Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 7/15 tsamba 20-23
  • Pulumutsani Moyo wa Mwana Wanu!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pulumutsani Moyo wa Mwana Wanu!
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Khalani Mabwenzi Awo
  • Chikondi cha Mulungu
  • Kuopa Mulungu
  • Mphotho Zopindulitsa
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 7/15 tsamba 20-23

Pulumutsani Moyo wa Mwana Wanu!

MICHAEL ndi Alphina amakhala ku chigwa cha kumidzi ku mapiri obiriŵira m’dera la KwaZulu-Natal ku South Africa. Anakumana ndi mavuto ambiri polera ana asanu ndi aŵiri. Ndi chithandizo cha mkazi wake, Michael anayesetsa kumvera lamulo la Baibulo kwa atate kuti: “Muwalere [iwo] m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Koma nthaŵi zina mavuto amabuka.

Mwachitsanzo, si zachilendo pakati pa abusa a m’Afirika kuphatikiza ng’ombe za makola osiyana nkumadyetsera pamodzi kuti akhale ndi nthaŵi yambiri yoseŵerera pamodzi. Nthaŵi zina amayamba makhalidwe oipa ndi kumanena zinthu zosayenera kukambitsirana. Pamene ana a Michael anapita kubusa kukadyetsera ng’ombe za banjalo, anawachenjeza mwamphamvu kuti asakaseŵere ndi ana ena ake. (Yakobo 4:4) Komabe, pobwera kuchokera ku ntchito, nthaŵi zina ankaŵapeza akuseŵera nawo. Motero, amawalanga.​—Miyambo 23:13, 14.

Kodi mukulingalira kuti Michael amawakhwimitsira malamulo ana akewo? Ena akhoza kuganiza choncho, koma Yesu Kristu ananena kuti “nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Michael ndi Alphina ankapangitsa panyumba pawo kukhala posangalatsa, amathera nthaŵi yochuluka ndi ana awo ndi kuwaphunzitsa nkhani za m’Baibulo ndi choonadi.

Michael ndi Alphina ali ndi ana aakazi anayi​—Thembekile, Siphiwe, Tholakele, ndi Thembekani. Onse ndi alaliki a nthaŵi zonse a uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Aŵiri mwa ana awo amuna akutumikira monga oyang’anira otsogoza m’mipingo ya Mboni za Yehova. Mwana wawo wachitatu, yemwenso mkazi wake ndi mlaliki wa nthaŵi zonse, akutumikira monga mtumiki wotumikira.

Makolo ambiri achikristu okhala ndi mabanja aakulu adalitsidwa mwakukhala ndi ana oleredwa bwino. Komabe, ana ena omwe amaphunzitsidwa bwino amasiya choonadi. Mosakayika, makolo awo amakumbuka fanizo la Yesu la mwana woloŵerera ndipo amayembekezera kuti mwana wawoyo adzalapa ndi kupeza chipulumutso.​—Luka 15:21-24.

Komabe, mwachisoni, makolo ena achikristu ana awo onse amapanduka nkuloŵerera mu zadziko. Makamaka izi zimachitika kaŵirikaŵiri m’mbali zina za Afirika kumene ana amaoneka kuti akuchita bwino kufikira paunyamata. Ndiye, kenaka paunyamatapo, amakopeka ndi makhalidwe oipa a dziko la Satana. (1 Yohane 5:19) Zotsatira zake, atate ambiri sakwaniritsa ziyeneretso kuti atumikire monga mkulu mumpingo. (1 Timoteo 3:1, 4, 5) Mwachionekere, tate wachikristu ayenera kuona chipulumutso cha a m’nyumba yake monga chinthu chofunika kwambiri. Tsopano nchiyani chimene makolo ayenera kuchita kuti apulumutse miyoyo ya ana awo?

Khalani Mabwenzi Awo

Yesu sanali chabe wangwiro komanso anali wapamwamba kwambiri kuposa munthu wina aliyense panzeru ndi kuzindikira zinthu. Komabe, amatenga ophunzira ake opanda ungwiro monga mabwenzi. (Yohane 15:15) Ndicho chifukwa chake amalakalaka kukhala naye ndipo amamva bwino akakhala naye. (Yohane 1:14, 16, 39-42; 21:7, 15-17) Makolo akhoza kuphunzirapo kanthu. Monga timbeu ting’onoting’ono tokhala ndi masamba otambasulidwa kudzuŵa kuti tipeze kufunda, ana amakula bwino pamene panyumba pali chikondi, ndi ubwenzi.

Makolo, kodi ana anu amachiona chosavuta kukuuzani mavuto awo onse? Kodi mumamvetsera? Musanaweruze, kodi mumawapangitsa kunena maganizo awo kuti mumvetsetse nkhaniyo? Kodi mumawathandiza moleza mtima kupeza mayankho a mafunso ena mwakufufuza pamodzi nawo m’zofalitsa za Baibulo?

Mayi wina ku South Africa anati: “Kuyambira tsiku lomwe anapita kusukulu koyamba, timamlimbikitsa mwana wathu nthaŵi zonse kunena zomwe wachita kusukuluko. Mwachitsanzo, ndimamfunsa kuti: ‘Umaseŵera ndi ndani pa buleki? Tandiuza aphunzitsi anu atsopano. Amaoneka bwanji? Kodi mlungu uno muchita zotani?’ Tsiku lina, mwana wathu anabwera kunyumba ndi kutiuza kuti mphunzitsi wachingelezi adzatenga kalasilo kukalionetsa kanema ndipo pambuyo pake adzalemba zomwe adzaonazo. Koma kanemayo inali yokayikitsa. Titafufuza, tinapeza kuti siinali yoyenera kwa Mkristu. Tinakambitsirana monga banja. Tsiku lotsatira mwana wathu anapita kwa mphunzitsiyo, ndi kumuuza kuti sakufuna kukaonerera nawo kanemayo, popeza zimene imaonetsa sizingagwirizane ndi chikhulupiriro chake chachikristu. Mphunzitsiyo analingalira bwino ndipo kenaka anathokoza mwana wathuyo, nanena kuti sanafune kutenga kalasi kukaona zinthu zomwe zikanachititsa mphunzitsiyo kumva chisoni.” Chisamaliro chachikondi chosalekeza cha makolo ameneŵa pa kutetezera mwana wawo chinabala zipatso zabwino. Iye tsopano ndi wosangalala, wa makhalidwe abwino, ndipo akutumikira monga wantchito wodzifunira pa ofesi ya nthambi ya Watch Tower Bible and Tract Society ku South Africa.

Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino cha mmene tiyenera kukhalira ndi ana a anthu ena. Ankasangalala kukhala nawo. (Marko 10:13-16) Makolo ayenera kusangalala chotani kuchita zinthu pamodzi ndi ana awo! M’madera ena a mu Afirika, tate amachita manyazi kupezeka akuseŵera mpira kapena maseŵera ena ndi ana ake. Koma tate wachikristu sayenera kudziona kukhala woopsa wosati nkuyenera kupezeka akuchita kenakake ndi ana ake. Achinyamata amafuna makolo amene amacheza nawo. Izi zimapangitsa kukhala kwapafupi kwa anawo kunena malingaliro awo. Ngati zimenezi zinyalanyazidwa, ana amataya mtima kapena kulunda, makamaka ngati mukuwadzudzula kaŵirikaŵiri.

Polembera Akolose za kakhalidwe kabanja, Paulo anati: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.” (Akolose 3:21) Izi zingasonyeze kuti pakhoza kukhala kupereka chilango monkitsa ndiponso kukonda popanda ubwenzi weniweni. Ana, kuphatikizapo achinyamata, amene amakondedwa ndi kuyamikiridwa kaŵirikaŵiri adzamvera msanga chiweruzo chofunika.

Chikondi cha Mulungu

Chinthu cha mtengo wapatali kwambiri chomwe makolo angapatse ana ndi chitsanzo chawo cha kusonyeza chikondi. Ana ayenera kuona ndi kumva makolo awo akunena ndi kusonyeza chikondi chawo kwa Mulungu. Wachinyamata wina amene amatumikira pa ofesi ya nthambi ya Watch Tower Bible and Tract Society ku South Africa anati: “Pamene ndinali kamnyamata, ndimathandiza atate ntchito za pakhomo. Ndimakonda kuŵathandiza chifukwa Atate amayamikira zochepa zomwe ndimachita. Amagwiritsira ntchito mpata umenewu kundiuza zochuluka za Yehova. Mwachitsanzo, ndikukumbukira Loŵeruka lina pamene tinali kalikiliki kukwapa udzu pakhomo. Kunatentha kwambiri. Atate anali kutuluka thukuta, motero ndinathamanga kukaŵatengera madzi m’matambula aŵiri ndi kuikamo ayezi. Atate anati: ‘Mwana wanga, kodi ukuona mmene Yehova alili wanzeru? Ayezi amayandama pamadzi. Akadamamira, zamoyo zonse pansi panyanja ndi maiŵe zikadafa. M’malo mwake, ayezi amakhala ngati bulangeti pamwamba pamadzi! Kodi izi sizitithandiza kudziŵa bwino Yehova?’a Pambuyo pake, pamene ndinali m’ndende chifukwa cha kusunga uchete kwanga, ndimapeza mpata wakumalingalira. Ndili wopsinjika maganizo m’ndendemo, usiku wina, ndinakumbukira mawu a Atatewa. Anali ndi tanthauzo bwanji! Ndidzalambira Yehova ku nthaŵi zonse ngati ndingathe kutero.”

Inde, ana amafunika kuona kukonda Mulungu kumene makolo ali nako pa zilizonse zimene makolowo achita. Kukonda Mulungu ndi kulakalaka kummvera ziyeneradi kuoneka monga chilimbikitso kuwonjezera pa kupezeka pa misonkhano yachikristu, kuchita utumiki wa m’munda, ndiponso kuŵerenga Baibulo ndi phunziro la banja. (1 Akorinto 13:3) Koma chofunika kwambiri, kukonda Mulungu kuyenera kuonekera m’pemphero la banja loperekedwa ndi mtima wonse. Palidi ubwino wakupatsa ana anu chinthu cha mtundu umenewu. Ndicho chifukwa chake Aisrayeli analamulidwa kuti: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse. Ndipo mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.”​—Deuteronomo 6:5-7; yerekezani ndi Mateyu 22:37-40.

Cholepheretsa chachikulu pa kukonda ndi kumvera Mulungu ndicho chibadwa chathu cha uchimo. (Aroma 5:12) Motero, Baibulo limalamulanso kuti: “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa” (Salmo 97:10) Malingaliro oipa nthaŵi zambiri amapangitsa kuchita zoipa. Kuti tipewe izi, mwana afunika kukulitsa khalidwe lina lofunika kwambiri.

Kuopa Mulungu

Chikondi chophatikizana ndi mantha akuopa kusakondweretsa Yehova ndi chinthu chosiririka kwambiri. Yesu Kristu iye mwini anationetsa ife chitsanzo changwiro chakukondwa ndi “mzimu wakudziŵa ndi wakuopa Yehova” (Yesaya 11:1-3) Mantha ameneŵa ndi ofunika kwambiri pamene wachinyamata ayamba kumva chilakolako cha kugonana. Kuopa Mulungu kungathandize wachinyamata kukana kusonkhezeredwa ndi dziko kuyamba makhalidwe achiwerewere. (Miyambo 8:13) M’madera ena, makolo amachita manyazi kuphunzitsa ana awo mmene angachitire akakumana ndi chiyeso cha zakugonana. Kunena zoona, ambiri amaona kuti nkulakwa kukamba zimenezi. Koma chakhala chotsatirapo nchiyani pamene makolo alekerera zinthu chonchi?

Akatswiri a zamakhwala atatu otchedwa Buga, Amoko, ndi Ncayiyana anafunsa atsikana 1,702 ndi anyamata 903 am’madera akumidzi ku Transkei, ku South Africa. Pa kufufuza kumeneku South African Medical Journal inanena kuti “76% ya atsikana ndi 90.1% ya anyamata anapezeka kuti anali atadziŵa kale zakugonana.” Avareji ya zaka za atsikanawo inali 15, ndipo ambiri anagonedwa mokakamiza. Oposa 250 anakhalapo ndi mimba kamodzi kapena kuposapo. Chotsatirapo china chinali chiŵerengero chachikulu cha okhala ndi matenda opatsirana mwakugonana.

Nzoonekeratu, kuti makolo ambiri sazindikira kufunika kwa kuphunzitsa ana momwe angapewere kugonana popanda ukwati. Mmalo mwake, nyuzipepalayo inapitiriza kunena kuti: “Kubala ana ndi kukhala nakubala kumaonedwa kolemekezetsa azimayi m’madera akumidzi ku Transkei, ndipo atsikana omwe angokula unamwali amadziŵa izi msanga.” Pali umboni wakuti m’madera ena adziko lapansi vuto limodzimodzili lilikonso.

Achinyamata ambiri mu Afirika akuimba makolo awo mlandu chifukwa chosawathandiza kumvetsetsa pa zakugonana. Makolo ena achikristu apeza kuti amachita manyazi kugwiritsira ntchito buku la Your Youth​—Getting the Best Out Of It.b Pa masamba 20-3, limanena za kugwiritsira ntchito moyenera ziŵalo zogonanirana ndi kusintha kwa thupi komwe kumachitika pa unyamata.

Makolo achikristu amene amatha kunena ndi ana awo mmene Mulungu amaonera zakugonana ayenera kuthokozedwa. Izi zimachitika bwino pang’onopang’ono, mogwirizana ndi momwe mwana angathere kumvetsetsa zinthu. Zimadalira pa usinkhu wa mwana, makolo anganene mosapsatira mawu ponena za ziŵalo ndi ntchito zake. Apo phuluzi, mwana wosamva zinthu msanga sangamvetse chimene mukunena.​—1 Akorinto 14:8, 9.

Tate wina wa ku South Africa wa ana aakazi aŵiri ndi mnyamata anati: “Nthaŵi zambiri, ndinali ndi mwaŵi wakunena zakugonana ngakhale ndi atsikanawa. Komabe, mkazi wanga, anasamalira kwambiri atsikana, akumagwiritsira ntchito buku la Your Youth​—Getting the Best Out Of It. [Onani masamba 26-31.] Pamene mnyamatayu anali ndi zaka 12, ndinayamba kumamtenga kupita kokayenda kutali kumapiri. Pa nthaŵi imeneyi, tinkakambitsirana za kusintha kwa thupi la mnyamata akamakula ndi mmene lidzagwirira ntchito mtsogolo muukwati. Ndinamuuzanso kufunika kwa kupewa chizoloŵezi choipa cha kuchita psotopsoto ndiponso kumakhala ndi atsikana mwaulemu​—monga momwe amachitira ndi amayi ndi alongo ake.”

Mphotho Zopindulitsa

Bambo ndi mayi ongotchulidwa kumenewa anachita mwakhama ndipo ngachimwemwe kuti ana atatuwo anakula bwino. Onse atatu ndi akuluakulu ndipo anakwatirana ndi Akristu okhulupirika. Mwana wamwamunayo ndiponso akamwini awo akutumikira monga akulu mumpingo wachikristu, ndipo aŵiri mwa mabanja ameneŵa akhala alaliki anthaŵi zonse kwa zaka zambiri.

Inde, makolo amene amachita mwakhama kuti banja lawo lipulumuke angayembekezere mphotho pa ana omwe amasankha kumvera chiphunzitso chotere cha Baibulo, poti Miyambo 23:24, 25 imati: “Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye. Atate wako ndi amako akondwere.” Lingalirani za banja lalikulu lotchulidwa pachiyambi pa nkhani ino. “Ndikaganiza mmene ana anga apitira patsogolo mwauzimu,” akutero Alphina, “mtima wanga umasangalala.” Ngati nkotheka makolo onse achikristu agwirirepo ntchito kuti apeze mphotho zosangalatsa zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

a Pamene madzi akufika poti nkuuma kusanduka ayezi, amapepuka nkuyandama pamwamba. Onani masamba 137-8 m’buku la Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Onaninso buku la Mafunso Achichepere Akufunsa Mayankho Amene Amathandiza, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 23]

Tate angasankhe malo abwino oti nkuuzirapo mwana nkhani zofunika pa moyo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena