtengo wake zosaŵerengeka. (Salmo 50:10-12) Sitingambwezere konse Mulungu kaamba ka mapindu ake onse kwa ife. Koma tingasonyeze chiyamikiro chathu chakuya kaamba ka iye ndi mwaŵi wakupereka utumiki wopatulika ku chitamando chake. Ndipo tingakhale otsimikizira kuti madalitso olemera adzatsanuliridwa kwa awo amene mooloŵa manja amachirikiza kulambira kowona ndi kulemekeza Yehova, Mulungu wachikondi ndi wooloŵa manja.—2 Akorinto 9:11.
[Bokosi patsamba 29]
MMENE ENA AMAPEREKERA KU NTCHITO YAUFUMU
◻ ZOPEREKA ZA NTCHITO YADZIKO LONSER: Ambiri amaika pambali kapena kupanga bajeti ndalama zimene amaika m’mabokosi azopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Sosaite za Ntchito Yadziko Lonse—Mateyu 24:14.” Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi kaya kumalikulu adziko lonse ku Brooklyn, New York, kapena ku ofesi yanthambi yapafupi kwambiri.
◻ MPHATSO: Zopereka zodzifunira za ndalama zingatumizidwe ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York 11201, kapena ku ofesi yanthambi ya Sosaite yakumaloko. Zokometsera kapena zinthu zina zamtengo wapatali zingaperekedwenso. Kalata yachidule yolongosola kuti zimenezo ziri zopereka zodzifunira iyenera kutsagana ndi zopereka zimenezi.
◻ MAKONZEDWE A CHOPEREKA CHAPANGANO: Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society kuti zisungidwe monga choikizira kufikira imfa ya woperekayo, ndi makonzedwe akuti patakhala kusoŵa kwaumwini, zingabwezeredwe kwa woperekayo.
◻ INSHUWALANSI: Watch Tower Society ingatchulidwe kukhala yodzapindula ndi makonzedwe a inshuwalansi ya moyo kapena makonzedwe a kuleka ntchito kapena kulandira penshoni. Sosaite iyenera kudziŵitsidwa za makonzedwe alionse oterowo.
◻ Maakaunti A Ku BANKI: Maakaunti a ku banki, masetifiketi a kusungitsa ndalama, kapena maakaunti a kuleka ntchito zingaikidwe mwa kuikizira kapena kudzalipiridwa pambuyo pa imfa ku Watch Tower Society, mogwirizana ndi ziyeneretso za banki zakumaloko. Sosaite iyenera kudziŵitsidwa za makonzedwe alionse oterowo.
◻ NDALAMA ZACHIWONGOLA DZANJA NDI ZACHIKOLE: Ndalama zachiwongola dzanja ndi zachikole zingaperekedwe ku Watch Tower Society kaya monga mphatso kapena pansi pa makonzedwe akuti phindu lake lipitirize kuperekedwa kwa woperekayo.
◻ MALO: Malo omwe angagulitsidwe angaperekedwe ku Watch Tower Society kaya mwakupereka monga mphatso kapena mwakuika malowo m’manja mwa Sosaite kwa moyo wonse wa woperekayo, amene angapitirize kukhala pamalowo kwa moyo wake wonse. Munthu ayenera kudziŵitsa Sosaite asanapereke malo alionse ku Sosaite.
◻ MAPANGANO AKUGAŴA CHUMA CHAMASIYE NDI KUIKIZA: Katundu kapena ndalama zingaikiziridwe ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania kupyolera mwa pangano la kugaŵa katundu loikidwa mwalamulo, kapena Sosaite ingatchulidwe kukhala yodzapindula ndi makonzedwe a kuikizidwa. Choikiza choperekedwa ku gulu lachipembedzo chingakhale ndi maubwino ena a msonkho. Kope la pangano lakugaŵa chuma chamasiye kapena kuikizidwa liyenera kutumizidwa ku Sosaite.
Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka ndi malangizo onena za nkhani zoterezi, lemberani ku Treasurer’s Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Box 21598, Kitwe, kapena ku ofesi yanthambi ya Sosaite yapafupi kwambiri.