Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 9/15 tsamba 30-31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Mungachite Ngati Muli Ndi Ngongole
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Ngongole! Kuloŵamo Kutulukamo
    Galamukani!—1990
  • Kodi Baibulo Lingathandize pa Nkhani ya Mavuto Azachuma Ndiponso Ngongole?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Kuloŵa m’Ngongole Kumathandiza?
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 9/15 tsamba 30-31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

M’nthaŵi za mavuto achuma zino, anthu ndi makampani owonjezerekawonjezereka akutembenukira ku lamulo la olephera kubweza ngongole. Kodi kuli koyenera mwa Malemba kwa Mkristu kulembetsa lamulo la olephera kubweza ngongole?

Yankho la funso limeneli limapereka chitsanzo chabwino cha mmene Mawu a Mulungu amaperekera chitsogozo chothandiza pankhani zimene zingakhale zamakono kwambiri. Maiko ambiri ali ndi malamulo a olephera kubweza ngongole. Malamulowo amasiyana m’maiko osiyanasiyana, ndipo sikuli kwa mpingo Wachikristu kupereka chilangizo cha lamulo pa zimenezi. Koma tiyeni tione lingaliro lachisawawa la kakonzedwe ka lamulo la olephera kubweza ngongole.

Chimodzi cha zifukwa zimene maboma amalolera anthu ndi makampani kulembetsa lamulo la olephera kubweza ngongole ndi chakuti ilo limapatsa okongoletsa ndalama kapena opatsa ngongole (okongoza) mlingo wa chitetezo kwa anthu kapena makampani amene amakongola ndalama kapena okhala ndi ngongole (angongole) koma osalipira zimene akongola. Kwa okongoza njira yokha yotembenukirako ingaoneke kukhala ya kupempha khoti kuchititsa wangongoleyo kulembetsa lamulo la olephera kubweza ngongole kotero kuti katundu wa wangongoleyo agaŵidwe monga gawo la malipiro a ngongoleyo.

Njira ina imene lamulo la olephera kubweza ngongole imagwirira ntchito ndiyo ya kukhala monga chitetezo kwa angongole amene moona mtima alephera kukhutiritsa owakongoza. Wangongoleyo angaloledwe kulembetsa lamulo la olephera kubweza ngongole, motero omukongoza angatenge wina wa katundu wake. Chikhalirechobe, lamulo lingamulole kukhalabe ndi nyumba yake kapena katundu wina wochepa ndi kupitirizabe ndi moyo popanda chiwopsezo chopitirizabe cha kutayikidwa kapena kulandidwa zinthu ndi omukongoza akale.

Pamenepo, nkwachionekere kuti malamulo ameneŵa ali ndi cholinga chopereka mlingo winawake wa chitetezo ponse paŵiri m’mapangano a ndalama ndi a malonda. Komabe, tiyeni tione uphungu wothandiza umene Baibulo limapereka.

Kukakhala kovuta kwa munthu kuŵerenga Baibulo kuchokera kuchikuto mpaka kuchikuto popanda kuona kuti ilo silimalimbikitsa kuloŵa m’ngongole. Timapeza machenjezo oterowo monga ngati Miyambo 22:7: “Wolemera alamulira osauka; ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.”

Kumbukiraninso fanizo la Yesu pa Mateyu 18:23-34 lonena za kapolo yemwe anali ndi ngongole yaikulu kwambiri. “Mbuye wake analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana ake omwe, ndi zonse ali nazo,” komano mbuyeyo, mfumu, anakhululuka ndi kusonyeza chifundo. Pamene kapoloyo pambuyo pake anasonyeza kupanda chifundo, mfumuyo inalamula kuti iye ‘aperekedwe kwa azunzi, kufikira akabwezere mangawa onse.’ Mwachionekere, njira yabwino koposa, njira yovomerezeka, ndiyo kupeŵa kukongola ndalama.

Atumiki a Mulungu mu Israyeli wakale anali ndi zochita za malonda, ndipo nthaŵi zina panali kukongola ndi kukongoletsa. Kodi Yehova anawalangiza kuchitanji? Ngati munthu anafuna kukongola ndalama kuti ayambire malonda kapena kuwakulitsa, kunali kololeka ndi lamulo ndi kwabwino kwa Mhebri kulipiritsa chiwongola dzanja. Komabe, Mulungu analangiza anthu ake kukhala opanda dyera pokongoletsa Mwisrayeli wosoŵa; iwo sanafunikire kupezera phindu pa mkhalidwe woipa mwa kulipiritsa chiwongola dzanja. (Eksodo 22:25) Deuteronomo 15:7, 8 amati: “Akakhala ndi inu munthu waumphawi, ndiye wina wa abale anu, . . . muzimtansira dzanja lanu ndithu ndi kumkongoletsa ndithu zofikira kusoŵa kwake, monga umo amasoŵa.”

Kukoma mtima kofananako kapena kulingalirana kunasonyezedwa m’malamulo olangiza kuti okongoza sanayenera kulanda zofunika zazikulu za moyo kwa wokongola, zonga ngati mphero ya banja kapena chovala chofunikira kufunditsa munthu usiku.​—Deuteronomo 24:6, 10-13; Ezekieli 18:5-9.

Zoonadi, si Ayuda onse omwe analandira ndi kugwiritsira ntchito mzimu wa malamulo achikondi amenewa ochokera kwa Woweruza wawo wamkulu ndi Wopereka Lamulo. (Yesaya 33:22) Ayuda ena aumbombo anachitira abale awo mwankhanza. Lerolinonso, okongoza ena angakhale ankhanza ndi osalingalira ena pofuna ngongole zawo, ngakhale kwa Mkristu wokhulupirika yemwe panthaŵiyo angakhale wosakhoza kulipira chifukwa cha chomgwera china chadzidzidzi. (Mlaliki 9:11) Chifukwa cha kuumirira kwawo pofuna ngongole zawo, okongoza akudziko angakakamize wokongola woteroyo kuloŵa mumkhalidwe umene angaone kukhala wowatetezera. Motani? Nthaŵi zina chinthu chokha chimene okongoza amalemekeza ndicho lamulo la olephera kubweza ngongole. Chotero Mkristu, yemwe sanali waumbombo kapena wosanyalanyaza ngongole zake, angatembenukire ku lamulo la olephera kubweza ngongole.

Komabe, tifunikira kudziŵa za mbali ina ya nkhaniyi. Mkristu angaloŵe m’ngongole chabe chifukwa chakuti sanagwiritsire ntchito kudziletsa pa chinthu kapena ndalama pa zimene anawononga kapena chifukwa chakuti iye sanalingalire molama popanga zosankha zake za malonda. Kodi iye ayenera kukhala wosadera nkhaŵa za ngongole yakeyo ndi kufulumira kupeza pothaŵira m’lamulo la olephera kubweza ngongole, motero akumapweteka ena chifukwa cha kusalingalira bwino kwake? Baibulo silimavomereza kusasamala kwa zandalama koteroko. Ilo limalimbikitsa mtumiki wa Mulungu kulola inde wake kukhaladi inde. (Mateyu 5:37) Kumbukiraninso mawu a Yesu onena za kuŵerengera mtengo munthu asanayambe kumanga nsanja. (Luka 14:28-30) Mogwirizana ndi zimenezo, Mkristu ayenera kulingalira bwino lomwe zotulukapo zosafunika zothekera asanatenge ngongole ya ndalama. Atatenga ngongole, ayenera kukumbukira thayo lake la kubwezera anthu kapena makampani omkongoletsa ndalamawo. Ngati ena ambiri aona Mkristu kukhala wosadalirika kapena wosakhulupirika, iye angawononge mbiri yabwino imene anamenyera nkhondo kuipeza ndipo samakhalanso ndi umboni wabwino kwa akunja.​—1 Timoteo 3:2, 7.

Kumbukirani zimene Salmo 15:4 limatiuza ponena za mtundu wa munthu amene Yehova amalandira. Timaŵerenga kuti: “Atalumbira [munthu woyanjidwa ndi Mulungu] kwa tsoka lake, sasintha ayi.” Inde, Mulungu amafuna Akristu kuchitira owakongoza awo monga momwe iwo angafunire kuchitiridwa.​—Mateyu 7:12.

Motero, kunena mwachidule, Baibulo silimatsutsa kuthekera kwakuti, mumkhalidwe wovuta kwambiri, Mkristu angagwiritsire ntchito chitetezero choperekedwa ndi Kaisara cha malamulo a olephera kubweza ngongole. Komabe, Akristu ayenera kukhala apadera ponena za kuona mtima ndi kudalirika. Chotero, iwo afunikira kukhala achitsanzo chabwino m’kukhala ndi chikhumbo choona mtima cha kulipira ngongole zawo za ndalama.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena