Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 5/1 tsamba 27-30
  • Kuchirikizidwa ndi Mulungu Amene Sanganame

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchirikizidwa ndi Mulungu Amene Sanganame
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Choloŵa Chachikristu
  • Chikhumbo Choyambirira cha Kulalikira
  • Kuzindikira “Khamu Lalikulu”
  • Njira Zatsopano za Kulalikira
  • Kubwerera Kumadzulo
  • Ukwati ndi Banja
  • Kuchita Utumiki Pakati pa Aaborijini
  • Chithandizo Chosalephera cha Yehova
  • Timadalitsidwa Tikamachita Zimene Yehova Amatiuza
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Ndine Wokonzeka Kuthandiza Ena
    Galamukani!—2005
  • Wokhala Ndekha Koma Wosasiyidwa
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 5/1 tsamba 27-30

Kuchirikizidwa ndi Mulungu Amene Sanganame

YOSIMBIDWA NDI MARY WILLIS

Ziyambukiro za kutsika kwa chuma kwa padziko lonse zinafika kudera lakutali lakumudzi la Western Australia mu 1932. Chaka chimenecho, pamene ndinali ndi zaka 19 zokha, Ellen Davies ndi ine tinalandira gawo lolalikiramo limene linakuta pafupifupi makilomita 100,000 mbali zonse zinayi. Malo athu oyambira anali pa tauni yaing’ono ya Wiluna, pafupifupi makilomita 950 kumpoto koma chakummaŵa kwa tauni yathu ya Perth, likulu la Western Australia.

PAMENE tinali pa ulendo wopita kumeneko, Ellen ndi ine tinakhala ndi mlonda wa sitima waubwenzi m’ngolo ya sitima yomangiriridwa kumbuyo. Pamene sitimayo inaima pa siteshoni iliyonse m’mphepete mwa njanjiyo, mlondayo anatiuza mokoma mtima kuti tikaimapo kwa utali wotani. Zimenezi zinatipatsa mwaŵi wa kutsika ndi kukalalikira kwa anthu okhala m’midzi yakutali ya m’mbali mwa njanji imeneyo. Pomalizira pake tinafika pa tauni ya mgodi ya Wiluna mkati mwa mkuntho wa fumbi.

Komabe, siteshoni ya sitima ya pa Wiluna inali pa mtunda wa pafupifupi makilomita atatu kuchokera m’tauniyo. Palibe aliyense wa ife amene anali wanyonga, ndipo tinali ndi makatoni a mabuku atatu olemera ndi masutukesi aŵiri. Kodi tikanachitanji? Tinalenjeka katoni pa ndodo, ndi kugwirizana ndodoyo. Mwa njira imeneyi tinanyamula makatoniwo imodzi imodzi. Tinayenda maulendo asanu ndi aŵiri kuti tipititse makatoni atatu ndi masutukesi athu kutauni ya pamtunda wa makilomita atatuyo. Tinkapuma mobwerezabwereza chifukwa chakuti manja athu anali kupweteka kwambiri.

Mosasamala kanthu za fumbilo, manja opwetekawo, ndi miyendo yotopa, tinasangalala ndi ntchito yosangalatsayo ndi zokumana nazo zake. Tonse tinaona kuti Yehova anali nafe, kuti anali kutichirikiza kuchita ndi chiyambi chopereka chiyeso chimenechi cha kulalikira kumalo akutali. Posakhalitsa tinaonanso dalitso lake pa ntchito yathu, popeza kuti chotulukapo cha zoyesayesa zathu za ulendo umenewo chinali chakuti Bob Horn wachichepereyo analandira chowonadi cha Baibulo. Tinakondwera kuti Bob anakhala kwa zaka zingapo muutumiki wa pa Beteli ndi kuti anapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka pafupifupi 50 kufikira pa imfa yake mu 1982.

Kuchokera ku Wiluna tinalalikira m’midzi ina tili pa ulendo wathu wa makilomita oposa 725 kupita ku Geraldton ku gombe. Kuchokera kumeneko tinabwerera ku Perth. Masiku ena tinagona m’nyumba zodikirira sitima zopanda kanthu ndipo kamodzi tinagona pa mulu wa zakudya za ziŵeto m’mphepete mwa njanji.

Tinanyamula thumba loikamo mtsamiro lodzaza ndi mabisiketi atirigu. Mabisiketiwa anali chakudya chathu chachikulu cha mbali yoyamba ya ulendo wathu. Panthaŵi zina tinkapeza chakudya chathu mwa kutsuka mbale ndi kusesa m’nyumba zogona anthu ndi zodyera. Panthaŵi zina tinkagwira ntchito yothyola kabaifa ndi nyemba dzuŵa likuswa mtengo. Zopereka zochokera kwa okondwerera amene analandira mabuku ofotokoza Baibulo zinathandizira kulipirira zowonongedwa zathu.

Chimene chinandilimbikitsa kupitirizabe kukhulupirira Yehova ndi kuchita mwachimwemwe ndi mikhalidwe yovuta yambiri m’masiku amenewo chinali chitsanzo ndi kuphunzitsa koyambirira kumene ndinalandira kwa mayi wanga.

Choloŵa Chachikristu

Amayi wanga anakhulupirira mwamphamvu Mlengi, ndipo kwa utali womwe ndingakumbukire, anali kulankhula ndi anafe za iye. Komabe, chikhulupiriro chawo chinayesedwa kotheratu ndi imfa ya mchimwene wathu wazaka zisanu ndi ziŵiri m’ngozi yowopsa ya kusukulu. Koma mmalo mokwiyira Mulungu, amayi anayamba kuphunzira Baibulo mwakhama. Ngati kunali kotheka, anafuna kudziŵa chifukwa chake ngozi zowopsa zotero zimachitika. Kufufuza kwawo chowonadi cha Baibulo kunafupidwa, ndipo anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu wowona, Yehova, mwa ubatizo wa m’madzi kuchiyambi kwa ma 1920.

Kuyambira pamenepo kumka mtsogolo, makambitsirano awo ndi ife kaŵirikaŵiri anagogomezera mmene malonjezo a Mulungu analiri otsimikizirika. Iwo anali kutilimbikitsa nthaŵi zonse kukumbukira kuti mosasamala kanthu za zimene zingachitike, ‘Mulungu sanganame.’ (Tito 1:2) Monga chotulukapo chake, mng’ono wanga ndi ine ndi achimwene athu aŵiri, limodzi ndi mabanja athu ndi adzukulu, tili otamanda Yehova Mulungu. Ana aamuna aŵiri a mng’ono wanga, Alan ndi Paul Mason, akutumikira monga oyang’anira oyendayenda.

Chikhumbo Choyambirira cha Kulalikira

Sindinali kuchita bwino kusukulu choncho ndinaisiya mu 1926, pamene ndinali ndi zaka 13. Komabe, ndinali ndi chikhumbo champhamvu cha kuuza ena zimene ndinali kuphunzira ponena za Baibulo. Atate anaganiza kuti sindinali wophunzira mokwanira kuthandiza aliyense, koma Amayi anati: “Ngakhale ngati atangouza anthu za kuyandikira kwa nkhondo ya Armagedo ndi kuti ofatsa adzalandira dziko lapansi, zimenezo zidzalengeza Ufumu wa Mulungu.” Chotero ndinayamba kutenga mbali m’ntchito yolalikira kukhomo ndi khomo kuchiyambi kwa zaka zanga za 13 ndi 19, ngakhale kuti ndinali ndisanabatizidwe kufikira mu 1930. Mwamsanga pambuyo pake, ndinayamba ntchito yolalikira ya nthaŵi yonse m’dera la pafupi ndi Perth.

Chaka chotsatira, 1931, tinayamba kugwiritsira ntchito dzina lathu latsopano lakuti Mboni za Yehova. Komabe, eninyumba ambiri anatsutsa kugwiritsira ntchito kwathu dzina lopatulika la Mulungu limeneli ndipo anayankha mwaukali. Komabe ndinapitiriza utumikiwo mosasamala kanthu za zokumana nazo zosasangalatsazo. Ndinali ndi chidaliro chakuti Mulungu samanama pamene alonjeza kuti atumiki ake ‘angadalire pa nyonga imene amapereka.’​—1 Petro 4:11, NW; Afilipi 4:13.

Kuzindikira “Khamu Lalikulu”

Mu 1935, ndinalandira gawo la kumbali ina ya dziko lalikulu la Australia. Motero, kwa zaka zingapo pambuyo pake ndinatumikira monga mpainiya m’chigawo cha pafupi ndi New England m’boma la New South Wales, mtunda wa makilomita pafupifupi 4,000 kuchokera kwathu kwakale ku Perth.

Kufikira nthaŵi imeneyo, ndinali kudya zizindikiro za mkate wopanda chotupitsa ndi kumwa vinyo wofiira pa Chikumbutso cha chaka ndi chaka cha imfa ya Yesu. Ngakhale kuti zimenezi zinalingaliridwa kukhala zinthu zoyenera kuchitidwa, makamaka ndi atumiki achangu a nthaŵi yonse, sindinali wokhutiritsidwa konse kuti ndinali ndi chiyembekezo cha kumwamba. Ndiyeno, mu 1935, zinamveketsedwa bwino kwa ife kuti panali khamu lalikulu lomwe linali kusonkhanitsidwa lokhala ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi. Ambirife tinakondwera kuzindikira kuti tinali mbali ya khamu lalikulu limenelo, ndipo tinaleka kudya zizindikirozo. (Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:9) Chowonadi cha Baibulo chinali kuŵala mopita patsogolo, monga momwe Yehova analonjezera.​—Miyambo 4:18.

Njira Zatsopano za Kulalikira

Mkati mwa ma 1930, tinayamba kugwiritsira ntchito galamafoni muutumiki wathu. Motero, njinga zathu zolimbazo zinayenera kuikidwa makaliyala a kutsogolo ndi kumbuyo onyamulira magalamafoni olemerawo ndi malekodi limodzinso ndi zikwama zathu za mabuku. Ndinayenera kusamala kwambiri pamene njinga yanga inali ndi katundu wambiri chifukwa chakuti ngati itagwa, ndikanalephera kuidzutsa chifukwa cha kulemera!

Pafupifupi panthaŵi imeneyo tinayambanso imene tinaitcha mikupiti yopereka chidziŵitso. Pamene tinayenda m’makwalala aakulu a matauni, tinavala zikwangwani, zimene zinasonyeza mawu oonekera bwino. Ndinapeza ntchitoyi kukhala chiyeso chachikulu cha chikhulupiriro, makamaka pamene ndinagwidwa ndi kutsekeredwa usiku umodzi m’lumande m’tauni ya Lismore. Zinali zochititsa manyazi kutengeredwa ku khoti tsiku lotsatira popanda kuloledwa ngakhale kupesa tsitsi langa! Koma kachiŵirinso Yehova anandichirikiza monga momwe analonjezera. Mlanduwo unalekedwa chifukwa chakuti chinenezo chokha cha wapolisi amene anandigwirayo chinali chakuti chikwangwani changa chinali chonyoza chipembedzo chake.

Kubwerera Kumadzulo

Kuchiyambi kwa ma 1940, ntchito yanga yolalikira ya upainiya inanditengeranso ku matauni akutali a Western Australia. Kunoko ndinasangalala ndi zokumana nazo zosaiŵalika ndi madalitso auzimu. Pamene ndinali m’gawo langa la ku Northam, ndinakumana ndi mkazi wina wapanyumba wotanganitsidwa, Flo Timmins, pa mtunda wa pafupifupi makilomita 11 kunja kwa tauni. Iye analandira buku la Reconciliation, ndipo posakhalitsa anakhala Mboni yodzipatulira ya Yehova Mulungu. Iye adakali wokangalika muutumiki wa Ufumu, ndipo mwana wake wamkazi, amene panthaŵiyo anali ndi zaka zinayi zokha, anakula kukhala mpainiya wapadera.

Koma kunali zokumana nazo zina zosaiŵalika. Panthaŵi ina, ine ndi mnzanga tinali kuwoloka ulalo mu Northam tili m’ngolo yathu yokokedwa ndi kavalo, pamene mwadzidzidzi kavaloyo anayamba kuthamanga kwambiri, akumatichititsa kuwoloka mwamantha madzi othamanga a mtsinje wa Avon. Patapita pafupifupi mtunda woposa kilomita imodzi, kavaloyo anayamba kuyenda pang’onopang’ono.

Ukwati ndi Banja

Mu 1950, ndinakwatiwa ndi Arthur Willis, amene analinso mpainiya kwa zaka zambiri. Tinakhazikika m’tauni yakutali ya Pingelly ya ku Western Australia, kumene tinadalitsidwa ndi mwana wamwamuna, Bentley, ndi mwana wamkazi, Eunice. Pamene anawo anali pafupi kumaliza sukulu, Arthur analingalira zolembetsanso monga mpainiya. Chitsanzo chabwino cha atate awo chinalimbikitsa ana athu aŵiriwo kuyamba upainiya wokhazikika mwamsanga pamene anayenerera.

Kaŵirikaŵiri Arthur anali kupita ndi anawo kumadera akumidzi yakutali kukalalikira. Nthaŵi zina, anali kukhala nawo kumeneko kwa mlungu umodzi kapena kuposapo, akumagona mumsasa usiku uliwonse. Panthaŵi zimene iwo kunalibe, ndinatsala kunyumba kusamalira bizinesi ya banjalo yopanga zinthu za matabwa, kukumatheketsa onse atatu kuchita upainiya.

Kuchita Utumiki Pakati pa Aaborijini

Mmaŵa wina banjalo litangobwerera kuchokera ku umodzi wa maulendo awo a kumidzi, tinalandira mlendo wosayembekezeredwa. Munthuyo anali wa fuko la Aaborijini, amene anafunsa kuti: “Kodi ndingachitenji kuti ndibwerere?” Poyamba tinadabwa. Ndiyeno Arthur anamzindikira kukhala mwamuna amene zaka zambiri kalelo anachotsedwa mumpingo Wachikristu chifukwa cha uchidakwa. Kuyambira panthaŵiyo anapanga mbiri yoipa ya kumwa mopambanitsa ndi kukongola zinthu.

Arthur anafotokoza zimene anafunikira kuchita kuti abwezeretsedwe m’gulu loyera la Yehova. Anachoka mwakachetechete popanda kunena zambiri, ndipo tonse tinadabwa kuti akachitanji. Palibe aliyense wa ife amene anayembekezera zimene zinachitika m’miyezi yotsatira yoŵerengeka. Masinthidwe amene munthuyo anapanga anali osakhulupiririka konse! Iye sanali kuchira ku vuto lake lakumwa lokha koma anayendera anthu a m’chigawocho, kuwakumbutsa za ngongole zake, ndiyeno anabweza ngongolezo! Lerolino alinso mbale m’chikhulupiriro, ndipo anatumikira kwa kanthaŵi monga mpainiya.

Munali anthu ambiri a fuko la Aaborijini m’Pingelly, ndipo tinakondwera ndi utumiki wokhutiritsa kwambiri, kuthandiza anthu odzichepetsa ameneŵa kuphunzira ndi kulandira chowonadi cha Mawu a Mulungu. Kwakhala kolimbitsa chikhulupiriro chotani nanga kwa ine kukhala ndi phande kuthandiza anthu ambiri a fuko la Aaborijini a ku Australia kuphunzira chowonadi!

Mpingo unayambidwa mu Pingelly, ndipo poyambapo, ziŵalo zake zambiri zinali za fuko la Aaborijini. Tinayenera kuphunzitsa ambiri a iwo kuŵerenga ndi kulemba. M’zaka zoyambirira zimenezo panali chidani kulinga kwa fuko limenelo, koma mwapang’onopang’ono anthu a m’tauniyo anayamba kulemekeza Mboni za fuko la Aaborijini chifukwa cha kakhalidwe kawo koyera ndi chifukwa chokhala nzika zodalirika.

Chithandizo Chosalephera cha Yehova

Mwamuna wanga wokondedwa, Arthur, amene anatumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka 57, anamwalira kuchiyambi kwa 1986. Iye anali kulemekezedwa kwambiri ndi anthu abizinesi onse mu Pingelly ndi anthu a m’chigawocho. Kachiŵirinso, Yehova anandichirikiza, akumandipatsa nyonga yofunikira kupirira kutayikiridwa kwa mwadzidzidzi kumeneku.

Mwana wanga wamwamuna, Bentley, akutumikira monga mkulu kumpoto kwa Western Australia, kumene iye ndi mkazi wake, Lorna, alerera banja lawo m’chowonadi. Magwero ena a chikondwerero chachikulu kwa ine ndi akuti mwana wanga wamkazi, Eunice, wapitiriza utumiki wanthaŵi yonse kufikira lerolino. Iye ndi mwamuna wake, Jeff, akutumikira monga apainiya. Tsopano ndikukhala ndi iwo ndipo ndadalitsidwa kukhala wokhoza kuchita upainiya wothandiza pa maziko okhazikika.

Kwa zaka zoposa 60, ndaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo lachikondi la Yehova la kulimbikitsa atumiki ake ndi kuwathandiza kuchita ndi mikhalidwe iliyonse yomwe angayang’anizane nayo. Iye amapereka chosoŵa chathu chilichonse ngati sitimkayikira konse kapena ngati sitilephera kusonyeza chiyamikiro. Chikhulupiriro changa chalimbitsidwa popeza ndaona dzanja la Mulungu likugwira ntchito, ndipo ndaona mmene amaperekera dalitso lake ngakhale kuposa mmene timalingalirira. (Malaki 3:10) Zowonadi, Mulungu sanganame!

[Chithunzi patsamba 27]

Mary mu 1933

[Zithunzi patsamba 29]

Mary ndi Arthur zaka zaposachedwapa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena