Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 8/1 tsamba 26-30
  • Yehova Amakumbukira Odwala ndi Okalamba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Amakumbukira Odwala ndi Okalamba
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yesetsani Kumvetsetsa
  • Kusonyeza Ulemu kwa Odwala ndi Okalamba
  • Chithandizo cha Kupeza Nyonga Yauzimu
  • Mmene Akristu Angathandizire Okalamba
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Banja Lachikristu Limathandiza Okalamba
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kumayang’anitsitsa pa Zikondwerero za Okalamba
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kusamalira Okalamba ndi Udindo wa Akristu
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 8/1 tsamba 26-30

Yehova Amakumbukira Odwala ndi Okalamba

KUYANG’ANIZANA ndi “nthaŵi ya tsoka” kungakhale kovuta kwambiri. (Salmo 37:18, 19, NW) Nthaŵi yoteroyo ingabwere mwa njira ya ukalamba ndi kufooka kumene umadzetsa. Ena amaloŵa m’nthaŵi ya tsoka pamene adwala matenda aakulu, otenga nthaŵi yaitali. Iwo angaone ngati kuti matendawo akulamulira moyo wawo wonse, kulamulira malingaliro awo onse ndi zochita zawo.

Komabe, kuli kolimbikitsa kukumbukira kuti Yehova amapenya atumiki ake onse. Kumasangalatsa mtima wake pamene atumiki ake odzipereka apitiriza kusonyeza kukhulupirika ndi nzeru mosasamala kanthu za ukalamba, matenda kapena mikhalidwe ina yopereka chiyeso. (2 Mbiri 16:9a; Miyambo 27:11) Mfumu Davide akutitsimikiziritsa kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa iye, . . . nadzamva kufuula kwawo.” Inde, iye akudziŵa za kulimbika kwawo; amawalimbitsa ndi mzimu wake. “Nadzawapulumutsa.” Amawakumbukira ndi kuwathandiza kupirira. (Salmo 145:18, 19) Koma bwanji nanga za ife? Kodi nafenso, mofanana ndi Yehova, timakumbukira odwala ndi okalamba?

Zofooka zochititsidwa ndi kudwala kapena ukalamba zili zinthu zenizeni za dongosolo lino. Izo ndizinthu zimene tidzayang’anizana nazo kufikira pamene Yehova adzakwaniritsa chifuno chake cha dziko lapansi ndi mtundu wa anthu. Lerolino, anthu owonjezerekawonjezereka amakhalabe ndi moyo kufikira ukalamba wa zaka zambiri, chotero anthu ambiri amadziŵa bwino lomwe zifooko zoterozo. Ndiponso, pamene adakali achichepere, ambiri amakanthidwa ndi ngozi kapena matenda owopseza moyo kapena opundutsa. Kufikira pamene dziko lakaleli lichoka, matenda ndi ukalamba zidzapitirizabe kukhala mavuto aakulu.

Timayamikira chotani nanga odwala ndi okalamba athu amene amapitirizabe kukhala zitsanzo zabwino za “kumva zoŵaŵa ndi kuleza mtima”! Inde, “tiwayesa odala opirirawo.” (Yakobo 5:10, 11) Okalamba ambiri amene mphamvu zawo tsopano zachepa akhala ndi phande kwa zaka makumi ambiri m’kuphunzitsa, kulangiza, ndi kuumba awo amene tsopano akutsogolera mumpingo. Okalamba ambiri akusangalalanso kuona kuti ana awo akukhala ndi phande muutumiki wanthaŵi yonse.​—Salmo 71:17, 18; 3 Yohane 4.

Mwanjira yofananayo, timayamikira awo okhala pakati pathu amene ali odwala kwambiri, komabe mosasamala kanthu za kuvutika kwawo, amatilimbikitsa mwa kukhulupirika kwawo. Pamene oterowo asonyeza umboni wa chikhulupiriro chawo popanda kugwedezeka, amakhala otsitsimula kwambiri ndi olimbikitsa chikhulupiriro. Mtendere wawo wa maganizo ndi chikhutiro chawo zimasonyeza chikhulupiriro choyeneradi kuchitsanzira.

Kumakhala kosautsa maganizo pamene munthu akanthidwa mwadzidzidzi ndi kansa, sitroko, kapena mkhalidwe wina umene umasintha kotheratu moyo wake. Kumakhalanso chiyeso choŵaŵa kwa makolo pamene ana adwala matenda aakulu kapena kuvutika chifukwa cha ngozi. Kodi ena angachitenji kuti athandize? Nthaŵi iliyonse ya tsoka yoteroyo imakhala chiyeso pa gulu lonse la Akristu. Umakhala mpata wosonyezera kuti ‘bwenzi lenileni ndiye mbale amene athandiza m’nthaŵi ya tsoka.’ (Miyambo 17:17) Mwachibadwa, siodwala onse ndi okalamba onse amene angayembekezere chithandizo chaumwini kwa chiŵalo chilichonse cha mpingo. Koma Yehova adzatsimikizira kuti kupyolera mwa mzimu wake ambiri adzasonkhezeredwa kuthandiza mwanjira zosiyanasiyana. Ndipo akulu ayenera kukhala maso kutsimikiriza kuti palibe amene akunyalanyazidwa.​—Onani Eksodo 18:17, 18.

Yesetsani Kumvetsetsa

Poyesa kuthandiza wina, nkofunika kwambiri kukhala ndi kulankhulana kwabwino, ndipo zimenezo zimatenga nthaŵi, kuleza mtima, ndi chisomo. Monga wothandiza, mwachibadwa inuyo mumafuna ‘kulimbikitsa ndi mawu’; koma mvetserani mosamalitsa musanalankhule kapena kuchita kanthu, pakuti mungakhale ‘wotonthoza mtima wolemetsa.’​—Yobu 16:2, 5.

Nthaŵi zina kungakhale kovuta kwa odwala ndi okalamba kubisa kulefulidwa kwawo. Ambiri asamalira kwambiri chiyembekezo chawo cha kukhalabe ndi moyo ndi kupyola chisautso chachikulu, koma tsopano akuona kuti akupikisana ndi nthaŵi, mpikisano umene sakuona kuti adzapambana popeza imfa ikuoneka kuwakhalira pafupi chisautsocho chisanafike. Ndiponso, kaŵirikaŵiri mkhalidwe wawo umawafooketsa ndi kuwapatsa nkhaŵa zambiri. Kusunga chikhulupiriro kukhalabe chamoyo ndi cholimba ndiko nkhondo, makamaka pamene munthu sathanso kuchita chimene mtima umakhumba, kukhala ndi phande lokwanira muutumiki Wachikristu. Mkulu wina Wachikristu anachezera mlongo wokalamba; popemphera pamodzi, mbaleyo anapempha kuti Yehova atikhulukire machimo athu. Atatha kupemphera anaona kuti mlongoyo alikulira. Mlongoyo analongosola kuti anafunikira chikhululukiro chapadera cha Yehova chifukwa chakuti sanakhozenso kulalikira kunyumba ndi nyumba. Inde, kudzimva kukhala wosakhoza kapena wopereŵera, ngakhale kuti kaŵirikaŵiri sikodzifunira, kungachititse munthu kukhala wachisoni kwambiri.

Dziŵani kuti nkhaŵa ndi kutopa zingayambukire kwambiri maganizo a munthu. Chifukwa cha zofooka za ukalamba kapena nkhaŵa ya matenda opuŵalitsa, munthu angadzimve kukhala wosiidwa ndi Yehova, mwinamwake akumanena kuti: “Kodi ndinalakwa chiyani? Kodi ine zandionanji?” Kumbukirani mawu a Miyambo 12:25 akuti: “Nkhaŵa iweramitsa mtima wa munthu; koma mawu abwino aukondweretsa.” Yesani kukamba mawu abwino otonthoza. Okalamba amene akuvutika angasonyeze chikhumbo cha kufuna kufa, mofanana ndi Yobu. Zimenezi siziyenera kukudabwitsani kwambiri; yesani kumvetsetsa. Kudandaula koteroko sikuli kwenikweni umboni wa kupanda chikhulupiriro kapena chidaliro. Yobu anapempherera ‘kubisidwa m’manda,’ komabe mawu ake otsatirapo akusonyeza chikhulupiriro chake cholimba chakuti Yehova akamuukitsa m’kupita kwa nthaŵi. Chikhulupiriro cholimba chimatheketsa kupirira nyengo zosautsa ndi kupsinjika maganizo komabe kukhalabe woyandikana ndi Yehova.​—Yobu 14:13-15.

Kusonyeza Ulemu kwa Odwala ndi Okalamba

Kuli kofunika kwambiri kuchitira odwala ndi okalamba mwaulemu. (Aroma 12:10) Ngati iwo sachita zinthu mwamsanga monga momwe anali kuchitira kale kapena ngati sathanso kuchita zochuluka, musataye mtima. Musakhale ofulumira kududukira ndi kuwapangira zosankha. Mosasamala kanthu kuti tili ndi cholinga chabwino motani, ngati tichita mwanjira yolamulira kapena yotsendereza, mosapeŵeka timalanda ulemu wa munthu winayo. M’nkhani ya kufufuza kwa madokotala kofalitsidwa mu 1988, wofufuza wina, Jette Ingerslev, anafotokoza zimene gulu la okalamba a zaka 85 anaziona kukhala zofunika kwambiri kuti moyo wawo ukhale waphindu: “Iwo anatchula mbali zitatu: kukhala pamodzi ndi achibale; thanzi labwino; ndiyeno kukhala okhoza kupanga zosankha zawozawo.” Onani kuti pamene kholo lakalelo Yakobo linakalamba, ana ake sanalichitire monga ngati mwana; zofuna zake zinalemekezedwa.​—Genesis 47:29, 30; 48:17-20.

Odwala ayenera kuchitiridwanso mwaulemu. Mkulu wina anatayikiridwa ndi mphamvu yake yakulankhula, kuŵerenga, ndi kulemba chifukwa cha opaleshoni yopangidwa molakwika. Zimenezi zinali zosautsa kwambiri, koma akulu anzake anaganiza za kuchita kalikonse kamene anakhoza kuti iyeyo asadzimve kukhala wopanda pake. Iwo tsopano amamuŵerengera makalata onse a mpingo ndipo amamloŵetsamo polinganiza nkhani zina za mpingo. Pa msonkhano wa akulu, iwo amayesa kumfunsa malingaliro ake. Amamchititsa kudziŵa kuti akumuonabe kukhala mkulu mnzawo ndi kuti amayamikira kukhalapo kwake. Mumpingo Wachikristu, tonsefe tingapange kuyesayesa kumeneko kotero kuti palibe wodwala kapena wokalamba amene adzimva ‘wotayidwa’ kapena wonyalanyazidwa.​—Salmo 71:9.

Chithandizo cha Kupeza Nyonga Yauzimu

Tonsefe timafunikira chakudya chauzimu kuti chikhulupiriro chathu chikhalebe chamoyo ndi cholimba. Ndicho chifukwa chake timalimbikitsidwa kuŵerenga Baibulo ndi mabuku ophunzirira Baibulo tsiku ndi tsiku ndi kukhala ndi phande mwachangu m’misonkhano Yachikristu ndi ntchito yolalikira. Kaŵirikaŵiri, odwala ndi okalamba amafunikira chithandizo kuti achite zimenezi, ndipo nkofunika kuchita zothandizadi malinga ndi mkhalidwe wawo. Mokondweretsa, ambiri ali okhoza kupezekabe pamisonkhano ngati athandizidwa ndi choyendera ndi kuwathandiza pang’ono m’zinthu zina pa Nyumba Yaufumu. Kupezekapo kwawo pamisonkhano yoteroyo kumalimbikitsa mpingo kwambiri. Kupirira kwawo kumatsitsimula ndi kulimbikitsa chikhulupiriro.

Kaŵirikaŵiri, odwala ndi okalamba nawonso akhoza kukhala ndi phande lopindulitsa muutumiki Wachikristu. Ena akhoza kuphatikizidwa m’gulu lopita ndi galimoto muutumiki, ndipo mosakayikira amatsitsimulidwa mwakukhala okhoza kufikira makomo angapo. Pamene zimenezi sizithekanso, iwo akhoza kupeza chisangalalo mwa kulalikira mwamwaŵi kwa anthu amene amakambitsirana nawo. Mlongo wina amene anakanthidwa ndi kansa anaganiza za kuthera nthaŵi yake yotsalayo m’moyo akuyesayesa mwapadera kulalikira mbiri yabwino. Kulalikira kwake kolimba mtima kunali kolimbikitsa kwa onse. Iye analinganiza ngakhale makonzedwe a maliro ake kotero kuti umboni wabwino ukaperekedwe kwa achibale osakhulupirira, anzake akuntchito, ndi anansi. Motero mikhalidwe yake yosautsayo inakhala ‘yothandizira uthenga wabwino,’ ndipo kutsimikiza mtima kwake kwa kusonyeza chikhulupiriro ndi chidaliro kunasonyeza masiku ake otsirizira kukhala atanthauzo lapadera.​—Afilipi 1:12-14.

Kumakhala bwino kuthandiza odwala ndi okalamba kuti alimbikitsidwe mwauzimu. Mabanja akhoza kuwaitana kudzacheza nawo madzulo, kapena nthaŵi zina angamakachitire phunziro lawo labanja kunyumba ya uyo amene satha kuyenda. Mayi wina anabweretsa ana ake ang’ono aŵiri kunyumba kwa mlongo wokalamba kudzaŵerengera pamodzi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Zimenezi zinachititsa mlongo wokalambayo kukhala wachimwemwe kwambiri, ndipo anawo anakondwera kwambiri ndi chisamaliro cha mlongoyo kwa iwo.

Komabe, pali nthaŵi zina pamene munthu wopunduka safunikira kudodometsedwa kwambiri, ndipo kungakhale bwino kwambiri kungomuŵerengera nkhani zina mofuula panthaŵi zina. Komabe, kumbukirani kuti ngati wina ali wofooka kwambiri kwakuti sakhoza kukambitsirana, munthu woteroyo angafunikirebe ndipo angakhumbe kuyanjana naye kwauzimu. Tikhoza kupemphera pamodzi ndi otero, kuŵerenga nawo, kapena kuwasimbira zokumana nazo; koma tiyenera kusamala kusakhala kwa nthaŵi yaitali kwambiri kuwopera kuwatopetsa.

Pali mtundu wina wa utumiki wopatulika umene ngakhale odwala ndi okalamba ambiri akhozabe kuuchita: kupempherera ena. Ophunzira oyambirira anaona utumiki umenewu kukhala wofunika kwambiri. Panthaŵi ina iwo anagaŵira mtolo wa ntchito kwa ena mumpingo kotero kuti atumwi aike chisamaliro chachikulu pakupemphera. Epafra wokhulupirikayo akunenedwa kukhala ‘wakulimbikira m’mapemphero kaamba ka ena.’ (Akolose 4:12; Machitidwe 6:4) Pemphero loterolo nlofunika kwambiri ndi lopindulitsa.​—Luka 2:36-38; Yakobo 5:16.

Yehova amakumbukira odwala ndi okalamba ndi kuwasamalira m’nthaŵi yawo ya tsoka. Iye moyenerera amafuna kuti nafenso tilingalire zimene tingachite kuti tiwathandize ndi kuwachilikiza. Chisamaliro chimene timasonyeza chimawonetsa kutsimikiza mtima kwathu kwa kufuna kusunga umphumphu wathu. Ndipo timakhala achimwemwe polingalira mawu a Mfumu Davide akuti: “Yehova adziŵa masiku a anthu angwiro: ndipo chosiyira chawo chidzakhala chosatha.”​—Salmo 37:18.

[Bokosi patsamba 28]

Kupereka Chithandizo Chogwira Ntchito ndi Kumvetsetsa

MABWENZI ndi achibale ayenera kukhala ndi chidziŵitso choyenera ponena za mmene angasamalirire odwala ndi okalamba. Chofunika koposa, iwo angalimbikitsidwe kukhala ndi kaonedwe kabwino ka moyo, kuti ali ofunika ndi oyamikiridwa, ndi kudziona kukhala olemekezeka. Motero mkhalidwe wa moyo udzakhalabe umene udzakulitsa chimwemwe chawo mwa Yehova, mosasamala kanthu za zoŵaŵa zawo ndi mavuto. Kwazindikiridwa kuti Mboni za Yehova zambiri zimakhalabe ndi moyo kufikira paukalamba weniweni. Mosakayikira, chochititsa chachikulu ndicho chikondwerero chawo chamoyo m’chiyembekezo chili patsogolo, mkhalidwe wawo wabwino wa maganizo, ndi kukhala kwawo ndi phande m’ntchito ya Ufumu monga momwe angathere. Malemu Frederick W. Franz, yemwe anali prezidenti wa Watch Tower Society, amene anamwalira mwamtendere m’chaka chake cha 100 pambuyo pa moyo wopindulitsa ndi wachimwemwe, anali chitsanzo chabwino koposa cha zimenezi.​—Yerekezerani ndi 1 Mbiri 29:28.

Kwenikweni, kupereka chisamaliro pankhani zazikulu za moyo wa tsiku ndi tsiku kungaloŵetsemo zambiri: udongo, zakudya zopatsa thanzi, kumwa zakumwa zokwanira ndi mchere, maseŵera olimbitsa thupi oyenera, mpweya wabwino, kuthoŵa thupi, ndi kukambitsirana kotsitsimula. Kudya chakudya choyenera chopatsa thanzi kungathandize kuwongolera kumva, kuona, kuganiza, ndi kukhala bwino kwathupi, limodzinso ndi kutetezera matenda. Kwa anthu okalamba, kungowapatsa chakudya chopatsa thanzi ndi zakumwa zochuluka kungawapangitse kukhala ndi mkhalidwe wabwino ndi kukhala osavuta. Pangafunikire kulingalira bwino kuti mudziŵe mtundu wa maseŵera amene adzayenerera munthuyo. Mlongo wina amene amadzaŵerengera mlongo wokalamba ndi wosatha kuona bwino, amayamba ndi kutsiriza kuchezera kwake kwa mlungu uliwonse mwakuvina pang’onopang’ono m’chipindamo limodzi ndi mlongoyo. Wailesi ya tepurikoda imakhala ili yokonzeka kale ndi nyimbo zosankhidwa, ndipo onse aŵiriwo amasangalala ndi “makonzedwe” ameneŵa.

M’maiko ambiri, magulu othandiza anthu angapereke chithandizo chabwino ndi kuperekanso chidziŵitso ndi malangizo pamikhalidwe yakutiyakuti ndi mmene angachitire nayo. (Ndithudi, Mkristu ayenera nthaŵi zonse kusamala kuti asagwere m’machitachita amene amadodometsa utumiki wathu weniweni Wachikristu.) Nthaŵi zina chithandizo chimaperekedwa mwakubwereka bedi ya kuchipatala, ndodo zoyendera, mpando wamagudumu, zipangizo zomvetserera, ndi zina zotero. Popeza kuti okalamba ambiri amalingalira kuti sikuli kofunikira kukhala ndi zinthu zatsopano zoterozo, achibale nthaŵi zonse ayenera kupereka uphungu woyenera kapena ngakhale kuwakakamiza. Kuwakonzera chotsegulira chitseko cha kuchimbudzi chimene iwo akhoza kugwiritsira ntchito kungawapatse chisangalalo chachikulu kuposa kuwapatsa maluŵa okongola.

Kusamalira okalamba kungakhale kopsinja maganizo kwambiri, makamaka ngati munthuyo akhala wokalipakalipa. Mtima waukali umayambika moŵenderera. Munthu wina akhoza kuutsekereza mwakusalola wodwalayo kukhala waulesi kwambiri. Munthu wokalipakalipa angayambe mwadzidzidzi kukwiyira ngakhale munthu amene anali kukonda kwambiri. Achibale ayenera kuzindikira kuti munthu amene akukalamba akhoza kuiŵala chilichonse chochita ndi chowonadi​—chotulukapo chomvetsa chisoni cha kunyonyotsoka kwa thupi, osati umboni wa kutaya chikhulupiriro.

Ngati wodwala ali m’chipatala kapena kunyumba yosamalira okalamba, kukambitsirana kwabwino ndi ogwira ntchito kumeneko kumakhala kofunika kuti iwo adziŵe zimene ziyenera kuchitidwa ponena za masiku akubadwa, Krisimasi, ndi maholide ena akudziko. Ngati pafunikira opaleshoni, achibale angafotokoze ndi kulemba malingaliro a wodwalayo ponena za kuthiridwa mwazi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena