Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 2/1 tsamba 20-23
  • Kupereka Nsembe Zovomerezeka kwa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupereka Nsembe Zovomerezeka kwa Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusankha Njira Zosiyana
  • Uphungu wa Yehova Ndiponso Zimene Kaini Anachita
  • Phunziro kwa Ife
  • Anthu Aŵiri a Pachibale Amene Anali ndi Mitima Yosiyana
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kaini Anakwiya Mpaka Anapha M’bale Wake
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Mwana Wabwino, ndi Woipa
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 2/1 tsamba 20-23

Kupereka Nsembe Zovomerezeka kwa Yehova

PANTHAŴI inayake m’mbiri, chinthu china chodabwitsa chinaonekera panjira ya kummaŵa yoloŵera m’munda wa Edene.a Kumeneko, akerubi amphamvu anaimirira monga alonda, maonekedwe awo oopsawo akumasonyezeratu kuti wina asayese kuloŵa m’mundawo. Chinanso choopsa chinali lupanga loyaka moto limene linali kuzungulira, limene liyenera kuti usiku linaunika mitengo yapafupi ndi moto wofiira woopsawo. (Genesis 3:24) Pokhala zoopsa motero, anthu alionse amene ankaona zimenezo sanafike pafupi.

Mwina Kaini ndi Abele anafikapo pamalo amenewo nthaŵi zambiri. Pokhala ana a Adamu ndi Hava obadwira kunja kwa mundawo, iwo anali kungoyerekezera mmene zinalili kukhala m’Paradaiso, mmene makolo awo anali panthaŵi ina, malo okhala ndi zomera zokongola zothiriridwa bwino ndi zipatso zambiri ndi zakudya zamasamba. Tsopano mbali yochepa ya Edene imene inali kuoneka mwachionekere inali yosalimidwa ndiponso yodzaza ndi zitsamba.

Ndithudi Adamu ndi Hava anawafotokozera ana awo chifukwa chimene mundawo sunali kusamalidwa ndiponso chifukwa chimene anachotsedweramo. (Genesis 2:17; 3:6, 23) Kaini ndi Abele ayenera kuti anadandaula kwambiri! Mundawo anali kuuona koma osaloŵamo. Iwo anali pafupi kwambiri ndi Paradaiso komanso anali kutali kwambiri. Kupanda ungwiro kunawaipitsa, ndipo palibe zimene Kaini ndi Abele akanachita.

Unansi wa pakati pa makolo awo sukanawongolera zinthu. Poweruza Hava, Mulungu anati: “Udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.” (Genesis 3:16) Mongadi momwe ulosiwo unanenera, Adamu ayenera kuti tsopano anali kulamulira mkazi wake pa zilizonse, mwina osamuonanso ngati mnzake ndi mthandizi wake. Ndipo mwina Hava anali kudalira mwamunayu momkitsa. Ndemanga ina mpaka imafika pofotokoza ‘kukhumba’ kwakeku kukhala “chikhumbo chotsala pang’ono kukhala nthenda.”

Baibulo silinena kuti mavuto a muukwatiŵa anakhudza motani ulemu wa anyamatawo kwa makolo awo. Koma n’zoonekeratu kuti Adamu ndi Hava anapereka chitsanzo choipa kwa ana awo.

Kusankha Njira Zosiyana

M’kupita kwa nthaŵi, Abele anakhala mbusa ndipo Kaini anakhala mlimi. (Genesis 4:2) Poŵeta nkhosa zake, mosakayikira Abele anali ndi nthaŵi yaikulu yosinkhasinkha za ulosi wapaderawo umene unaperekedwa makolo ake asanachotsedwe mu Edene, wakuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15) Abele ayenera kuti anasinkhasinkha kuti, ‘Kodi lonjezo la Mulungu lonena za mbewu imene idzatswanya njoka lidzakwaniritsidwa motani, nanganso njokayi idzalalira motani chitende cha mbewuyi?’

Panthaŵi inayake, mwina Kaini ndi Abele atakula, aliyense wa iwo anapereka nsembe kwa Yehova. Popeza kuti Abele anali mbusa, n’zosadabwitsa kuti anapereka “mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe.” Koma Kaini anapereka “zipatso za nthaka.” Yehova analandira nsembe ya Abele, koma “sanayang’anira Kaini ndi nsembe yake.” (Genesis 4:3-5) Chifukwa?

Ena amati n’chifukwa chakuti nsembe ya Abele inali ya ‘mwana woyamba wa nkhosa zake,’ pamene ya Kaini inali ya “zipatso za nthaka” basi. Koma vuto silinali mkhalidwe wa zinthu zimene Kaini anapereka, popeza nkhaniyo imanena kuti Yehova anayang’anira ‘Abele ndi nsembe yake,’ ndipo sanayang’anira ‘Kaini ndi nsembe yake.’ Choncho Yehova anali kuyang’ana zimene zinali mumtima wa wolambirayo makamaka. Atatero, kodi anaonanji? Ahebri 11:4 amanena kuti Abele anapereka nsembe yake “ndi chikhulupiriro.” Choncho Kaini ayenera kuti analibe chikhulupiriro chimene chinapangitsa nsembe ya Abele kukhala yovomerezeka.

Pamenepa, chochititsa chidwi n’chakuti nsembe ya Abele inaloŵetsapo kukhetsa mwazi. Ayenera kuti anafika pozindikira molondola kuti lonjezo la Mulungu lonena za mbewu imene idzalaliridwa chitende idzaloŵetsapo kuperekedwa nsembe kwa moyo winawake. Choncho nsembe ya Abele mwina inali yochonderera chitetezo, ndipo inasonyeza chikhulupiriro chakuti Mulungu adzapereka nsembe yowawombola ku machimo panthaŵi yake.

Koma Kaini ayenera kuti sanaiganizire kwambiri nsembe imene anali kuperekayo. “Nsembe yake inali yongosonyeza kuvomereza kuti Mulungu ndiye mwini zonse,” anatero wina wothirira ndemanga pa Baibulo wa m’zaka za zana la 19. “Inasonyeza bwino lomwe kuti iye sanaone vuto lililonse lokhudza unansi wake ndi Mlengi wake, kapena kufunika kulikonse kwa kuvomereza tchimo kapena kufunika kwa chitetezo.”

Ndiponso, monga woyamba kubadwa, mwina Kaini anaganizanso modzikuza kuti iyeyo ndiye mbewu yolonjezedwa imene idzawononga Njoka, Satana. Mwinanso Hava naye anali ndi chiyembekezo chachikulu ngati chimenecho pa mwana wake woyambayo. (Genesis 4:1) Ndithudi, ngati ndizo zimene Kaini ndi Hava anali kuyembekezera, anali olakwa kwambiri.

Baibulo silinena mmene Yehova anasonyezera kuti wavomereza nsembe ya Abele. Ena amati inanyeketsedwa ndi moto wochokera kumwamba. Mulimonse mmene zinalili, atazindikira kuti nsembe yake yakanidwa, “Kaini . . . anakwiya kwambiri, niigwa nkhope yake.” (Genesis 4:5) Kaini anali pafupi kugwera m’mavuto.

Uphungu wa Yehova Ndiponso Zimene Kaini Anachita

Yehova anam’yankhula Kaini. Iye anam’funsa kuti: “Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako?” Umenewu unali mpata woti Kaini afufuze malingaliro ndi zolinga zake. “Ukachita zabwino,” anapitiriza motero Yehova, “sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzam’lamulira iye [“kodi sungaulamulire?,” NW].”​—Genesis 4:6, 7. (Onani bokosi patsamba 23.)

Kaini sanamvere. M’malo mwake, iye anatengera Abele kumunda namupha. Pambuyo pake, Yehova atafunsa kumene kunali Abele, Kaini anawonjezapo bodza pa tchimo lake. “Sindidziŵayi,” iye anayankha motero mwamwano. “Kodi ndine woyang’anira mphwanga?”​—Genesis 4:8, 9.

Nthaŵi zonse ziŵiri asanaphe Abele ndiponso atamupha, Kaini anakana ‘kuchita zabwino.’ Iye anasankha kulola uchimo kum’lamulira, ndipo pachifukwachi, Kaini anachotsedwa kumalo kumene kunali kukhala banja la anthu. “Chizindikiro,” mwinamwake lamulo, chinaikidwa kuti aliyense asabwezere imfa ya Abele mwa kupha Kaini.​—Genesis 4:15.

Kaini anapita namanga mzinda, nautcha dzina la mwana wake. N’zosadabwitsa kuti mbadwa zake zinadziŵika chifukwa cha chiwawa chawo. M’kupita kwa nthaŵi, mzere wa Kaini unatha pamene Chigumula cha Nowa chinasesa anthu onse osalungama.​—Genesis 4:17-24; 7:21-24.

Nkhani ya m’Baibulo yonena za Kaini ndi Abele sinasungidwe kuti tizingoiŵerenga ngati nthano wamba. M’malo mwake, ‘inalembedwa kutilangiza’ ndipo ‘ipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano.’ (Aroma 15:4; 2 Timoteo 3:16) Kodi tingaphunzireponji pankhaniyi?

Phunziro kwa Ife

Monga Kaini ndi Abele, Akristu lerolino akuuzidwa kuti apereke nsembe kwa Mulungu​—osati nsembe yeniyeniyo yowotcha, koma “nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” (Ahebri 13:15) Panopo zimenezi zikuchitika padziko lonse lapansi, pamene Mboni za Yehova zikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’mayiko oposa 230. (Mateyu 24:14) Kodi mukuchita nawo ntchitoyo? Ndiye mutha kukhala otsimikiza kuti “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.”​—Ahebri 6:10.

Monga momwe zinalili ndi nsembe ya Kaini ndi Abele, nsembe yanu siyesedwa mwa maonekedwe ake akunja​—mwachitsanzo, mwa kungoyang’ana chiŵerengero cha maola amene munathera mu utumiki. Yehova amayang’ana m’kati mwenimweni. Yeremiya 17:10 amanena kuti iye ‘asanthula mtima’ ngakhalenso ‘kuyesa imso’​—malingaliro a pansi penipeni pa mtima ndi zisonkhezero za umunthu wa munthu. Choncho nkhani yaikulu ndiyo cholinga, osati kuchuluka. Ndithudi, kaya nsembe ikhale yaikulu kapena yaing’ono, iyo imakhala yom’kondweretsa Mulungu ngati iperekedwa ndi mtima wosonkhezeredwa ndi chikondi.​—Yerekezerani Marko 12:41-44 ndi 14:3-9.

Komanso, tiyenera kudziŵa kuti Yehova salandira nsembe zopuŵala, monga momwe sanalandirire nsembe ya Kaini yosachokera pansi pa mtima. (Malaki 1:8, 13) Yehova amafuna kuti mum’patse zabwino koposa, kuti mum’tumikire ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, nzeru zanu zonse, ndi mphamvu zanu zonse. (Marko 12:30) Kodi mukuchita zimenezo? Ndiye kuti muli ndi chifukwa chabwino chokhalira wokondwera ndi nsembe yanu. Paulo analemba kuti: “Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.”​—Agalatiya 6:4.

Kaini ndi Abele analeredwa pamodzi. Koma nthaŵi ndi mikhalidwe inapatsa aliyense wa iwo mpata wa kukhala ndi mikhalidwe yosiyana aliyense payekha. Maganizo a Kaini pang’onompang’ono anadzaza nsanje, udani, ndi ukali.

Komabe, Abele akukumbukiridwa ndi Mulungu kuti anali munthu wolungama. (Mateyu 23:35) Kufunitsitsa kwake kuti akondweretse Mulungu zivute zitani kunapangitsa Abele kukhala wabwino mosiyana ndi anthu osayamikira a m’banja mwake​—Adamu, Hava, ndi Kaini. Baibulo limatiuza kuti ngakhale kuti Abele anamwalira, iye “alankhulabe.” Utumiki wake wokhulupirika kwa Mulungu uli mbali ya mbiri yachikhalire ya m’Baibulo. Tiyeni titsatire chitsanzo cha Abele mwa kupitiriza kupereka nsembe zovomerezeka kwa Mulungu.​—Ahebri 11:4.

[Mawu a M’munsi]

a Ena amanena kuti munda wa Edene unali m’dera lamapiri chakummaŵa kwa dziko lamakono la Turkey.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 23]

Chitsanzo cha Aphungu Achikristu

UKWIYIRANJI? Yagweranji nkhope yako?” Pofunsa mafunso ameneŵa, Yehova anakambirana naye mokoma mtima Kaini. Iye sanakakamize Kaini kuti asinthe, popeza kuti Kaini anali ndi ufulu wa kudzisankhira. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 30:19.) Komabe, Yehova sanazengereze kulongosola zotsatirapo za njira yachitayiko ya Kaini. Anam’chenjeza Kaini kuti: “Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake.”​—Genesis 4:​6, 7.

Chochititsa chidwi n’chakuti ngakhale kuti anam’dzudzula mwamphamvu chotero, Yehova sanaone Kaini ngati munthu wosathandizika. M’malo mwake, anauza Kaini za madalitso amene angakhale nawo atasintha njira zake, ndipo anasonyeza chidaliro chakuti Kaini atha kuthetsa vuto lake atafuna kutero. “Ukachita zabwino,” anatero Yehova, “sudzalandiridwa kodi?” Anafunsanso Kaini za mkwiyo wake wofuna kupha nawo munthu umenewo kuti: “Kodi sungaulamulire?”

Lerolino, akulu a mumpingo wachikristu ayenera kutsanzira chitsanzo cha Yehova. Monga momwe 2 Timoteo 4:2 amanenera, nthaŵi zina iwo ayenera ‘kutsutsa’ ndi ‘kudzudzula,’ kusonyeza mosapita m’mbali zotsatirapo za njira yachitayiko ya munthu wolakwa. Panthaŵi imodzimodziyo, akulu ayenera ‘kuchenjeza.’ Liwu lachigirikilo pa·ra·ka·leʹo limatanthauza “kulimbikitsa.” “Uphunguwo sukhala wopyoza, waukali, kapena wosuliza,” ikutero Theological Dictionary of the New Testament. “Popeza kuti chitonthozo ndicho tanthauzo lake lina, ndiye kuti uphunguwo umakhaladi wotonthoza.”

Komanso, liwu lina lachigiriki lofanana nalo, pa·raʹkle·tos, lingatanthauze mthandizi kapena woimira munthu wina pamlandu. Choncho, ngakhale pamene akulu apereka uphungu wosapita m’mbali, iwo ayenera kukumbukira kuti ndi othandiza​—osati adani​—​a munthu wofunikira uphunguyo. Monga Yehova, akulu ayenera kukhala n’chiyembekezo chabwino, akumasonyeza chidaliro chakuti munthu amene akum’patsa uphunguyo atha kulithetsa vutolo.​—Yerekezerani ndi Agalatiya 6:1.

Koma zonse zitachitidwa, zili kwa munthuyo kutsatira uphunguwo. (Agalatiya 6:5; Afilipi 2:12) Aphungu angaone kuti ena samvera machenjezo awo, monga momwe Kaini anasankhira kunyalanyaza uphungu wa Mlengi weniweniyo. Komabe, pamene akulu atsanzira Yehova, Chitsanzo changwiro cha aphungu achikristu, iwo angakhale otsimikiza kuti achita zimene ayenera kuchita.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena