Kodi Nchifukwa Ninji Akupepesa?
LINGALIRO lakuti matchalitchi ayenera kulapa pa zolakwa zawo ndi kuwongola makhalidwe awo silachilendo. Dikishonale yachipembedzo yotchedwa Religioni e miti (Zipembedzo ndi Nthanthi), imafotokoza kuti lingaliro la tchalitchi choyambirira lokhazikitsa umodzi linasangalatsa anthu ambiri m’Nyengo Zapakati ndipo linawasonkhezera kupempha kuti awongolere zinthu.
Mu 1523, Martin Luther atasiya kugwirizana ndi Roma, Papa Adrian VI anayesa kuthetsa kusagwirizanako mwa kutumiza uthenga uwu kwa Diet (msonkhano wa akalonga) ya ku Nuremberg: “Tikudziŵa bwino kuti zinthu zoipitsitsa zimene zakhala zikuchitika kwa zaka zambiri zakhudza Holy See . . . Tidzayesetsa mwakhama kuwongolera zinthu zonse zochitika mu Roman Curia (mabungwe onse a Roma Katolika), kumene mwina zoipa zonsezi zinachokera.” Komabe, kuvomereza kumeneko sikunathandize kuthetsa magaŵanowo ndipo sikunathetsenso zoipa zimene zimachitika m’mabungwe oyang’aniridwa ndi papa.
Posachedwapa matchalitchi awaimba mlandu chifukwa chokhala chete nthaŵi ya Chipululutso cha Anazi. Iwo aimbidwanso mlandu chifukwa cholephera kuletsa mamembala awo kuti asamatenge mbali m’nkhondo. Mu 1941, panthaŵi ya Nkhondo Yadziko II, wansembe wotchedwa Primo Mazzolari anafunsa kuti: “Kodi nchifukwa chiyani Rome sinatsutse mkhalidwe wa kunyalanyaza ziphunzitso zachikatolika monga momwe inkachitira kale, ndiponso monga momwe yakhala ikuchitira, pankhani za ziphunzitso zosaopsa kwenikweni?” Ziphunzitso zosaopsa kwenikweni kusiyana ndi chiyani? Wansembeyo anali kunena za utundu woyambitsa nkhondo umene unali kusokoneza chitukuko panthaŵiyo.
Komabe, chenicheni nchakuti zipembedzo zayamba posachedwapa kuvomereza kulakwa. Mu 1832, poyankha anthu ena omwe analimbikira kunena kuti Tchalitchi cha Katolika ‘chisinthe zochita zake,’ Gregory XVI anati: “Nkupusa kwenikweni ndiponso nkwangozi kulingalira za ‘kukonzanso ndi kuwongolera zinthu’ kaamba ka chitetezo [cha tchalitchi] ndi kukula kwake, monga kuti chimalakwa.” Nanga bwanji za zolakwa zoonekeratu moti sangakane? Iwo anagwiritsira ntchito njira zosiyanasiyana kuti apereke zodzikhululukira. Mwachitsanzo, akatswiri ena a zaumulungu akhala akunena kuti tchalitchi nchoyera komanso nchochimwa. Tchalitchi chenichenicho amati nchoyera—chotetezeredwa ndi Mulungu ku uchimo. Komabe, mamembala ake ngochimwa. Choncho, pamene nkhanza zichitidwa m’dzina la tchalitchi, tchalitchi chenichenicho sichiyenera kuimbidwa mlandu, koma anthu a m’tchalitchimo ndiwo ayenera kuimbidwa mlandu. Kodi zimenezo nzanzeru? Osati kwa katswiri wa zaumulungu wa Roma Katolika Hans Küng, amene analemba kuti: “Palibe Tchalitchi changwiro chosakhudzidwa ndi zochita za anthu.” Iye anafotokoza kuti: “Palibe Tchalitchi chimene chinganene kuti chilibe machimo.”
Chigwirizano cha Akristu ndi Makhalidwe Abwino
Mwina mungafune kudziŵa zinthu zimene zapangitsa kuti matchalitchi alingalire zopepesa lerolino. Choyamba, Aprotestanti ndi a Orthodox anavomereza kuti ndiwo anayambitsa “magaŵano akale” a m’matchalitchi osiyanasiyana. Anachita zimenezi pamsonkhano wa chigwirizano cha Akristu wa mutu wakuti “Chikhulupiriro ndi Bata” umene unakachitikira ku Lausanne, Switzerland, mu 1927. Tchalitchi cha Roma Katolika pomalizira pake chinachitanso chimodzimodzi. Makamaka pambuyo pa Vatican II,a atsogoleri akuluakulu achipembedzo, kuphatikizapo apapa, akhala akupepesa kuposa kale lonse chifukwa chopangitsa magaŵano m’Dziko Lachikristu. Ncholinga chotani? Mwachionekere, akufuna kuti m’Dziko Lachikristu mukhale chigwirizano champhamvu. Wodziŵa mbiri ya Katolika Nicolino Sarale anafotokoza kuti “ntchito [ya John Paul II] ‘yovomereza kulakwa,’ ili ncholinga chake, ndicho kukhazikitsa chigwirizano cha Akristu onse.”
Komabe, zimenezi sizikukhudza chigwirizano cha Akristu chokha ayi. Lerolino, nkhani ya makhalidwe oipa kwambiri a Dziko Lachikristu njofala. “Chikatolika sichingangonyalanyaza mbiri yonse imeneyi,” anatero katswiri wa zaumulungu Hans Urs von Balthasar. “Tchalitchi chenichenicho cha papayo chachita kapena chalola kuchita zinthu zimene sitingazivomereze nkomwe lerolino.” Choncho, papa wakhazikitsa gulu loti “liulule nkhani zoipa za tchalitchi pofuna kuti . . . apepese.” Choncho, chifukwa china chopangitsa kuti matchalitchi akhale ofunitsitsa kuvomereza zolakwa zawo chikuoneka kuti nchikhumbo chakuti awongolere makhalidwe awo.
Mofananamo, pothirira ndemanga pankhani ya kupepesa kwa matchalitchi, wolemba mbiri Alberto Melloni, analemba kuti: “Kwenikweni, nthaŵi zina amapempha kuti asawaimbe mlandu.” Ndithudi, Tchalitchi cha Katolika chikuoneka kuti chikuyesetsa kupeŵa liwongo la machimo akale pofuna kuti anthu ayambenso kuchikhulupirira. Komabe, kunena zoona, tiyenera kunena kuti chikuoneka kuti chikudera nkhaŵa kwambiri za kukhala pamtendere ndi dziko osati ndi Mulungu.
Makhalidwe ameneŵa akutikumbutsa za Sauli, mfumu yoyamba ya Israyeli. (1 Samueli 15:1-12) Iye anachita tchimo lalikulu, ndipo pamene zimenezi zinadziŵika, poyamba anayesa kulungamitsa mlanduwo—kupeza chodzikhululukira—kwa Samueli, mneneri wokhulupirika wa Mulungu. (1 Samueli 15:13-21) Pomalizira pake, mfumuyo inavomereza pamaso pa Samueli niti: “Ndinachimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova.” (1 Samueli 15:24, 25) Inde, iye anavomereza kulakwa kwake. Koma mawu ake otsatira kwa Samueli akuvumbula zimene anali kulingalira: “Ndinachimwa, koma mundichitire ulemu tsopano pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Israyeli.” (1 Samueli 15:30) Mwachionekere, Sauli anali kudera nkhaŵa kwambiri za kaimidwe kake mu Israyeli osati kufunitsitsa kuyanjananso ndi Mulungu. Mzimu umenewu unapangitsa kuti Mulungu asakhululukire Sauliyo. Kodi mukuganiza kuti mzimu wofananawo udzachititsa Mulungu kukhululukira matchalitchi?
Si Onse Akugwirizana Nazo
Si onse amene amagwirizana ndi zoti matchalitchi azipepesa pamaso pa anthu onse. Mwachitsanzo, Aroma Katolika ambiri sasangalala pamene papa wawo apepesa chifukwa chochirikiza ukapolo kapena pamene abwezeretsa “ampatuko” monga Hus ndi Calvin. Malinga nkunena kwa ofalitsa nkhani za ku Vatican, chikalata chimene chinatumizidwa kwa akadinala chonena za lingaliro la “kuyesa chikumbumtima” pankhani za Chikatolika za zaka chikwi zapitazo chinatsutsidwa ndi akadinala amene anachita msonkhano wawo ndi papa m’June 1994. Komabe, pamene papa anafuna kuphatikizapo nkhani imeneyo m’kalata yake, kadinala wa ku Italy Giacomo Biffi anatulutsa kalata ya apasitala momwe iye anagogomezera kuti: “Tchalitchi chilibe tchimo.” Komabe, iye anavomereza kuti: “Kupepesa kaamba ka zolakwa zakale za tchalitchi . . . kungakometse mbiri yathu.”
“Kuvomereza machimo ndi imodzi mwa nkhani zodzetsa mkangano kwambiri m’Tchalitchi cha Katolika,” anatero wothirira ndemanga wa ku Vatican Luigi Accattoli. “Pamene papa avomereza machimo a amishonale, pali amishonale ena amene amakwiya nazo pazifukwa zawo zabwino.” Ndiponso, mtolankhani wa Roma Katolika analemba kuti: “Ngati papa akudziŵadi mbiri yochititsa mantha imeneyo ya Tchalitchi, nzovuta kumvetsa kuti iye tsopano akuvomereza kuti Tchalitchi chomwecho ndicho chingayambitse kuchirikiza ‘ufulu wachibadwidwe,’ kuti ndicho ‘mayi ndi mphunzitsi’ yekhayo amene angatsogoze anthu kuwaloŵetsa m’zaka chikwi zachitatu zoyembekezeredwa kwambiri zimenezo.”
Baibulo limachenjeza za kulapa kwachiphamaso kumene kumachitika chifukwa chokana kuchita manyazi zoipazo zitadziŵika. Kulapa kotero sikumapangitsa munthu wolapayo kusintha makhalidwe ake kwachikhalire. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 7:8-11.) Kulapa kumene kuli kwatanthauzo pamaso pa Mulungu kumatsagana ndi ‘zipatso zakuyenera kulapa mtima’—zimene zimachitira umboni kulapa koona mtima.—Luka 3:8.
Baibulo limanena kuti munthu amene alapa ndi kuvomereza machimo ake ayenera kusiya ntchito zoipa, kuleka kuzichita. (Miyambo 28:13) Kodi zimenezi zachitika? Chabwino, Tchalitchi cha Roma Katolika ndi matchalitchi ena atavomereza zolakwa zawo, kodi chinachitika nchiyani m’nkhondo zautundu zaposachedwapa chapakati pa Afirika ndiponso ku Eastern Europe, kumene “Akristu” miyandamiyanda anakhudzidwa? Kodi matchalitchiwo anagwira ntchito yolimbikitsa kuti pakhale mtendere? Kodi atsogoleri awo onse anatsutsa mogwirizana nkhanza zimene mamembala awo anali kuchita? Ayi. Kwenikweni, atumiki ena achipembedzo nawonso anapha nawo anthu!
Chiweruzo cha Mulungu
Ponena za kuvomereza kulakwa kwa papa kobwerezabwerezako, Kadinala Biffi anafunsa mokuluŵika kuti: “Kodi sikungakhale bwino kwa tonsefe kuti tiyembekeze chiweruzo cha dziko lonse kaamba ka machimo akale?” Ndithudi, chiweruzo cha mtundu wonse wa anthu chayandikira. Yehova Mulungu akudziŵa bwino nkhani zonse zoipa za m’mbiri ya chipembedzo. Posachedwapa, iye adzaŵerengera mlandu wa ochimwa onse. (Chivumbulutso 18:4-8) Pakali pano, kodi nzotheka kupeza mtundu wa kulambira wosadetsedwa ndi liwongo la mwazi, wopanda zambanda, ndi upandu wina wambiri umene wapangitsa kuti matchalitchi a m’Dziko Lachikristu apepese? Inde.
Kodi tingazichite motani zimenezo? Mwa kutsatira njira yonenedwa ndi Yesu Kristu yakuti: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.” Mbiri yakale, imene atsogoleri ena achipembedzo angafune kuti iiŵalike, imatithandiza kuzindikira osati awo okha amene Yesu anawatcha “aneneri onyenga” komanso awo amene abala “zipatso zokoma.” (Mateyu 7:15-20) Kodi ameneŵa ndi ayani? Tikukupemphani kuti mudzipezere nokha mwa kusanthula Baibulo ndi Mboni za Yehova. Pezani anthu amene akuyesetsadi kutsatira Mawu a Mulungu lerolino m’malo mofunafuna kutchuka m’dziko lapansi.—Machitidwe 17:11.
[Mawu a M’munsi]
a Bungwe la chigwirizano cha Akristu la 21 limene linakumana m’zigawo zinayi ku Rome kuyambira 1962-65.
[Chithunzi patsamba 5]
Matchalitchi akupepesa chifukwa cha nkhanza yonga iyi
[Mawu a Chithunzi]
The Complete Encyclopedia of Illustration/J. G. Heck