Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 1/1 tsamba 18-23
  • Opani Yehova Ndipo Lemekezani Dzina Lake Loyera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Opani Yehova Ndipo Lemekezani Dzina Lake Loyera
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwopa Mulungu Kumadzetsa Chilakiko
  • Kuchita Zinthu Mowopa Yehova
  • Kondani Chabwino, Idani Choipa
  • Opani Yehova Ndipo Mtamandeni
  • Lemekezani Yehova Kwamuyaya
  • Khalani ndi Mtima Woopa Yehova
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kuphunzira Kupeza Chisangalalo M’kuwopa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Nchifukwa Ninji Tiyenera Kuwopa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kuwopa Mulungu Kodi Kungakupindulitseni?
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 1/1 tsamba 18-23

Opani Yehova Ndipo Lemekezani Dzina Lake Loyera

“Kodi ndani amene sadzakuwopanidi inu, Yehova, ndi kulemekeza dzina lanu, chifukwa inu nokha ndinu wokhulupirika?”​—CHIVUMBULUTSO 15:4, NW.

1, 2. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova anatsegulira mazenera akumwamba mu 1991? (b) Kodi nchokumana nacho cha m’moyo chotani chimene chinasonkhezera mishonale wokhulupirika kupereka uphungu wakuti: “Opani Yehova”? (Onaninso 1991 Yearbook, masamba 187-9.)

YEHOVA ‘anatsegula mazenera akumwamba ndi kutsanula mdalitso wakuti anasoŵeka malo akuulandirira.’ Mawuŵa akhoza kugwiritsiridwa ntchito mobwerezabwereza pa Mboni za Yehova m’nthaŵi zaposachedwapa. (Malaki 3:10) Mwachitsanzo, m’chaka chautumiki cha 1991, chisangalalo cha Mboni zochokera kwina ndi osonkhana akumaloko chinasonyezedwa mwakuyanjana pamodzi kwa Akristu pamisonkhano yapadera yochitidwa kuzungulira dziko lonse lapansi​—kuyambira ku misonkhano ya “Chinenero Choyera” m’Buenos Aires ku South America; ndi Manila, Taipei, ndi Bangkok Kum’maŵa; mpaka ku Misonkhano ya “Okonda Ufulu” ku Budapest, Prague, ndi Zagreb (August 16-18, 1991) Kum’maŵa kwa Yuropu.

2 Chinali chosangalatsa chotani nanga kwa nthumwi zochokera kumaiko akutali kudzakumana ndi Mboni zokhulupirika zakale m’malo amenewo! Mwachitsanzo, m’Bangkok, Frank Dewar​—yemwe panthaŵi ina anali wofalitsa Ufumu yekha m’Thailand​—anasimba za utumiki wake waumishonale wa zaka 58. Ntchito zake zinafalikira kuchokera ku zisumbu za Pacific mpaka ku Southeast Asia, ndipo ngakhale kuloŵa m’Tchaina. Iye anayang’anizana ndi maupandu kuyambira pa kusweka kwa chombo, zilombo zolusa m’nkhalango, matenda a kumalo otentha, ndi ulamuliro wankhalwe wa atsogoleri ankhondo Achijapani. Pamene anafunsidwa kuti ndi uphungu wotani umene angapereke kwa osonkhanawo, yankho lake linali lokhweka lakuti: “Opani Yehova!”

3. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kusonyeza mantha aumulungu?

3 “Opani Yehova!” Ha, nkofunika chotani nanga kwa tonsefe kuti tikulitse mantha oyenera amenewo! ‘Kumuwopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.’ (Salmo 111:10) Kuwopa kumeneku sindiko mantha achinthenthe akuwopa Yehova. Mmalomwake, uli ulemu wakuya kaamba ka ukulu wake wowopsa ndi mikhalidwe yaumulungu, wozikidwa pa chidziŵitso chimene timalandira kupyolera m’phunziro la Mawu a Mulungu. Pa Chivumbulutso 15:3, 4, nyimbo ya Mose ndi ya Mwanawankhosa ikulengeza kuti: ‘Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, [Yehova, NW] Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zowona, Mfumu inu ya nthaŵi zosatha. Ndani adzakhala wosawopa ndi wosalemekeza dzina lanu [Yehova]? Chifukwa inu nokha muli [wokhulupirika, NW].’ Pokhala wokhulupirika kwa olambira ake, Yehova ali ndi ‘bukhu la chikumbutso lolembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.’ Iwo amafupidwa ndi moyo wosatha.​—Malaki 3:16; Chivumbulutso 20:12, 15.

Kuwopa Mulungu Kumadzetsa Chilakiko

4. Kodi nchipulumutso chamakedzana chotani chimene chiyenera kutilimbikitsa kuwopa Yehova?

4 Pamene Israyeli anatuluka mu Igupto wa Farao, Mose anasonyeza bwino lomwe kuti iye anawopa Yehova yekha. Posapita nthaŵi, Aisrayeli anatsekerezedwa pakati pa Nyanja Yofiira ndi gulu lankhondo lamphamvu la Igupto. Kodi iwo akachitanji? ‘Mose ananena ndi anthu, Musawope, chirimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aigupto mwawawona leroŵa, simudzawawonanso konse. Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete.’ Mozizwitsa, Yehova anagaŵanitsa madziwo. Aisrayeli anawoloka pakati panyanja powuma. Kenako madziwo anabwerera ndikuwombana mwamphamvu. Gulu lankhondo la Farao linafafanizidwa. Yehova anapulumutsa mtundu wowopa Mulungu umenewo, komanso panthaŵi imodzimodziyo anapereka chiweruzo pa Igupto wonyoza Mulungu. Mofananamo lerolino, iye adzasonyeza kukhulupirika kwake mwakulanditsa Mboni zake zowopa Mulungu ku dziko la Satana.​—Eksodo 14:13, 14; Aroma 15:4.

5, 6. Kodi nzochitika zotani m’nthaŵi ya Yoswa zimene zimasonyeza kuti tiyenera kuwopa Yehova koposa munthu?

5 Atachoka mu Igupto, Mose anatumiza azondi 12 m’Dziko Lolonjezedwa. Khumi anachita mantha pamene anawona nzika zonga zimphona ndi kuyesa kuwopseza Israyeli kusaloŵa m’dzikolo. Koma ena aŵiri, Yoswa ndi Kalebi, anasimba kuti: ‘Ndilo dziko lokometsetsa ndithu. Yehova akakondwera nafe, adzatiloŵetsa m’dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamawopa anthu a m’dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wawo wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.’​—Numeri 14:7-9.

6 Komabe, Aisrayeli amenewo anawopa munthu. Monga chotulukapo, iwo sanafike ku dziko la lonjezano. Koma Yoswa ndi Kalebi, pamodzi ndi mbadwo watsopano wa Aisrayeli, anakhala ndi mwaŵi wakuloŵa m’dziko lokongola limenelo ndi kulima minda yake ya mpesa ndi azitona. M’nkhani yake yotsazikira kwa Aisrayeli osonkhana pamodzi, Yoswa anapereka uphungu uwu: ‘Opani Yehova ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro ndi wowona.’ Ndipo Yoswa anawonjezera kuti: ‘Koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.’ (Yoswa 24:14, 15) Ha, ndimawu olimbikitsa chotani nanga kwa mitu yabanja ndi ena onse kuwopa Yehova pamene tikukonzekera kuloŵa m’dziko latsopano lolungama la Mulungu!

7. Kodi ndimotani mmene Davide anasonyezera kufunika kwa kuwopa Mulungu?

7 Davide, pamene anali mbusa wachinyamata anasonyezanso chitsanzo chabwino cha kuwopa Yehova pamene anatokosa Goliati m’dzina la Mulungu. (1 Samueli 17:45, 47) Ali pafupi kufa, Davide analengeza kuti: ‘Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine, ndi mawu ake anali pa lilime langa. Mulungu wa Israyeli anati, Thanthwe la Israyeli linalankhula ndi ine; Kudzakhala woweruza anthu molungama; woweruza m’kuwopa Mulungu. Iye adzakhala ngati kuunika kwa m’maŵa, potuluka dzuŵa, m’maŵa mopanda mitambo; pamene msipu uphuka kutuluka pansi, chifukwa cha kuŵala koyera, italeka mvula.’ (2 Samueli 23:2-4) Kuwopa Mulungu kumeneku sikumapezeka pakati pa olamulira a dziko lino, ndipo zimenezi nzochititsa tsoka lotani nanga! Zidzakhala zosiyana chotani nanga pamene Yesu, “Mwana wa Davide,” adzalamulira dziko lapansi m’kuwopa Yehova!​—Mateyu 21:9.

Kuchita Zinthu Mowopa Yehova

8. Kodi nchifukwa ninji Yuda anakhupuka pansi pa Yehosafati, zikusonyeza chiyani kaamba ka lerolino?

8 Pafupifupi zaka zana limodzi pambuyo pa imfa ya Davide, Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda. Iyenso anali mfumu imene inatumikira m’kuwopa Yehova. Anabwezeretsa dongosolo lateokratiki mu Yuda, kuika oweruza m’dziko lonselo, nawapatsa malangizo aŵa: ‘Simuweruzira anthu koma Yehova; ndipo ali nanu iyeyu pakuweruza mlandu. Ndipo tsono, kuwopa Yehova kukhale pa inu, musamalire ndi kuchita; pakuti palibe chosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu, kapena kulandira [chiphuphu, NW]. . . . Muzitero ndi kuwopa Yehova mokhulupirika ndi mtima wangwiro.’ (2 Mbiri 19:6-9) Chotero, Yuda anakhupuka kaamba ka kuwopa Yehova, monga momwe anthu a Mulungu amapindulira ndi utumiki wa oyang’anira achifundo lerolino.

9, 10. Kodi Yehosafati analakika motani chifukwa cha kuwopa Yehova?

9 Komabe, Yuda anali ndi adani. Aŵa anafunitsitsa kufafaniza mtundu wa Mulungu. Magulu ankhondo ogwirizana a Amoni, Moabu, ndi phiri la Seiri analoŵerera m’dera la Yudeya ndi kuwopseza Yerusalemu. Chinali chigulu champhamvu zedi. Yehosafati anatembenukira kwa Yehova m’pemphero pamene ‘Ayuda onse anakhala chiriri pamaso pa Yehova, pamodzi ndi makanda awo, akazi awo, ndi ana awo.’ Ndiyeno, poyankha pempherolo, mzimu wa Yehova unatsikira pa Mlevi Yahazieli, yemwe anati: ‘Atero nanu Yehova, Musawope musatenge nkhaŵa chifukwa cha aunyinji ambiri aŵa; pakuti nkhondoyi siyanu, koma ya Mulungu. Maŵa muwatsikire. . . . Sikwanu kuchita nkhondo kuno ayi; chirimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musawope, kapena kutenga nkhaŵa; maŵa muwatulukire, popeza Yehova ali ndi inu.’​—2 Mbiri 20:5-17.

10 M’maŵa mwake, amuna a Yuda analaŵira m’mamaŵa. Pamene anamuka mwachimvero kukakumana ndi adani, Yehosafati anaima chiriri nati: ‘Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala m’Yerusalemu, limbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzalemerera.’ Akuguba kutsogolo kwa amuna onyamula zida, oyimbira Yehova anathira mang’ombe nati: ‘Yamikani Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chosatha.’ Yehova anasonyeza chifundo chimenecho mwakuchititsa magulu ankhondo a adaniwo kusokonezeka kwakuti anaphana okhaokha. Pamene anthu a Yuda anakwera ku nsanja ya olonda m’chipululu, mitembo ya adani yokha ndiyo inatsala iri ngundangunda.​—2 Mbiri 20:20-24.

11. Ponena za kuwopa, kodi ndimotani mmene mitundu imasiyanira ndi anthu a Mulungu?

11 Pamene mitundu yapafupi inamva za kulanditsidwa kozizwitsa kumeneku, “kuopsa kwa Mulungu” kunawagwera. Kumbali ina, mtundu umene unamvera m’kuwopa Yehova tsopano ‘unachita bata.’ (2 Mbiri 20:29, 30) Mofananamo, pamene Yehova apereka chiweruzo pa Armagedo, mitundu idzagwidwa ndi mantha aakulu akuwopa Mulungu ndi Mwana wake Wakupha, Yesu Kristu, ndipo sadzatha kuima patsiku lalikulu la ukali waumulungu.​—Chivumbulutso 6:15-17.

12. Kodi ndimotani mmene kuwopa Yehova kunawafupira a m’nthaŵi zakale?

12 Mantha oyenera kwa Yehova amabweretsa madalitso olemeretsa. Nowa “anasonyeza mantha aumulungu ndipo anamanga chingalawa chopulumutsiramo a m’nyumba yake.” (Ahebri 11:7, NW) Ndipo kunalembedwa ponena za Akristu a m’zaka za zana loyamba kuti, pambuyo pa nyengo ya chizunzo, mpingowo ‘unali nawo mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m’kuwopa [Yehova, NW] ndi m’chitonthozo cha mzimu woyera, nuchuluka’​—monga momwe zikuchitikiradi Kum’maŵa kwa Yuropu lerolino.​—Machitidwe 9:31.

Kondani Chabwino, Idani Choipa

13. Kodi ndinjira iti yokha imene tingakhalire ndi dalitso la Yehova?

13 Yehova ngwabwino m’zonse. Chifukwa chake, ‘kuwopa Yehova ndiko kuda zoipa.’ (Miyambo 8:13) Zolembedwa zimati ponena za Yesu: ‘Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa; mwa ichi Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani ndi mafuta a chikondwerero chenicheni koposa anzanu.’ (Ahebri 1:9) Ngati ife, mofanana ndi Yesu, timakhumba dalitso la Yehova, tiyenera kunyansidwa ndi zoipa, chisembwere, chiwawa, ndi umbombo wa dziko lonyada la Satana. (Yerekezerani ndi Miyambo 6:16-19.) Tiyenera kukonda zimene Yehova amakonda ndi kuda zimene iye amada. Tiyenera kuwopa kuchita chirichonse chimene chikamnyansa Yehova. ‘Apatuka pa zoipa powopa Yehova.’​—Miyambo 16:6.

14. Kodi ndimotani mmene Yesu akutipatsira chitsanzo?

14 Yesu anatisiira chitsanzo chakuti titsatire mapazi ake mosamalitsa. ‘Pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zoŵaŵa, sanawopsa, koma anapereka mlandu kwa iye woweruza kolungama.’ (1 Petro 2:21-23) Powopa Yehova, nafenso tikhoza kupirira zitonzo, kusekedwa, mazunzo, zimene dziko la Satana limadzetsa pa ife.

15. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuwopa Yehova mmalo mwa amene angaphe thupi?

15 Pa Mateyu 10:28, Yesu akutichenjeza kuti: ‘Musamawopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muwope iye, wokhoza kuwononga moyo ndi thupi lomwe m’gehena.’ Ngakhale ngati munthu wowopa Yehova angaphedwe ndi mdani, zoŵaŵa za imfa zimakhala zakanthaŵi. (Hoseya 13:14) Pamene adzaukitsidwa, munthuyo adzakhoza kunena kuti: ‘Imfawe, chigonjetso chako chiri kuti? Imfaŵe, mbola yako iri kuti?’​—1 Akorinto 15:55.

16. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuwopa Yehova ndi kumlemekeza?

16 Yesu iyemwini amapereka chitsanzo chabwino koposa kwa onse okonda chilungamo cha Yehova ndi kuda choipa. Kuwopa kwake Yehova kumasonyezedwa ndi mawu ake omalizira kwa ophunzira ake, opezeka pa Yohane 16:33 akuti: ‘Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa ine mukakhale nawo mtendere. M’dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi ine.’ Cholembedwa cha Yohane chikupitiriza kuti: ‘Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo mmene anakweza maso ake kumwamba, anati, Atate, yafika nthaŵi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni inu . . . Ndaliwonetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa ine m’dziko lapansi.’​—Yohane 17:1-6.

Opani Yehova Ndipo Mtamandeni

17. Kodi chitsanzo cha Yesu tingachitsatire mwanjira zotani?

17 Kodi ife lerolino tikhoza kutsatira chitsanzo cha Yesu cha kulimba mtima? Ndithudi tingatero mwakuwopa Yehova! Yesu watidziŵitsa dzina laulemerero la Yehova ndi mikhalidwe yake. Mwakumuwopa Yehova monga Mfumu Ambuye wathu, timamkweza kwenikweni pamwamba pa milungu ina yonse, kuphatikizapo Utatu wachinsinsi wopanda dzina wa Chikristu Chadziko. Yesu anatumikira Yehova ndi mantha aulemu, akupeŵa kugwidwa m’msampha wa kuwopa munthu. ‘Ameneyo, m’masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa iye amene anakhoza kumpulumutsa iye mu imfa, ndipo anamveka popeza anawopa Mulungu.’ Mofanana ndi Yesu, nafenso timuwopetu Yehova pamene tipitiriza kuphunzira kumvera mwa zinthu zimene timavutika nazo​—nthaŵi zonse tikukhala ndi chonulirapo chathu cha chipulumutso chosatha.​—Ahebri 5:7-9.

18. Kodi ndimotani mmene tingaperekere utumiki wopatulika kwa Mulungu ndi mantha aumulungu?

18 Pambuyo pake m’kalata imeneyo yopita kwa Akristu Achihebri, Paulo akufulumiza Akristu odzozedwa kuti: ‘Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.’ Lerolino, ‘khamu lalikulu’ limakhala ndi phande muutumiki wopatulika umenewo. Ndipo kodi umaphatikizapo chiyani? Atafotokoza kukoma mtima kwachisomo kwa Yehova m’kupereka nsembe ya Mwana Wake, Yesu Kristu, Paulo akuti: ‘Mwa iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.’ (Ahebri 12:28; 13:12, 15) Pomvetsetsa kukoma mtima kwachisomo kwa Yehova, tidzafuna kupereka mphindi iriyonse yopezeka kuutumiki wake wopatulika. Monga atsamwali okhulupirika a Akristu odzozedwa otsalira, akhamu lalikulu lerolino akuchita mbali yaikulu koposa ya utumiki umenewo. Aŵa amawona chipulumutso kuchokera kwa Mulungu ndi Kristu, pamene akuimirira mophiphiritsira pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ‘akumtumikira iye usana ndi usiku.’​—Chivumbulutso 7:9, 10, 15.

Lemekezani Yehova Kwamuyaya

19, 20. Kodi ndimantha a mitundu iŵiri ati amene adzawonekera pa ‘tsiku la Yehova’?

19 Tsiku lalikulu la kulemekeza Yehova likufika mofulumira! ‘Tawonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng’anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lirinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu.’ Nthaŵi ya tsoka imeneyo ndiyo ‘tsiku lalikulu ndi lowopsa la Yehova.’ (Malaki 4:1, 5) Lidzachititsa ‘kuwopsa’ m’mitima ya oipa, ndipo ‘sadzapulumuka konse.’​—Yeremiya 8:15; 1 Atesalonika 5:3.

20 Komabe, anthu a Yehova amasonkhezeredwa ndi mantha a mtundu wosiyana. Mngelo wokhala ndi ‘uthenga wabwino wosatha’ akulengeza kwa iwo ndi mawu aakulu, akumati: ‘Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake.’ (Chivumbulutso 14:6, 7) Tidzakhaladi ndi mantha aulemu pa chiweruzocho pamene ukali wa Harmagedo udzapsereza dziko la Satana. Kuwopa Yehova koyenera kudzakhomerezedwa kwachikhalire pa mitima yathu. Pamenepo tiyeni tipezetu chiyanjo chakukhala pakati pa ‘opulumutsidwa omwe aitanira pa dzina la Yehova’!​—Yoweli 2:31, 32; Aroma 10:13.

21. Kodi kuwopa Yehova kudzatitsogolera ku madalitso otani?

21 Madalitso odabwitsa adzatsatira, kuphatikizapo “zaka za moyo” zomka muyaya! (Miyambo 9:11; Salmo 37:9-11, 29) Chotero, kaya chiyembekezo chathu nchakulandira Ufumu kapena kutumikira m’malo ake a padziko lapansi, tiyeni tipitirizebe tsopano kupereka kwa Mulungu utumiki wopatulika ndi mantha aumulungu ndi ulemu. Tipitirizetu kulemekeza dzina lake loyera. Kodi padzatuluka madalitso otani? Chiyamikiro chamuyaya ngati tisamala uphungu wanzeru wa kuwopa Yehova nthaŵi zonse!

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi ‘kuwopa Yehova’ kumatanthauzanji?

◻ Kodi ndimotani mmene kuwopa Mulungu kunapindulira anthu amakedzana?

◻ Kodi Yesu anatisiira chitsanzo chotani cha kuwopa Mulungu?

◻ Kodi ndimotani mmene tingasungire umphumphu m’kuwopa Yehova?

[Chithunzi patsamba 18]

M’bukhu la Chivumbulutso, abale a Yesu akuwonedwa akuimba ‘nyimbo ya Mose,’ nyimbo yotamanda Yehova

[Chithunzi patsamba 20]

Gulu lankhondo la Yehosafati likulakika m’kuwopa Yehova

[Chithunzi patsamba 23]

Zaka za moyo zomka muyaya zidzakhala mphotho ya owopa Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena