Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi tinganene kuti atumiki a Mulungu lerolino amene ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi ali ndi mzimu wa Mulungu wolingana ndi uja umene Akristu odzozedwa ndi mzimu ali nawo?
Funso limeneli si latsopano ayi. Nkhani imodzimodziyi inafotokozedwa mu “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda ya September 1952. Ambiri akhala Mboni kuyambira nthaŵiyo, chotero tingapendenso funsoli ndipo mwakutero kubwereza zimene nkhani yoyamba ija inanena.
Kwenikweni, yankho nlakuti, inde, abale ndi alongo okhulupirika a gulu la nkhosa zina angalandire mzimu woyera wa Mulungu wolingana ndi umene amalandira odzozedwa.—Yohane 10:16.
Ndithudi, zimenezi sizikutanthauza kuti mzimuwo umagwira ntchito mofanana pa anthu onse. Kumbukirani atumiki okhulupirika amene anakhalako Chikristu chisanakhaleko, amene analandiradi mzimu wa Mulungu. Ndi mphamvu ya mzimuwo, ena a iwo anapha zilombo zolusa, anachiritsa odwala, ngakhale kuukitsa akufa. Ndipo anafunikira mzimu kuti alembe mabuku a Baibulo. (Oweruza 13:24, 25; 14:5, 6; 1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:17-37; 5:1-14) Nsanja ya Olonda inati: “Ngakhale sa[na]li a gulu la odzozedwa, iwo anadzazidwa ndi mzimu woyera.”
Kumbali ina, lingalirani za amuna ndi akazi m’zaka za zana loyamba amene anadzozedwa ndi mzimu woyera, kukhala ana auzimu a Mulungu okhala ndi chiyembekezo chakumwamba. Onse anadzozedwa, koma zimenezi sizikutanthauza kuti zitachitika zimenezo mzimuwo unagwira ntchito mofanana pa onsewo. Zimenezo zikusonyezedwa bwino ndi 1 Akorinto chaputala 12. Mmenemo mtumwi Paulo anafotokoza mphatso za mzimu. M’mavesi 8, 9, ndi 11 timaŵerenga kuti: ‘Kwa mmodzi kwapatsidwa mwa mzimu mawu a nzeru; koma kwa mnzake mawu a chidziŵitso, monga mwa mzimu womwewo: kwa wina chikhulupiriro, mwa mzimu womwewo; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa mzimu umodziwo. . . . Koma zonse izi uchita mzimu umodzi womwewo, nugaŵira yense payekha monga ufuna.’
Kwenikweni, si odzozedwa onse amene anali ndi mphatso zozizwitsa za mzimu kalelo. Mu 1 Akorinto chaputala 14, Paulo anatchula msonkhano wa mpingo pamene wina anali ndi mphatso ya malilime, koma panalibe amene anali ndi mphatso ya kumasulira. Chikhalirechobe, poyamba, aliyense wa iwo anadzozedwa ndi mzimu. Kodi kungakhale koyenera kunena kuti mbale amene anali ndi mphatso ya malilime anali ndi mzimu wochuluka kuposa ena omwe analipo? Iyayi. Odzozedwa enawo sanali osoŵa, monga ngati osakhozanso kumvetsa Baibulo monga iye kapena osakhoza kulimbana ndi ziyeso. Mzimu unagwira ntchito mwapadera pa mbale amene akanatha kulankhula malilime. Ngakhale zili choncho, iyeyo ndi iwo anafunikira kuyandikira kwa Yehova ndi ‘kudzala nawo mzimu,’ malinga ndi zimene Paulo analemba.—Aefeso 5:18.
Ponena za aja otsalira lerolino, iwo alandiradi mzimu wa Mulungu. Panthaŵi ina unagwira ntchito pa iwo mwapadera—nthaŵi imene anadzozedwa ndi kukhala ana auzimu. Pambuyo pake ‘amadzalabe nawo mzimu,’ ukumawathandiza pamene afuna kumvetsetsa Baibulo bwino kwambiri, kutsogolera pa ntchito yolalikira, kapena polimbana ndi ziyeso—za munthu mwini kapena za gulu.
A “nkhosa zina,” ngakhale kuti sanadzozedwe, amalandira mzimu woyera m’mbali zina. Nsanja ya Olonda ya September 1952 inati:
‘“Nkhosa zina” lerolino zichita ntchito yofanana yakulalikira monga umo amachita otsalira, pansi pa mikhalidwe yofanana yovuta, ndi kusonyeza kukhulupirika, ndi umphumphu wofanana. Zimadyera pa gome lofanana la uzimu, zilikudya chakudya chofanana, zilikulandira zoona zofanana. Pokhala za gulu lolandira dziko lapansi, ndi ziyembekezero za padziko lapansi ndi kukondwera kwambiri mu zinthu za dziko lapansi, izo zingadzikondweretse koposa . . . m’malemba onena za mikhalidwe ya m’dziko lapansi latsopano; pamene otsalira odzozedwa, ndi ziyembekezero zakumwamba ndi kukondwera kwakukulu iwo eni mu zinthu za uzimu, angaphunzire ndi changu choposa zinthu zimenezo m’Mawu a Mulungu. . . . Komabe chenicheni chitsalira chakuti zoona zomwezo ndi kuzindikira kofanana zili zothekera kwa magulu onse aŵiriwo, ndipo kuli kokha mmene anthu osiyanasiyana amadziperekera iwo eni m’kuphunzira kumene kumatsimikizira kuzindikira za zinthu zakumwamba ndi zadziko lapansi kumene iwo akulandira. Mzimu wa Ambuye uli pafupi m’muyezo wofanana kwa magulu aŵiriwo, ndipo chidziŵitso ndi kuzindikira zaperekedwa mofanana kwa onse aŵiriwo, ndi mwaŵi wofanana wakuulandira uwo.’