Kuumirira Mwambo Kufalikira
KUUMIRIRA MWAMBO—zaka makumi angapo zapita, kagulu kochirikiza zimenezi kanali kochepa m’matchalitchi a Chiprotesitanti. Koma zinthu zasintha bwanji! Bruce B. Lawrence, wothirira ndemanga zachipembedzo, analemba kuti zaka 30 zapitazo, ndi oŵerengeka okha omwe akanadziŵa kuti pamapeto pa zaka za zana la 20, nkhani ya fundamentalisma (kuumirira mwambo) idzakhala yofunika ngakhalenso yovutitsa mopambanitsa kwa ofalitsa nkhani ndi ofufuza a pamayunivesite.
Komatu zimenezo ndizo zachitika. Malipoti a m’nyuzipepala a zionetsero zachiwawa m’makwalala, mbanda, magulu otsutsa kuchotsa mimba, magulu achipembedzo osonkhezera kayendetsedwe ka ndale, ndi kutentha poyera mabuku oyesedwa amwano, nthaŵi zonse amakumbutsa ntchito za oumirira mwambo. Magazini ya zachuma yachitaliyana ya mlungu ndi mlungu Mondo Economico inatero kuti zichita ngati kuti kulikonse oumirira mwambo “akutsutsa m’dzina la Mulungu.”
Nthaŵi zambiri oumirira mwambo amasonyezedwa kuti ali omkitsa ndi oyaluka, ochita ziŵembu ndi uchigaŵenga. Anthu akuchita mantha chifukwa cha kukula kwa magulu onga Comunione e Liberazione m’Chiroma Katolika, Gush Emunim m’Chiyuda, ndi Mgwirizano wa Akristu m’Chiprotesitanti cha ku North America. Nchifukwa ninji kuumirira mwambo kukufalikira? Kodi nchiyani chikukusonkhezera? Kodi mwina ndiko “chilango cha Mulungu,” malinga ndi zonena za Mfalansa wina, katswiri wa kakhalidwe ka anthu, Gilles Kepel?
[Mawu a M’munsi]
a Fundamentalist (munthu woumirira mwambo) ndiye uja amene amatsata mwaliuma njira zamwambo za chipembedzo. Tanthauzo lake la “kuumirira mwambo” lidzafotokozedwa bwino kwambiri m’nkhani yotsatira.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Nina Berman/Sipa Press