Mulungu Ndiye Pothaŵira Panga ndi Mphamvu Yanga
YOSIMBIDWA NDI CHARLOTTE MÜLLER
“Unayeneradi kukhala zaka zisanu ndi zinayi m’manja mwa Hitler,” anatero woweruza wa Komyunizimu. “Unalimbadi kutsutsa nkhondo, koma tsopano ukutsutsa mtendere wathu!”
IYE ANALI kunena za nthaŵi yomwe ndinali m’ndende ya Anazi ndi a Sosholizimu mu German Democratic Republic. Poyamba ndinasoŵa chonena, kenako ndinayankha: “Mkristu samamenyera nkhondo mtendere weniweni m’njira imene anthu ena amachitira. Ndimangoyesa kutsatira lamulo la m’Baibulo la kukonda Mulungu ndi mnansi wanga. Mawu a Mulungu amandithandiza kusunga mtendere m’mawu ndi m’zochita.”
Tsiku lomwelo, pa September 4, 1951, a Komyunizimu anandimanga zaka zisanu ndi zitatu m’ndende—kungopereŵera chaka chimodzi pazaka zimene boma la Nazi linandimanga.
Pamene ife Mboni za Yehova tinkazunzidwa ndi a Sosholizimu ndi a Komyunizimu, ndinapeza chitonthozo m’lemba la Salmo 46:1: “Mulungu ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso.” Yehova yekhayo anandipatsa mphamvu yakupirira nayo, ndipo pamene ndinasamala kwambiri Mawu ake, ndinakhalanso wolimba kwambiri.
Kulimbitsidwa Kaamba ka Mtsogolo
Ndinabadwa mu 1912 ku Gotha-Siebleben mu Thuringia, Germany. Ngakhale kuti makolo anga anali Aprotesitanti, bambo anali kufunafuna choonadi cha m’Baibulo ndi boma lolungama. Pamene makolo anga anaona kanema ya “Photo-Drama of Creation,” anachita chidwi.a Bambo anapeza chomwe ankafunafuna—Ufumu wa Mulungu.
Mayi ndi Bambo, limodzi ndi ife ana awo asanu ndi mmodzi, tinaleka tchalitchicho pa March 2, 1923. Tinali kukhala ku Chemnitz mu Saxony, ndipo kumeneko tinagwirizana ndi Ophunzira Baibulo. (Abale anga aŵiri ndi mlongo wanga mmodzi anakhala Mboni za Yehova.)
Pamisonkhano ya Ophunzira Baibulo, Malemba ndi choonadi cha mtengo wapatali zinandikhudza kwenikweni, ndipo zinandipatsa chimwemwe chachikulu pausinkhu wanga waung’ono. Choyamba panali malangizo omwe Akristu achinyamatafe oposa 50, tinawalandira pa Sande, ndipo ine ndi mbale wanga Käthe tinawalandira kwa kanthaŵi. Kagulu kathu kanaphatikizapo Konrad Franke, yemwe anakonza maulendo ndipo ankaimba nafe. Pambuyo pake, kuchokera mu 1955 mpaka 1969, Mbale Franke anali woyang’anira nthambi ya Watch Tower mu Germany.
Zaka za m’ma 1920 zinali zovuta, nthaŵi zina ngakhale kwa anthu a Mulungu. Ena, amene sanaonenso Nsanja ya Olonda kukhala “zakudya panthaŵi yake,” anatsutsa ntchito ya kunyumba ndi nyumba. (Mateyu 24:45) Zimenezi zinachititsa mpatuko. Koma ‘chakudya’ chimenecho ndicho chinatipatsa mphamvu imene inali yofunika kwambiri kwa ife panthaŵiyo. Mwachitsanzo, panali nkhani za mu Nsanja ya Olonda yakuti “Odala Ali Awo Opanda Mantha” (1919) ndi yakuti “Ndani Adzalemekeza Yehova?” (1926) Ndinafuna kulemekeza Yehova mwa kulimbika mtima pantchito, choncho ndinagaŵira timabuku ndi mabuku ambirimbiri a Mbale Rutherford.
M’March 1933, ndinabatizidwa ndi kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Chaka chomwecho, ntchito yathu yolalikira inaletsedwa mu Germany. Pa ubatizo, lemba la Chivumbulutso 2:10 linaŵerengedwa kupereka chilangizo cha zamtsogolo: “Usaope zimene uti udzamve kuŵaŵa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.” Ndinasinkhasinkha mozama pa vesi limeneli, ndikumadziŵa bwino lomwe kuti patsogolo panga pali mayesero oopsa. Izi zinachitikadi.
Pakuti sitinakhale ndi mbali iliyonse m’ndale, anansi athu ambiri anatikayikira. Pambuyo pa chisankho cha zandale, asilikali a Nazi anafuula kutsogolo kwa nyumba yathu, “Akapirikoni amakhala pano!” Nkhani yakuti “Musawaope,” imene inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya Chijeremani mu December 1933, inandilimbikitsa kwambiri. Ndinafuna kukhalabe Mboni yokhulupirika ya Yehova ngakhale m’mikhalidwe yovuta kwenikweni.
Kuponya m’Ndende—Njira ya Mdaniyo
Kunatheka kutulutsa Nsanja ya Olonda mwakabisira mu Chemnitz kufikira m’chirimwe cha 1935. Pambuyo pake makina osindikizira omwe ankagwiritsiridwa ntchito anawasamutsira ku Beierfeld kumapiri otchedwa Ore, kumene anawagwiritsira ntchito kusindikiza mabuku mpaka August 1936. Ine ndi Käthe tinagaŵira makopewo kwa abale omwe Bambo anatipatsa makeyala awo. Panthaŵiyo zonse zinayenda bwino. Komano a Gestapo anayamba kundiyang’anira, ndipo mu August 1936 anadzandigwira panyumba panga ndi kundisunga m’ndende, mmene ndinayembekeza tsiku lokamba mlandu.
Mu February 1937, abale 25 ndi alongo aŵiri—kuphatikizapo ine—tinakaonekera pamaso pa khoti lapadera mu Saxony. Mlandu unali wakuti gulu la Mboni za Yehova linali loukira boma. Abalewo omwe anasindikizanso Nsanja ya Olonda anawamanga zaka zitatu m’ndende. Ine anandimanga zaka ziŵiri.
M’malo moti andimasule nditamaliza chilango changa, a Gestapo anadzanditenga. Anati ndisaine kalata yonena kuti sindidzakhala Mboni ya Yehova. Ndinakana zolimba, moti ofesalayo anakwiya, nanyamuka mwaukali ndi kupereka chikalata chakuti andiikenso m’ndende. Chikalatacho ndi ichi chikuoneka pachithunzipa. Atakana kundilola kukaona makolo anga, nthaŵi yomweyo anandipereka ku msasa wachibalo waung’ono wa akazi ku Lichtenburg pafupi ndi mtsinje wa Elbe. Posapita nthaŵi ndinakumana ndi Käthe. Poyamba anali mu msasa wachibalo ku Moringen kuchokera mu December 1936, koma pamene msasawo anautseka, iye, limodzi ndi alongo ena ambiri, anabwera ku Lichtenburg. Bambo analinso m’ndende, ndipo sindinawaonenso mpaka 1945.
Ku Lichtenburg
Sanandilole kugwirizana ndi Mboni zina zazikazi nthaŵi yomweyo, pakuti zinali pachilango pachifukwa china. Ndinaona m’holo ina magulu aŵiri a akaidi—akazi amene nthaŵi zonse ankakhala pamathebulo ndi Mboni zomwe zinkakhala patimipando topanda choyedzamira tsiku lonse osadya kanthu.b
Ndinalandira ntchito iliyonse mosavuta, ndikumaganiza kuti tsiku lina ndikakumana ndi Käthe. Ndipo zinachitikadi zimenezo. Anali kupita kukagwira ntchito ndi akaidi ena aŵiri pamene tinakumana. Mwachisangalalo, ndinamkumbatira mwamphamvu. Komabe mlonda wachikazi anakatinenera nthaŵi yomweyo. Tinakafunsidwa mafunso, ndipo kuchokera nthaŵiyo sanalolenso kuti tikhale pamodzi. Zimenezo zinali zovuta kwambiri.
Palinso zochitika zina ziŵiri ku Lichtenburg zimene sindimaiŵala. Nthaŵi ina akaidi onse anayenera kusonkhana m’bwalo kuti amvetsere pawailesi mawu a Hitler pankhani zandale. Ife Mboni za Yehova tinakana, pakuti zinaphatikizapo miyambo yotamanda dzikolo. Basi pompo alondawo anatsegula mipope ya madzi paife, natithira madzi otuluka mwamphamvu ndi kutipitikitsa kuchokera pansanjika yachitatu mpaka pabwalo. Anatiimika chilili pamenepo, titanyoŵeratu thupi lonse.
Nthaŵi ina, ine ndi Gertrud Oehme ndi Gertel Bürlen, anatiuza kuika magetsi okometsera pamalikulu a asilikali, pamene tsiku la kubadwa la Hitler linali kuyandikira. Tinakana, pozindikira machenjera a Satana oyesa kutichititsa kutaya kukhulupirika kwathu mwa kugonja pazinthu zazing’ono. Aliyense wa ife alongo achitsikana anapatsidwa chilango chotsekeredwa milungu itatu m’kachipinda kamdima ka wekha. Koma Yehova anakhala pafupi nafe, ndipo ngakhale m’malo osautsa oterowo, anakhalabe pothaŵirapo pathu.
Mu Ravensbrück
M’May 1939 akaidi a ku Lichtenburg anasamutsidwira kumsasa wachibalo wa Ravensbrück. Kumeneko ndinapatsidwa ntchito m’chipinda chochapira, pamodzi ndi Mboni zina zazikazi. Nkhondo itaulika, tinayenera kunyamula mbendera ya swastika, koma tinakana. Chifukwa cha zimenezo, aŵirife, ine ndi Mielchen anatiika mumsasa wa asilikali. Chinali chimodzi cha zilango zoŵaŵa kopambana ndipo tinafunikira kugwira ntchito tsiku lililonse, ngakhale pa Sande, mulimonse mmene kwachera. Nthaŵi zonse chilango chachikulu chinali miyezi itatu, koma ife tinakhala mmenemo chaka chonse. Popanda chithandizo cha Yehova, sindikanapulumuka.
Mu 1942, zinthu zinapepukako kwa akaidi m’ndende, ndipo ndinapatsidwa ntchito yoyeretsa m’nyumba ya ofesala wa SS pafupi ndi kampuyo. Banjalo linandipatsako ufulu. Mwachitsanzo, tsiku lina pamene ndinali kuwongola miyendo ndi ana awo, ndinakumana ndi Josef Rehwald ndi Gottfried Mehlhorn, akaidi aŵiri okhala ndi zizindikiro zotchedwa purple triangle, omwe ndinakambitsirana nawo zolimbikitsana.c
Zaka Zovuta Pambuyo pa Nkhondo
Mu 1945 pamene asilikali a adani anafika pafupi, banja lomwe ndinali kugwirako ntchito linathaŵa, inenso ndinapita nawo. Pamodzi ndi mabanja ena a SS, anapanga mndandanda wautali wa magalimoto ndi kulinga kumadzulo.
Kutatsala masiku oŵerengeka kuti nkhondo ithe, kunali chipolowe ndi zoopsa. Pomaliza pake, tinakumana ndi asilikali achimereka omwe anandilola kulembetsa m’tauni yotsatira kuti ndinali munthu womasuka. Muganiza ndinakumana ndi yani kumeneko? Josef Rehwald ndi Gottfried Mehlhorn. Iwo anali atamva kuti Mboni zonse zomwe zinali mumsasa wachibalo ku Sachsenhausen zinafika ku Schwerin paulendo woŵaŵitsa wa ku imfa. Choncho atatufe tinanyamuka kupita ku tauni imeneyo, imene inali pamtunda wa makilomita ngati 75. Kunali chisangalalo chadzaoneni ku Schwerin pamene tinakumana ndi abale okhulupirika onsewo, opulumuka m’misasa yachibalo, kuphatikizapo Konrad Franke.
Pofika December 1945 mkhalidwe unali utakhalapo bwino moti ndinakhoza kuyenda pasitima. Choncho ndinatenga ulendo wopita kwathu! Komabe, ulendowo unaphatikizapo kugona padenga pa ngolo yasitima ndi kuimirira pakhomo. Titafika ku Chemnitz, ndinatsika pa siteshoni ndi kupita kumene banja lathu linkakhala. Koma pamsewu umene asilikali a Nazi anaimirirapo ndi kufuula kuti “Akapirikoni amakhala pano!” panalibe ngakhale nyumba imodzi yotsalapo. Mudzi wonsewo anauphulitsa kotheratu ndi mabomba. Komabe, mtima wanga unakhala pansi pamene ndinapeza kuti Mayi, Bambo, Käthe, ndi alongo ndi abale anga akali ndi moyo.
Mkhalidwe wa zachuma m’Germany pambuyo pa nkhondo unali woopsa. Komabe, mipingo ya anthu a Mulungu inayamba kuchuluka m’Germany yense. Watch Tower Society inachita zonse zotheka kutikonzekeretsa ntchito yolalikira. Ntchito yomwe anatseka Anazi pa Beteli ku Magdeburg inayambiranso. M’chilimwe cha 1946, anadiitana kukagwira ntchito kumeneko ndipo anandiika m’khichini.
Ntchito Iletsedwanso Ndipo Ndiloŵanso m’Ndende
Magdeburg ili m’chigawo cha Germany chimene chinali m’manja mwa a Komyunizimu. Iwo analetsa ntchito yathu pa August 31, 1950, natseka Beteli ya ku Magdeburg. Mpamene panathera ntchito yanga ya pa Beteli, ndipo ndinaphunzira zambiri. Ndinabwerera ku Chemnitz, ndili wotsimikiza mtima kuti ngakhale mu ulamuliro wa a Komyunizimu ndidzagwirabe zolimba choonadi ndi kulengeza za Ufumu wa Mulungu kuti ndiwo chiyembekezo chokha chenicheni kwa anthu ovutika.
Mu April 1951, ndinapita ndi mbale wina ku Berlin kukatenga makope a Nsanja ya Olonda. Titabwerako, tinadabwa kupeza kuti siteshoni ya sitima mu Chemnitz inali itazingidwa ndi atekitivi. Kunali koonekeratu kuti anali kufunafuna ife, ndipo anatigwira pompo.
Pofika ku ndende yoyembekezera mlandu, ndinali nditanyamula kalata yosonyeza kuti ndinali m’ndende ya Anazi zaka zambiri. Choncho alonda andende anachita nane mwaulemu. Mmodzi wa alonda aakulu wamkazi anati: “Inu Mboni za Yehova sindinu apandu; ndende si malo anu iyayi.”
Nthaŵi ina iye anabwera m’chipinda changa, mmene ndinali ndi alongo ena aŵiri, ndipo mwakabisira anaika kanthu kena munsi mwa bedi imodzi. Kodi kanthuko kanali chiyani? Baibulo lake, limene anatipatsa. Nthaŵi ina, anakafika kwa makolo anga, pakuti amakhala pafupi ndi ndendeyo. Anatenga makope a Nsanja ya Olonda ndi zakudya zina, nazibisa m’chovala chake, kenako anazizembetsera m’chipinda changa.
Palinso kanthu kena komwe ndimakonda kukakumbukira. Nthaŵi zina pa Sande mmaŵa, tinkaimba nyimbo zateokrase mofuula kwambiri moti akaidi ena anakondwera ndi kuwomba m’manja panyimbo iliyonse.
Mphamvu ndi Chithandizo Chochokera kwa Yehova
Pokamba mlanduwo m’khoti pa September 4, 1951, woweruza ananena mawu omwe ndatchulawo kuchiyambi kwa nkhani ino. Ndinaloŵera ndende ku Waldheim, kenako ku Halle, ndiyeno ku Hoheneck. Chochitika chimodzi chachidule kapena ziŵiri zidzasonyeza mmene Mulungu analili pothaŵira ndi mphamvu yathu ife Mboni za Yehova ndi mmene Mawu ake anatipatsira nyonga.
M’ndende ya ku Waldheim, alongo onse, Mboni, amasonkhana pamodzi nthaŵi zonse m’holo, moti tinakhoza kuchita misonkhano yachikristu. Sanatilole kuloŵa ndi pepala kapena pensulo, koma alongo ena analoŵa ndi tidutswa ta nsalu ndi kupanga nsalu yolembapo lemba la chaka cha 1953, limene linati: “Lambirani Yehova ndi malaya oyera.”—Salmo 29:2, American Standard Version.
Mlonda wina wamkazi anaona zimenezo ife osadziŵa nakatinenera nthaŵi yomweyo. Mkulu wa ndende anabwera nauza aŵiri a ife alongo kunyamula m’mwamba nsaluyo. “Kodi ndani anapanga ichi?” anafunsa. “Kodi nchiyani chimenechi?”
Mmodzi wa alongowo anafuna kudzipereka kuti atipulumutse, koma mwamsanga tinanong’onezana ndi kumvana kuti mlanduwo ugwere tonse. Choncho tinayankha kuti: “Tinachipanga kuti chilimbikitse chikhulupiriro chathu.” Analanda nsaluyo, ndipo anatilanga mwa kutimana chakudya. Koma panthaŵi yonse yokambirana nawo zimenezo, alongowo anali chinyamulire m’mwamba nsaluyo kuti tiloŵeze pamtima lemba lolimbikitsalo.
Pamene anatseka ndende ya akazi ku Waldheim, ife alongo anatisamutsira ku Halle. Kunoko anatilola kulandira zinthu, ndipo nchiyani chimene Bambo anabisa m’nsapato zimene ananditumizira? Nkhani za mu Nsanja ya Olonda! Ndikukumbukirabe mitu yake, wakuti “Chikondi Chenicheni Chili ndi Ntchito” ndi wakuti, “Mabodza Amatayitsa Moyo.” Nkhani zimenezi pamodzi ndi zina zinalidi chakudya chokoma, ndipo pamene tinapatsirana mwakabisira, aliyense analemba mfundo zake.
Tsiku lina pofufuza, mlonda wina anapeza pepala lolembapo mfundo zanga m’materesi a udzu. Pambuyo pake, anandiitana kuti andifunse naati anafuna kudziŵa kuti nkhani yakuti “Zimene Oopa Yehova Akuyembekezera mu 1955,” inatanthauzanji. Iye, pokhala wa Komyunizimu, anada nkhaŵa kwambiri ndi imfa ya mtsogoleri wake, Stalin, mu 1953, ndipo anali wopanda chiyembekezo. Kwa ife, tinali ndi chiyembekezo chakuti mikhalidwe m’ndendemo idzakhalako bwino, koma ndinali ndisanadziŵebe zimenezo. Ndi chidaliro ndinafotokoza kuti Mboni za Yehova zinali kuyembekezera zinthu zabwino kwambiri. Chifukwa ninji? Ndinagwira mawu lemba la mutu wa nkhaniyo, Salmo 112:7: “Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazikika, wokhulupirira Yehova.”
Yehova Akhalabe Pothaŵira Panga ndi Mphamvu Yanga
Chifukwa cha kudwala matenda oopsa, anandimasula kutatsala zaka ziŵiri, mu March 1957. Akuluakulu a boma a ku East Germany anandivutanso chifukwa cha utumiki wanga kwa Yehova. Choncho, pa May 6, 1957, ndinathaŵira ku West Berlin, kuchoka uko ndinapita ku West Germany.
Ndinadzachira bwino pambuyo pa zaka zambiri. Koma ndi lero lomwe ndidakali ndi njala yabwino ya chakudya chauzimu ndipo ndimayembekezera ndi chidwi kope lililonse latsopano la Nsanja ya Olonda. Nthaŵi ndi nthaŵi, ndimadzipenda ndekha. Kodi ndidakali ndi maganizo auzimu? Kodi ndakhala ndi mikhalidwe yabwino? Kodi chikhulupiriro changa choyesedwa chimadzetsa chitamando ndi ulemu kwa Yehova? Cholinga changa ndicho kukondweretsa Mulungu m’zinthu zonse, kuti akhalebe pothaŵira panga ndi mphamvu yanga kosatha.
[Mawu a M’munsi]
a Kanemayo ya “Photo-Drama” inali ya masilaidi ndi zithunzi zoyenda, ndipo kuyambira mu 1914, nthumwi za Watch Tower Bible and Tract Society zinaionetsa m’malo ambiri.
b Magazini yakuti Trost (Chitonthozo), yofalitsidwa ndi Watch Tower Society mu Bern, Switzerland, pa May 1, 1940, patsamba 10, inasimba kuti nthaŵi ina Mboni za Yehova zazikazi mu Lichtenburg sizinalandire chakudya chamasana masiku 14 chifukwa anakana kusonyeza chizindikiro chaulemu pamene nyimbo zotamanda Nazi zinali kuimbidwa. Mboni za Yehova pamenepo zinalipo 300.
c Nkhani ya Josef Rehwald inatuluka mu Galamukani! ya February 8, 1993, masamba 20-3.
[Chithunzi patsamba 26]
Ofesi ya SS ku Ravensbrück
[Mawu a Chithunzi]
Pamwambapo: Stiftung Brandenburgische Gedenkstätten
[Chithunzi patsamba 26]
Chiphaso changa chokagwira ntchito kunja kwa ndende