Matchalitchi Avomereza Kulakwa
“Papa Aimba Mlandu Tchalitchi.” “Bwalo la Inquisition Ndiponso Kudana ndi Ayuda—Tchalitchi Chikukonzekera Zovomereza Kulakwa Kwake.” “Kuvomereza Kulakwa Pa Chipululutso cha Anazi.” “A Methodist Apepesa kwa Amwenye a ku Far West.”
KODI munaŵerengako mitu ya nkhani yonga imeneyi? Zikuonetsa kuti matchalitchi akuvomereza moŵirikiza kuposa kale kuti analakwa ndipo akupepesa chifukwa cha zimene akhala akuchita kwa zaka mazana ambiri. Ofalitsa nkhani akhala akulengeza mobwerezabwereza kuti papa wavomerezanso kulakwa kwinakwake.
Pamene Papa Apepesa
M’zaka za pakati pa 1980 ndi 1996, John Paul II ‘anazindikira za zolakwa zimene Tchalitchi chachita kapena anapepesa’ pafupifupi nthaŵi 94, akutero wothirira ndemanga wa ku Vatican Luigi Accattoli m’buku lake lakuti Quando il papa chiede perdono (Pamene Papa Apepesa). Malinga nkunena kwa Accattoli, “m’Tchalitchi cha Katolika, papa yekha ndiye ali woyenerera kuvomereza kulakwa.” Ndipo iye wachita zimenezi pankhani zambiri zoipitsa mbiri ya Katolika—Nkhondo za Mtanda, nkhondo, kuchirikiza ulamuliro wopondereza, magaŵano a m’matchalitchi, kudana ndi Ayuda, Mabwalo a Inquisition, Amafia, ndi kusankhana mafuko. M’chikalata chimene anatumiza mu 1994 kwa akadinala (chimene ena amachilingalira kukhala chikalata chofunika koposa m’nthaŵi ya papayu), John Paul II anapereka lingaliro lakuti “avomereze machimo onse ndi machimo ochitidwa m’zaka chikwi.”
Atsogoleri angapo achipembedzo anatsatira chitsanzo cha papa. M’December 1994 nyuzipepala ya ku Italy yotchedwa Il Giornale inalengeza kuti: “Abishopu ambiri a ku America anaonekera pawailesi yakanema ndipo anapepesa pamaso pa onse.” Chifukwa chiyani? Chifukwa cha kunyalanyaza vuto la ansembe ogona ana, limene lavulaza ana aang’ono ambiri. M’January 1995 nyuzipepala yotchedwa La Repubblica inalengeza za “nkhani yachilendo m’mbiri ya Chikatolika chamakono”—vuto la kusanenapo kanthu kwa Papa Pius XII pankhani ya Chipululutso cha Anazi linasamaliridwa. M’January 1995 nyuzipepala imodzimodziyo inalengeza kuti ofesi ya abishopu ku Germany inapepesa chifukwa cha “zolakwa zambiri” za Aroma Katolika amene anachirikiza upandu wa Anazi. Matchalitchi angapo achiprotestanti avomerezanso kulakwa kwawo.
Chifukwa Ninji?
Baibulo limatilimbikitsa kupepesa pamene talakwa, ndipo ambiri amayamikira kwambiri pamene matchalitchi avomereza kulakwa kwawo. (Yakobo 5:16) Koma kodi nchifukwa ninji matchalitchi akuchita zimenezi? Kodi zimenezi ziyenera kukhudza motani mmene ife timawaonera?