Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w07 10/1 tsamba 8-11
  • Moyo Wawo Unali Wovuta Koma “Anamanga Nyumba ya Isiraeli”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo Wawo Unali Wovuta Koma “Anamanga Nyumba ya Isiraeli”
  • Nsanja ya Olonda—2007
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Anakumana ndi Mlendo Pachitsime
  • Banja Losasangalala
  • Ana a Rakele
  • Imfa Ndiponso Zimene Anasiya
  • Yakobo ali ndi Banja Lalikulu
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kufuna kukondedwa
    Galamukani!—2006
  • Yakobo Amka ku Harana
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yakobo Anaona Zinthu Zauzimu Kukhala Zofunika
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2007
w07 10/1 tsamba 8-11

Moyo Wawo Unali Wovuta Koma “Anamanga Nyumba ya Isiraeli”

KUNJA kutayamba kucha, Leya anadziwa kuti amuzindikira. Yakobo anali atatsala pang’ono kutulukira kuti mkazi yemwe anali naye sanali Rakele, koma anali mkulu wake, Leya. Atauzidwa ndi bambo ake, Leya yemwe mwina anadziphimba kwambiri, anakagona pa bedi limene linakonzedwera Yakobo ndi Rakele kuti agone pambuyo pa mwambo wa ukwati wawo.

Taganizani mmene Yakobo anamvera atadziwa kuti wapusitsidwa. Iye anakwiya ndipo anakangana ndi bambo a Leya, a Labani. Leya ayenera kuti anali kuganizira kwambiri za chinyengo chimene iyeyo ndi bambo ake anachita ndi zotsatira zake. Nkhani ya Leya ndi Rakele ndi imodzi mwa nkhani zofunika kwambiri m’Baibulo. Nkhaniyi imasonyezanso kufunika kokhala ndi mkazi mmodzi ndiponso kukhala wokhulupirika muukwati.

Anakumana ndi Mlendo Pachitsime

Zaka 7 zinali zitadutsa pamene Rakele anakumana ndi mlendo pachitsime n’kuthamangira kunyumba kukauza bambo ake za mlendoyo, yemwe anati ndi m’bale wawo. Iye anali msuweni wake, Yakobo, mwana wa mchemwali wa Labani ndipo anali wolambira Yehova. Patapita mwezi umodzi, Yakobo anapempha kugwira ntchito kwa Labani zaka 7 kuti akwatire Rakele. Labani anavomereza zimenezi ataona kuti Yakobo anali wolimbikira ntchito ndiponso chifukwa choti zinali zofala mumtundu wawo kuti anthu azikwatirana pachibale.​—Genesis 29:1-19.

Yakobo sanangotengeka maganizo koma anakondadi Rakele. Zaka 7 zimene iwo anakhala pachibwenzi ‘zidamuonekera Yakobo ngati masiku owerengeka chifukwa cha chikondi chimene anam’konda nacho Rakele.’ (Genesis 29:20) Rakele ayenera kuti anali ndi makhalidwe abwino. Tikutero chifukwa Yakobo anam’konda kwambiri mpaka pamene Rakeleyo anafa.

Kodi Leya nayenso ankafuna kukwatiwa ndi munthu yemwe ankalambira Yehova mokhulupirika? Baibulo silitiuza. Koma limatiuza zimene Labani ankafuna pa nkhani imeneyi. Panthawi yoti Rakele akwatiwe, Labani anapanga phwando la ukwati. Baibulo limanena kuti madzulo ake, Labani anatenga Leya n’kupita naye kwa Yakobo n’cholinga choti Yakoboyo agone naye.​—Genesis 29:23.

Kodi Leya anagwirizana nazo kuti achitire Yakobo zachinyengo? Kapena kodi anangochita zimenezi pomvera bambo ake? Kodi Rakele anali kuti nthawi imeneyo? Kodi ankadziwa zimene zinali kuchitika? Ngati ankadziwa, kodi anamva bwanji m’mtima mwake? Kodi bambo ake anali wovuta moti iye sakanawakanira? Baibulo silitipatsa mayankho a mafunso amenewa. Kaya Rakele ndi Leya anamva bwanji, zimene tikudziwa n’zoti Yakobo anakwiya kwambiri atatulukira zimenezi. Ndipotu, Yakobo anakangana ndi Labani osati ana akewo. Yakobo anati: “Kodi sindinakutumikira iwe chifukwa cha Rakele? Wandinyenga ine bwanji?” Labani anayankha kuti: “Satero . . . , kupatsa wamng’ono asanapatse wamkulu. Umalize sabata lake la uyu, ndipo ndidzakupatsa uyonso chifukwa cha utumiki umene udzanditumikirawo kuwonjezera zaka zina zisanu ndi ziwiri.” (Genesis 29:25-27) Motero, Yakobo anakakamizidwa kuchita mitala, ndipo zimenezi zinayambitsa nsanje yoopsa m’banja lake.

Banja Losasangalala

Yakobo ankakonda Rakele. Mulungu ataona kuti poyerekezera ndi Rakele, Yakobo “anamuda” Leya, anatsegula m’mimba mwake koma Rakele anali wosaberekabe. Leya sanangofuna mwana basi, anafunanso kuti Yakobo azimukonda. Ndipo poona kuti Yakobo ankakonda Rakele, iye anakhumudwa kwambiri. Leya atabereka mwana wake wamwamuna woyamba, Rubeni, dzina lotanthauza “Onani, Mwana Wamwamuna,” anaganiza kuti Yakobo ayamba kumukonda. Leya anali ndi chifukwa chabwino popatsa mwana wake dzina limeneli. Anati: “Chifukwa kuti tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.” Ngakhale kuti Leya anabereka mwanayu ndiponso mwana wina wamwamuna, zimenezi sizinachititse Yakobo kum’konda. Leya anatcha mwana wachiwiriyo Simeoni, dzina lotanthauza kuti “Kumva.” Anaganiza kuti: “Chifukwa anamva Yehova kuti anandida ine, anandipatsa ine mwana wamwamuna uyunso.”​—Genesis 29:30-33.

Mawu oti “anamva Yehova” akusonyeza kuti Leya anapemphera za vuto lake. Choncho, ayenera kuti iye anali mkazi wokhulupirika. Koma anavutikabe maganizo ngakhale pamene anabereka mwana wake wamwamuna wachitatu, Levi. Leya anafotokoza chifukwa chimene anam’patsira dzina lotanthauza “Kuphatika” pamene anati: “Tsopano lino mwamuna wanga adzadziphatika kwa ine chifukwa ndam’balira iye ana aamuna atatu.” Koma zikuoneka kuti Yakobo sanakondebe Leya. Ndipo mwina Leya anazindikira kuti Yakobo sadzam’kondanso, chifukwa dzina limene anapatsa mwana wake wachinayi linalibe tanthauzo lokhudza ubwenzi wake ndi Yakobo. M’malo mwake, dzina limene anapatsa mwanayo lakuti Yuda, linangokhala loyamikira Mulungu. Dzinali limatanthauza “Kuyamikira,” kapena “Kuyamikiridwa.” Leya anangonena kuti: “Tsopano ndidzam’yamikira Yehova.”​—Genesis 29:34, 35.

Mofanana ndi Leya, Rakele nayenso anali wosasangalala. Iye anachonderera Yakobo kuti: “Ndipatse ana ndingafe.” (Genesis 30:1) Yakobo ankakonda Rakele koma Rakeleyo ankafunanso ana. Leya anali ndi ana koma ankafunanso kukondedwa. Aliyense ankasirira chimene mnzake anali nacho, ndipo onse awiri anali osasangalala. Onse ankakonda Yakobo ndipo ankafuna kum’berekera ana. Choncho, aliyense ankachitira mnzake nsanje. Ndithudi, banjali linali ndi moyo wovuta kwambiri.

Ana a Rakele

Nthawi imeneyo, munthu akakhala wosabereka ankaonedwa ngati wotembereredwa. Mulungu analonjeza Abulahamu, Isake, ndi Yakobo kuti banja lawo ndi limene lidzabereka “mbewu” ndipo kudzera mwa mbewuyo mabanja onse adzadalitsidwa. (Genesis 26:4; 28:14) Rakele analibe mwana. Koma Yakobo ankadziwa kuti ndi Mulungu yekha amene angapatse Rakele ana kuti madalitsowo adzerenso mwa iye. Rakele sanathe kudikira. Iye anati: “Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye.”​—Genesis 30:2, 3.

Mwina ife sitingamvetse zimene Rakele anachita. Koma mapangano akale onena za ukwati, omwe anapezedwa ku Near East, amasonyeza kuti zinali zofala kuti mkazi wosabereka apatse mwamuna wake mdzakazi kuti am’berekere mwana.a (Genesis 16:1-3) Ndipo nthawi zina, ana a mdzakaziyo ankatengedwa kuti ndi a mkazi wosaberekayo.

Pamene Biliha anabereka mwana wamwamuna, Rakele ananena mosangalala kuti: “Mulungu wandiweruzira ine, namva mawu anga, nandipatsa ine mwana.” Mwanayo anam’patsa dzina lakuti Dani, limene limatanthauza kuti “Woweruza.” Rakele nayenso anali atapemphera za vuto lake. Pamene Biliha anabereka mwana wake wachiwiri dzina lake Nafitali, limene limatanthauza “Ndalimbana,” Rakele anati: “Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkulu wanga, ndipo ndapambana.” Maina a anawa amasonyeza kuti panali kupikisana pakati pa akazi awiriwa.​—Genesis 30:5-8.

Mwina Rakele ankaganiza kuti akuchita zogwirizana ndi mapemphero ake popereka Biliha kwa Yakobo. Komatu, imeneyi siinali njira ya Mulungu yom’patsira ana. Zimenezi zikutiphunzitsa kuti tikapemphera kwa Yehova, tizimudikira kuti ayankhe. Iye angayankhe mapemphero athu m’njira yosayembekezereka ndiponso panthawi yomwe sitikuyembekezera.

Potsatira zimene Rakele anachita, Leyanso anapatsa Yakobo mdzakazi wake, Zilipa, yemwe anabereka Gadi ndiponso Aseri.​—Genesis 30:9-13.

Zimene zinachitika pamene mwana wa Leya, Rubeni, anapeza zipatso zomwe iwo ankakhulupirira kuti ndi mankhwala othandiza kubereka, zimasonyeza bwino kusagwirizana komwe kunalipo pakati pa Rakele ndi Leya. Rakele anapempha zipatsozo koma Leya anayankha mokwiya kuti: “Kodi m’pachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga?” Ena amati mawu amenewa amasonyeza kuti Yakobo ankakhala kwambiri ndi Rakele kuposa Leya. Mwina Rakele anamvetsa kudandaula kwa Leya, chifukwa anayankha kuti: “Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako.” Choncho, Yakobo atabwera kunyumba madzulo, Leya anamuuza kuti: “Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipirira iwe ndi mankhwala a mwana wanga.”​—Genesis 30:15, 16.

Leya anabereka mwana wachisanu dzina lake Isakara. Anaberekanso wina dzina lake Zebuloni. Kenako Leya anati: “Tsopano mwamuna wanga adzakhala ndi ine, chifukwa ndam’balira iye ana aamuna asanu ndi mmodzi.”b​—Genesis 30:17-20.

Zipatso zija sizinathandize. Patapita zaka 6 ali m’banja, Rakele anabereka Yosefe chifukwa choti Yehova ‘anam’kumbukira’ ndipo anayankha mapemphero ake. Apa m’pamene iye anatha kunena kuti: “Mulungu wachotsa manyazi anga.”​—Genesis 30:22-24.

Imfa Ndiponso Zimene Anasiya

Rakele anamwalira pobereka mwana wake wachiwiri, Benjamini. Yakobo anakonda kwambiri Rakele ndi ana ake awiri amene anabereka. Patadutsa zaka zambiri ndiponso atatsala pang’ono kufa, Yakobo anakumbukira imfa yosayembekezereka ya mkazi wake wokondedwa, Rakele. (Genesis 30:1; 35:16-19; 48:7) Koma ponena za imfa ya Leya, timangodziwa zoti Yakobo anamuika m’phanga lomwe anafuna kuti iyenso adzaikidwe.​—Genesis 49:29-32.

Atakalamba, Yakobo anavomereza kuti moyo wake ndiponso ukwati wake, unali wamavuto. (Genesis 47:9) Mosakayikira, moyo wa Leya ndi Rakele unalinso wamavuto. Zimene anakumana nazo muukwati wawo zimasonyeza kuipa kwa mitala ndiponso chifukwa chake Yehova analamula kuti mwamuna azikhala ndi mkazi mmodzi. (Mateyo 19:4-8; 1 Timoteyo 3:2, 12) Ngati mwamuna kapena mkazi angayambe kukondana ndi munthu wina, zotsatirapo zake zimakhala nsanje. Chimenechi ndi chimodzi mwa zifukwa zimene Mulungu amaletsera dama ndiponso chigololo.​—1 Akorinto 6:18; Aheberi 13:4.

Ngakhale kuti moyo wawo unali wovuta chonchi, Mulungu anapitiriza kuwagwiritsa ntchito, ndipo akupitirizabe kugwiritsa ntchito amuna ndi akazi opanda ungwiro koma okhulupirika pokwaniritsa cholinga chake. Mofanana ndi tonsefe, Rakele ndi Leya ankalakwitsa zinthu zina. Komabe, kudzera mwa akazi awiriwa Yehova anayamba kukwaniritsa zimene analonjeza Abulahamu. N’chifukwa chake timati Rakele ndi Leya “anamanga nyumba ya Isiraeli.”​—Rute 4:11.

[Mawu a M’munsi]

a Pangano lina limene linapezedwa ku Nuzi, m’dziko la Iraq linati: “Kelim-ninu tam’pereka kwa Shennima kuti akhale mkazi wake. . . . Ngati Kelim-ninu sadzabereka [ana], Kelim-ninu adzakatenge mkazi [mdzakazi] ku dera la Lullu kuti akhale mkazi wa Shennima.”

b Mwana wina wa Leya dzina lake Dina, ndiye mwana wamkazi yekhayo wa Yakobo amene tikudziwa dzina lake.​—Genesis 30:21; 46:7.

[Chithunzi patsamba 9]

Leya ndi Rakele ankasirira chimene wina anali nacho, ndipo onse awiri anali osasangalala

[Chithunzi patsamba 10]

Mtundu wa Isiraeli unachokera kwa ana aamuna 12 a Yakobo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena