Mmene Akristu Angathandizire Okalamba
“SITIFOOKA koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa mkati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku. . . . Popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthaŵi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.” Anatero mtumwi Paulo m’kalata yake yachiŵiri kwa Akorinto.—2 Akorinto 4:16-18.
M’nthaŵi zakale, amuna ndi akazi achikhulupiriro anayang’ana pazinthu zosaoneka, zimene zinaphatikizapo zinthu zonse zimene Mulungu wawo, Yehova, anali atalonjeza kudzachita munthaŵi yake yokwanira. M’buku la Ahebri, Paulo amafotokoza moyamikira kwambiri za anthu oterowo, amene anasunga chikhulupiriro chawo kufikira paimfa yawo—ndipo ena a iwo anakhala ndi moyo kufikira atakalamba kwambiri. Iye amanena za iwo kukhala chitsanzo chathu, akumati: “Iwo onse adamwalira m’chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali.”—Ahebri 11:13.
Lerolino tili pafupi kwambiri ndi kukwaniritsidwa kwa malonjezo ameneŵa. Koma tili ndi anthu odwala ndi okalamba pakati pathu amene samatsimikizira kuti adzaona mapeto a dongosolo lino loipa. Mwinamwake ena a ameneŵa adzafanso ali okhulupirika popanda kuona malonjezo onse akukwaniritsidwa mkati mwa moyo wawo. Kwa oterowo mawu a Paulo pa 2 Akorinto 4:16-18, ogwidwa pamwambapowo, ngolimbikitsa kwambiri.
Yehova amakumbukira okhulupirika ake onse, kuphatikizapo anthu odwala ndi okalamba. (Ahebri 6:10) Anthu okalamba okhulupirika amatchulidwa mwaulemu m’malo angapo m’Baibulo, ndipo m’Chilamulo cha Mose, kutchulidwa kwapadera kwa ulemu umene uyenera kusonyezedwa kwa okalamba kwapangidwa. (Levitiko 19:32; Salmo 92:12-15; Miyambo 16:31) Pakati pa Akristu oyambirira, anthu okalamba anachitiridwa mwaulemu (1 Timoteo 5:1-3; 1 Petro 5:5) Buku lina la m’Baibulo lili ndi mafotokozedwe abwino kwambiri a chisamaliro chachikondi ndi kudzimana kwakukulu kosonyezedwa ndi mkazi wina wachichepere kwa apongozi ake aakazi okalamba. Bukulo moyenerera lili ndi dzina la mkaziyo, Rute.
Mthandizi Wodzipereka
Moyo unali wopweteka kwambiri kwa Naomi wokalambayo. Njala ndiyo imene inaumiriza iyeyo limodzi ndi banja lake laling’onolo, kusiya mabwenzi ake ndi choloŵa ku Yuda ndi kukakhala kummaŵa kwa mtsinje wa Yordano m’dziko la Moabu. Kunoko ndiko kumene kunafera mwamuna wa Naomi, akumamsiya yekha ndi ana ake aamuna aŵiri. Ameneŵa, m’kupita kwa nthaŵi, anakula nakwatira, komano nawonso anafa. Naomi anatsala wopanda woloŵa nyumba kuti amusamalire.
Anali wokalamba kwambiri wosakhoza kukwatiwanso, ndipo moyo unali wosapindulitsa. Mopanda dyera, anafuna kuti atumize Rute ndi Olipa, akazi amasiye a ana ake aŵiri aamuna, kumudzi kwa amawo kotero kuti akakwatiwenso ndi amuna ena. Koma iye akabwerera yekha kudziko lakwawo. Lerolinonso, okalamba ena ali opsinjika maganizo, makamaka ngati atayikiridwa ndi wokondedwa muimfa. Mofanana ndi Naomi, iwo angafune munthu wowasamalira, koma samafunanso kukhala olemetsa.
Komabe, Rute, sanasiye apongozi akewo. Iye anakonda mkazi wokalamba ameneyu, ndipo anakonda Yehova, Mulungu amene analambiridwa ndi Naomi. (Rute 1:16) Chotero, onsewo anapanga ulendo wobwerera ku Yuda. M’dziko limenelo, munali makonzedwe achikondi pansi pa Lamulo la Yehova lakuti anthu osauka akhoza kukunkha m’munda, kapena kusonkhanitsa, zilizonse zimene zinatsalira m’minda kututa kutachitidwa. Rute, amene anali wachicheperepo, mofunitsitsa anadzipereka kuchita ntchito imeneyi, akumati: “Mundilole ndimuke.” Iye anagwira ntchitoyo mosatopa kaamba ka phindu la aŵiri onsewo.—Rute 2:2, 17, 18.
Kukhulupirika ndi kukonda Yehova kwa Rute kunali chilimbikitso champhamvu kwa Naomi, amene anayamba kuganiza m’njira yolongosoka ndi yomangirira. Kudziŵa kwake Chilamulo ndi miyambo ya dzikolo tsopano kunali kothandiza. Anapereka malangizo anzeru kwa mthandizi wake wodziperekayo kotero kuti mkazi wachichepereyo, kupyolera m’kakonzedwe ka chokolo, akatha kupezanso choloŵa cha banja ndi kubala mwana wamwamuna wopitiriza kukhalapo kwa dzina la banjalo. (Rute, chaputala 3) Rute ali chitsanzo chabwino kwambiri kwa awo amene amadzimana kuti asamalire odwala kapena okalamba. (Rute 2:10-12) Mofananamo, lerolino mumpingo, zambiri zikhoza kuchitidwa kuthandiza odwala ndi okalamba. Motani?
Kulinganiza Nkofunika
Mumpingo Wachikristu woyambirira, munasungidwa mpambo wa akazi amasiye ofuna chithandizo chakuthupi. (1 Timoteo 5:9, 10) Mofananamo, lerolino, m’zochitika zina akulu angalembe mpambo wa odwala ndi okalamba amene akufunikira chisamaliro chapadera. M’mipingo ina mkulu amapemphedwa kusamalira nkhani imeneyi monga thayo lake lapadera. Popeza kuti okalamba ambiri, mofanana ndi Naomi, samakonda kufunafuna chithandizo, mbale amene ali ndi thayo lotero afunikira kukhala waluso popenda mikhalidwe ndipo—mwanjira yochenjera ndi yanzeru—akumatsimikizira kuti zinthu zoyenera zikuchitidwa. Mwachitsanzo, iye akhoza kuona ngati Nyumba Yaufumu ili ndi ziwiya zokwanira zothandizira odwala ndi okalamba. Ngati kuli kothandiza, akhoza kulingalira zinthu zonga podzeretsera mipando ya magudumu ya opunduka, ziwiya zoyenera za m’chimbudzi, ziwiya zothandizira kumva, ndi malo awo okhala apadera. Mbale ameneyu angatsimikizirenso kuti anthu onse amene ali osakhoza kufika ku Nyumba Yaufumu akhoza kubwereka kaseti yojambulidwamo nkhani za misonkhanoyo kapena kumvetsera misonkhanoyo patelefoni.
Pangakhalenso kufunika kwa kulinganiza zoyendera kumka kumisonkhano yampingo ndi misonkhano ina yaikulu. Mlongo wina wokalamba anali ndi vuto chifukwa chakuti munthu amene anali kumtenga kumka naye kumsonkhano anali atachoka. Iyeyo anafunikira kuimbira telefoni anthu ambiri asanapeze munthu womka naye kumisonkhano ndipo potsirizira pake analingalira kuti anali mtolo wolemetsa. Makonzedwe amene akanapangidwa ndi mkulu amene akanasamalira nkhaniyo akanathetsa kuvutika mtima kwakeko.
Mkulu ameneyu angapemphenso mabanja osiyanasiyana ngati angasinthane kukawona okalambawo. Mwanjira imeneyi ana akatha kuphunzira kuti kusamalira anthu okalamba kuli mbali ya moyo Wachikristu. Nkwabwino kuti ana aphunzire kusenza thayo limeneli. (1 Timoteo 5:4) Woyang’anira dera wina anati: “M’kudziŵa kwanga, pali ana oŵerengeka kwambiri kapena achichepere amene amakacheza ndi anthu okalamba kapena odwala mosatumidwa.” Mwinamwake iwo samaganiza kuchita zimenezo, kapena mwinamwake amakayikira za zimene adzachita kapena kunena; makolo akhoza kuwaphunzitsa kuchita zimenezi.
Komabe, kumbukirani kuti okalamba ambiri angayamikire ngati atadziŵiratu pasadakhale kuti bwenzi lawo likubwera. Zimenezi zimawapatsa chisangalalo chowonjezereka cha kuyembekezera mlendo. Ngati alendowo abweretsa zakudya, monga ngati khofi kapena keke, ndipo mwamsanga natsuka mbale potsirizira pake, mtolo wina pa okalamba umapeŵedwa. Banja lina la okalamba, limene lidakali ndi nyonga, lili ndi tsiku lokhazikitsidwa mlungu uliwonse pamene amalongedza zakudya za pikiniki m’basiketi ndi kukacheza ndi okalamba ena a mumpingo. Kuyendera anzawo koteroko kumayamikiridwa kwambiri.
Kuti okalamba apindule, mipingo yambiri imachita Phunziro la Buku la Mpingo kudakali koŵala. Kumalo ena mabanja ena ndi ofalitsa amene ali mbeta anapemphedwa ngati ali ofunitsitsa ndi okhoza kuchilikiza timagulu totero, ndipo chotsatirapo chinali chakuti kagulu ka phunziro la buku ka okalamba ndi achichepere okhoza kusamalirana kanaumbidwa.
Zimenezitu siziyenera kungotulidwira akulu okha kuti ayambirire kuchitapo kanthu. Tonsefe tiyenera kuzindikira za zosoŵa za odwala ndi okalamba. Tingawalonjere m’Nyumba Yaufumu ndi kupatula nthaŵi yolankhula nawo. Kuwaitana kuti ticheze nawo kungayamikiridwe. Kapena tikhoza kuwapempha kutsagana nafe kokayenda kapena kutchuthi. Mboni ina kaŵirikaŵiri imatenga ofalitsa okalamba m’galimoto yake pamene ikupita kunja kwa tauni pokayendera za ntchito. Nkofunika kuthandiza okalamba kupitirizabe kukhala otanganitsidwa. Musawalole kudzipatula, monga momwe Naomi anafuna kuchitira, kumene kumakalambitsa munthu mofulumira kapena kutha nzeru.
Achichepere amene ali opunduka kapena odwala amafunikiranso kusamaliridwa. Mboni ina imene inali ndi anyamata atatu odwala nthenda yosachiritsika, ndipo aŵiri a iwowa anafa, inati: “Kungakhale kovuta kuti mpingo upitirizebe kusamalira pamene munthu wina ali ndi nthenda yosachiritsika. Bwanji osasankha ofalitsa ena achichepere kuti adzichititsa lemba la tsiku ndi kuŵerengera bwenzi lawo lodwala chaputala chimodzi m’Baibulo tsiku lililonse? Achichepere, kuphatikizapo apainiya, akhoza kumasinthana.”
Pamene Imfa Ioneka Kukhala Yosapeŵeka
Atumiki a Yehova nthaŵi zonse ayang’anizana molimba mtima ndi imfa, kaya idze chifukwa cha kudwala kapena chizunzo. Pamene ovutikawo ayamba kuona kuti imfa ili pafupi, nkwachibadwa kwa iwo kukhala ndi malingaliro osakhazikika osiyanasiyana. Imfa yawo itachitika, nawonso achibale awo amapyola nyengo ya kusintha kwa zinthu, chisoni, ndi kuvomereza imfayo. Chotero, kaŵirikaŵiri nkwabwino kwa munthu wodwalayo kunena za kukhosi ponena za imfa yake, monga momwe anachitira Yakobo, Davide, ndi Paulo.—Genesis, machaputala 48 ndi 49; 1 Mafumu 2:1-10; 2 Timoteo 4:6-8.
Mboni ina imenenso ili dokotala inalemba kuti: “Tiyenera kunena moona pankhani imeneyi. Muntchito yangayi sindinapezepo kuti kubisa chenicheni chakuti wodwalayo sadzachira kumathandiza.” Komabe, tiyenera kuzindikira zimene wodwala mwiniyo akufuna kudziŵa, ndipo nthaŵi imene iyeyo akufuna kudziŵa zimenezi. Odwala ena mwachiwonekere amasonyeza kuti akuzindikira kuyandikira kwa imfa yawo, ndipo amafuna kufotokoza malingaliro awo pazimenezi. Ena amaumirira pakuyembekezera kusintha kwa zinthu, ndipo mabwenzi awo amachita bwino kugwirizana nawo.—Yerekezerani ndi Aroma 12:12-15.
Munthu wina amene akuyandikira imfa angakhale wotopa kapena wosokonezeka maganizo kwakuti nkovuta kwa iye kupemphera. Wodwala woteroyo mwinamwake angatonthozedwe ndi mawu a m’lemba la Aroma 8:26, 27 akuti Mulungu amamva “zobuula zosatheka kuneneka.” Yehova amadziŵa kuti pansi pa kutsenderezeka kwa maganizo kotero munthu akhoza kusoŵa mawu a pemphero.
Pamene kuli kotheka, kupemphera ndi wodwalayo nkofunika. Mbale wina akusimba kuti: “Pamene amayi anali kufa apo nkuti alibenso mphamvu yakuti alankhule, anasonyeza mwakupinda manja awo kuti anafuna kuti tipemphere nawo. Titapemphera, tinaimba nyimbo imodzi ya Ufumu, popeza kuti amayi anali munthu wokonda nyimbo kwambiri nthaŵi zonse. Choyamba, tinkangong’ung’udza nyimboyo, ndiyeno tinayamba kuimba chapansipansi mawu ake. Anasangalala nayodi. Mosakayikira, nyimbo zimenezi zimene timazigwirizanitsa ndi moyo wathu monga Mboni za Yehova zili ndi malingaliro amene mwinamwake ali ovuta kufotokoza.”
Kulankhula ndi munthu amene ali pafupi kufa kumafunikira chikondi, luso, ndi kumvera chisoni. Munthu wodzaona wodwala akhoza kulinganiza kutchula zinthu zomangirira ndi zolimbitsa chikhulupiriro, ndipo ayenera kusamala kuti apeŵe kunena zosamangirira ponena za anthu ena ndi mavuto awo. Ndiponso, nthaŵi ya kuona wodwalayo iyenera kugwirizana ndi mkhalidwe umene uli woyenerera. Ngati wodwalayo akuwonekera kukhala wosazindikira, kuli bwino kukumbukira kuti iyeyo mwina angakhalebe wokhoza kumva zimene zikunenedwa. Chotero samalani ndi zimene mukunena.
Thayo Limene Timathandizana Kuchita
Kusamalira odwala ndi okalamba kuli thayo lolemera. Kwa awo okhala pafupi kwambiri ndi wodwala, ndiko ntchito yofuna zambiri, ponse paŵiri mwakuthupi ndi mwamalingaliro. Iwo amafuna ndipo amayenerera kumvedwa ndi kuthandizidwa ndi mpingo wonse. Awo amene amasamalira ziŵalo za banja zodwala kapena okhulupirira anzawo akuchita chinthu chabwino, ngakhale ngati zimenezi zingawachititse kuphonya misonkhano ina kapena ngati kukhala ndi phande kwawo muutumiki wakumunda kukutsika kwanyengo yakutiyakuti. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:8.) Iwo adzalimbikitsidwa ndi mkhalidwe wa kuzindikira wa mpingo. Panthaŵi zina mbale kapena mlongo wina angakhale wokhoza kusamalira anthuwo kwakanthaŵi kotero kuti munthu wosamalira nthaŵi zonseyo apite kumisonkhano kapena kukasangalala ndi maola angapo otsitsimula muntchito yolalikira.
Ndithudi, ngati inu mwininu muli wodwala, mukhoza kuchitanso kanthu kena. Kupanda chiyembekezo ndi kusoŵa chochita ponena za kudwala kwanu kungakuwawitseni mtima, komatu kuwawidwa mtima kumachititsa munthu kukhala wodzipatula ndipo kumapangitsa ena kukuthaŵani. Mmalomwake yesani kunena moyamikira ndi kukhala wogwirizana ndi ena. (1 Atesalonika 5:18) Pemphererani ena amene akuvutika. (Akolose 4:12) Sinkhasinkhani za chowonadi cha Baibulo chokondweretsacho, ndiyeno kambitsiranani zimenezi ndi odzakuonani. (Salmo 71:17, 18) Yenderani limodzi mwachangu ndi kupita patsogolo kolimbitsa chikhulupiriro kwa anthu a Mulungu. (Salmo 48:12-14) Thokozani Yehova chifukwa cha zochitika zokondweretsazi. Kusinkhasinkha pazinthu zonga, kuloŵa kwa dzuŵa kumene kumapereka kuunika kothumirira kuposa pamene dzuŵa lili pamutu, kumakondweretsa m’zaka zathu zotsiriza zaukalamba.
Tonsefe tiyenera kumenyera nkhondo yosunga chiyembekezo, makamaka m’nthaŵi za mayeso, chimene chimatetezera maganizo athu monga chisoti. (1 Atesalonika 5:8) Kuli bwino kusinkhasinkha za chiyembekezo cha chiukiriro ndi maziko ake amphamvu. Tikhoza kuyembekezera mwa chitsimikizo ndi chiyembekezo chaphamphu kaamba ka nthaŵiyo pamene sikudzakhalanso matenda kapena kufooka kwa thupi chifukwa cha ukalamba. Panthaŵiyo, aliyense adzakhala wopeza bwino. Ngakhale akufa adzauka. (Yohane 5:28, 29) “Zinthu zosaoneka” zimenezi timaona ndi maso athu achikhulupiriro ndi mtima. Zisazimiririke konse m’maso mwanu.—Yesaya 25:8; 33:24; Chivumbulutso 21:3, 4.